Kuuzindikira Mzimu Woyera
KODI munkadziŵa kuti mzimu woyera umayambukira moyo wa aliyense wa ife? Ndipo kodi munkazindikira kuti ungapange ziwongolero zazikulu m’moyo mwanu? Izi zingakudabwitseni. Kwenikweni, inu mungafunse kuti: ‘Kodi mzimu woyera ndani kapena nchiyani?’
Ngati mumapita ku chimodzi cha matchalitchi a Chikristu Chadziko, mwinamwake munamvapo mtsogoleri wachipembedzo akubatiza mwana “m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera.” (Mateyu 28:19, The New English Bible) Pamene afunsidwa kuuzindikiritsa mzimu woyera, atsogoleri achipembedzo ambiri amayankha mofulumira kuti: ‘Mzimu woyera ndi munthu wachitatu wa Utatu, wolingana m’njira zonse ndi Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Kristu.’
Komabe, lingaliro limeneli silinasungidwe m’zaka mazana angapo oyambirira a Nyengo Yathu ino. Kuti tichitire fanizo: Zaka mazana atatu pambuyo pa imfa ya atumwi a Yesu Kristu, Gregory wa ku Nazianzus analemba motere: “Ena amalingalira kuti [mzimu woyera] ndi mphamvu (energeia), ena amati ndi cholengedwa, ena amati ndi Mulungu, ena sangasankhepo pa zonsezi.”
Lerolino, matchalitchi ambiri a Chikristu Chadziko amavomereza lingaliro la Utatu la mzimu woyera. Koma kodi zimenezo nzimene Baibulo limachilikiza? Kapena kodi ndi lingaliro wamba lozikidwa pa mwambo? Kwenikweni, Baibulo silimalankhula konse za mzimu woyera m’njira yofanana ndi mmene limalankhulira za Mulungu kapena Yesu. Mwachitsanzo, m’Baibulo, mzimu woyera ulibe dzina laumwini.
Kodi imeneyo ndi mfundo yosafunikira kwenikweni? Ayi, maina ngofunika kwambiri m’Baibulo. Mulungu anagogomezera kufunika kwa dzina lake pamene anati: “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.” (Yesaya 42:8) Kufunika kwa dzina la Yesu Kristu kunagogomezeredwa asanabadwe pamene mngelo anamuuza Mariya kuti: ‘Nudzamutcha dzina lake Yesu.’ (Luka 1:31) Ngati maina a Atate ndi Mwana ngofunika kwenikweni, kodi nchifukwa ninji mzimu woyera ulibe dzina laumwini? Ndithudi, mfundo imeneyi yokha iyenera kupangitsa munthu kulingalira kaya ngati mzimu ulidi wolingana ndi Atate ndi Mwana.
Malemba ndi Mzimu Woyera
M’Malemba Achihebri, kapena “Chipangano Chakale,” muli zilozero ku ‘mzimu woyera’ ndi “mzimu wanga [wa Mulungu].” (Salmo 51:11; Yoweli 2:28, 29) Timaŵerenga kuti mzimu woyera ungadzaze munthu, kudza pa iye, ndi kumkuta. (Eksodo 31:3; Oweruza 3:10; 6:34) Mzimu woyera wina wa Mulungu ungachotsedweko pa munthu mmodzi ndikuperekedwa kwa munthu wina. (Numeri 11:17, 25) Mzimu woyera ungayambe kugwira ntchito mwa munthu wina, kumtheketsa kuchita zinthu zachilendo kwa munthu.—Oweruza 14:6; 1 Samueli 10:6.
Kodi nchiyani chomwe chingatsimikiziridwe molingalirika kuchokera m’ndemanga zoterozo? Ndithudi osati kuti mzimu woyera ndi munthu. Kodi ndimotani mmene mbali ina ya munthu ingatengedwere kuchoka kwa munthu mmodzi ndikuperekedwa kwa wina? Kuwonjezerapo, palibe umboni wakuti pamene Yesu anali padziko lapansi, Ayuda okhulupirika analingalira mzimu woyera kukhala munthu wolingana ndi Atate. Iwo ndithudi sanalambire mzimu woyera. Mmalomwake, kulambira kwawo kunalunjikitsidwa kotheratu kwa Yehova, Uyo amene Yesu iyemwini anamutcha “Atate wanga” ndi “Mulungu wanga.”—Yohane 20:17.
Mofanana ndi mbali yotchedwa Chipangano Chakale, mbali ya Baibulo yotchedwa Malemba Achikristu Achigiriki, kapena “Chipangano Chatsopano,” imanena kuti mzimu woyera ‘ungadzaze’ munthu kapena ‘kukhala’ pa iye. (Machitidwe 2:4; Luka 2:25-27) Mzimu woyera ‘unaperekedwa,’ ‘kuthiridwa,’ ndipo ‘unagaŵiridwa.’ (Luka 11:13; Machitidwe 10:45; Ahebri 2:4) Pa Pentekoste wa 33 C.E., ophunzira analandira ‘cha’ mzimu wa Mulungu. (Machitidwe 2:17) Malemba amalankhulanso za ubatizo wa mzimu woyera ndi zakudzozedwa nawo.—Mateyu 3:11; Machitidwe 1:5; 10:38.
Ndemanga za m’Baibulo zoterozo zimatsimikizira kuti mzimu woyera simunthu. Chitsimikizo chimenechi chikutsimikiziridwa pamene tiwona kuti mzimu woyera wandandalitsidwa ndi zinthu zina zomwe sianthu. Mwachitsanzo, Baibulo limafotokoza kuti Stefano anali ‘wodzala ndi chikhulupiriro ndi mzimu woyera.’ (Machitidwe 6:5) Ndipo mtumwi Paulo anadziyamikira yekha monga mtumiki wa Mulungu ‘m’mayeretsedwe, m’chidziŵitso, m’chilekerero, m’kukoma mtima, mwa mzimu woyera, m’chikondi chosanyenga.’—2 Akorinto 6:4-6.
Zowonadi, nthaŵi zina Baibulo limausonyeza mzimu woyera monga munthu. Mwachitsanzo, Yesaya ananena kuti opanduka ena ‘anamvetsa chisoni mzimu woyera wa Mulungu.’ (Yesaya 63:10) Paulo ananena kuti ungathe ‘kumva chisoni.’ (Aefeso 4:30) Ndipo malemba ena ambiri amanena kuti mzimu woyera umaphunzitsa, kutsogoza, kulankhula, ndi kuchitira umboni. (Yohane 14:26; 16:13, 14; 1 Yohane 5:7, 8) Koma Baibulo limasonyezanso monga anthu zinthu zopanda moyo, zonga ngati nzeru, imfa, ndi tchimo. (Miyambo 1:20; Aroma 5:17, 21) Kwenikweni iyi ndinjira yosavuta kuimva imene Malemba nthaŵi zina amalongosolera zinthu.
Lerolino, timalankhula za Baibulo m’njira yofananayo pamene timanena kuti ilo limanena chinachake kapena kuphunzitsa chiphunzitso. Pogwiritsira ntchito mawu oterowo, sitimatanthauza kuti Baibulo ndi munthu, kodi timatero? Chotero Baibulo silimatanthauzanso kuti mzimu woyera ndi munthu pamene limagwiritsira ntchito mawu ofananawo.
Pamenepo, kodi mzimu woyera nchiyani? Iwo simunthu. Mmalomwake, ndi mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu mwini, yogwiritsiridwa ntchito ndi iye kukwaniritsa chifuniro chake. (Genesis 1:2) Koma kodi miyoyo yathu imayambukiridwa motani ndi mzimu woyera? Ndipo kodi ife patokha tingapindule motani ndi ntchito yake?