Kenturiyo Wokoma Mtima Wachiroma
AKENTURIYO Achiroma adalibe mkhalidwe wakukoma mtima. Pogaŵiridwa kutsogolera gulu la asirikali okwanira zana limodzi okhwimitsidwa ndi nkhondo, kenturiyo anafunikira kukhala wogubitsa perete wojintcha, wopereka chilango wokhaulitsa, ndipo nthaŵi zina, ngakhale wakupha. Komabe, Baibulo limatiuza za kenturiyo Wachiroma wa gulu la Augusto yemwe anasonyeza kuoloŵa manja kwenikweni ndi chifundo kwa mtumwi Paulo. Dzina lake? Yuliyo.
Baibulo limatidziŵitsa mwamuna ameneyu m’mutu 27 wa Machitidwe. Mtumwi Paulo adapempha kuti apilu yake ikamvedwe ndi Kaisara ku Roma. Chotero, Paulo, pamodzi ndi andende ena angapo, anaperekedwa ku chisamaliro cha ‘kenturiyo dzina lake Yuliyo, wa gulu la Augusto.’ Iwo ananyamuka ndi ngalawa pa Kaisareya, mzinda wapadoko kumpoto koma chakumadzulo kwa Yerusalemu umene unatumikira monga malikulu a asirikali Achiroma. Wolemba mbiri Luka akunena kuti: ‘M’mawa mwake tinangokocheza ku Sidoni; ndipo Yuliyo anachitira Paulo mwachikondi, namlola apite kwa abwenzi ake amchereze.’—Machitidwe 27:1-3.
Chifukwa chenicheni chimene Yuliyo anasonkhezeredwera kusonyeza kukoma mtima koteroko sichinatchulidwe m’Baibulo. Mwinamwake iye ankatsatira malangizo operekedwa ndi Kazembe Festo akuchitira Paulo mwapadera. Kapena mwina pokhala atadziŵa zochitika za kumangidwa kwa Paulo, Yuliyo angakhale anangokhumbira kulimba mtima ndi umphumphu wa Paulo. Mulimonse mmene zingakhalire, Yuliyo anawonekera kukhala anazindikira kuti Paulo sanali wandende wamba.
Komabe, Yuliyo anasankha kusamvera chenjezo la Paulo lotsutsa kunyamuka ndi ngalawa pamalo otchedwa Pokocheza Pokoma. Posapita nthaŵi ngalawayo inagwidwa m’chimphepo cha namondwe chimene chinawopseza kuitsakamitsa pabondo lamchenga lokhala patali ndi gombe la kumpoto kwa Afirika. (Machitidwe 27:8-17) Namondweyo ali pakati, Paulo anaimirira nawatsimikizira okweramo onse ochita manthawo kuti ‘sadzatayika wamoyo mmodzi mwa iwo, koma ngalawa ndiyo.’ Chikhalirechobe, ena a amalinyerowo pambuyo pake anayesa kuthaŵa. Pamenepo Paulo anauza Yuliyo kuti: “Ngati awa sakhala m’ngalawa inu simukhoza kupulumuka.”—Machitidwe 27:21, 22, 30, 31.
Panthaŵiyi, Yuliyo anasankha kumvetsera kwa Paulo, ndipo amalinyerowo sanaloledwe kuthaŵa. Monga momwedi Paulo analoserera, ngalawayo inatsakamira pamalo osaya nisweka. Powopa kuti andendewo angathaŵe, asirikali amene anali m’ngalawamo anafunitsitsa kuwapha onse. Komabe, kachiŵirinso, Yuliyo analoŵererapo nawaletsa amuna ake, mwakutero anapulumutsa moyo wa Paulo.—Machitidwe 27:32, 41-44.
Baibulo silimanena zimene zinachitikira kenturiyo wokoma mtima ameneyo kaya analandira chikhulupiriro Chachikristu. Kukoma mtima kulikonse kumene anakusonyeza kunali chisonyezero cha zochita za chikumbumtima chopatsidwa ndi Mulungu. (Aroma 2:14, 15) Komabe, Akristu amachita zoposa kukoma mtima wamba kwachibadwa ndipo amasonyeza kukoma mtima kwaumulungu kumene kumatulukapo pokhala ndi mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22) Ndithudi, ngati msirikali wakunja amene sanadziŵe Mulungu anakhoza kusonyeza kukoma mtima, anthu a Mulungu ayenera kusonkhezeredwa koposapo motani nanga kuchita tero!