Lipoti la Olengeza Ufumu
Mayendedwe Omwe Amakometsera Uminisitala Wathu Wachikristu
MTUMWI Petro akuchenjeza Akristu kuti: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma.” (1 Petro 2:12) Mtumwi Paulo akusonyeza kuti mwa mayendedwe athu abwino, ‘timakometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m’zinthu zonse.’ (Tito 2:10) Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse ziri ndi dzina labwino kaamba ka mayendedwe abwino. Tawonani zitsanzo zina.
Kukondweretsedwa ndi Mayendedwe Abwino kwa Mphunzitsi
◻ Ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ku Costa Rica ikusimba kuti chiŵerengero chachikulu cha achichepere m’dzikolo amakhazikitsa chitsanzo chabwino. Mbale wina akusimba chimene chinamkokera ku chowonadi. Iye akunena kuti: “Chimene chinandikopa kwambiri chinali mayendedwe okoma a ponse paŵiri achichepere ndi achikulire koma makamaka achichepere. Pamene ndinkagwira ntchito monga mphunzitsi, ndinali ndi mwaŵi wakuwonetsetsa Mboni pasukulu panga. Ndipo popeza kuti ndinkakhala moyandikana ndi banja la Mboni za Yehova, ndinawonetsetsanso mayendedwe a ana kumeneko.
“Sindikanachitira mwina koma kuwona kusiyana pakati pa ophunzira amene anali Mboni ndi ophunzira ena m’sukulu langa. Mboni zinali kufika mofulumira nthaŵi zonse ndipo zodzisungira, sizinanene bodza, ndipo nthaŵi zonse zinachita ntchito yawo yopatsidwa. Ndiponso ndinawona kuti izo zinali zowona mtima polemba mayeso, ngakhale kuti ophunzira ena mwachisawawa anachita chinyengo. Kuwonjezerapo, izo zinali zofatsa kwambiri ndi zaulemu kwa ine monga mphunzitsi wawo. Pokondweretsedwa ndi Mboni zachicheperezo kusukulu ndi kunyumba komwe ndimakhala, ndinayamba kufufuza chipembedzo chimenechi ndipo pomalizira pake ndinalandira chowonadi.”
Mayendedwe Achikristu pa Msonkhano Akhala ndi Zotulukapo Zabwino
◻ Mmodzi wa Mboni za Yehova mumpingo wina m’dera lakumadzulo kwa El Salvador anafunitsitsa kugaŵana mbiri yabwino ya Ufumu ndi abale ake aŵiri akuthupi. Mmodzi anamvetsera nayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Mbale winayo anali wa tchalitchi cha Evanjeliko chotchedwa Prince of Peace, ndipo anati kwa mbale wake: “Usamandilankhuza; ukutumikira maubwino a Mdyerekezi.”
Pamene nthaŵi ya msonkhano wachigawo inafika, yemwe anali kuphunzira anaitanira mbale wake kupita naye ku msonkhano. Mbaleyo anati: “Chabwino, ndidzapita nawe; ndikupita kokha kukawona pamene ndingapeze chifukwa ndi Mboni.” Abale aŵiriwo anapezeka ku msonkhano pamodzi. Chiŵerengero chachikulu ndi dongosolo labwino pamsonkhanowo zinakondweretsa m’Evanjelikoyo, yemwe anati sanawonepo nkalelonse chirichonse chofanana nacho. Atafika kunyumba, iye anauza mbale wake kuti: “Gwira m’manja.” Mbale wake anafunsa kuti: “Kodi nkwanji?” Yankho linali lakuti: “Tangondipatsa dzanja lako.” Anagwirana chanza, ndipo mchimwene yemwe anali wa tchalitchi cha Evanjeliko anati: “Kuchokera lero kunkabe mtsogolo ndidzaphunzira ndi Mboni za Yehova. Ndithudi, sindinadziŵe chimene ndinali kuphonya.” Tsopano iyenso ndi wolengeza mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu wokangalika ndi wachangu.