Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 8/15 tsamba 4-7
  • Thanzi Ndi Chimwemwe—kodi Mungazipeze Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thanzi Ndi Chimwemwe—kodi Mungazipeze Motani?
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Thanzi ndi Chimwemwe​—Mwachidule
  • Ufumuwo, Kapena Boma, la Mulungu
  • Kodi Tingasangalale ndi Thanzi ndi Chimwemwe Tsopano?
  • Thanzi Lanu, Chimwemwe Chanu
  • Thanzi ndi Chimwemwe—Kodi Zingakhale Zanu?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Zimene Tingachite Kuti Tikhale Osangalala
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kufunafuna Moyo Wachimwemwe
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Chimwemwe Chenicheni Chingapezeke Kuti?
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 8/15 tsamba 4-7

Thanzi Ndi Chimwemwe​—kodi Mungazipeze Motani?

MUNTHU wazindikira kwa nthaŵi yaitali kugwirizana kokhala pakati pa thanzi ndi chimwemwe. Hippocrates, wolingaliridwa kukhala “tate wa mankhwala,” ananena kuti: “Munthu wanzeru ayenera kulingalira kuti thanzi ndilo madalitso a munthu aakulu koposa.” Arthur Schopenhauer, wanthanthi Wachijeremani anati: “Adani aŵiri a chimwemwe cha munthu ndiwo kupweteka ndi kusungulumwa.”

M’bukhu lakuti Anatomy of an Illness as Perceived by the Patient, Norman Cousins anasimba chokumana nacho chake chakugwiritsira ntchito chiphwete kuchiritsa matenda owopseza moyo wake. Iye anati mbali ina yothandizira kuchira kwake inali kuseka kwapwipwiti kumene anasangalala nako pamene ankawonerera akanema oseketsa. Adokotala otchuka ayamba kufufuza phindu lothekera la makemikolo ena ake otchedwa endorphin, omwe amatulutsidwa m’thupi pamene tiseka. Chotero tikhoza kuiwona nzeru ya mwambi wouziridwa wakuti: ‘Mtima wosekerera uchiritsa bwino.’​—Miyambo 17:22.

Komabe, modabwitsa, ofufuza apeza kuti thanzi labwino silimapereka chitsimikizo kwenikweni chakukhala ndi chimwemwe, chifukwa chakuti anthu ambiri athanzi ali opanda chimwemwe. Kufufuza kozikidwa pa mafunso olembedwa ndi mayankho a anthu oposa 100,000 ofunsidwa kunapangitsa Jonathan Freedman kupereka chigamulo chosayembekezereka chakuti oposa pa 50 peresenti a anthu omwe sanali achimwemwe ndi miyoyo yawo kwakukulukulu anali athanzi.

Thanzi ndi Chimwemwe​—Mwachidule

Pamenepa, kodi nkuti kumene tiyenera kuyang’anako kuti tipeze msanganizo wovuta umenewu wa thanzi ndi chimwemwe? Chidziŵitso chosangalatsa chinaperekedwa zaka mazana ambiri zapitazo ndi Confucius kuti: “Boma labwino limapambana pamene awo okhala pafupi apangitsidwa kukhala achimwemwe, ndipo okhala kutali akopedwa.” Chapafupi ndi nthaŵi yathu, nduna yaboma Thomas Jefferson inanena kuti chonulirapo chokha cha boma chiyenera kukhala “kupeza mlingo waukulu koposa wa chimwemwe chothekera kwa anthu aunyinji okhala pansi pake.”

Kwenikwenidi, kufufuza kosamalitsa kumavumbula kuti yankho lotheratu la kufunafuna thanzi ndi chimwemwe kwa anthu limasumika pa chinthu chimodzi​—boma.

Kupyola m’nyengo za nthaŵi, anthu ayang’ana kumeneko​—ku boma​—kaamba ka chimwemwe chawo. Mwachitsanzo, Chilengezo cha Ufulu Wakudzilamulira cha United States chiri ndi mawu otchuka aŵa: “Tikufuna kuti mfundo zowona izi ziwonekere zokha, kuti anthu onse analengedwa olingana, kuti Mlengi wawo anawapatsa Zoyenerera zakutizakuti zosakhoza kulandidwa, kuti pakati pa zimenezi pali Moyo, Ufulu ndi kulondola Chimwemwe.” Onani kuti boma limenelo linalonjeza nzika zake kokha kuyenerera kwa kulondola chimwemwe. Ponena za thanzi, maboma ambiri moyamikirika apititsa patsogolo maprogramu akuwongolera thanzi la nzika zawo. Chikhalirechobe, thanzi labwino la onse latsimikizira kukhala lovuta kupeza.

Komabe bwanji ponena za boma limene limalonjeza kupereka ngakhale zowonjezereka? Bwanji ngati lilonjeza osati kulondola chimwemwe kokha koma kuchigaŵiradi chimwemwe chenichenicho? Ndipo bwanji ngati lilonjeza, osati chitsimikizo cha thanzi, koma kugaŵira thanzi lenilenilo? Kodi simukasangalala kuti m’boma limeneli ndimo muli mfungulo yeniyeni ya kufunafuna thanzi ndi chimwemwe kwa anthu?

Ambiri lerolino angalingalire zimenezi kukhala loto chabe, komabe boma loterolo linanenedweratu ndi kulongosoledwa mwatsatanetsatane. Tikhoza kupeza chidziŵitso chodalirika m’Baibulo Lopatulika, ndipo bomalo ndilo Ufumu Waumesiya wa Mulungu.

Ufumuwo, Kapena Boma, la Mulungu

Kaŵirikaŵiri Baibulo limalankhula za “ufumu wa Mulungu.” Kodi uwo kwenikweni uli chiyani? Webster’s New World Dictionary of the American Language imatanthauzira “ufumu” kukhala “boma kapena dziko lotsogozedwa ndi mfumu kapena mfumukazi.” Kunena mokhweka, Ufumu wa Mulungu ndiboma, boma lachifumu lotsogozedwa ndi Mwana wodzozedwa wa Mulungu yemwenso ndi Mfumu, Yesu Kristu. Kodi boma limeneli nlofunika motani m’chifuniro cha Mulungu? Lolani kuti mawu a Yesu ayankhe: ‘Koma muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake . . . Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu . . . Kundiyenera ine ndilalikire uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu ku midzi inanso: chifukwa ndinatumidwa kudzatero. . . . Ulalikidwa uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu, ndipo munthu aliyense akangamira kuloŵamo.’​—Mateyu 6:33; 24:14, NW; Luka 4:43; 16:16.

Liwu lakuti “ufumu” limagwiritsiridwa ntchito kwanthaŵi zoposa zana limodzi m’nkhani za Uthenga Wabwino wa moyo wa Yesu, nthaŵi zina kuloza mwachindunji ku thanzi ndi chimwemwe. Onani Mateyu 9:35: ‘Ndipo Yesu anayendayenda m’mizinda yonse ndi m’midzi, namaphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalalikira uthenga wabwino wa ufumuwo, nachiritsa nthenda iriyonse ndi zofooka zonse.’ Ngakhale kuti Yesu anagwirizanitsa kudzetsa thanzi labwino ndi kuphunzitsa kwake za Ufumuwo, tiyenera kudziŵa kuti kuchiritsa kwake matenda kunali kwachiŵiri ku kulalikira kwake ndi kuphunzitsa. Iye anadziŵika monga “Mphunzitsi,” osati “Wochiritsa.” (Mateyu 26:18; Marko 14:14; Yohane 1:38) Iye sanasumike kwakukulukulu pakuchiritsa anthu kapena kupereka chisamaliro kwa odwala. Nthaŵi zonse nkhaŵa yake yaikulu inali Ufumuwo. Mwakusamalira mavuto a anthu, iye anasonyeza chifundo chake chachikulu ndipo anawonetsa kuti iye anali ndi chichirikizo chaumulungu.

Kuchiritsa kwa Yesu kunatumikiranso monga kuwoneratu zamtsogolo kwa kubwezeretsa thanzi laumunthu kumene adzakuchita pamene Ufumu wa Mulungu uchita ulamuliro wokwanira wa dziko lapansi. Zimenezi zimatsimikiziridwa ndi masomphenya amene akulongosoledwa pa Chibvumbulutso 22:1, 2 kuti: ‘Ndipo anandiwonetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa. Pakati pa khwalala lake, ndi tsidya iri la mtsinje, ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziŵiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nawo amitundu.’

Koma kodi nkuti kumene zidzakhala zotheka kwa ife kusangalala ndi zimenezi? Zingawonekere kukhala zabwino koposa pakukhala zowona kuti tiyembekezere kuchiritsa kodabwitsa koteroko kuchitika padziko lapansi. Komabe, kumbukirani mawu a Yesu, amene mwina inumwini munawanenapo m’pemphero akuti: ‘Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.’​—Mateyu 6:10.

Pamenepo, mu Ufumu Waumesiya wa Mulungu, ndimmene muli chiyembekezo chathu chenicheni, chodalirika, cha thanzi ndi chimwemwe mtsogolo. Komabe, funso liripobe.

Kodi Tingasangalale ndi Thanzi ndi Chimwemwe Tsopano?

Ngakhale tsopano, kutsatira kwathu malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo kungatitheketse kusangalala ndi mlingo wokulirapo wa thanzi, pamodzi ndi chimwemwe chowonjezereka. Monga momwe zatchulidwira mobwerezabwereza m’masamba a magazini ano, awo amene amagwiritsira ntchito Baibulo m’moyo wawo wa tsiku ndi tsiku nthaŵi zonse amatetezeredwa ku mavuto a thanzi ndi otuluka m’chisembwere, kusuta, uchidakwa, ndi kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala oledzeretsa. Iwo amasangalalanso ndi mapindu a moyo wabata ndi maunansi abwinopo ndi achibale ndi anthu ena.

Ngakhale ndichoncho, tawona kale kuti kukhala ndi thanzi labwino sikumatulukira nthaŵi zonse m’chimwemwe chokhalitsa. Kodi chofunika kwa inu nchiyani kuti musangalale ndi mlingo wokulirapo wa chimwemwe?

M’kufufuza kotchulidwa poyambirirapo, Jonathan Freedman anapenda funsolo mwakuya. Iye anayang’ana pa mfundo zonga “Chikondi ndi Kugonana,” “Uchichepere ndi Ukalamba,” “Ndalama Zopezedwa ndi Maphunziro,” ngakhale “Mzinda ndi Mudzi.” Zingakukondweretseni kudziŵa kuti iye anapeza mfundo zimenezi kukhala ndi chiyambukiro chochepa pa chimwemwe chenicheni cha munthu. Mwachitsanzo, potchula zochitika za anthu omwe anali ndi zinthu zambiri zakuthupi komanso opanda chimwemwe, iye anagamula kuti: “Tawona kuti, nzodabwitsa mwanjira inayake kuti, kaya ndalama zopezedwa kapena maphunziro sizimawonekera kuchita mbali yaikulu m’chimwemwe.”

Zigamulo zake zinakumbutsa lingaliro la wolemba Baibulo wanzeru, mtumwi Paulo, yemwe anati: “Ndaphunzira, mumkhalidwe uliwonse umene ndingakhalemo, kukhala wokhutiritsidwa.” (Afilipi 4:11, King James Version) Kumbukiraninso, mawu a Yesu akuti: ‘Yang’anirani, mudzisungire kupeŵa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.’​—Luka 12:15.

Ndithudi, Profesa Freedman anapeza izi: “Nthaŵi ndi nthaŵi, pamene tiwona ndemanga zoperekedwa ndi anthu opanda chimwemwe owonekera kukhala nazo zinthu zonse, timapeza kuti iwo amanena zakuti miyoyo yawo iribe tanthauzo ndi chifuno.” Iye anawonjezera kuti: “Ndimazengereza kuchita zimenezi mopambanitsa, koma zikuwoneka kuti mapindu auzimu amapatsa malingaliro abwino ponena za zinthu zenizeni za m’moyo, pamene kuli kwakuti kukhala wopanda iwo kumaluluza kapena kusokoneza chirichonse kumlingo winawake.”

M’tsiku lathu timawona umboni wa chowonadi cha ndemanga zimenezi. Wunguzaniwunguzani. Kodi simumawona kuti pafupifupi anthu onse​—ena okhala ndi zinthu zochepa, ena ndi zochuluka​—amalondola chimwemwe koma samasangalala ndi chochuluka? Zowona, ena ataya mtima namangokhala osoŵa chochita, komabe ambiri angatsogoze miyoyo yawo monga othamangitsa mphepo, kumachitsatira, koma osachipeza chimene akuchilondola. Ena amakwatira kuti apeze chimwemwe, ngakhale pamene kuli kwakuti mnansi wawo akusudzulana kaamba ka chifukwa chofananacho. Ena amadzitopetsa ndi ntchito, pamene enanso amaleka ntchito kwa nthaŵi yaitali ndipo mwinamwake kupita pa matchuthi odya ndalama zambiri. Onse amafunafuna chonulirapo chovuta chofananacho, kukhala athanzi ndi achimwemwe. Kodi iwo amachipeza? Kodi inuyo mwachipeza?

Thanzi Lanu, Chimwemwe Chanu

Chenicheni nchakuti, inuyo mukhoza kukhala ndi mlingo waukulu wa thanzi ndi chimwemwe tsopanoli. Motani?

Ndithudi kuli kwanzeru kuyesayesa kusamalira thanzi lanu mwanjira yolinganizika, monga ngati mwakugwiritsira ntchito uphungu wothandiza wa Baibulo. Kudzathandizanso kuwona zinthu mwanjira yeniyeni. Zimenezo zimaloŵetsamo kuzindikira kuti matupi athu opanda ungwiro akhoza kudwala, komabe sitidzakhwethemuka maganizo pamene zimenezo zichitika. Ichi chingafunikiritse kuyesayesa kokulirapo kwakusunga lingaliro lachiyembekezo pamene tikuyang’ana pa lonjezo la thanzi langwiro m’dziko latsopano limene likudzalo.

Kuti muwone ngati muli ndi mlingo waukulu wa chimwemwe tsopano, tadzifunsani mafunsoŵa: 1. Kodi ndimakhoza kwenikweni kulamulira moyo wanga? 2. Kodi ndiri pamtendere kwakukulukulu inemwini ndi awo ondizinga? 3. Kodi mwachisawawa ndine wosangalatsidwa ndi zimene ndakwaniritsa m’moyo wanga zitayesedwa ndi chowonadi cha Baibulo? 4. Kodi banja langa ndi ineyo timasangalala kukhala okhoza kutumikira Mulungu?

Kwakukulukulu, chosankha chiri chathu. Ambirife tingakhale athanzi, ndipo tiri nacho chosankha chakukhalanso achimwemwe. Koma tiyenera kukhala ndi zonulirapo zauzimu kenaka kugwirira ntchito pakuzifikira. Kumbukirani mawu a Yesu akuti: ‘Kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.’ (Mateyu 6:21) Ndipo tiri ndi chifukwa chozikidwa pa Baibulo chakuyang’ana kutsogolo ku thanzi labwinopo ndi chimwemwe pansi pa ulamuliro wangwiro wa Ufumu Waumesiya. Panthaŵi imeneyo thanzi lokwanira kotheratu ndi chimwemwe zikhoza kukhala zathu.

[Chithunzi patsamba 7]

Anthu achimwemwe amasangalala kugaŵana ndi ena chiyembekezo chawo cha thanzi langwiro

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena