Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 8/1 tsamba 23-25
  • Aroma Amva Mbiri Yabwino Koposa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Aroma Amva Mbiri Yabwino Koposa
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • PAULO NDI AROMA
  • CHIKHULUPIRIRO NDI CHILAMULO
  • CHILUNGAMO KUPYOLERA M’CHIKHULUPIRIRO
  • KUYANKHA ZITSUTSO
  • CHILUNGAMO NDI AYUDA AKUTHUPI
  • MALAMULO AMAKHALIDWE ABWINO ACHILUNGAMO
  • KWA ODZOZEDWA NDI NKHOSA ZINA
  • Kondwerani ndi Chilungamo cha Yehova
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Pali Uthenga Wabwino Wofunika Kuti Anthu Onse Amve
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Nkulondoleranji Chilungamo?
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 8/1 tsamba 23-25

Aroma Amva Mbiri Yabwino Koposa

KODI ndimotani mmene munthu wochimwa angakhalire wolungama m’maso mwa Mulungu ndipo motero kupeza moyo wosatha? Funso ili linapangitsa kukambitsirana kwamphamvu m’zaka za zana loyamba la Nyengo yathu ino Yachisawawa. Kodi mukulidziŵa yankho? Kaya mukulidziŵa kapena ayi, inuyo mufunikira kudziŵerengera kukambirana kwaluso kwa mtumwi Paulo kwavutoli m’bukhu la Baibulo la Aroma. Kuchita tero kudzakuthandizani kumvetsetsa unansi wofunika womwe ulipo pakati pa chikhulupiriro, ntchito, chilungamo, ndi moyo.

PAULO NDI AROMA

Bukhu la Aroma ndi kalata yolembedwa ndi Paulo pafupifupi 56 C.E. kwa Akristu a mu Roma. Kodi nchifukwa ninji iye anailemba? Ngakhale kuti Paulo mu 56 C.E. anali asadachezerebe Roma, iye mwachionekere anadziŵa Akristu ambiri kumeneko, popeza kuti m’kalata yake iye anatchula ambiri a awa mwa maina. Kuwonjezera apa, Paulo anafuna kwambiri kupita ku Roma ncholinga chokalimbikitsa abale Achikristu kumeneko, ndipo iye akuonekeranso kukhala anakonzekera kupanga Roma kukhala poyambira pa ulendo wake waumishonale wolinganizidwira kunka ku Spanya.​—Aroma 1:11, 12; 15:22-24.

Komabe, chifuno chachikulu cha Paulo polemba kalatayi chinali kuyankha funso lakuti: Kodi anthu angapeze bwanji chilungamo chotsogolera kumoyo? Yankho lake limatembenuka kukhala mbiri yabwino koposa. Chilungamo chimaŵerengedwa pamaziko a chikhulupiriro. Paulo akupanga mfundoyi ndi kukhazikitsa mutu wa kalata yake pamene akulemba motere: ‘Pakuti uthenga wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu ali yense wakukhulupira; kuyambira Myuda, ndiponso Mhelene. Pakuti mmenemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.’​—Aroma 1:16, 17.

CHIKHULUPIRIRO NDI CHILAMULO

M’zaka za zana loyamba, saliyense amene anavomereza kuti chilungamo chinaŵerengedwa pamaziko a chikhulupiriro. Oŵerengeka aliuma anaumirira kuti zambiri zinafunikira. Kodi Yehova sanapereke Chilamulo cha Mose? Kodi ndimotani mmene aliyense angakhalire wolungama yemwe sanagonjere ku makonzedwe ouziridwa amenewo? (Onani Agalatiya 4:9-11, 21; 5:2.) M’chaka cha 49 C.E., funso la kumamatira ku Chilamulo linakambitsiridwa ndi bungwe lolamulira m’Yerusalemu, ndipo iwo anamaliza kuti Akunja omwe anavomereza mbiri yabwino sanafunikire kudulidwa ndi kugonjera ku malamulo a Chilamulo Chachiyuda.​—Machitidwe 15:1, 2, 28, 29.

Pafupifupi zaka zisanu ndi ziŵiri pambuyo pake, Paulo analemba kalata yake kwa Aroma akumachilikiza mfundo ya chosankhachi. Ndithudi, iye anapita patali. Chilamulo sichinali kokha chosayenerera kwa Akristu Achikunja koma Ayuda omwe anadalira pa kuchimvera sakadalengezedwa kukhala olungama kaamba ka moyo.

CHILUNGAMO KUPYOLERA M’CHIKHULUPIRIRO

Pamene muŵerenga bukhu la Aroma, inu mudzaona mmene Paulo akumangirira mosamalitsa nkhani yake, kuchilikiza ndemanga zake ndi mawu ogwidwa ambiri kuchokera m’Malemba Achihebri. Pamene ankalankhula kwa Ayuda, omwe angakhale anali ndi vuto la kuvomereza chiphunzitso chake chouziridwa, iye anasonyeza chifundo ndi kudera nkhaŵa. (Aroma 3:1, 2; 9:1-3) Komabe, iye akupereka nkhani yake momvekera kwenikweni ndi mosapikisanika.

Mu Aroma mutu 1 mpaka mutu 4, Paulo akuyamba ndi chowonadi chakuti aliyense ngwaliwongo lauchimo. Chotero, njira yokha imene anthu angalengezedwere kukhala olungama njapamaziko a chikhulupiriro. Zowona, Ayuda anayesera kukhala olungama mwakusunga Chilamulo cha Mose. Koma analephera. Chotero, Paulo ananena izi molimba mtima: ‘Ayuda ndi Ahelene omwe, kuti onsewa agwidwa ndi uchimo.’ Iye akutsimikizira chowonadi chachilendo ichi ndi Malemba ogwidwa mawu ambiri.​—Aroma 3:9.

Popeza kuti ‘palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo,’ kodi pali chiyembekezo chotani? Mulungu adzalengeza anthu kukhala olungama monga mphatso yaulere pamaziko ansembe yadipo ya Yesu. (Aroma 3:20, 24) Kuti azoloŵerane okha ndi ichi, iwo afunikira kukhala ndi chikhulupiriro m’nsembeyo. Kodi chiphunzitso chimenechi chakuti anthu amalengezedwa olungama pamaziko a chikhulupiriro nchoseketsa? Kutalitali. Abrahamu iyemwini analengezedwa wolungama chifukwa cha chikhulupiriro chake Chilamulo chisanakhazikitsidwe.​—Aroma 4:3.

Pokhala atakhazikitsa kufunika kwachikhulupiriro, Paulo m’mutu 5 akukambirana maziko a chikhulupiriro Chachikristu. Uyu ndi Yesu, amene njira yake yachilungamo imathetsa ziyambukiro zoipa za chimo la Adamu kwa anthu okhala ndi chikhulupiriro mwa Iye. Chotero, ‘mwa chilungamitso chimodzi,’ osati mwa kumvera Chilamulo cha Mose, ‘chilungamo cha moyo chinafikira anthu onse.’​—Aroma 5:18.

KUYANKHA ZITSUTSO

Komabe, ngati Akristu sali pansi pa Chilamulo, kodi nchiyani chomwe chikaŵaletsa kupitirizabe ndi kuchita zolakwa ndi kudziŵerengera kukhala olengezedwabe olungama, kuyamikira chisomo cha Mulungu? Paulo akuyankha chitsutsochi mu Aroma mutu 6. Akristu afa kunjira yawo yauchimo yakale. Moyo wawo watsopano mwa Yesu umawalamulira kulimbana ndi zofooka zawo zakuthupi. Iye akuchonderera motere: ‘Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m’thupi lanu la imfa.’​—Aroma 6:12.

Koma kodi Ayuda, sakamamatirabe ku Chilamulo cha Mose? M’mutu 7, Paulo akulongosola mosamalitsa kuti ichi sichiri tero. Monga mmene mkazi wokwatiwa amakhalira womasuka ku chilamulo cha mwamuna wake pamene mwamunayo amwalira, chotero imfa ya Yesu inamasula akhulupiriri Achiyuda ku kugonjera ku Chilamulo. Paulo akunena motere: ‘Inunso munayesedwa akufa ku chilamulo ndi thupi la Kristu.’​—Aroma 7:4.

Kodi ichi chimatanthauza kuti panali chinachake cholakwika ndi Chilamulo? Kutalitali. Chilamulo chinali changwiro. Vuto linali lakuti anthu opanda ungwiro sakachimvera Chilamulochi. ‘Pakuti tidziŵa kuti chilamulo chiri chauzimu,’ analemba tero Paulo, ‘koma ine ndiri wathupi, wogulitsidwa kapolo wa uchimo.’ Munthu wopanda ungwiro sangasunge Chilamulo changwiro cha Mulungu ndipo chotero amatsutsidwa nacho. Pamenepa, nkwabwino kwambiri chotani nanga kuti “iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa”! Akristu odzozedwa atengedwa ndi mzimu kukhala ana a Mulungu. Mzimu wa Yehova umawathandiza kulimbana ndi kupanda ungwiro kwathupi. “Ndani adzaneneza osankhidwa a Mulungu? Mulungu ndiye amene awayesa olungama.” (Aroma 7:14; 8:1, 33) Palibe chimene chingawalekanitse iwo ndi chikondi cha Mulungu.

CHILUNGAMO NDI AYUDA AKUTHUPI

Ngati Chilamulo nchosafunikanso, kodi ichi chimausiya pati mtundu wa Israyeli? Ndipo bwanji ponena za malemba onsewo olonjeza za kubwezeretsedwanso kwa Israyeli? Mafunsowa atengedwa mu Aroma mutu 9 mpaka 11. Malemba Achihebri ananeneratu kuti ochepera okha a Aisrayeli akapulumutsidwa ndi kuti Mulungu akatembenuzira chisamaliro chake ku mtunduwo. Mogwirizana ndi ichi, maulosi onena za kupulumuka kwa Israyeli akwaniritsidwa osati ndi Israyeli wakuthupi koma ndi mpingo Wachikristu, wopangidwa ndi Ayuda akuthupi okhulupirira ndi kudzazidwa ndi Akunja a mtima wolunjika.​—Aroma 10:19-21; 11:1, 5, 17-24.

MALAMULO AMAKHALIDWE ABWINO ACHILUNGAMO

Mu Aroma mutu 12 mpaka 15, Paulo akupitiriza kulongosola njira zopindulitsa zimene Akristu odzozedwa angakhalire ndi moyo mogwirizana ndi kulengezedwa kwawo olungama. Mwachitsanzo, iye akunena kuti: “Mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu.” (Aroma 12:1, 2) Tiyenera kukhulupirira m’mphamvu za zabwino ndi kusagwiritsira ntchito choipa kulimbana ndi choipa. Mtumwiyo analemba kuti, ‘Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.’​—Aroma 12:21.

Roma anali malo apakati amphamvu a ndale zadziko m’tsiku la Paulo. Chotero, Paulo akulangiza Akristu mwanzeru kuti: ‘Anthu onse amvere maulamuliro aakulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu.’ (Aroma 13:1) Zochita za Akristu kwa wina ndi mnzake zirinso mbali yakukhala ndi moyo mogwirizana ndi chilungamo. “Musakhale ndi mangawa kwa munthu ali yense,” akutero Paulo, ‘koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo.’​—Aroma 13:8.

Ndiponso, Akristu ayenera kulingalira chikumbumtima cha ena ndi kusakhala wopereka chiweruzo. Paulo akuchonderera kuti: ‘Tilondore zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.’ (Aroma 14:19) Ndi uphungu wabwino chotani nanga wa kugwiritsira ntchito mbali iriyonse ya moyo Wachikristu! Kenaka, m’mutu 16, Paulo akumaliza ndi moni waumwini ndi mawu omalizira achilimbikitso ndi uphungu.

KWA ODZOZEDWA NDI NKHOSA ZINA

Nkhani yokambitsiridwa mu Aroma inali yofunika m’zaka za zana loyamba ndipo idakali yofunika lerolino. Chilungamo ndi moyo wosatha nzokondweretsa molimbikitsa kwa atumiki onse a Yehova. Zowona, Aroma analembedwera ku mpingo wa Akristu odzozedwa, pamene kuli kwakuti lerolino unyinji waukulu wa Mboni za Yehova uli wa ‘khamu lalikulu’ ndipo ali ndi chiyembekezo cha padziko lapansi. (Chibvumbulutso 7:9) Komabe, kalatayi iri ndi uthenga wofunika kwa awanso. Kodi iwo ndi uti?

Bukhu la Aroma limatsimikizira kuti Akristu alengezedwa kukhala olungama ndi chikhulupiriro. Kwa odzozedwa, ichi chimaloza ku kukhala kwawo olamulira anzake ndi Yesu mu Ufumu wakumwamba. Komabe, ziŵalo za khamu lalikulu zalengezedwanso kukhala zolungama, koma monga ‘mabwenzi a Mulungu,’ monga mmene analiri kholo Abrahamu. (Yakobo 2:21-23) Chilungamo chawo ncholoza ku kupulumuka kwawo chisautso chachikulu, ndipo chazikidwa pa chikhulupiriro m’mwazi wa Yesu, monga mmene ziriri kwa odzozedwa. (Salmo 37:11; Yohane 10:16; Chibvumbulutso 7:9, 14) Chotero, kukambirana kwa Paulo mu Aroma nkofunika kwenikweni kwa nkhosa zina limodzi ndi odzozedwa. Ndipo uphungu wabwino wa bukhulo wakukhala ndi moyo mogwirizana ndi kulengezedwa kwathu olungama ngofunika kwa Akristu onse.

The Book of Life, lolembedwa ndi Dokotala Newton Marshall Hall ndi Dokotala Irving Francis Wood, limati: “Ponena za zigomeko ndi mbali ya ziphunzitso [Aroma] amafikira mfundo yapamwamba ya kuphunzitsa kouziridwa kwa Paulo. Ilo nlamachenjera, nlaluso, komabe lamphamvu. . . . Kuphunzira kwa kalatayi kumabweretsa kulemerera kwake ndi mfupo zochuluka.” Bwanji osaŵerenga bukhulo inu nokha ndi kusangalala ndi ‘mbiri yabwino’ imene ilimo, imene ili ‘mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa.’​—Aroma 1:16.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 24]

‘Palibe ulamuliro [wakudziko] wina koma wochokera kwa Mulungu.’ Ichi sichimatanthauza kuti Mulungu amaika wolamulira aliyense m’malo. M’malomwake, olamulira akudziko amakhalapo kokha mwa kuloledwa ndi Mulungu. Kaŵirikaŵiri, olamulira aumunthu anaonedwa ndi kunenedweratu ndi Mulungu ndipo mwakutero iwo “a[na]ikidwa ndi Mulungu.”​—Aroma 13:1.

[Mawu a Chithunzi]

Museo della Civiltà Romana, Roma

Bokosi/​Chithunzi patsamba 25]

Akristu auzidwa kuti: ‘Valani inu Ambuye Yesu Kristu.’ Ichi chimatanthauza kuti ayenera kutsatira mapazi a Yesu mosamalitsa, kumtsanzira mwakuika zikondwerero zawo zauzimu m’malo mwa zakuthupi choyamba m’miyoyo yawo, mwakutero, ‘kusaganizira zathupi kuchita zofuna zake.’​—Aroma 13:14.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 25]

Paulo anauza Aroma ‘kulankhulana wina ndi mnzake ndi kumpsyompsyo- nana kopatulika.’ Komabe, panopa iye sanali kukhazikitsa mwambo watsopano Wachikristu kapena mwambo wachipembedzo. M’tsiku la Paulo, kumpsyompsyonana pamphumi, pakamwa, kapena padzanja kaŵirikaŵiri kunaperekedwa monga chizindikiro cha moni, chikondi, kapena ulemu. Chotero, Paulo panopa anali kulozera chabe ku mwambo womwe unali wofala m’tsiku lake.​—Aroma 16:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena