Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 8/1 tsamba 10-14
  • Achichepere Achimwemwe mu Utumiki wa Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achichepere Achimwemwe mu Utumiki wa Yehova
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chikhulupiriro Chanuchanu
  • Pezani Chidziŵitso
  • Kulani ndi Kuyamikira
  • Pitani Patsogolo m’Kutumikira Mulungu
  • Achinyamata, Khalani ndi Mtima Wokonda Kwambiri Kutumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Ndine Wokonzeka Kubatizidwa?
    Galamukani!—1990
  • Achinyamata, Sankhani Kutumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kodi Achinyamata Ayenera Kubatizidwa?
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 8/1 tsamba 10-14

Achichepere Achimwemwe mu Utumiki wa Yehova

“Ngakhale mwana adziŵika ndi zochita zake, ngati mkhalidwe wake uli woyera ngakhale wolungama.”​—MIYAMBO 20:11, “New International Version.”

1. Kodi ndi zinthu zapadera zina ziti zimene Baibulo limanena ponena za Samueli?

SAMUELI wachichepere angakhale anali ndi zaka zitatu kapena zisanu zokha zakubadwa pamene anayamba ‘kutumikira’ paguwa lansembe la Yehova mu Silo. Imodzi ya ntchito zake inali ‘kutsegula zitseko za nyumba ya Yehova.’ Baibulo limati “Samueli anakulakula, ndipo Yehova ndi anthu omwe anamkomera mtima.” Atakula, iye anabwezeretsa Israyeli ku kulambira kowona. Iye anatumikira Mulungu ‘masiku onse a moyo wake.’ Ngakhale pamene iye anali “wokalamba waimvi” iye adasonkhezerabe anthu kuti “mumuope Yehova, ndi kumtumikira koona.” Kodi sichikakhala chabwino kwambiri ngati anthu anali okhoza kunena zinthu zabwinozi ponena za inu monga mmene Baibulo limazinenera ponena za Samueli?​—1 Samueli 1:24; 2:18, 26; 3:15; 7:2-4, 15; 12:2, 24.

2. Kodi ana amaphunziranji pa misonkhano ya anthu a Yehova lerolino?

2 Ngati ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova kapena ngati mumapezeka pa misonkhano yawo Yachikristu, penyetsetsani m’Nyumba Yaufumu mmene phunziro iri limaphunziridwa. Inu mudzawona anthu a misinkhu yonse. Mwinamwake ali anthu omwe ali kale ‘okalamba a imvi.’ Palinso makolo, achichepere, ana ang’ono, ndipo ngakhale makanda ofukatiridwa. Kodi ang’onowa ayamba kale kuphunzira? Inde. Tangofunsani anthu omwe anabweretsedwa ku misonkhanoyi pamene adali aang’ono. Iwo adzakuuzani moona mtima kuti kuyambira pa msinkhu wawo wa zaka zachichepere, iwo adaphuznira kulemekeza Mulungu, kukonda anthu ake, ndi kuyamikira malo kumene iye amalambiridwirako. Pamene nthaŵi ipita, ana amaphunzira zowonadi zodabwitsa. Achichepere ambiri, pambuyo pa kupeza chidziŵitso ndi kuzindikira, amakhala mbali ya ‘anyamata ndi anamwali, okalamba ndi ana’ amene wamasalmo anawachonderera ‘kulemekeza dzina la Yehova, pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka.’​—Salmo 148:12, 13.

3. Kodi ndimotani kuti achichepere omwe amadziŵa Baibulo amawona moyo mosiyana ndi omwe samatero?

3 Ngati ndinu wachichepere amene makolo anu amakubweretsani mokhazikika ku misonkhano yoteroyo, inu mwadalitsidwa mwapadera. Achichepere ambiri akuvutitsidwa ndi mavuto adziko. Ena angakhale ndi mantha akuti anthu adzawononga dziko lapansi. Inu mumadziŵa kuti Mulungu sadzalola chimenecho kuchitika, ndi kuti iye sadzalola anthu kupitirizabe kuwononga pulaneti lokongolali. M’malo molola ichi kuchitika, Mulungu adzatha, mogwirizana ndi kunena kwa Baibulo, “kuononga iwo akuononga dziko.” Inu mumadziŵa kuti Baibulo limalonjeza kuti mtsogolo mowala m’dziko latsopano lolungama la Mulungu muli pafupi.​—Chibvumbulutso 11:18; Salmo 37:29; 2 Petro 3:13.

Chikhulupiriro Chanuchanu

4. Kodi ndi thayo lotani limene kudziŵa njira za Mulungu kumaika pa achichepere, ndipo kodi ndimotani mmene Samueli wachichepere anali chitsanzo chabwino cha ichi?

4 Poyamba, njira ya chowonadi Chachikristu ingakhale inali yolondoledwa ndi makolo anu. Mwinamwake inu munabwera ku misonkhano Yachikristu chifukwa chakuti iwo anakubweretsani, ndipo mungakhale munagawana mu utumiki waumulungu chifukwa chakuti iwowo anachita tero. Komabe, pamene nthaŵi ipita, kutumikira ndi kumvera Yehova kungakhale chisangalalo chanuchanu. Mayi wa Samueli wachichepere anamuyambitsa panjira yolungama, koma iye yekha anafunikira kuitsatira. Timaŵerenga motere: “Ngakhale mwana adziŵika ndi zochita zake, ngati mkhalidwe wake uli woyera ngakhale wolungama.”​—Miyambo 20:11, NIV.

5. (a) Kodi Baibulo nlaphindu lalikulu lotani? (b) Kodi nchiyani chimene Paulo anauza Timoteo ponena za kufunika kwa Mawu a Mulungu olembedwa?

5 Malemba amatiuza zimene Mulungu amafuna kwa ife. Iwo amatisonyeza mosabisa mmene tingamkondweretsere, kutipatsa chidziŵitso chambiri chomwe chingatichitire zabwino zambiri. Mtumwi Paulo anauza womuthandizira wake wachichepere Timoteo kuti: ‘Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iriyonse yabwino.’​—2 Timoteo 3:16, 17.

6. Kodi nchiyani chimene bukhu la Miyambo limanena ponena za kufunika kwa chidziŵitso ndi nzeru yaumulungu?

6 Baibulo limatiuzanso kuti ‘timve mwambo ndi kukhala anzeru.’ Ilo limati ‘tisunge’ malamulo a Mulungu, ‘kuitana luntha,’ ndi ‘kufunafunabe’ kuzindikira monga mmene mukafunira chuma chobisika. Ngati inu mutsatira uphungu uwu, pompo ‘mudzazindikira kuopa Yehova ndi kumdziŵadi Mulungu.’ Timapezamonso uphungu uwu: “Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, ngwodala akusunga njira zanga. . . . Pakuti wondipeza ine apeza moyo; Yehova adzamkomera mtima.” Kodi mumawona Baibulo kukhala laphindu kwambiri ndi kuika kuyesayesa koteroko pa kuphunzira zinthu zimene ilo limanena?​—Miyambo 2:1-5; 8:32-35.

Pezani Chidziŵitso

7. Kodi ndi ziti zimene ziri zinthu zofunika zimene tiyenera kuphunzira?

7 Achichepere ena amadziŵa machenjera onse a zamaseŵera, kapena iwo angakuuzeni chirichonse ponena za gulu loimba nyimbo la pamtima pawo. Iwo amapeza zinthu izi kukhala zosavuta kuziphunzira ndi kukumbukira chifukwa chakuti ngwokondweretsedwa nazo. Koma funso lofunika kwambiri ndi ili, Kodi iwo amadziŵanji ponena za Mulungu? Tangoganizirani zimene iye wachita. Mulungu anapanga thambo. Iye ananeneratu chimene anthu akachita ndi chimene chikachitika kalekale zochitikazo zisanachitike. Baibulo silimatiuza kokha ponena za Mulungu koma limatiphunzitsa mmene tingamukondweretsere. Ilo limatisonyeza mmene tingakhalire ndi moyo wachimwemwe tsopano ndi mmene tingapezere moyo wosatha m’dziko lake latsopano lolungama. Kodi ichi sichofunika kwenikweni kuposa kudziŵa amene anapambana mpira wachitanyu kapena kudziŵa maina a oimba nyimbo amene anthu adzawaiwala mofulumira?​—Yesaya 42:5, 9; 46:9, 10; Amosi 3:7.

8. Kodi nchitsanzo chabwino chiti chomwe chinakhazikitsidwa ndi onse aŵiri Yosiya ndi Yesu?

8 Pamene Mfumu yachichepere Yosiya inali ndi zaka 15 zakubadwa, iye ‘anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lake.’ Pamene Yesu anali ndi zaka 12, nayenso anapezeka ‘ali kukhala pakati pa aphunzitsi’ m’kachisi wa Yehova, “namva iwo, nawafunsanso mafunso.”a Mosasamala kanthu za msinkhu wanu, kodi inu, mofanana ndi Yosiya ndi Yesu, mwakulitsa chikondwerero chenicheni cha kuphunzira ponena za zinthu zimene Mulungu wachita ndi zimene adzachitabe?​—2 Mbiri 34:3; Luka 2:46.

9. (a) Kodi ndi vuto liti limene achichepere ambiri ali nalo? (b) Kodi nchiyani chingapangitse kuŵerenga ndi kuphunzira kukhala kosavuta, ndipo kodi inuyo panokha mwapeza ichi kukhala chowona?

9 Komabe, inu munganene kuti: ‘Kuphunzira ndi ntchito yovuta.’ Anthu ambiri, achichepere ndi achikulire, sanaŵerenge mokwanira kuti kuŵerengako kukhale kopepuka. Mutaŵerenga kwambiri, kuŵerengako kumakhalanso kopepuka. Mutaphunzira kwambiri, kuphunzirako kumakhalanso kopepuka. Inu mumawonjezera malingaliro atsopano ku zinthu zomwe mumadziŵa kale, kuchipanga kukhala chosavuta kuzimvetsetsa ndi kuzikumbukira.

10. (a) Kodi mungapeze zambiri motani m’misonkhano Yachikristu? (b) Kodi chokumana nacho chanu nchotani pa ichi?

10 Kodi nchiyani chimene chingakuthandizeni kuphunzira zambiri ponena za Mulungu? Mwinamwake inu muyenera kukhala okhazikika kwenikweni kupezeka pa misonkhano Yachikristu. Kodi mungakonzekere pasadakhale ndi kukhalamo ndi phandedi? Mwachitsanzo, kodi inu mungapeze chidziŵitso chakuya kuchokera m’phunziro ili mwa kuŵerenga Malemba omwe aikidwamo koma osagwidwa mawu? Kodi inuyo mwalemba liwu limodzi kapena aŵiri m’danga okukumbutsani chimene lirilonse la malemba awa limaonjezera ku ndimeyo kapena phunziroli? Kodi muli ndi chizoloŵezi cha kuphatikizapo pafupifupi limodzi la malembawa m’ndemanga chimene chimasonyeza kuyamikira kwanu kukambirana Malemba? Mkulu wa pa mpingo amene wapezeka pamisonkhano mokhazikika kwa zaka zambiri ananena motere: “Ndimachipeza kukhala chovuta kwenikweni kugwirizanitsa maganizo anga ndi phunziro limene sindinakonzekeredi, koma chimandisangalatsa kwabasi kutsatira limene ndaliphunzira mokwanira.”

11. Kodi mungapeze zambiri motani mu nkhani zozikidwa pa Baibulo, ndipo kodi nchifukwa ninji ichi chiri chofunika?

11 Pamene mumvetsera ku nkhani za Baibulo, kodi mumalemba nsonga zachidule zokuthandizani kusanthula mmene nkhaniyo ikukambidwira ndi kusungabe maganizo anu pa zomwe zikunenedwa? Kodi mumayerekeza zomwe mukumva ndi zomwe mumadziŵa kale kotero kuti mungaimvetsetse mopepuka ndi kuikumbukira bwino? Yesu anapemphera motere: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Kodi chidziŵitso chimene chimatsogolera ku moyo wosatha sichidziŵitso chabwino kwabasi chimene inuyo mungachipeze mothekera? Onani chimene Baibulo linanena za ichi: ‘Pakuti Yehova apatsa nzeru; kudziŵa ndi kuzindikira kutuluka mkamwa mwake. Pakuti nzeru idzaloŵa mu mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziŵa; kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakuchinjiriza.’​—Miyambo 2:6, 10, 11.

Kulani ndi Kuyamikira

12. Kodi ndi zinthu zina zapadera ziti zimene Mulungu watichitira?

12 Kodi timayamikiradi chimene Mulungu watichitira? Iye analenga dziko lapansi lokongolali ndi kulikonzekera kaamba ka moyo. Iye analenga makolo athu oyambirira, mwakutero kuchipanga kukhala chothekera kwa ife kuti tibadwe. Iye anatikonzekera kuchilikizidwa ndi mabanja ndi mpingo wachikondi. (Genesis 1:27, 28; Yohane 13:35; Ahebri 10:25) Iye anatumiza Mwana wake woyamba kubadwa kudziko lapansi kudzatiphunzitsa zambiri ponena za Iyemwini ndi kupereka dipo limene limapangitsa moyo wosatha kukhala wothekera. Kodi inu mumayamikiradi mphatso zodabwitsa zoterozo? Kodi izo zimakusonkhezerani kuvomereza chiitano chake cha kuphunzira ponena za iye ndi kumtumikira?​—Mateyu 20:28; Yohane 1:18; Aroma 5:21.

13. Kodi nchifukwa ninji mumalingalira kuti Mulungu ngwokondweretsedwa mwa anthu?

13 Mlengi wa chilengedwe chonse ngwokondweretsedwa ndi anthu. Iye anatcha Abrahamu “bwenzi langa,” ndipo anati kwa Mose: “Ndikudziwa dzina lako.” (Yesaya 41:8; Eksodo 33:12) Bukhu la Chibvumbulutso limasonyeza kuti Mulungu ali ndi bukhu lophiphiritsira, kapena “buku la moyo,” lokhala ndi maina a atumiki ake okhulupirika ‘chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi.’ Kodi dzina lanu lidzaphatikizidwamo?​—Chibvumbulutso 3:5; 17:8; 2 Timoteo 2:19.

14. Kodi ndimotani mmene kutsatira malamulo a makhalidwe abwino a Mulungu kungaongolere moyo wanu?

14 Malamulo a makhalidwe abwino a Mulungu amagwira ntchito. Kuchita zinthu m’njira yake kumakankhira mavuto pambali​—chisembwere, kumwerekera ndi mankhwala ogodomalitsa, uchidakwa, mimba zosafunidwa, matenda opatsirana mwa kugonana, chiwawa, mbanda, ndipo ndi ndandanda yaitalidi ya zoipa zina. Kutsatira njira zake kudzakuthandizaninso kupeza mabwenzi a pondapo nane mpondepo ndi kukhala ndi moyo wachimwemwe. Kodi ichi sichabwinopo? (1 Akorinto 6:9-11) Ngakhale wachichepere amene ali wosankhapo kale kuchita zinthu m’njira ya Mulungu angapeze mphamvu zowonjezereka za kuchita chimene chiri chabwino. Baibulo limati: ‘Pa wachifundo [Yehova] adzakhala wachifundo.’ Ilo limatitsimikiziranso kuti iye ‘sadzataya okondedwa ake’ kapena ‘kusiya anthu ake.’​—Salmo 18:25; 37:28; 94:14; Yesaya 40:29-31.

Pitani Patsogolo m’Kutumikira Mulungu

15. Kodi ndi uphungu waumulungu uti umene Solomo anapereka kwa achichepere?

15 Kodi zonulirapo zanu zazikidwa pa dziko lakale lomafali kapena m’dziko latsopano lolungama? Kodi mumamvera Mulungu, kapena kodi mumamvera anthu anzeru akudziko omwe amamtsutsa? Kodi zosangulutsa, maphunziro apamwamba, kapena ntchito yakuthupi yakutha nthaŵi imakhala patsogolo pa Mulungu ndi utumiki wake? Mfumu yanzeru Solomo analemba bukhu la Baibulo lonse la Mlaliki kusonyeza chimene chiyenera kukhala choyamba m’miyoyo yathu. Iye anamaliza motere: ‘Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo. Mawu atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.’​—Mlaliki 12:1, 13.

16. Kodi ndimotani mmene achichepere angafikire mwaŵi wowonjezereka?

16 Abale Achikristu achikulire onse omwe mumadziŵa​—akulu, apainiya, ndi oyang’anira anu adera ndi achigawo​—panthaŵi ina anali ana. Kodi nchiyani chinatsogolera ku madalitso amene iwo akusangalala nawo lerolino? Iwo anakonda Mulungu ndi kufuna kumtumikira. Ambiri a iwo pamene anali achichepere anatenga mwaŵi wa nthaŵi yapadera imene anali nayo kupezera chidziŵitso ndi kuzoloŵera. Iwo anaphunzira ndi kugawanamo m’misonkhano. Iwo anakhala ndi phande m’kuphunzitsa, ndipo anafikira mwaŵi wowonjezereka​—upainiya, utumiki wa pa Beteli, kapena ntchito ina yake yamphotho. Iwo sanali ‘achichepere oposa onse’; iwo anali ndi zikondwerero zachibadwa ndi nkhaŵa monga zimene muli nazo. Komabe, iwo anagwirizana okha ndi uphungu uwu: ‘Chirichonse chomwe mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa [Yehova, NW], osati kwa anthu ayi.’​—Akolose 3:23; yerekezerani ndi Luka 10:27; 2 Timoteo 2:15.

17. Kodi nchiyani chimene chingathandize achichepere kupita patsogolo mu utumiki wa Mulungu?

17 Bwanji ponena za inu? Kodi mumayamikiradi zinthu zaumulungu? Kodi mumasankha mabwenzi pakati pa anthu omwe amaika zinthu zauzimu kukhala zoyamba? Kodi mumalimbikitsa ena kugawana m’ntchito Yachikristu? Kodi mumatulukira mu utumiki Wachikristu ndi achikulire, ozoloŵera kwenikweni kuti muphunzire kwa iwo, kulaŵa chisangalalo chawo, ndi kulimbikitsidwa ndi ntchito zawo zabwino? Mboni ina imakumbukira tsiku lina, pafupifupi zaka 20 zapitazo, pamene kwanthaŵi yoyamba munthu wachikulire anamuitana kutsagana naye mu uminisitala wakumunda. Ichi, msungwanayu akutero, chinali posinthira m’moyo wake: “Kwanthaŵi yoyamba ndinatulukira chifukwa chakuti ine ndinafuna kutero, osati kokha chifukwa chakuti makolo anga ankatulukira nane.”

18. Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kuganizapo tisanadzipereke ku ubatizo?

18 Ngati inuyo mukupanga kupita patsogolo m’kuchita zinthu m’njira ya Mulungu, inu posachedwapa mungayambe kuganizira za ubatizo. Nkofunika kukumbukira kuti ubatizo suli njira zodutsira kunka ku uchikulire. Iwo sumasonyeza kuti inuyo mukukula, kapena kukhala chinachake chimene muyenera kuchita chifukwa chakuti mabwenzi anu atenga sitepi limeneli. Musanapemphe kuti mubatizidwe, inu muyenera kukhala ndi chidziŵitso choyambirira cha chowonadi ndi kukhala ndi moyo mogwirizana ndi Mawu a Mulungu. Inu muyenera kukhala ndi kuzoloŵera kolama m’kugawana chidziŵitso chimenechi ndi ena ndi kuzindikira kuti iyi ndiyo mbali yofunika ya kulambira kowona. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Inu muyeneranso kudziŵa kuti mutatenga sitepi lofunika Lachikristu ili mudzayembekezeredwa kukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo ya makhalidwe abwino yolungama ya Baibulo.b Mumtima mwanu, muyenera kukhala mutapereka moyo wanu kwa Atate wanu wachikondi wakumwamba.​—Yerekezerani ndi Salmo 40:8, 9.

19. Kodi ndi liti pamene munthu ayenera kubatizidwa?

19 Ubatizo uli sitepi limene inu mumatenga pamene mwasankhapo molimba mtima kuti mosasamala kanthu za chimene chingachitike m’moyo wanu wonse, inu mudzatumikira Mulungu. Ichi nchizindikiro chapoyera chakuti inuyo mwapanga kudzipereka kotheratu, ndi kodzikana, ndi kopanda malire kwa Yehova kupyolera mwa Yesu Kristu kuchita chifuniro cha Mulungu. Mkulu wina Wachikristu amakumbukira tsiku lina, pafupifupi theka la zaka zana limodzi zapitazo, pamene anazindikira izi: “Ine ndiyenera kuchita chinachake ponena za icho!” Michelle, Mboni yachichepere yobatizidwa mu Newcastle, ku Mangalande, zaka zochepera zapitazo, akuti: “Pa msinkhu wa zaka 13, ndinazindikira kuti ndinafunikira kupereka moyo wanga ndi kubatizidwa; panalibe chirichonse chimene ndikadachita kuposa kutumikira Mulungu.”

20. (a) Kodi nchitsanzo chabwino chiti chomwe chakhazikitsidwa kale ndi achichepere zikwi makumi ambiri? (b) Kodi sitepi limeneli liyenera kulingaliridwa motani?

20 Achichepere zikwi makumi ambiri abatizidwa posachedwapa. Iwo adaphunzira Mawu a Mulungu ndi kuphunzira njira zake, ndipo pambuyo pake, mwa ubatizo wa m’madzi, iwo anagwirizana mwachisangalalo ndi okalamba ambiri m’kuchitira chithunzi poyera kudzipereka kwawo kwa Mulungu. Iwo amadziŵa kuti ubatizo sindiwo mapeto koma chiyambi chokha chonkera ku njira yokha yodzipereka mowonadi imene asankhapo kulondola mu utumiki wa Yehova kosatha.

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani yakuti “Atumiki Achichepere m’Nthaŵi za Baibulo” patsamba 4.

b Ichi sichimatanthauza kuti kunena kuti ‘Sindinabatizidwebe’ kuli chodzikhululukira kuchita cholakwa. Mwamsanga titadziŵa chimene Mulungu akufuna, ife mwachiwonekere tiri ndi thayo la kumumvera iye.​—Yakobo 4:17.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi nchifukwa ninji chidziŵitso cha Mawu a Mulungu chiri chofunika chotero?

◻ Kodi ndimotani mmene mungapindulire zambiri pa misonkhano Yachikristu?

◻ Kodi ndi madalitso otani ochokera kwa Mulungu omwe angatisonkhezere kum’mvera?

◻ Kodi mungapite patsogolo motani mu utumiki wa Mulungu?

◻ Kodi ndi liti pamene munthu ayenera kubatizidwa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena