Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Yesu Ngwamoyo!
PAMENE akaziwo apeza kuti manda a Yesu ngopanda kanthu, Mariya wa Magadala athamanga kukauza Petro ndi Yohane. Komabe, akazi ena mwachiwonekere atsala kumandako. Posapita nthaŵi, mngelo awonekera ndi kuwaitanira mkati.
Munomu akaziwo awonanso mngelo wina, ndipo mmodzi wa angelowo anena nawo kuti: ‘Musawope inu; pakuti ndidziŵa inu mulikufuna Yesu, amene anapachikidwa. Iye mulibe muno iyayi; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzawone malo m’mene anagonamo Ambuye. Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ake, kuti, wauka kwa akufa.’ Chotero mwamantha ndi chimwemwe chachikulu, akaziŵa nawonso athamanga napita.
Panthaŵiyi, Mariya wapeza Petro ndi Yohane, ndipo awasimbira nati: ‘Anachotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziŵa kumene anamuika iye.’ Pomwepo atumwi aŵiriwo achoka chothamanga. Yohane ngwaliŵiro—mwachiwonekere pokhala wamng’onopo—ndipo iye ayamba kufika kumandako. Panthaŵiyi akaziwo achokako kale, chotero palibe aliyense pamalopo. Akuŵerama, Yohane asunzumira m’mandamo nawona nsalu zokulungira, koma akhalabe kunja.
Pamene Petro afika, iye sakuzengereza koma apitirira naloŵa mkati. Awona nsalu zokulungira ziri pansi mkatimo ndiponso nsalu yomwe inagwiritsiridwa ntchito kukulunga mutu wa Yesu. Yaunjikidwa pamalo amodzi. Yohane nayenso tsopano aloŵa m’mandamo, ndipo iye akhulupirira lipoti la Mariya. Koma Petro ngakhale Yohane sakumvetsetsa kuti Yesu waukitsidwa, ngakhale kuti Iye anawauza kaŵirikaŵiri kuti Iye akatero. Ali odabwa, aŵiriwo abwerera kunyumba, koma Mariya, yemwe wabweranso kumanda, atsala.
Pakali pano, akazi ena afulumira kukauza ophunzira kuti Yesu waukitsidwa, monga momwe angelo awalamulira. Pamene iwo akuthamanga mofulumira ndithu, Yesu akumana nawo nati: “Tikuoneni.” Iwo agwera kumapazi ake namgwadira. Ndiyeno Yesu akuti: “Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko.”
Poyambirira, pamene chivomezi chinachitika ndipo angelo atawonekera, asirikali polonda anachita mantha nakhala ngati anthu akufa. Atagalamuka, mwamsanga analoŵa mumzinda nauza ansembe aakulu chomwe chidachitika. Pambuyo popangana upo ndi ‘akulu’ a Ayuda, chosankha chipangidwa cha kuyesayesa kuibisa nkhaniyo mwa kupatsa asirikali chiphuphu. Iwo alangizidwa kuti: ‘Kazinenani, kuti ophunzira ake anadza usiku, namuba uja m’mene ife tinali m’tulo.’
Popeza kuti asirikali Achiroma angalandire chilango chaimfa chifukwa chogona tulo pamalo awo antchito, ansembewo akulonjeza kuti: ‘Ndipo ngati ichi [chakuti munagona tulo] chidzamveka kwa kazembe, ife tidzamgwetsa mtima, ndipo tidzakukhalitsani opanda nkhaŵa.’ Popeza kuti mlingo wa chiphuphu ngwaukulu mowakhutiritsa, asirikaliwo achita monga momwe alangizidwira. Monga chotulukapo, lipoti lonama la kubedwa kwa mtembo wa Yesu likufalikira pakati pa Ayuda.
Mariya wa Magadala, yemwe watsalira kumandako, wagwidwa ndi chisoni. Kodi Yesu angakhale kuti? Aŵeramira kutsogolo kuti ayang’ane m’mandamo, iye awona angelo aŵiri ovala zoyera, omwe awonekanso! Mmodzi wakhala chakumutu ndi winayo chakumapazi kwa malo amene mtembo wa Yesu unagonapo. “Mkazi, uliranji?” iwo akufunsa.
‘Chifukwa anachotsa Ambuye ŵanga,’ Mariya akuyankha, ‘ndipo sindidziŵa kumene anamuika iye.’ Ndiyeno atembenuka nawona munthu wina yemwe abwereza funsolo kuti: “Mkazi uliranji?” Ndipo iyeyu afunsanso kuti: “Ufuna yani?”
Akumayesa munthuyo kukhala wosamalira munda umene muli mandawo, iye akunena kwa munthuyo nati: ‘Mbuye ngati mwamnyamula iye, ndiuzeni kumene mwamuika iye, ndipo ndidzamchotsa.’
‘Mariya!’ akutero munthuyo. Ndipo pomwepo adziŵa, mwa njira yozoloŵereka imene iye amalankhula naye, kuti ameneyo ndi Yesu. “Raboni!” (kutanthauza kuti ‘Mphunzitsi!’) iye afuula motero. Ndipo ndichisangalalo chosefukira, iye amkupatira. Koma Yesu akuti: “Usandikhudze, pakuti sindinatha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.”
Tsopano Mariya athamangira kumene atumwi ndi ophunzira anzake asonkhanako. Iye awonjezera chokumana nacho chake ku lipoti limene akazi enawo apereka kale lonena zakuwona Yesu woukitsidwayo. Chikhalirechobe, amuna amenewo, sanakhulupirire akazi oyambirirawo, mwachiwonekere sakumkhulupirira ngakhale Mariya. Mateyu 28:3-15; Marko 16:5-8; Luka 24:4-12; Yohane 20:2-18.
◆ Atapeza kuti manda ngopanda kanthu, kodi Mariya wa Magadala akuchitanji, ndipo kodi akazi enawo akhala ndi chokumana nacho chotani?
◆ Kodi Petro ndi Yohane akuchita motani atapeza kuti mandawo ngopanda kanthu?
◆ Kodi akazi enawo akukumana nchiyani panjira pamene akupita kukasimba kwa ophunzirawo za kuuka kwa Yesu?
◆ Kodi nchiyani chichitikira asirikali olonda, ndipo kodi ansembewo akuyankha motani ku lipoti lawo?
◆ Kodi nchiyani chikuchitika pamene Mariya wa Magadala ali yekha pa mandapo, ndipo kodi ophunzirawo akuyankha motani ku malipoti a akazi?