Umodzi Ngwotsimikizirika mwa Kristu
Mfundo Zazikulu Kuchokera ku Aefeso
KUCHIYAMBIYAMBI mu 52 C.E., mtumwi Paulo analalikira mu Efeso. Mzinda wazamalonda wolemera umenewu wa ku Asia Minor udalinso maziko a chipembedzo chonyenga. Koma Chikristu chinafalikiranso kumeneko pambuyo pakuti Paulo anabwerera ku Efeso, mwinamwake m’nyengo yachisanu ya 52/53 C.E. Iye anapereka nkhani zatsiku ndi tsiku m’nyumba yosonkhanira yapasukulu nachitira umboni kunyumba ndi nyumba m’kukhalako kwake kwa zaka zitatu.—Machitidwe 19:8-10; 20:20, 21, 31.
Pamene adali m’ndende m’Roma pafupifupi 60-61 C.E., Paulo anaŵalembera Akristu a ku Efeso. Umodzi mwa Kristu ndiwo mutu wa kalata yake. Kwenikweni, iyo iri ndi zilozero 13 ku ‘umodzi mwa Kristu,’ kuposa kalata ina iriyonse imene Paulo analemba. Mofanana ndi Aefeso, nafenso tingapindule ndi mawu a Paulo onena za ntchito ya Kristu, kupeŵa chisembwere ndikutsutsa makamu a mizimu yoipa.
Umodzi Ndiwo Chifuno cha Mulungu
Poyamba, Paulo analongosola mmene Mulungu akabweretsera umodzi mwa Kristu. (1:1-23) Yehova anafuna kusonkhanitsanso pamodzi zinthu zonse m’mwamba ndi padziko lapansi kupyolera mwa “makonzedwe” (njira yoyendetsera zinthu). Mwa Kristu, Mulungu akagwirizanitsa kwa iyemwini osankhidwa kaamba ka moyo wakumwamba ndi ena amene akakhala ndimoyo padziko lapansi. Lerolino, Mulungu wagwirizanitsa odzozedwa ndi ‘khamu lalikulu,’ ndipo ‘kusonkhanitsidwa kwa zinthu zonse padziko lapansi’ kudzapitiriza kufikira awo amene ali m’manda achikumbikiro adzamva mawu a Yesu natulukira. (Chibvumbulutso 7:9; Yohane 5:28, 29) Tiyenera kukhala oyamikira za chimenechi, mongadi mmene Paulo anapempherera Aefeso kuti ayamikire makonzedwe a Mulungu kaamba ka iwo.
Kenaka chisamaliro chinalunjikitsidwa kwa Akristu Achikunja, omwe panthaŵi ina anali akufa m’tchimo. (2:1–3:21) Kupyolera mwa Kristu, Lamulo linachotsedwa ndipo panaikidwa maziko a kugwirizana kwa Ayuda ndi Akunja ndikukhala kachisi wa Mulungu wokhalidwa ndi mzimu. Udindo wa Paulo udali kudziŵikitsa chinsinsi chopatulika chakuti Akunja angakhale ogwirizana ndi Kristu, mwa amene iwo angamfikire Mulungu ndi ufulu wakulankhula. Paulo anawapemphereranso Aefeso, panthaŵiyi akumapempha kuti Yehova awapangitse kukhala okhazikika molimba m’chikhulupiriro ndi chikondi.
Mfundo Zopititsa Patsogolo Umodzi
Paulo anasonyeza kuti Mulungu anapereka mfundo zogwirizanitsira. (4:1-16) Pakati pa izi pali thupi limodzi lauzimu lomwe ndimpingo. Thupi limeneli limagwira ntchito mogwirizana pansi pa umutu wa Kristu. Ndipo iye amapereka mphatso mwa amuna kuthandiza onse kufikira umodzi m’chikhulupiriro.
Yehova amachipanganso kukhala chotheka kusonyeza mikhalidwe Yachikristu imene imapititsa patsogolo umodzi. (4:17–6:9) Pokhala atavala “umunthu watsopano,” Akristu amapeŵa kusapembedza monga ngati kalankhulidwe koipa. Iwo amayenda mwanzeru, kulemekeza Kristu, ndikusonyeza chigonjero choyenera.
Kuwonjezera apa, Mulungu amaŵatheketsa Akristu kutsutsa makamu a mizimu yoipa ofuna kuwononga umodzi wathu. (6:10-24) Chitetezo choterocho chimaperekedwa ndi zida zauzimu zochokera kwa Mulungu. Choncho tiyeni tizigwiritsire ntchito ndikupemphera mofunitsitsa, kuwaphatikizamo akhulupiriri anzathu m’mapembedzero athu.
Ndiuphungu wabwino chotani nanga umene Paulo adawapatsa Aefeso! Tiyeni tiulabadire mwakupeŵa chisembwere ndikutsutsa makamu a mizimu yoipa. Ndipo tiyeni tiyamikire kwenikweni umodzi umene tikusangalala nawo mwa Yesu Kristu.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 24]
Mivi Yoyaka Moto: Zida zauzimu zimaphatikizapo ‘chikopa cha chikhulupiriro’ chozimira, kapena kuthetsa mphamvu “mivi yoyaka moto” ya Satana. (Aefeso 6:16) Mivi ina imene inkagwiritsiridwa ntchito ndi Aroma inali mabango amphako okhala ndi nsupa yachitsulo pansi pa nsonga yake yomwe inadzazidwa ndi naphtha yoyaka. Iyo inkaponyedwa ndi mauta okhwefuka kuopera kuzima motowo, ndipo kuinyika m’madzi kudangowonjezera ukali wa malaŵiwo. Koma zikopa zazikulu zinachinjiriza asilikali ku mivi yoteroyo, mongadi mmene chikhulupiriro mwa Yehova chimatheketsera atumiki ake ‘kuzima mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’ Inde, chikhulupiriro chimatithandiza kupeŵa zinthu zonga ngati kuukiridwa ndi mizimu yoipa limodzinso ndi mayeso akuchita cholakwa, kulondola njira yamoyo yokondetsa zinthu zakuthupi, ndikugonjera ku mantha ndi kukaikira.