Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 10/1 tsamba 19
  • ‘Achimwemwe Ali Anjala Yauzimu’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Achimwemwe Ali Anjala Yauzimu’
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Kukhutiritsa Anjala Mwauzimu—Pa Sukulu
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Mmene Ena Anapezera Mayankho
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kuvomereza Mbiri Yabwino m’Belgium
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • “Wodala Ndiwopeza Nzeru”
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 10/1 tsamba 19

Lipoti la Olengeza Ufumu

‘Achimwemwe Ali Anjala Yauzimu’

YESU anati: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3, NW) Oterowo adzafunafuna chidziŵitso chopatsa moyo kuchokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo, ndipo kupeza chidziŵitso chimenechi kudzawatsogolera ku moyo wosatha.​—Mateyu 4:4; Yohane 17:3.

◻ Munthu wanjala yauzimu m’dziko lina la ku Afirika anayenda pansi kwa maola anayi mumdima kukuzizira kuti akapeze kope la Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Pamene anafika m’mudzi mmene Mboni za Yehova zinali kulalikira, anagwiritsidwa mwala kwenikweni kupeza kuti bukhu lomalizira linagaŵiridwa. Iye anakhala m’mudzimo kwa masiku atatu kufikira mabuku ena owonjezereka anafika, ndiyeno pomalizira pake anali wachimwemwe kukhala nacho chidziŵitso chabwino chauzimu chimenechi.

Mkati mwa mwezi womwe zinakhala kudera lakutali limeneli, Mbonizo zinagaŵira mabuku 55, mabrosha 365, ndi magazini 145, ndipo zinapeza masabusikripishoni 5. Zinakondweretsedwa kwambiri pamene, nthaŵi yochoka inafika, akulu ndi ana omwe anawadalitsa m’chinenero cha Kpelle kuti: “Yehova akhale nanu!” Zoyesayesa zikupangidwa zakutsatira okondwerera.

Munthu wina m’dziko limodzimodzilo analinso ndi njala yauzimu. Iye anali msungi chuma wa tchalitchi chake ndiponso anali nduna ya zamaseŵera m’dera lake. Pamene Mboni zinamfikira, anavomereza ndi misozi kuti tchalitchi chake chinalephereratu kufikiritsa miyezo ya Baibulo ya Chikristu. Mbonizo zinamsonyeza m’Baibulo lake mmene angazindikirire chipembedzo chowona. Ndiyeno anafikapo pamisonkhano iŵiri pa Nyumba Yaufumu ndipo pambuyo pake anati: “Zomwe ndawona ndi kumva zandikhutiritsadi kuti ichi nchowonadi.” Anakondweretsedwa ndi misonkhano ndi khalidwe la opezekapo. Iye anawona kuti zimene Mboni zomwe zinamfikira zinanena sizinali zopeka koma zenizeni. Chiyambire pamenepo iye wapanga makonzedwe akumasuka ku unansi wake ndi tchalitchi, ndipo kunatulukapo umboni wabwino m’mudzimo.

◻ Wophunzira katikizimu wachichepere wa Chimelanesia mu New Caledonia anali ndi njala yauzimu. Iye anapeza kope la bukhu la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya pagome m’nyumba mwa amayi ŵake, ndipo anaŵerenga mitu 2 ndi 3. Malemba Abaibulo a Eksodo 20:4, 5 ndi Yohane 4:23, 24 omwe anafotokozedwa m’menemo anakhudza mtima wake. Polingalira zimene malembaŵa amanena, iye anafunsa wansembe wake chifukwa chimene Tchalitchi cha Katolika chimalolera kugwiritsira ntchito mafano m’kulambira. Wansembeyo analizemba funsolo. Mwamunayu anapita ku zipembedzo zina zingapo “Zachikristu,” koma sanampatse mayankho okhutiritsa a mafunso ake. Pomalizira pake anagamulapo zofika pamsonkhano wa Mboni za Yehova ndi amayi ŵake, omwe anasonyeza kale chikondwerero m’chowonadi. Chikondi ndi ziphunzitso zozikidwa pa Baibulo za Mbonizo zimene anawona zinamkondweretsa kwambiri.

Mosasamala kanthu za mtunda wautali, anakwera matola mosalekeza kupita kumisonkhano, kutenga mbali yake ku chowonadi, ndipo anabatizidwa. Tsopano ndi mtumiki wotumikira. Amayi ŵake ndi achemwali ake aŵiri anakhalanso Mboni za Yehova. Mwamuna wachichepereyu analalikira kwa fuko lake ndipo anayambitsa maphunziro Abaibulo ambiri. Tsopano anthu angapo a fuko lake amafika pamisonkhano m’derali​—zonsezi nchifukwa cha mwamuna wachichepere yemwe anawona bukhu lofotokoza Baibulo liri pagome, analiphunzira, ndipo anakhulupirira ndi kugwiritsira ntchito zimene anaphunzira.

Yehova ali ndi programu yaikulu yodyetsa lerolino, ndipo makamu akupindula nayo. Yesaya analosera moyenerera ponena za iyo pamene anati: “Taonani atumiki anga adzadya, koma inu [ziŵalo za chipembedzo chonyenga] mudzakhala ndi njala.” (Yesaya 65:13) Ndife achimwemwe ngati timapindula ndi makonzedwe a Yehova akukhutiritsa njala yathu yauzimu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena