Ripoti la Olengeza Ufumu
Chowonadi cha Baibulo Chilaka Miyambo
MIYAMBO yachipembedzo ingayale mizu kwambiri. Anthu mamiliyoni ambiri amalingalira kuti nkolakwa kwa munthu kusintha chipembedzo chake. Saulo, yemwe anadzakhala mtumwi Paulo, mwachiwonekere analingalira mwanjirayo, pakuti anati: ‘Ndinakhala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga [kuposa ambiri amsinkhu wanga].’ Koma pamene anasonyezedwa chowonadi, iye anasintha Chiyudacho nakhala Mkristu. (Agalatiya 1:13-l6) Anthu ambiri lerolino azindikira kuti chowonadi cha Baibulo chimachokera kumagwero oposa kwambiri miyambo. Tawonani mmene chowonadi cha Baibulo chinalakira mu Italy.
Mkazi wina akufotokoza motere: “Ine ndi mchemwali wanga tinaleredwera m’banja lalikulu lozama m’miyambo Yachikatolika, ndipo tidali Akatolika okangalika. M’kupita kwa nthaŵi, ndinakwatiwa. Kenaka mwamuna wanga anamwalira, ndipo ndinakhala mkazi wamasiye kwa zaka zambiri ndiri ndekha ndi ana anga. Mwana wamkazi wa mchemwali wanga ankaphunzitsa katikizimu, ndipo iye anamfunsafunsabe wansembe mafunso a Baibulo, koma sanayankhidwepo mokhutiritsidwa.
“Pamene ndinapita kukacheza kumudzi kwathu, ndinakumana kwanthaŵi yoyamba ndi Mboni za Yehova ndipo ndinavomereza phunziro la Baibulo. Mabwenzi anga onse Achikatolika akalewo anandiseka kaamba ka kuphunzira Baibulo. Komabe, sindinakhumudwitsidwe. Ndinakhala nalo Baibulo langalanga kwanthaŵi yoyamba, ndipo palibe munthu yemwe akadandilanda. Mchemwali wanga anatenganso kaimidwe kwa Yehova, ndipo m’zaka zosakwanira ziŵiri, aŵirife tinabatizidwa.
“Ndinavutitsidwa choyamba pamene ndinapatuka m’tchalitchicho chifukwa chakuti ndinali ndi mantha a kuleka miyambo imene inayala mizu mwa ine kwa zaka 76. Koma tsopano ndiri wosangalala kuyenda m’njira za Yehova ndikuchita zomwe ndingathe kuthandiza ena kutuluka mumdima wauzimu!”—Yerekezerani ndi 1 Petro 2:9.
Wometa Anthu Tsitsi Awongolera Malingaliro Ake Olakwa
Wometa anthu tsitsi m’Japan anali ndi chizoloŵezi chosimba za ziŵanda ndi za UFO pometa akasitomala ake tsitsi. Komabe, pamene anayamba kuphunzira Baibulo, iye anadzazindikira mmene kachitidweka kanaliri koipa. Chotero mmalo mwakutero anawaitana akasitomala ake kugwirizana naye m’kuphunzira kwake Baibulo. Anachitira umboni kwa akasitomala achichepere ponena za chilengedwe. Mlungu uliwonse anaoda Mabaibulo ndi makope a bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi kuchokera kwa Mboni yomwe inkaphunzira naye kotero kuti akaŵagaŵire kwa akasitomala ake.
Chinkana kuti anali asanakhalebe Mboni, iye anagaŵira Mabaibulo ndi mabuku a Mungathe Kukhala ndi Moyo oposa 30 m’chaka chake choyamba cha kuphunzira. Anthu oposa 25 anayamba kuphunzira Baibulo monga chotulukapo chaumboni wake wamwamwaŵi. Nthaŵi zina anthu okwanira khumi anapezekapo pa gulu lake lophunzira Baibulo. Tsopano anthu asanu ndi aŵiri a amene iye anawachitira umboni powameta tsitsi lawo awongolera malingaliro awo ndipo ndi Mboni zobatizidwa za Yehova!