Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 7/15 tsamba 12-17
  • Mkondweretseni Yehova Mwakusonyeza Kukoma Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mkondweretseni Yehova Mwakusonyeza Kukoma Mtima
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chimene Kukoma Mtima Kuli
  • Peŵani Kukoma Mtima Kolakwika
  • Kukoma Mtima Kugwirizanitsidwa ndi Chikondi
  • Mphotho za Kukoma Mtima
  • Yamikirani Kukoma Mtima Kosatiyenerera kwa Mulungu
  • Anthu a Mulungu Ayenera Kukonda Khalidwe la Kukoma Mtima
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kukhala Okoma Mtima M’dziko Losaganiziranali
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kukoma Mtima Ndi khalidwe Limene Limasonyezedwa M’mawu ndi Zochita
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • “Lamulo la Kukoma Mtima Kosatha” Lizikutsogolerani
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 7/15 tsamba 12-17

Mkondweretseni Yehova Mwakusonyeza Kukoma Mtima

‘Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda [kukoma mtima, “NW”] ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?’​—MIKA 6:8.

1. Kodi nchifukwa ninji siziyenera kutidabwitsa kuti Yehova amayembekezera anthu ake kusonyeza kukoma mtima?

YEHOVA amayembekezera anthu ake kusonyeza kukoma mtima. Ichi sichiyenera kutidabwitsa. Mulungu iyemwini ali wokoma mtima kwa onse, ngakhale kwa anthu oipa osayamika. Ponena za chimenechi Yesu Kristu anauza ophunzira ake kuti: ‘Koma takondanani nawo adani anu, ndi kuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa iye achitira zokoma anthu osayamika ndi oipa. Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo.’​—Luka 6:35, 36.

2. Kodi ndimafunso otani onena za kukoma mtima amene tifunikira kuwalingalira?

2 Monga momwe Mika 6:8 akulengezera, amene amayenda ndi Mulungu ayenera ‘kukonda kukoma mtima.’ Mwachiwonekere, Yehova amakondweretsedwa pamene atumiki ake akonda kukoma mtima ndi kukusonyeza mwanjira yochokera kumtima. Koma kodi kukoma mtima nchiyani? Kodi ndi mapindu otani omwe amadza mwakukusonyeza? Ndipo kodi mkhalidwe umenewu ungasonyezedwe motani?

Chimene Kukoma Mtima Kuli

3. Kodi mungakulongosole motani kukoma mtima?

3 Kukoma mtima ndimkhalidwe wa kukhala ndi chikondwerero chokangalika mwa ena. Kumasonyezedwa mwa machitidwe othandiza ndi mawu olingalira ena. Kukhala wokoma mtima kumatanthauza kuchita zabwino mmalo mwa chirichonse chovulaza. Munthu wokoma mtima amakhala waubwenzi, wofatsa, wachifundo, ndi wachisomo. Iye amakhala ndi mkhalidwe woolowa manja ndi wolingalira kulinga kwa ena. Ndipo kukoma mtima ndiko mbali ya chovala chophiphiritsira cha Mkristu wowona aliyense, popeza kuti Paulo anafulumiza kuti: ‘Valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima.’​—Akolose 3:12.

4. Kodi ndimotani mmene Yehova watsogolera m’kusonyeza kukoma mtima kulinga kwa anthu?

4 Yehova amatsogolera m’kusonyeza kukoma mtima. Monga momwe mtumwi Paulo ananenera, nchifukwa chakuti ‘kukoma mtima, ndi chikondi cha pa anthu, cha Mpulumutsi wathu Mulungu zidawoneka’ kuti ‘monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a mzimu woyera.’ (Tito 3:4, 5) Mulungu amayeretsa, kapena ‘kutsuka,’ Akristu odzozedwa m’mwazi wa Yesu, akugwiritsira ntchito mtengo wa nsembe yadipo ya Kristu kaamba ka iwo. Iwo amapangidwanso atsopano kupyolera mumzimu woyera, kukhala “wolengedwa watsopano” monga ana obadwa ndi mzimu a Mulungu. (2 Akorinto 5:17) Ndithudi, kukoma mtima kwa Mulungu ndi chikondi kaamba ka anthu zimapitanso kwa ‘khamu lalikulu’ lamitundu yonse, amene ‘atsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.’ (Chibvumbulutso 7:9, 14; 1 Yohane 2:1, 2) Ndiponso, odzozedwa ndi khamu lalikulu, lokhala ndi chiyembekezo chapadziko lapansi, onse ali pansi pa goli la “kukoma mtima” la Yesu.​—Mateyu 11:30, NW.

5. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuyembekezera otsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu kusonyeza kukoma mtima kwa ena?

5 Kukoma mtima kulinso mbali ya chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito. Paulo ananena kuti: ‘Chipatso cha mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.’ (Agalatiya 5:22, 23) Pamenepo, kodi tiyenera kuyembekezeranji ponena za amene amatsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu? Ndithudi, iwo ayenera kusonyeza kukoma mtima kwa ena.

6. Kodi kukoma mtima kuyenera kupangitsa akulu ndi Akristu ena kuchita mwanjira yotani?

6 Kukoma mtima kungasonyezedwe m’njira zambiri. Timasonyeza kukoma mtima pamene tikhala achifundo. Mwachitsanzo, akulu Achikristu amakhala okoma mtima pamene asonyeza chifundo kwa wochimwa wolapa ndi kufuna kumthandiza mwauzimu. Mkhalidwe wopatsidwa ndi Mulungu wa kukoma mtima umapangitsa oyang’anira kukhala oleza mtima, olingalira ena, achifundo, ndi odekha. Kumawasonkhezera ‘kuchitira gulu mwachifundo.’ (Machitidwe 20:28, 29, NW) Kwenikweni, chipatso cha mzimu cha kukoma mtima chiyenera kuchititsa Akristu onse kukhala achifundo, oleza mtima, olingalira ena, achisoni, aubwenzi, ndi ochereza.

Peŵani Kukoma Mtima Kolakwika

7. Kodi nchifukwa ninji munganene kuti kukoma mtima kolakwika ndichifooko?

7 Anthu ena amalingalira kukoma mtima kukhala chifooko. Amalingalira kuti munthu ayenera kukhala wouma mtima, nthaŵi zina ngakhale wamwano, kotero kuti ena achite chidwi ndi nyonga yake. Koma kwanenedwa bwino lomwe kuti “mwano ndiwo kunamizira mphamvu kwa munthu wofooka.” Kwenikwenidi, ponse paŵiri kukhala wokoma mtima weniweni ndi kupeŵa kukoma mtima kolakwika kumalira nyonga yeniyeni. Kukoma mtima kumene kuli chipatso cha mzimu wa Mulungu sikuli kofooka, maganizo ololera molakwa mkhalidwe woipa. Mmalomwake, kukoma mtima kolakwika ndiko chifooko chimene chimachititsa munthu kulolera kuchita cholakwa.

8. (a) Ponena za ana ake aamuna, kodi Eli anakhaladi wofeŵa motani? (b) Kodi nchifukwa ninji akulu ayenera kuchenjera motsutsana ndi kugonja ku kukoma mtima kolakwika?

8 Eli, mkulu wansembe wa Israyeli anali wofeŵa polangiza ana ake aamuna, Hofeni ndi Pinehasi, omwe anatumikira monga ansembe pa chihema. Posakhutiritsidwa ndi mbali ya nsembe yogaŵiridwa kwa iwo ndi Chilamulo cha Mulungu, iwo ankalamula kalinde kutengako nyama yaiŵisi kwa wopereka nsembe mafuta a nsembeyo asanatenthedwe pa guwa. Ana a Eli anachitanso chisembwere ndi akazi otumikira pa chipata cha chihema. Komabe, mmalo mwakuchotsa Hofeni ndi Pinehasi paudindo, Eli anangowadzudzula mopepuka, akulemekeza ana ake kuposa Mulungu. (1 Samueli 2:12-29) Nzosadabwitsa kuti ‘masiku aja mawu a Yehova anamveka kamodzi kamodzi’! (1 Samueli 3:1) Chotero akulu Achikristu sayenera kugonja ku malingaliro onyenga kapena kusonyeza kukoma mtima kolakwika kumene kungaike paupandu uzimu wa mpingo. Kukoma mtima kwenikweni sikulephera kuwona mawu ndi machitidwe oipa amene amalakwira miyezo ya Mulungu.

9. (a) Kodi ndikaimidwe kamaganizo kotani kamene kangatithandize kupeŵa kugonja ku kukoma mtima kolakwika? (b) Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera nyonga pochita ndi akatswiri achipembedzo ampatuko?

9 Ngati titi tipeŵe kusonyeza kukoma mtima kolakwika, tiyenera kupempherera chithandizo cha Mulungu kuti tikhale ndi nyonga monga momwe zinawonekera m’mawu a wamasalmo akuti: ‘Mundichokere ochita zoipa inu; kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.’ (Salmo 119:115) Tifunikiranso kutsatira chitsanzo cha Yesu Kristu, amene sanakhalepo waliŵongo la kusonyeza kukoma mtima kolakwika. Kwenikweni, Yesu anali chitsanzo chenicheni cha kukoma mtima kowona. Mwachitsanzo, ‘iye, powona makamuwo, anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.’ Chifukwa chake, anthu owona mtima anadzimva omasuka kumfikira Yesu, ngakhale kubweretsa ana awo aang’ono kwa iye. Ndipo tangoyerekezerani kukoma mtima ndi chisoni zomwe anasonyeza pamene ‘anatiyangata [tianato, NW], natidalitsa’! (Mateyu 9:36; Marko 10:13-16) Ngakhale kuti Yesu anali wokoma mtima, iye anali wolimba pachimene chinali cholondola pamaso pa Atate wake wakumwamba. Yesu sanalolere konse choipa; iye anali ndi nyonga yopatsidwa ndi Mulungu ya kudzudzula atsogoleri achipembedzo onyenga. Pa Mateyu 23:13-26, iye anabwerezabwereza chidzudzulo chakuti: “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga!” Nthaŵi iriyonse, Yesu anapereka chifukwa cha chiweruzo chaumulungu.

Kukoma Mtima Kugwirizanitsidwa ndi Chikondi

10. Kodi ndimotani mmene ophunzira a Yesu amasonyezera kukoma mtima ndi chikondi kwa okhulupirira anzawo?

10 Ponena za otsatira ake, Yesu anati: ‘Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.’ (Yohane 13:35) Ndipo kodi ndimbali iti ya chikondicho imene imazindikiritsa ophunzira owona a Yesu? Paulo anati: ‘Chikondi chikhala chilezere, chiri chokoma mtima.’ (1 Akorinto 13:4) Kukhala woleza mtima ndi wokoma mtima kumatanthauza kuti tiyenera kupirira ndi zophophonya ndi zolakwa za ena, monga momwedi Yehova amachitira mokoma mtima. (Salmo 103:10-14; Aroma 2:4; 2 Petro 3:9, 15) Chikondi Chachikristu ndi kukoma mtima zimawonekeranso pamene zovuta zigwera okhulupirira anzathu kwinakwake padziko lapansi. Pochitapo kanthu koposa ndi “kukoma mtima kwaumunthu,” Akristu kulikonse amasonyeza chikondi cha paubale mwakupereka zinthu zakuthupi kuthandiza olambira a Yehova oterowo.​—Machitidwe 28:2, NW.

11. Kunena mogwirizana ndi Malemba, kodi kukoma mtima kwachikondi nchiyani?

11 Kukoma mtima kumagwirizanitsidwa ndi chikondi m’liwu lakuti “kukoma mtima kwachikondi,” (NW) logwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri m’Malemba. Uku ndiko kukoma mtima kochokera m’chikondi chokhulupirika. Nauni Yachihebri yomasuliridwa “kukoma mtima kwachikondi” (cheʹsedh) imaphatikizapo zoposa lingaliro lokoma. Ndikukoma mtima kumene kumamamatira mwachikondi ku chinthucho kufikira pamene chifuno chake chikwaniritsidwa. Kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova, kapena chikondi chokhulupirika, kumasonyezedwa m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, kumasonyezedwa m’machitidwe ake a kupulumutsa ndi kutetezera.​—Salmo 6:4; 40:11; 143:12.

12. Pamene atumiki a Yehova apempherera chithandizo kapena chipulumutso, kodi angakhale otsimikizira ponena za chiyani?

12 Nkosadabwitsa kuti kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova kumakokera anthu kwa iye! (Yeremiya 31:3) Pamene atumiki okhulupirika a Mulungu afunikira chipulumutso kapena chithandizo, amadziŵa kuti kukoma mtima kwake kwachikondi kulidi chikondi chokhulupirika, kumene sikudzawagwiritsa mwala. Chotero, iwo angapemphere mwachikhulupiriro, monga momwe anachitira wamasalmo yemwe anati: ‘Koma ine ndakhulupira pa [kukoma mtima kwachikondi kwanu, NW]; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.’ (Salmo 13:5) Popeza kuti chikondi cha Mulungu nchokhulupirika, atumiki ake samakhulupirira m’kukoma mtima kwake kwachikondi mwachabe. Pamene apemphera kaamba ka chithandizo chake kapena chipulumutso, iwo ali ndi chitsimikizo ichi: ‘Yehova sadzasiya anthu ake, ndipo sadzataya cholandira chake.’​—Salmo 94:14.

Mphotho za Kukoma Mtima

13, 14. Kodi nchifukwa ninji munthu wokoma mtima amakhala ndi mabwenzi okhulupirika?

13 Potsanzira Yehova, atumiki ake ‘amachitira yense mnzake chifundo ndi kukoma mtima.’ (Zekariya 7:9; Aefeso 5:1) ‘Chotikondetsa munthu ndicho kukoma mtima kwake [kwachikondi, NW]’ ndipo munthu wosonyeza mkhalidwe umenewu amatuta mphotho zolemeretsa. (Miyambo 19:22) Kodi zina za zimenezi nzotani?

14 Kukoma mtima kumatipangitsa kukhala ochenjera ndipo kumatithandiza kusunga unansi wabwino ndi ena. Munthu wochenjera amanena ndi kuchita zinthu kapena kusamalira mikhalidwe yovuta mwanjira zolingalira ena ndi zosakwiitsa. Pamene kuli kwakuti “wankhanza” amaingidwa, ‘[wa kukoma mtima kwachikondi, NW] achitira moyo wake zokoma.’ (Miyambo 11:17) Anthu amapeŵa munthu wankhanza koma amakopeka kwa amene awasonyeza kukoma mtima kwachikondi. Chotero, munthu wokoma mtima amakhala ndi mabwenzi okhulupirika.​—Miyambo 18:24.

15. Kodi kukoma mtima kungakhale ndi chiyambukiro chotani m’nyumba yogaŵikana mwachipembedzo?

15 Mkazi Wachikristu wokhala ndi mwamuna wosakhulupirira angamkopere ku chowonadi cha Mulungu mwa mkhalidwe wonga kukoma mtima. Mkaziyo asanaphunzire chowonadi ndi kuvala “umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chenicheni ndi kukhulupirika,” iye angakhale anali wosakoma mtima, ngakhale wandewu. (Aefeso 4:24, NW) Ngati mwamuna wake anadziŵako miyambi inayake, angavomereze kuti ‘makangano a mkazi ndiwo kudonthadonthabe’ ndikuti ‘kukhala m’chipululu kufunika kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wong’ung’udza.’ (Miyambo 19:13; 21:19) Koma tsopano mkhalidwe wachiyero wa mkazi Wachikristuyo ndi ulemu waukulu, limodzi ndi mikhalidwe monga kukoma mtima, ingathandize kukopa mnzake wamuukwati ku chikhulupiriro chowona. (1 Petro 3:1, 2) Inde, ichi chingakhale mphotho ya kukoma mtima kwake.

16. Kodi ndimotani mmene tingapindulire ndi kukoma mtima kosonyezedwa kwa ife?

16 Kukoma mtima kosonyezedwa kwa ife kungakhale kopindulitsa mwakutipangitsa kuwonjezeka m’chifundo ndi kukhululukira. Mwachitsanzo, ngati tinafunikira chithandizo chauzimu ndipo tinachitiridwa mwanjira yokoma mtima ndi yachifatso, kodi zimenezo sizikatisonkhezera kufuna kuchitira ena mwanjira yofananayo? Eya, kuchitiridwa kokoma mtima ndi kwachifatso kungayembekezeredwe kwa amuna oyeneretsedwa mwauzimu, popeza kuti Paulo analemba kuti: ‘Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze woteroyo mu mzimu wachifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.’ (Agalatiya 6:1) Akulu oikidwa amalankhula mwachifatso ndi mokoma mtima pamene akufuna kuthandiza okhulupirira anzawo olakwa. Komabe, kaya ngati tinalandirapo chithandizo cha mtundu umenewo kapena ayi, kodi Mulungu amayembekezeranji kwa onse omtumikira? Akristu onse ayenera kusonyeza ena kukoma mtima ndipo ayenera kulabadira uphungu wa Paulo wakuti: ‘Mukhalirane okoma wina ndi mnzake, amtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.’ (Aefeso 4:32) Ndithudi, ngati tinakhululukidwa ndi winawake kapena tinathandizidwa m’vuto lauzimu mwanjira yokoma mtima, ichi chiyenera kuwonjezera ukulu wa kukhululukira kwathu, chifundo, ndi kukoma mtima.

Yamikirani Kukoma Mtima Kosatiyenerera kwa Mulungu

17. Popeza kuti tinabadwa ochimwa, kodi ndikukoma mtima kuti kumene tiyenera kuyamikira mwapadera?

17 Popeza kuti tonsefe tinabadwa ochimwa oweruzidwira ku imfa, pali kukoma mtima kumene tiyenera kukuyamikira kwenikweni. Ndiko kukoma mtima kosatiyenerera kwa Yehova Mulungu. Kuti ochimwa amasulidwe ku chiweruzo cha imfa ndikuti alengezedwe olungama kuli kukoma mtima kosatiyenerera kotheratu. Paulo, yemwe anatchula kukoma mtima kosatiyenerera kwa Mulungu nthaŵi 90 m’makalata ake 14 ouziridwa mwaumulungu, anauza Akristu ku Roma wakale kuti: ‘Onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu; ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi [kukoma mtima kosatiyenerera, NW], mwa chiwombolo cha mwa Kristu Yesu.’ (Aroma 3:23, 24) Ha, ndimotani nanga mmene tiyenera kuyamikira kukoma mtima kosatiyenerera kosonyezedwa ndi Yehova Mulungu!

18, 19. Kodi ndimotani mmene tingapeŵere kuphonya chifuno cha kukoma mtima kosatiyenerera kwa Mulungu?

18 Mwakukhala osayamikira, tikhoza kuphonya chifuno cha kukoma mtima kosatiyenerera kwa Mulungu. Ponena za chimenechi, Paulo anati: ‘Chifukwa chake tiri atumiki m’malo mwa Kristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m’malo mwa Kristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu. Ameneyo sanadziŵa uchimo anamyesera uchimo m’malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa iye. Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire [kukoma mtima kosatiyenerera kwa, NW] Mulungu kwachabe inu, pakuti anena, [pa Yesaya 49:8, Septuagint]: M’nyengo yolandirika ndinamva iwe, ndipo m’tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza; tawonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, tawonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso; osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chirichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe; koma m’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu.’ (2 Akorinto 5:20–6:4) Kodi Paulo anatanthauzanji?

19 Akristu odzozedwa ali oimira a Kristu, ndipo a khamu lalikulu ali athenga ake. Pamodzi amafulumiza anthu kuyanjanitsidwanso kwa Mulungu kotero kuti apeze chipulumutso. Paulo sanafune kuti wina aliyense alandire kukoma mtima kosatiyenerera kwa Yehova Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu ndi kuphonya chifuno chake. Zimenezo zikhoza kuchitika kwa ife ngati tilephera kugwira ntchito imene kukoma mtima kosatiyenerera kumeneko kunatiyeneretsa. Pokhala ndi maunansi aubwenzi ndi Mulungu monga oyanjanitsidwanso kwa iye, sitidzalandira mwachabe kukoma mtima kwake kosatiyenerera ngati tichita ‘utumiki wa chiyanjanitso; ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Kristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa iye yekha.’ (2 Akorinto 5:18, 19) Tidzakhala tikusonyezanso ena kukoma mtima kwakukulu mwakuwathandiza kuyanjanitsidwanso kwa Mulungu.

20. Kodi chotsatira chimene tidzasanthula nchiyani?

20 Atumiki a Yehova amagwiritsira ntchito nthaŵi yawo ndi chuma m’machitidwe a kukoma mtima pamene akuyesayesa kuthandiza ena mwauzimu kupyolera muuminisitala Wachikristu. Koma kodi tingaphunzirenji ku zitsanzo za m’Malemba za kukoma mtima kosonyezedwa? Chotsatira tiyeni tisanthule zina za zimenezi ndi kupenda njira zina zokondweretsera Yehova mwakusonyeza kukoma mtima.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi kukoma mtima nchiyani?

◻ Kodi ndimotani mmene tingapeŵere kugonja ku kukoma mtima kolakwika?

◻ Kodi nchifukwa ninji anthu a Yehova angakhulupirire kukoma mtima kwake kwachikondi?

◻ Kodi mphotho zina za kukoma mtima nzotani?

◻ Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tisonyeze chifuno cha kukoma mtima kosatiyenerera kwa Mulungu?

[Chithunzi patsamba 13]

Kukoma mtima kumapangitsa akulu Achikristu kukhala oleza mtima, olingalira ena, ndi achisoni

[Chithunzi patsamba 15]

Kukoma mtima kwa mkazi Wachikristu kungathandize kukopa mwamuna wake ku chikhulupiriro chowona

[Chithunzi patsamba 17]

Tingasonyeze ena kukoma mtima kwakukulu koposa mwakuwathandiza kuyanjanitsidwanso kwa Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena