Yendanibe M’kuwunika ndi M’chikondi
Mfundo Zazikulu Zochokera m’Yohane Woyamba
YEHOVA ndiye Magwero a kuwunika ndi chikondi. Tiyenera kuyang’ana kwa Mulungu kaamba ka kuwunika kwauzimu. (Salmo 43:3) Ndipo chikondi chiri chimodzi cha zipatso za mzimu wake woyera.—Agalatiya 5:22, 23.
Kuwunika, chikondi, ndi nkhani zina zafotokozedwa m’kalata yoyamba youziridwa ya mtumwi Yohane, mwachiwonekere yolembedwa pafupifupi 98 C.E. mu Efeso kapena chapafupi. Chifukwa chachikulu choilembera chinali chakuti ichinjirize Akristu ku mpatuko ndikuwathandiza kupitirizabe kuyenda m’kuwunika. Popeza kuti timayang’anizana ndi zitokoso za chikondi chathu, chikhulupiriro, ndi umphumphu ku chowonadi, mosakaikira kuilingalira kalatayi kudzatipindulitsa.
‘Yendani m’Kuwunika’
Yohane anakumveketsa bwino kuti Akristu okhulupirika ayenera kuyenda m’kuwunika kwauzimu. (1:1–2:29) Iye anati: ‘Mulungu ndiye kuwunika, ndipo mwa iye monse mulibe mdima [mulibe choipa, chisembwere, bodza, kapena chodetsedwa].’ Chifukwa chakuti Akristu odzozedwa ndi mzimu ‘amayenda m’kuwunika,’ iwo ‘amayanjana’ ndi Mulungu, Kristu, ndi wina ndi mnzake. Iwo ayeretsedwanso ku uchimo ndi mwazi wa Yesu.
Kaya ndife Akristu odzozedwa okhala ndi chiyembekezo chakumwamba kapena tikuyembekezera moyo wamuyaya padziko lapansi, tidzapitirizabe kupindula ndi nsembe ya Yesu kokha ngati tikonda abale athu koma osati dziko. Tiyeneranso kupeŵa kusonkhezeredwa ndi ampatuko, onga ngati ‘okana Kristu,’ omwe amakana onse aŵiri Atate ndi Mwana. Ndipo tisaiŵale kuti moyo wosatha udzasangalalidwa kokha ndi awo omamatira ku chowonadi ndi ochita chilungamo.
Ana a Mulungu Amasonyeza Chikondi
Chotsatirapo Yohane anazindikiritsa ana a Mulungu. (3:1–4:21) Chenicheni nchakuti, iwo amachita chimene chiri cholungama. Iwo amamveranso malamulo a Yehova Mulungu ‘kuti akhulupirire dzina la Mwana wake Yesu Kristu, ndikukondana wina ndi mnzake.’
Munthu ‘womzindikira Mulungu’ amadziŵa za zifuno za Yehova ndi mmene chikondi Chake chimasonyezedwera. Izi ziyenera kumthandiza munthuyo kusonyeza chikondi. Ndithudi, ‘iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.’ Chikondi chaumulungu chinasonyezedwa pamene Mulungu ‘anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.’ Ngati Yehova anatikonda mokulira chotero, nafenso tiri ndi thayo lokondana wina ndi mnzake. Inde, yense wonena kuti akonda Mulungu ayeneranso kukonda mbale wake wauzimu.
Chikhulupiriro ‘Chimalilaka Dziko Lapansi’
Chikondi chimasonkhezera ana a Mulungu kusunga malamulo ake, koma iwo ‘amalilaka dziko lapansi’ kupyolera m’chikhulupiriro. (5:1-21) Chikhulupiriro chathu mwa Mulungu, m’Mawu ake, ndi mwa Mwana wake chimatitheketsa ‘kulilaka dziko lapansi’ mwakukana kulingalira kwake kolakwa ndi njira zake ndi mwakusunga malamulo a Yehova. Mulungu wapatsa ‘olilaka dziko lapansi’ chiyembekezo cha moyo wamuyaya ndipo amamva mapemphero awo omwe amagwirizana ndi chifuniro chake. Popeza kuti ‘yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu’ sachita tchimo, Satana samamgwira munthu woteroyo. Koma onse aŵiri odzozedwa ndi atumiki a Yehova okhala ndi ziyembekezo za padziko lapansi ayenera kukumbukira kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.”
[Bokosi/Chithunzi patsamba 29]
Nsembe Yachiombolo: Yesu ndiye ‘chiombolo cha machimo athu [a atsatiri ake odzozedwa]; koma osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi,’ anthu onse. (1 Yohane 2:2) Imfa yake inali ‘chiombolo’ (Chigiriki, hi·la·smosʹ, kutanthauza “njira yotonthozera” “chitetezo”) koma osati m’lingaliro loziziritsa kupwetekedwa kwa Mulungu. Mmalomwake, nsembe ya Yesu inatonthoza, kapena kukhutiritsa zofuna za chilungamo chaumulungu changwiro. Motani? Mwakupereka maziko olunjika ndi olungama kaamba ka chikhululukiro cha machimo, kotero kuti Mulungu “akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye [wobadwa muuchimo] amene akhulupirira Yesu.” (Aroma 3:23-26; 5:12) Mwakupereka njira yokhutiritsira kotheratu kaamba ka machimo a anthu, nsembe ya Yesu inachipangitsa kukhala chothekera, kapena choyanjika kwa anthu kufuna ndikulandira kubwezeretsedwa ku unansi wabwino ndi Yehova. (Aefeso 1:7; Ahebri 2:17) Tonsefe tiyenera kukhala oyamikira chotani nanga kaamba ka ichi!