Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 8/1 tsamba 4-7
  • Atumiki Achichepere m’Nthaŵi za Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Atumiki Achichepere m’Nthaŵi za Baibulo
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mose ndi Ena Okhulupirika mu Uchichepere
  • Davide, Yosiya, ndi Yeremiya
  • Danieli, Yesu, ndi Timoteo
  • Kodi ndi Mtsogolo Mwamtundu Wanji Mmene Inu Mumafuna?
  • Achichepere Achimwemwe mu Utumiki wa Yehova
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Phunzirani Njira za Yehova
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Mumamudziwa Bwino Yehova?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Kutumikira Mulungu “M’masiku Otsiriza”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 8/1 tsamba 4-7

Atumiki Achichepere m’Nthaŵi za Baibulo

BAIBULO limasimba za achichepere abwino kwambiri omwe anatenga utumiki wawo kwa Mulungu mosamalitsa ndi omwe anadalitsidwa molemera kaamba ka kuchita chimenecho. Kaya tiri achichepere kapena okalamba ndi a imvi, zitsanzo zabwino za m’Baibulo zimenezi zingapereke chilimbikitso chachikulu.

Yosefe anali ndi zaka 17 zokha zakubadwa pamene anagulitsidwa mu ukapolo mu Igupto. Kumeneko, kutali ndi banja lake ndipo mosaonana ndi omwe anamdziŵa, Yosefe anatsimikizira umphumphu wake. Pamene mkazi wa Potifara anayesera kumkopa Yosefe, iye anati: ‘Nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?’ Ngakhale pamaso pa Farao wamkulu, mfumu yamphamvu koposa ya m’tsiku lake, Yosefe anatenga mwaŵi wa kupereka ulemerero kwa Mulungu kaamba ka kumasulira maloto a Farao. Iye anadalitsidwa molemera. Mulungu anamgwiritsira ntchito kupulumutsa ponse paŵiri Aigupto ndi banja lake ku imfa yobweretsedwa ndi njala ndi kubweretsa atate ake, Yakobo, ndi banja lake ku Igupto.​—Genesis 37:2; 39:7-9; 41:15, 16, 32.

Mose ndi Ena Okhulupirika mu Uchichepere

Mwana wamkazi wa Farao anatenga Mose kukhala mwana wake, koma amake Mose ndi atate wake anali okhoza kumphunzitsa ponena za Mulungu wowona. Baibulo limati pamene anakula, Mose ‘anakana kutchedwa mwana wake wa mwana wamkazi wa Farao; nasankhula kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthaŵi.’ Mulungu anagwiritsira ntchito Mose kutulutsa anthu ake mu Igupto, kulandira Chilamulo pa Sinai, ndikulemba mbali yaikulu ya Baibulo. Mosasamala kanthu za msinkhu wanu, kodi mukukulitsa chitsimikiziro cha kutumikira Mulungu monga mmene anachitira Mose?​—Ahebri 11:23-29; Eksodo 2:1-10.

Malemba amatisimbira za “ana ang’ono” omwe anamvetsera limodzi ndi mtundu wonsewo pamene Chilamulo cha Mulungu chinkaŵerengedwa kwa Israyeli. (Deuteronomo 31:10-13) ‘Yense wakumva ndi kuzindikira’ anaima ‘kuyambira mbanda kucha kufikira msana’ kumvetsera Chilamulo m’masiku a Nehemiya. (Nehemiya 8:1-8) Ngakhale ngati ana ang’onowo sanamvetsetse chirichonse, iwo akayamikira kuti anayenera kukonda, kulambira, ndi kumvera Yehova Mulungu. Mosasamala kanthu za msinkhu wanu, kodi mwamvetsera misonkhano yaikulu ndi misonkhano kumene Mawu a Mulungu anafotokozedwa? Kodi mwaphunzira kufunika kwa kumumvera iye, monga mmene anachitira Aisrayeli achicheperewo?

Davide, Yosiya, ndi Yeremiya

Mulungu anasankha Davide, wam’ng’ono wa abale asanu ndi atatu, kaamba ka utumiki wapadera ndipo anati ponena za iye: ‘Ndapeza Davide, mwana wa Jese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse.’ Mulungu anamsankha iye kukhala “mbusa” wa anthu ake, ndipo Davide anachita utumiki umenewo, pamene ankatsimikizira chikondi chake kaamba ka Yehova kwa zaka zambiri. Iye analemba Masalmo oposa 70 ndipo anakhala kholo la Yesu Kristu. Kaya ndinu achichepere kapena achikulire, kodi mumayamikira njira za Mulungu, ndipo kodi mumachita zinthu zimene iye amakonda, monga mmene anachitira Davide?​—Machitidwe 13:22; Salmo 78:70, 71, NW; 1 Samueli 16:10, 11; Luka 3:23, 31.

Yosiya anakhala mfumu pamene anali ndi zaka zisanu ndi zitatu zokha zakubadwa. Pamene anali pafupifupi zaka 15, ‘akali mnyamata, anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lake.’ Asanafike zaka 20, Yosiya anayamba ndawala yolimbana ndi kulambira konyenga. Pambuyo pake, iye anakonzanso kachisi ndipo anabwezeretsa kulambira kowona m’dzikomo. Timaŵerenga motere: ‘Masiku ake onse iwo sanapambuka kusamtsata Yehova Mulungu wa makolo awo.’ Tonsefe sitingakhale mfumu mofanana ndi Yosiya, koma tingatumikire Mulungu ndi kuima nji molimbana ndi kulambira konyenga, mosasamala kanthu za msinkhu wathu.​—2 Mbiri 34:3, 8, 33.

Mulungu wamphamvuyonse anauza Yeremiya motere: “Ndisanakulenge iwe m’mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu.” Yeremiya anakana motere kuti iye anali wam’ng’ono kwenikweni kukhala mneneri: “Ha, Ambuye Mulungu! taonani, sindithai kunena pakuti ndiri mwana.” Yehova anayankha motere: ‘Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza.’ Kwa zaka zoposa 40 Yeremiya anachita zimenezo, ndipo ngakhale pamene iye anafuna kuleka, iye sanakhoze kuleka. Mawu a Mulungu anatsimikizira kukhala “ngati moto wotentha wotsekedwa m’mafupa [ake].” Iye anafunikira kulankhula! Mosasamala kanthu ndi msinkhu wanu, kodi mukukulitsa mtundu wachikhulupiriro umene Yeremiya anali nawo, kupita patsogolo mu utumiki wa Mulungu m’njira imene iye anachitira?​—Yeremiya 1:4-8; 20:9.

Danieli, Yesu, ndi Timoteo

Kodi simunamvepo za Danieli? Iye angakhale anali ndi zaka zosakwanira 20 pamene anatengedwa limodzi ndi “ana” ena monga akapolo m’bwalo la Nebukadinezara wamphamvu, mfumu ya Babulo. Mosasamala kanthu zauchichepere wa Danieli, iye anasankhapo kumvera Mulungu. Danieli ndi atsamwali ake anakana kudziipitsa okha ndi zakudya zomwe zingakhale zidapotoza Chilamulo cha Mulungu kapena kuipitsidwa ndi miyambo yachikunja. Kwa zaka zoposa 80, Danieli sanafooke, akumasunga umphumphu wake ku mlingo wakukana kuleka kupemphera kwa Mulungu, ngakhale kuti ichi chikatulukapo kuponyedwa kwake kwa mikango. Kodi mumalingalira utumiki ndi mapemphero anu kwa Mulungu kukhala ofunika chotero? Muyenera kutero.​—Danieli 1:3, 4, 8; 6:10, 16, 22.

Pa msinkhu wa zaka 12, Yesu anapezedwa alikhale pakati pa aphunzitsi achipembedzo pakachisi m’Yerusalemu, ‘namva iwo nawafunsanso mafunso. Ndipo onse amene anamva [Yesu wachichepereyo] anadabwa ndi chidziwitso chake, ndi mayankho ake.’ Kodi kukambirana Malemba ndi akulu pakachisi kukanakusangalatsani monga mmene kunachitira Yesu? Kodi ena angadabwe ndi chidziŵitso chanu ndi mayankho anu? Lerolino, Mboni zambiri zachichepere zomwe zimaphunzira, kumvetsera mosamalitsa, ndi kukhalamo ndi phande m’misonkhano Yachikristu ziri ndi chidziŵitso cha Malemba chomwe chimadabwitsa achikulire.​—Luka 2:42, 46, 47.

Kodi ndinu ofanana ndi Timoteo, amene monga mwana anaphunzitsidwa “malembo opatulika”? Pamene anali wachichepere, Timoteo ‘anamchitira umboni wabwino abale’ pafupifupi m’mipingo iŵiri. Mtumwi Paulo anasankha Timoteo kuyenda naye, osati kungokhala monga wonyamula katundu, koma kuthandiza Paulo m’kuphunzitsa ena. Kodi inuyo mungasankhidwe kaamba ka mwaŵi woterewu? Kodi ntchito yanu ‘yachitiridwa umboni wabwino,’ osati kokha mu mpingo wanu komanso mu ina?​—2 Timoteo 3:15; Machitidwe 16:1-4.

Kodi ndi Mtsogolo Mwamtundu Wanji Mmene Inu Mumafuna?

Kodi nkothekera kwa achichepere lerolino kukhala okhulupirika mofanana ndi Yosefe, Mose, Davide, ndi ena? Inde, nkothekera. Zowona, achichepere ambiri ngwosangalatsidwa ndi kukhala ndi nthaŵi yabwino yokha. Koma ena akugwiritsira ntchito uchichepere wawo mwanzeru, kudziŵa Mulungu ndi chifuniro chake kwa iwo. Awa amakwaniritsa ulosi uwu wa Baibulo: ‘Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu. . . . Muli nawo mame a ubwana wanu.’​—Salmo 110:3.

Achichepere abwino otere amasonyeza nzeru yoposa zaka zawo, popeza kuti Mulungu angawathandize kupanga kupita patsogolo pa moyo wa tsopano lino limodzinso ndi kuwapatsa mtsogolo mwaulemerero m’dziko latsopano likudzalo. (1 Timoteo 4:8) Komabe, kodi ndimotani mmene wachichepere wamakono angakulitsire chikhulupiriro chofanana ndi achichepere otchulidwa m’Baibulo? Ngati inu mukufuna kudziŵa, tikukuitanani kuŵerenga nkhani yakuti “Achichepere Achimwemwe mu Utumiki wa Yehova,” yoyambira pa tsamba 10 ya magazine ano.

[Zithunzi patsamba 5]

Mose wachichepere sananyengedwe ndi chuma cha mu Igupto

Davide wachichepere wa pamtima pa Yehova

[Zithunzi patsamba 6]

Ngakhale kuti Yeremiya anadzimva kuti anali “mwana,” iye analalikira molimba mtima uthenga wachilendo

Pa msinkhu wa zaka 12, Yesu anadabwitsa akulu ake ndi chidziŵitso chake cha Mawu a Mulungu

[Chithunzi patsamba 7]

Mu Israyeli ngakhale ana ang’ono anamvetsera pamene Chilamulo cha Mulungu chinaŵerengedwa. Kodi inu mumatero?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena