Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 7/15 tsamba 18-22
  • Nthaŵi Zonse Londolani Kukoma Mtima Kwachikondi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nthaŵi Zonse Londolani Kukoma Mtima Kwachikondi
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukoma Mtima Kumatipangitsa Kukhala Opanda Dyera ndi Ochereza
  • Kukoma Mtima Kumatipangitsa Kukhala Olingalira Ena
  • Kukoma Mtima Kumalimbitsa Maunansi
  • Pamene Akazi Asonyeza Kukoma Mtima
  • Pitirizanibe Kulondola Kukoma Mtima Kwachikondi
  • Komerani Mtima Anthu Osoŵa Thandizo
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Muzitsatira Lamulo la Kukoma Mtima Polankhula
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kupindula ndi Kukoma Mtima kwa Yehova
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Mkondweretseni Yehova Mwakusonyeza Kukoma Mtima
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 7/15 tsamba 18-22

Nthaŵi Zonse Londolani Kukoma Mtima Kwachikondi

“Wolondola chilungamo ndi kukoma mtima kwachikondi adzapeza moyo, chilungamo ndi ulemerero.”​—MIYAMBO 21:21, NW.

1. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuyembekezera amene amatsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu kusonyeza kukoma mtima?

YEHOVA ali wokoma mtima ndi wachisoni. Iye ali ‘Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa [kukoma mtima kwachikondi, NW] ndi wachowonadi.’ (Eksodo 34:6, 7) Momvekera bwino lomwe, chipatso cha mzimu wake chimaphatikizapo chikondi ndi kukoma mtima.​—Agalatiya 5:22, 23.

2. Kodi tsopano tidzalingalira zitsanzo zotani?

2 Amene amatsogozedwa ndi mzimu woyera wa Yehova, kapena mphamvu yogwira ntchito, amasonyeza chipatso chake cha kukoma mtima. Iwo amasonyeza kukoma mtima kwachikondi m’maunasi awo ndi ena. Ndithudi, iwo amatsatira chitsanzo cha mtumwi Paulo, akumadziyeneretsa monga aminisitala a Mulungu “m’kukoma mtima” ndi m’njira zina. (2 Akorinto 6:3-10) Mzimu wawo wa kukoma mtima, chisoni, ndi kukhululukira umagwirizana ndi umunthu wa Yehova, amene ali “wochuluka m’kukoma mtima kwachikondi” ndi amene Mawu ake ali ndi zitsanzo zambiri za kukoma mtima. (Salmo 86:15, NW; Aefeso 4:32) Kodi tingaphunzirenji ndi zina za zimenezi?

Kukoma Mtima Kumatipangitsa Kukhala Opanda Dyera ndi Ochereza

3. Kodi ndimotani mmene Abrahamu anakhalira chitsanzo m’kusonyeza kukoma mtima, ndipo kodi Paulo akupereka chilimbikitso chotani m’zimenezi?

3 Kholo Abrahamu (Abramu)​—“bwenzi la [Yehova, NW]” ndi “kholo la onse okhulupirira”​—anakhazikitsa chitsanzo chabwino m’kusonyeza kukoma mtima. (Yakobo 2:23; Aroma 4:11) Iye ndi banja lake, kuphatikizapo mphwake Loti, anasamuka mumzinda wa Akaldayo wa Uri naloŵa m’Kanani polamulidwa ndi Mulungu. Ngakhale kuti Abrahamu anali mwamuna wokalamba ndi mutu wabanja, iye anali wokoma mtima ndi wopanda dyera m’kulola Loti kusankha malo okhala ndi busa labwino koposa, pamene iye mwiniyo anatenga otsalawo. (Genesis 13:5-18) Kukoma mtima kofananako kungatisonkhezere kulola ena kupezera mwaŵi pa ife. Kukoma mtima kopanda dyera koteroko kumagwirizana ndi uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: ‘Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.’ Paulo iye mwini ‘anakondweretsa anthu onse m’zinthu zonse, osafuna ubwino wake yekha koma wa ambiri, kuti mwina iwo angapulumutsidwe.’​—1 Akorinto 10:24, 33, NW.

4. Kodi ndimotani mmene Abrahamu ndi Sara anafupidwira kaamba ka kusonyeza kukoma mtima mwanjira ya kuchereza?

4 Nthaŵi zina kukoma mtima kumakhala mwa mtundu wa kuchereza kochokera kumtima. Abrahamu ndi mkazi wake, Sara, anali okoma mtima ndi ochereza kwa alendo atatu odzera pawo tsiku lina. Abrahamu anawakakamiza kukhalabe kwakanthaŵi, pamene iye ndi mkazi wake Sara mofulumira anakonzera alendowo chakudya chokoma. Pambuyo pake alendowo anazindikiridwa kukhala angelo a Yehova, amene mmodzi wa iwo anapereka lonjezo lakuti Sara wokalamba ndi wopanda mwana akakhala ndi mwana wamwamuna. (Genesis 18:1-15) Inali mphotho yotani nanga ya kukoma mtima ndi kuchereza!

5. Kodi Gayo anasonyeza kukoma mtima mwanjira yotani, ndipo kodi ndimotani mmene tingachitire chinachake chofanana?

5 Njira ina imene Akristu onse angasonyezere kukoma mtima ndiyo mwakukhala ochereza. (Aroma 12:13; 1 Timoteo 3:1, 2) Moyenerera, atumiki a Yehova mokoma mtima amakhala ochereza kwa oyang’anira oyendayenda. Ichi chimakumbutsa za kukoma mtima kumene Gayo, Mkristu wa m’zaka za zana loyamba anakusonyeza. Iye anachita ‘chokhulupirika nacho’ m’kulandira abale mochereza​—ndipo anali “alendo” omwe kale sanaŵadziŵepo. (3 Yohane 5-8) Kaŵirikaŵiri, timadziŵa amene tingawachereze mokoma mtima. Mwinamwake timawona kuti mlongo wauzimu winawake akunyanyalidwa. Mwamuna wake angakhale wosakhulupirira kapena munthu wochotsedwa. Ndimwaŵi wotani nanga wakuti tisonyeze kukoma mtima mwakumamuitana kudzasangalala ndi kuyanjana kwauzimu ndi chakudya pamodzi ndi banja lathu kwanthaŵi ndi nthaŵi! Ngakhale kuti sitingachite kupanga phwando, ndithudi banja lathu lidzasangalala m’kusonyeza mlongo woteroyo kukoma mtima. (Yerekezerani ndi Miyambo 15:17.) Ndipo iye mosakaikira adzasonyeza chiyamikiro chake kaamba ka chimenechi mwa mawu apakamwa kapena mwakulemba kalata yachiyamikiro.

6. Kodi ndimotani mmene Lidiya anasonyezera kukoma mtima, ndipo kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kusonyeza kukoma mtima kaamba ka machitidwe abwino?

6 Pambuyo pakuti Lidiya mkazi wopembedza anabatizidwa, ‘anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera [Paulo ndi anzake] ine wokhulupirika kwa [Yehova, NW] muloŵe m’nyumba yanga, mugone m’menemo. Ndipo anatiumiriza ife,’ anawonjezera motero Luka. Mosakaikira, kukoma mtima kwa Lidiya kunayamikiridwa. (Machitidwe 16:14, 15, 40) Koma kulephera kusonyeza chiyamikiro kungakhale kosakaza. Panthaŵi ina, mlongo wazaka 80 zakubadwa wochepa mphamvu ndi ndalama anayesayesa zolimba mokoma mtima kukonza chakudya cha alendo oŵerengeka. Iye anakhumudwa kwambiri pamene mwamuna wachichepere mmodzi sanamdziŵitse nkomwe kuti sakabwera. Panthaŵi inanso, alongo aŵiri anaphonya chakudya chimene mkazi wachichepere anawakonzera. “Ndinakhumudwa kwadzawoneni,” iye anatero, “popeza kuti onse aŵiri sanaiŵale. . . . Ndikanakonda kumva kuti anaiŵala za chakudya chamadzulocho, koma mmalomwake palibe ngakhale mmodzi wa alongowo anandichitira mokoma mtima kapena kunditumira foni mwachikondi.” Kodi chipatso cha mzimu woyera cha kukoma mtima chikakusonkhezerani kukhala woyamikira ndi wolingalira pansi pa mikhalidwe yofananayo?

Kukoma Mtima Kumatipangitsa Kukhala Olingalira Ena

7. Kodi ndimfundo yotani ya kukoma mtima imene ikufotokozedwa mwafanizo mwazimene zinachitidwa potsatira zikhumbo za Yakobo za maikidwe amaliro?

7 Kukoma mtima kuyenera kutipangitsa kukhala olingalira ena ndi zikhumbo zawo zoyenerera. Tifotokoze mwafanizo motere: Yakobo (Israyeli) anapempha mwana wake wamwamuna Yosefe kusonyeza kukoma mtima kwachikondi kulinga kwa iye mwakusamuika mu Igupto. Ngakhale kuti izi zinalira kuti mtembo wa Yakobo unyamulidwe kwa mtunda wautali, Yosefe ndi ana ena aamuna a Yakobo ‘anamnyamula iye kuloŵa naye m’dziko la Kanani, ndi kumuika iye m’phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efroni Mhiti, patsogolo pa Mamre.’ (Genesis 47:29; 49:29-31; 50:12, 13) Mogwirizana ndi chitsanzo chimenecho, kodi kukoma mtima kwachikondi sikuyenera kutisonkhezera kutsatira maikidwe amaliro ovomerezedwa ndi Malemba okhumbidwa ndi chiŵalo cha banja Chachikristu?

8. Kodi nkhani ya Rahabi imatiphunzitsanji ponena za kubwezera kukoma mtima?

8 Pamene ena atisonyeza kukoma mtima kwachikondi, kodi sitiyenera kusonyeza chiyamikiro kapena kuchitapo kanthu mwanjira inayake? Ndithudi tiyenera kutero. Rahabi mkazi wachigololo anasonyeza kukoma mtima mwakubisa azondi Achiisrayeli. Chotero, Aisrayeliwo anasonyeza kukoma mtima kwachikondi mwakumsunga iye ndi banja lake pamene anapereka mzinda wa Yeriko ku chiwonongeko. (Yoswa 2:1-21; 6:20-23) Nchitsanzo chabwino chotani nanga chosonyeza kuti tiyenera kubwezera kukoma mtima mwakukhala olingalira ena ndi okoma mtima!

9. Kodi nchifukwa ninji munganene kuti nkoyenera kupempha winawake kutisonyeza kukoma mtima kwachikondi?

9 Kaamba ka chimenecho, nkoyenera kwa ife kupempha winawake kusonyeza kukoma mtima kulinga kwa ife. Ichi chinachitidwa ndi Yonatani, mwana wamwamuna wa Sauli, mfumu yoyamba ya Israyeli. Yonatani anapempha Davide, bwenzi lake locheperapo lokondedwa kusonyeza banja lake kukoma mtima kwachikondi. (1 Samueli 20:14, 15; 2 Samueli 9:3-7) Davide anakumbukira chimenechi pamene anabwezera Agibeoni olakwiridwa ndi Sauli. Pokumbukira “lumbiro la kwa Yehova” pakati pa iye ndi Yonatani, Davide anasonyeza kukoma mtima kwachikondi mwakusapha Mefiboseti, mwana wamwamuna wa Yonatani. (2 Samueli 21:7, 8) Kodi nafenso ‘timalola Inde wathu [kutanthauza, NW] Inde’? (Yakobo 5:12) Ndipo ngati ndife akulu a mumpingo, kodi ndife achifundo mofananamo pamene okhulupirira anzathu afunikira kusonyezedwa kukoma mtima kwachikondi?

Kukoma Mtima Kumalimbitsa Maunansi

10. Kodi kukoma mtima kwachikondi kwa Rute kunadalitsidwa motani?

10 Kukoma mtima kwachikondi kumalimbitsa maunansi abanja ndi kupititsa patsogolo chimwemwe. Izi zinasonyezedwa m’chochitika cha mkazi Wachimoabu Rute. Iye anagwira ntchito zolimba monga wotola khunkha m’munda wa Boazi wokalamba pafupi ndi Betelehemu, akudzipezera chakudya chake ndi cha Naomi, apongozi ake amasiye ndi osoŵa. (Rute 2:14-18) Boazi pambuyo pake anauza Rute kuti: ‘[Kukoma mtima kwachikondi, NW] kwako wakuchita potsirizira pano, kuposa koyamba kuja, popeza sunatsata anyamata, angakhale osauka angakhale achuma.’ (Rute 3:10) Choyamba, Rute anasonyeza kukoma mtima kwachikondi kwa Naomi. ‘Potsirizira,’ mkazi Wachimoabuyo anasonyeza kukoma mtima kwachikondi mwakufunitsitsa kukwatiwa ndi Boazi wokalambayo kotero kuti amuukitsire mbewu mwamuna wake wakufayo ndi Naomi wokalambayo. Kwa Boazi, Rute anakhala amayi wa Obedi, agogo aamuna a Davide. Ndipo Mulungu anampatsa “mphotho yokwanira” yakukhala kholo lalikazi la Yesu Kristu. (Rute 2:12; 4:13-17; Mateyu 1:3-6, 16; Luka 3:23, 31-33) Ndimadalitso otani nanga amene kukoma mtima kwachikondi kwa Rute kunambweretsera iye ndi banja lake! Lerolino, madalitso, chimwemwe, ndi kulimbitsa maunansi abanja zimachitikanso pamene kukoma mtima kwachikondi kukula m’mabanja opembedza.

11. Kodi kukoma mtima kwa Filemoni kunali ndi chiyambukiro chotani?

11 Kukoma mtima kumalimbitsa maunansi mkati mwa mipingo ya anthu a Yehova. Mwamuna Wachikristu Filemoni anadziŵidwa chifukwa chakusonyeza kukoma mtima kwachikondi kwa okhulupirira anzake. Paulo anamuuza kuti: ‘Ndiyamika Mulungu wanga nthaŵi zonse, ndi kukumbukira iwe m’mapemphero anga, pakumva za chikondi chako ndi chikhulupiriro uli nacho chakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa oyera mtima onse; . . . Pakuti ndinali nacho chimwemwe chambiri ndi chisangalatso pa chikondi chako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale.’ (Filemoni 4-7) Malemba samanena mmene malingaliro achikondi anatsitsimulidwira kupyolera mwa Filemoni. Komabe, iye ayenera kuti anasonyeza kukoma mtima kwachikondi kwa odzozedwa anzake mwanjira zosiyanasiyana zimene zinakhaladi zotsitsimula kwa iwo, ndipo chimenechi mosakaikira chinalimbitsa maunasi awo. Zochitika zofananazo zimachitika pamene Akristu amasonyeza kukoma mtima kwachikondi lerolino.

12. Kodi kukoma mtima kosonyezedwa ndi Onesiforo kunatulukapo chiyani?

12 Kukoma mtima kwa Onesiforo nakonso kunali ndi chiyambukiro chabwino. ‘Ambuye achitire banja la Onesiforo chifundo,’ anatero Paulo, ‘pakuti anatsitsimutsa ine kaŵirikaŵiri, ndipo sanachita manyazi ndi unyolo wanga; komatu pokhala m’Roma iye anandifunafuna ine ndi khama, nandipeza. Ambuye ampatse iye apeze chifundo ndi [Yehova, NW] tsiku lijalo; ndi muja ananditumikira m’zinthu zambiri m’Efeso, uzindikira iwe bwino.’ (2 Timoteo 1:16-18) Ngati tiyesayesa mwamphamvu kusonyeza kukoma mtima kwachikondi kwa olambira anzathu, tidzakhala achimwemwe ndipo tidzakhala tikulimbitsa maunansi a chikondi cha paubale mkati mwa mpingo Wachikristu.

13, 14. Kodi ndimotani mmene mpingo wa ku Filipi unaliri wachitsanzo, ndipo ndimotani mmene Paulo anachitirapo kanthu pa kukoma mtima kwawo?

13 Pamene mpingo wonse usonyeza kukoma mtima kwachikondi kulinga kwa olambira anzawo, ichi chimalimbitsa unansi pakati pawo. Unansi wathithithi woterowo unalipo pakati pa Paulo ndi mpingo mumzinda wa Filipi. Kwenikweni, chifukwa china chimene analembera kalata yake kwa Afilipi chinali kusonyeza chiyamikiro kaamba ka kukoma mtima ndi chithandizo chakuthupi. Iye analemba kuti: ‘M’chiyambi cha uthenga wabwino, pamene ndinachoka kutuluka m’Makedoniya, sunayanjana nane mpingo umodzi wonse m’makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha; pakuti m’Tesalonikanso munanditumizira pa chosoŵa changa kamodzi kapena kaŵiri. . . . ndiri nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.’​—Afilipi 4:15-18.

14 Choncho nchifukwa chake Afilipi okoma mtimawo anali m’mapemphero a Paulo! Iye anati: ‘Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse; nthaŵi zonse m’pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndichita pembedzerolo ndi kukondwera, chifukwa cha chiyanjo chanu chakuthandizira uthenga wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino.’ (Afilipi 1:3-5) Chichirikizo cha mtima wabwino ndi chooloŵa manja choterocho cha ntchito yolalikira Ufumu sichimapangitsa mpingo kukhala wosauka. Pambuyo pakuti Afilipi anachita zonse zomwe anatha mokoma mtima m’zimenezi, Paulo anawatsimikiziritsa kuti: ‘Mulungu wanga adzakwaniritsa chosoŵa chanu chirichonse monga mwa chuma chake muulemerero mwa Kristu Yesu.’ (Afilipi 4:19) Inde, Mulungu amabwezera kukoma mtima ndi kuolowa manja. Mawu ake amati: ‘Chokoma chirichonse yense achichita, adzambwezera chomwechi [Yehova, NW].’​—Aefeso 6:8.

Pamene Akazi Asonyeza Kukoma Mtima

15, 16. (a) Kodi kukoma mtima kwa Dorika kunakumbukiridwa motani, ndipo nchiyani chimene chinachitika pamene anamwalira? (b) Kodi ndimotani mmene akazi Achikristu a mtima wokoma amachulukira m’ntchito zabwino lerolino?

15 Kukoma mtima kwa wophunzira Dorika (Tabita) wa ku Yopa sikunakhale kopanda mphotho. ‘Mkazi ameneyo anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene anazichita,’ ndipo pamene ‘anadwala iye, namwalira,’ ophunzirawo anatuma anthu kukaitana Petro ku Luda. Pamene anafika, ‘anapita naye ku chipinda cha pamwamba; ndipo amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuwonetsa malaya ndi zovala zimene Dorika adasoka, pamene anali nawo pamodzi.’ Tachiwonani m’diso lanu lamaganizo chochitikacho: Akazi amasiye achisoni, ogwetsa misoziwo anauza mtumwiyo mmene Dorika analiri wokoma mtima ndipo anamsonyeza zovala monga umboni wa chikondi chake ndi kukoma mtima. Atawatulutsa onse, Petro anagwada pansi ndi kupemphera natembenukira ku mtembowo. Tamverani! Iye anati: “Tabita, uka.” Ndipo taonani! ‘Anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga. Ndipo Petro anamgwira dzanja, namnyamutsa; ndipo mmene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.’ (Machitidwe 9:36-41) Ndidalitso lotani nanga lochokera kwa Mulungu!

16 Ichi chinali chiukiriro choyamba kulembedwa chochitidwa ndi mtumwi wa Yesu Kristu. Ndipo zochitika zotsogoza ku chozizwitsa chochititsa chidwi chimenechi zinazikidwa pakukoma mtima. Kodi ndani anganene kuti Dorika akadaukitsidwa ku moyo ngati sanachuluke m’ntchito zabwino ndi mphatso zachifundo​—ngati sanachuluke m’kukoma mtima kwachikondi? Sikokha kuti Dorika ndi akazi amasiyewo anadalitsidwa koma chozizwitsa cha chiukiriro chake chinapereka umboni ku ulemerero wa Mulungu. Inde, ‘kudadziŵika ku Yopa konse: ndipo ambiri anakhulupirira Ambuye.’ (Machitidwe 9:42) Lerolino, akazi Achikristu a mitima yokoma amachulukanso m’ntchito zabwino​—mwinamwake kusokera zovala okhulupirira anzawo, kuphikira chakudya okalamba okhala pakati pathu, kukhala ochereza kwa ena. (1 Timoteo 5:9, 10) Ndiumboni wotani nanga umenewu kwa openyerera! Choposa zonse, ndife achimwemwe chotani nanga kuti kudzipereka kwaumulungu ndi kukoma mtima kwachikondi zimasonkhezera ‘khamu lalikulu la akazi [limeneli] kulalikira uthenga wabwino’ ku ulemerero wa Mulungu wathu, Yehova!​—Salmo 68:11.

Pitirizanibe Kulondola Kukoma Mtima Kwachikondi

17. Kodi nchiyani chimene chikunenedwa pa Miyambo 21:21, ndipo ndimotani mmene mawuwo amagwirira ntchito kwa anthu opembedza?

17 Onse okhumba chiyanjo cha Mulungu ayenera kulondola kukoma mtima kwachikondi. “Wolondola chilungamo ndi kukoma mtima kwachikondi adzapeza moyo, chilungamo ndi ulemerero,” umatero mwambi wanzeru. (Miyambo 21:21, NW) Munthu wopembedza amalondola mwakhama chilungamo cha Mulungu, nthaŵi zonse akumatsogozedwa ndi miyezo yaumulungu. (Mateyu 6:33) Iye amapitirizabe kusonyeza chikondi chokhulupirika, kapena kukoma mtima kwachikondi, kwa ena mwanjira zakuthupi ndipo makamaka zauzimu. Motero, iye amapeza chilungamo, chifukwa chakuti mzimu wa Yehova umamthandiza kukhala ndi moyo mwanjira yachilungamo. Kwenikweni, iye ‘amavala chilungamo’ monga momwe analiri Yobu munthu wopembedza. (Yobu 29:14) Munthu woteroyo samafuna ulemerero wa iyemwini. (Miyambo 25:27) Mmalomwake, iye amatenga ulemerero uliwonse umene Yehova amamlola kulandira, mwinamwake mwanjira ya ulemu wochokera kwa anthu anzake osonkhezeredwa ndi Mulungu kuchita naye mokoma mtima chifukwa cha kukoma mtima kwake kwachikondi kulinga kwa iwo. Ndiponso, amene amachita chifuniro cha Mulungu mokhulupirika adzapeza moyo​—osati kokha kwa zaka zoŵerengeka zotha mofulumira koma kwamuyaya.

18. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulondola kukoma mtima kwachikondi?

18 Chotero, onse okonda Yehova Mulungu apitirizetu kulondola kukoma mtima kwachikondi. Mkhalidwe umenewu umatipangitsa kukondedwa ndi Mulungu ndi ena. Umapititsa patsogolo kuchereza ndipo umatipangitsa kukhala olingalira ena. Kukoma mtima kumalimbitsa maunansi mkati mwa banja ndi mpingo Wachikristu. Akazi amene amasonyeza kukoma mtima kwachikondi amayamikiridwa ndi kulemekezedwa kwambiri. Ndipo onse olondola mkhalidwe wokongola umenewu amadzetsa ulemerero kwa Mulungu wa kukoma mtima kwachikondi, Yehova.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi ndimotani mmene Abrahamu analiri wachitsanzo m’kusonyeza kukoma mtima?

◻ Kodi nkhani ya Rahabi imatiphunzitsanji ponena za kubwezera kukoma mtima?

◻ Kodi ndimotani mmene mpingo wa ku Filipi unasonyezera kukoma mtima?

◻ Kodi ndimotani mmene akazi Achikristu a mtima wokoma amachulukira m’ntchito zabwino lerolino?

◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulondola kukoma mtima kwachikondi lerolino?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena