Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 8/15 tsamba 3-4
  • Thanzi ndi Chimwemwe—Kodi Zingakhale Zanu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thanzi ndi Chimwemwe—Kodi Zingakhale Zanu?
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Thanzi Ndi Chimwemwe—kodi Mungazipeze Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kufunafuna Moyo Wachimwemwe
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Zimene Mungachite
    Galamukani!—2018
  • Chimwemwe Chowona Potumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 8/15 tsamba 3-4

Thanzi ndi Chimwemwe​—Kodi Zingakhale Zanu?

KUUTALI wonse umene amuna ndi akazi opanda ungwiro akhalapo, alakalaka thanzi ndi chimwemwe. Ngakhale kuti izi ndiziŵiri za zikhumbo zazikulu koposa za anthu, zakhaladi zovuta kuzipeza.

Anthu apereka malingaliro ambiri, ndi uphungu wochuluka pa kufunafuna zimenezi. Dr. Dennis Jaffe ananena kuti: “Lerolino, mfungulo yopezera thanzi ndi chimwemwe zokhalitsa kaŵirikaŵiri imakhala m’khalidwe lanu lenilenilo.” Abraham Lincoln nthaŵi ina anati: “Anthu amakhala opanda chimwemwe malinga ndi mmene amasankhira kukhalira.” Kodi mukuvomereza? Kodi chimwemwe mumachikhumba mokulira chotani? Kodi ndimokulira chotani mmene kuchipeza kumadalira pakukhala ndi thanzi labwino?

Anthu afunafuna chimwemwe kulikonse, akumatenga njira zowonekera kukhala zosatha. Iwo afufuza maphunziro a zanthanthi, zamalingaliro, ndi za mikhalidwe yachibadwa. M’kufufuza kwawo kofuna chimwemwe, ena asanthula sayansi, zaumisiri, ndi nyimbo. Komabe pali chikaikiro chochepa m’kunena kuti mbali yaikulu ya chimwemwe chenicheni imakhudza kukhala ndi thanzi labwino. “Ngati muli ndi thanzi labwino, muli ndi pafupifupi zinthu zonse,” inatero nkhani ya malonda yotchuka ya pawailesi yakanema.

Polondola njira yopezera chimwemwe imeneyi, anthu ambiri afufuza nthanthi zosiyanasiyana zonena za thanzi, ponse paŵiri zamwambo ndi zosakhala zamwambo. Pafupifupi laibulale ya unyinji iriyonse imasonyeza mabuku ofotokoza njira zosaŵerengeka zochirikizira thanzi ndi mitundu ya kuchiritsa. “Mabuku ambiri alembedwa onena za thanzi, kuyambira m’nthaŵi zamakedzana,” anatero Dr. Paul Dudley White, katswiri wotchuka wochiritsa mtima. “Limodzi lotchuka koposa linali Regiment of Helthe lolembedwa pafupifupi zaka chikwi zapitazo.”

Mosasamala kanthu za zonsezi, kufufuza kofuna thanzi ndi chimwemwe kwakhala kogwiritsa mwala kwa anthu ambiri. Kodi zimenezi zikukudabwitsani, polingalira za kupita patsogolo kwa kutsungula kwathu? Mwachiwonekere, sayansi siinachotsepo matenda, ukalamba, ndi imfa.

Koma kodi zikakudabwitsaninso mutadziŵa kuti tidakali opanda njira yoyesera chimwemwe ndipo tiribe tanthauzo labwino la chimene icho chiri? Popereka nkhani yonena za “Malingaliro pa Chimwemwe,” Pierre Teilhard de Chardin anagamula kuti: “Kwa zaka mazana ambiri iyi yakhala nkhani yopezeka m’mabuku osaŵerengeka, m’kufufuza, kufufuza koyesa kwa munthu payekha ndi kwa magulu, kumodzi pambuyo pa kunzake; ndipo, nzachisoni kunena kuti, pakhala kulephera kotheratu kuchifikira chivomerezo cha onse. Kwa ambirife, chotulukapo chake nchakuti, chigamulo chokha chogwira ntchito chofikiridwa m’kukambitsirana konseku nchakuti kuli kosaphula kanthu kupitiriza ndi kufufuzako.”

Kodi ndilo lingaliro lanu ponena za chimwemwe? Dzifunseni nokha mafunso aumwini koma owona mtima. Kodi inu mulidi wachimwemwe tsopano? Kapena kodi chimwemwe chenicheni chimapezeka kumwamba kokha? Kodi pali chiyembekezo chotsimikizirika chirichonse chakuti tikhoza kukhala ndi thanzi ndi chimwemwe, ndipo ngakhale kukhala nazo pompano pa dziko lapansi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena