Kukoma Mtima Ndi Khalidwe Limene Limasonyezedwa M’mawu ndi Zochita
MUNTHU akasonyezedwa kukoma mtima amakhala wosangalala komanso amalimbikitsidwa kwambiri. Aliyense amayamikira akaona kuti munthu wina amamuganizira. Koma kodi tingatani kuti tikhale ndi khalidwe labwinoli?
Munthu wokoma mtima amaganizira kwambiri za anthu ena ndipo amasonyeza khalidweli pa zimene amalankhula komanso kuchita. Sikuti munthu amangolankhula modzichepetsa komanso mwaulemu kuti anthu amuone. Munthu amasonyeza kukoma mtima chifukwa choti amakonda anthu komanso amazindikira mmene anthuwo akumvera mumtima mwawo. Kukoma mtima kotereku ndi khalidwe limene mzimu wa Mulungu umatulutsa ndipo Akhristufe timalimbikitsidwa kukhala nalo. (Agal. 5:22, 23) Popeza tiyenera kukhala okoma mtima, tiyeni tikambirane mmene Yehova ndi Yesu amasonyezera khalidweli ndiponso zimene tingachite kuti tiziwatsanzira.
YEHOVA NDI WOKOMA MTIMA KWA ANTHU ONSE
Yehova ndi wokoma mtima ndipo amaganizira anthu onse kuphatikizapo ‘osayamika ndi oipa.’ (Luka 6:35) Mwachitsanzo, Yehova “amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mat. 5:45) Ngakhale anthu amene savomereza kuti Mulungu ndi amene analenga zinthu, amalandira zinthu zowathandiza kuti akhale ndi moyo n’kumasangalala.
Zimene Yehova anachitira Adamu ndi Hava zimasonyeza kuti iye ndi wokoma mtima kwambiri. Mwachitsanzo, iwo atachimwa “anadzisokera masamba a mkuyu n’kupanga zovala zomangira m’chiuno.” Koma Yehova anazindikira kuti anthuwo adzafunika zovala zabwino kuti azikhala bwinobwino pa nthaka imene inatembereredwa n’kumera “minga ndi zitsamba zobaya.” Choncho Yehova anawathandiza powapangira “zovala zazitali zachikopa.”—Gen. 3:7, 17, 18, 21.
Ngakhale kuti Yehova amasonyeza kukoma mtima kwa “anthu oipa ndi abwino,” iye amafunitsitsa kusonyeza khalidweli kwa atumiki ake okhulupirika. Mwachitsanzo, m’masiku a mneneri Zekariya, mngelo wina anamva chisoni ataona kuti ntchito yomanganso kachisi ku Yerusalemu yaima. Yehova atamvetsera nkhawa za mngeloyo, anamuuza “mawu abwino ndiponso olimbikitsa.” (Zek. 1:12, 13) Yehova anachitanso chimodzimodzi ndi mneneri Eliya. Pa nthawi ina, mneneriyu anakhumudwa kwambiri moti anapempha Yehova kuti angomupha. Yehova anazindikira mmene Eliya ankamvera mumtima mwake ndipo anatumiza mngelo kuti akamulimbikitse. Iye anatsimikiziranso mneneriyu kuti sanali yekha. Eliya atalimbikitsidwa komanso kuthandizidwa anapitiriza utumiki wake. (1 Maf. 19:1-18) Pa atumiki a Mulungu onse, kodi ndi ndani amene ali pa nambala wani pa nkhani yotsanzira kukoma mtima kwa Yehova?
YESU NDI WOKOMA MTIMA KWAMBIRI
Yesu ali padzikoli ankadziwika kuti ndi wokoma mtima komanso woganizira anthu ena. Iye sanali wankhanza kapena wotopetsa. Paja ananena mokoma mtima kuti: “Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani . . . pakuti goli langa ndi lofewa.” (Mat. 11:28-30) Anthu ataona kuti Yesu ndi wokoma mtima ankamutsatira kulikonse kumene ankapita. Popeza Yesu ‘ankawamvera chifundo,’ anawadyetsa, kuwachiritsira odwala komanso kuwaphunzitsa “zinthu zambiri” zokhudza Atate ake.—Maliko 6:34; Mat. 14:14; 15:32-38.
Yesu ankawamvetsa anthu komanso kuzindikira mmene akumvera mumtima mwawo, ndipo zimenezi zimasonyeza kuti anali wokoma mtima. Iye ankalandira anthu mokoma mtima ngakhale atamupempha kuti awachitire zinthu zooneka kuti n’zovuta. (Luka 9:10, 11) Mwachitsanzo, iye sanakalipire mzimayi wodetsedwa yemwe anapita mwamantha kukagwira chovala chake kuti achire matenda ake oopsa. (Lev. 15:25-28) Yesu anamvera chisoni mayiyu chifukwa anadwala matenda akewo kwa zaka 12 ndipo anamuuza kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere, matenda ako aakuluwo atheretu.” (Maliko 5:25-34) Apatu Yesu anasonyeza kukoma mtima kwambiri.
MUNTHU WOKOMA MTIMA AMATHANDIZA ANTHU
M’zitsanzo zimene takambiranazi, taona kuti zochita za munthu n’zimene zimasonyeza kuti ndi wokoma mtima. Fanizo la Yesu la Msamariya wachifundo limasonyeza bwino zimenezi. Ngakhale kuti Ayuda ndi Asamariya sankagwirizana, Msamariya wamufanizoli anamvera chisoni munthu amene anafwambidwa n’kusiyidwa atatsala pang’ono kufa. Kukoma mtima kwake kunamuchititsa kuti amuthandize. Anasamalira mabala ake n’kupita naye kumalo ogona alendo. Msamariyayo anapereka ndalama kwa mwini wa malo ogonawo kuti asamalire munthu wovulalayo ndipo analonjeza kuti ngati pangafunike ndalama zowonjezera adzalipira.—Luka 10:29-37.
Koma munthu wokoma mtima amalankhulanso mawu abwino ndi olimbikitsa. M’pake kuti Baibulo limanena kuti “Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.” (Miy. 12:25) Tikakhala okoma mtima komanso abwino, tikhoza kuuza anthu mawu olimbikitsa moti anthuwo angayambe kumva bwino mumtima mwawo.a Mawu oterewa amasonyeza kuti timawaganizira anzathuwo. Munthu akalimbikitsidwa zimamuthandiza kuti apirire mayesero amene angakumane nawo.—Miy. 16:24.
TINGATANI KUTI TIKHALE OKOMA MTIMA?
Popeza tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, aliyense akhoza kusonyeza khalidwe la kukoma mtima. (Gen. 1:27) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mkulu wa asilikali dzina lake Yuliyo amene anatenga Paulo kupita naye ku Roma. Baibulo limanena kuti iye “anakomera mtima kwambiri Paulo ndipo anamulola kupita kwa mabwenzi ake kuti akamusamalire.” (Mac. 27:3) Pa ulendo womwewu, anthu apachilumba cha Melita anasonyezanso “kukoma mtima kwapadera” kwa Paulo ndi anzake pamene chombo chinawaswekera. Anthuwo anafika pokoleza moto kuti opulumuka panyanjawo awothe. (Mac. 28:1, 2) Zimene anthuwa anachita zinali zabwino ndithu, koma kuti munthu akhaledi wokoma mtima amafunika kuchita zambiri.
Kuti tisangalatse Mulungu, tiyenera kukhala okoma mtima nthawi yonse ya moyo wathu. N’chifukwa chake Yehova amatiuza kuti ‘valani kukoma mtima.’ (Akol. 3:12) N’zoona kuti si zophweka kukhala okoma mtima nthawi zonse. Ena amalephera kukhala okoma mtima chifukwa cha manyazi, mantha, kutsutsidwa kapena kamtima kodzikonda. Koma tikamadalira mzimu wa Mulungu komanso kutsanzira Yehova pa nkhaniyi, tikhoza kukhala okoma mtima.—1 Akor. 2:12.
Kodi tingadziwe bwanji zimene tiyenera kusintha kuti tikhale okoma mtima kwambiri? Ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimamvetsera mwachifundo munthu akamandilankhula? Kodi ndimazindikira zimene munthu wina akufunikira? Ndi liti pamene ndinasonyeza kukoma mtima kwa munthu woti si wachibale kapena mnzanga?’ Ndi bwino kuyesetsa kuti tizidziwa bwino anthu amene timakhala nawo, makamaka mumpingo. Tikatero tidzazindikiranso mmene zinthu zilili pa moyo wawo komanso zimene akusowa. Kenako tiziwachitira zinthu zabwino zimene ifeyo tikanafuna kuchitiridwa zikanakhala kuti mavuto awowo agwera ifeyo. (Mat. 7:12) Pomaliza, tiyenera kudziwa kuti Yehova adzatidalitsa tikamayesetsa kukhala okoma mtima komanso tikamamupempha kuti atithandize kukhala ndi khalidweli.—Luka 11:13.
ANTHU AMAKOPEKA NDI MUNTHU WOKOMA MTIMA
Paulo anatchula zinthu zimene zinkathandiza anthu kudziwa kuti iye ndi mtumiki wa Mulungu ndipo khalidwe lina limene anatchula ndi ‘kukoma mtima.’ (2 Akor. 6:3-6) Anthu ankakopeka ndi uthenga wa Paulo chifukwa choti iye ankawaganizira, kuwalankhula molimbikitsa komanso kuwachitira zinthu zabwino. (Mac. 28:30, 31) Anthu akhozanso kukopeka ndi choonadi akaona kuti ndife okoma mtima. Tikamasonyeza kukoma mtima ngakhale kwa anthu amene amatitsutsa tingafewetse mtima wawo moti amasiya kudana nafe. (Aroma 12:20) Pakapita nthawi, akhoza kukopeka ndi uthenga wa m’Baibulo.
M’paradaiso, anthu oukitsidwa adzasangalala kwambiri kuona kuti akuchitiridwa zinthu mokoma mtima kwambiri ndipo kwa ena kadzakhala koyamba kuona zimenezi. Poyamikira zimene akuchitiridwa, nawonso akhoza kuyamba kukomera mtima anzawo. Aliyense amene azidzalephera kukomera mtima anzake sadzaloledwa kukhalabe mu Ufumu wa Mulungu. Koma anthu achikondi komanso okoma mtima ndi amene Mulungu adzawalole kuti akhale kosatha. (Sal. 37:9-11) Anthu onse azidzakhala mwamtendere komanso motetezeka. Koma kodi kukhala okoma mtima kungatithandize bwanji panopa pamene tikuyembekezera dziko latsopano?
UBWINO WOSONYEZA KUKOMA MTIMA
Baibulo limanena kuti: “Munthu wosonyeza kukoma mtima kosatha amapindulitsa moyo wake.” (Miy. 11:17) Anthu amakopeka ndi munthu wokoma mtima moti nawonso amamukomera mtima. Paja Yesu ananena kuti: “Muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.” (Luka 6:38) N’chifukwa chake munthu wokoma mtima amapeza anzake mosavuta ndipo ubwenziwo sutha msanga.
Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Efeso kuti: “Khalani okomerana mtima, achifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse.” (Aef. 4:32) Mpingo umayenda bwino kwambiri ngati muli Akhristu okoma mtima amene amafunitsitsa kuthandiza anzawo. Anthu otero salankhula mawu achipongwe, odzudzula kapena opweteka. M’malo mokhalira kunena miseche, amayesetsa kulankhula molimbikitsa kwa anzawo. (Miy. 12:18) Zimenezi zimathandiza kuti aliyense mumpingo azisangalala.
Taona kuti zolankhula ndi zochita za munthu n’zimene zimasonyeza kuti ndi wokoma mtima. Tikakhala okoma mtima, timatsanzira Mulungu wathu yemwe ndi wachikondi komanso wowolowa manja. (Aef. 5:1) Zotsatira zake n’zakuti timalimbikitsa mpingo komanso kuthandiza anthu kuti akopeke ndi choonadi. Tiyeni nthawi zonse tizisonyeza kukoma mtima.
a Munkhani yotsatira yofotokoza makhalidwe amene mzimu woyera wa Mulungu umatulutsa tidzakambirana za ubwino.