Kondwerani m’Chiyembekezo cha Ufumu!
‘Kondwerani m’chiyembekezo, pirirani m’masautso.’—AROMA 12:12.
1. Kodi nchifukwa ninji tingathe kupeza chimwemwe mwakugwirizana ndi Yehova, ndipo kodi Paulo anafulumiza Akristu kuchitanji?
“MULUNGU wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Ha, mawuŵa amamlongosola bwino chotani nanga Yehova! Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ntchito zake zonse zimampatsa chimwemwe chachikulu. Popeza kuti Yehova ndiye Magwero a zinthu zonse zabwino ndi zopatsa chimwemwe, zolengedwa zake zonse zaluntha zitha kupeza chimwemwe mwakugwirizana naye. Moyenerera, mtumwi Paulo anafulumiza Akristu kuyamikira mwaŵi wawo wodzetsa chimwemwe wakudziŵa Yehova Mulungu, kumthokoza kaamba ka mphatso Zake zonse zodabwitsa za chilengedwe, ndi kukondwera m’kukoma mtima kwake kwachikondi kumene Iye amazisonyeza. Paulo analemba kuti: ‘Kondwerani mwa Ambuye nthaŵi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.’—Afilipi 4:4; Salmo 104:31.
2. Kodi nchiyembekezo chotani chimene chimabweretsa chimwemwe chachikulu, ndipo kodi Akristu akufulumizidwa kuchitanji ponena za chiyembekezo chimenechi?
2 Kodi Akristu amalabadira chilangizo cha Paulo chimenechi? Ndithudi amatero! Abale auzimu a Yesu Kristu akukondwera m’chiyembekezo chaulemerero chimene Mulungu wawatsegulira. (Aroma 8:19-21; Afilipi 3:20, 21) Inde, iwo amadziŵa kuti adzakhala ndi mbali m’kukwaniritsa chiyembekezo chachikulu cha mtsogolo mwa anthu, kwa ponse paŵiri amoyo ndi akufa, mwakutumikira limodzi ndi Kristu m’boma Laufumu lakumwamba. Tangoyerekezerani chimwemwe chachikulu chomwe adzakhala nacho m’mwaŵi wawo monga olamulira anzake, akutumikira monga mafumu ndi ansembe! (Chibvumbulutso 20:6) Ha, nchimwemwe chotani nanga chimene adzakhala nacho pothandiza anthu okhulupirika kufikira ungwiro ndi kuthandizira m’kubwezeretsa Paradaiso pa dziko lathu lapansi! Mowonadi, atumiki onse a Mulungu ali ndi maziko a ‘chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthaŵi zosayamba.’ (Tito 1:2) Polingalira za chiyembekezo chachikulu chimenechi, mtumwi Paulo akulimbikitsa Akristu onse kuti: ‘Kondwerani m’chiyembekezo.’—Aroma 12:12.a
Chimwemwe Chenicheni—Mkhalidwe wa Mtima
3, 4. (a) Kodi liwu lakuti “kukondwera” limatanthauzanji, ndipo kodi Akristu ayenera kukondwera kaŵirikaŵiri motani? (b) Kodi chimwemwe chenicheni nchiyani, ndipo kodi chimadalira pachiyani?
3 “Kukondwera” kumatanthauza kumva chimwemwe ndi kuchisonyeza; sikumatanthauza kukhala mumkhalidwe wansangala wosalekeza, kapena kukondwa kopambanitsa. Mawu a mneni ofanana ndi mawu Achihebri ndi Achigiriki ogwiritsiridwa ntchito m’Baibulo kutanthauza “chimwemwe,” “chisangalalo,” ndi “kukondwera” amasonyeza ponse paŵiri kumva chimwemwe kwamkati ndi kuchisonyezera kunja. Akristu amalimbikitsidwa ‘kupitiriza kukondwera,’ ‘kukondwera nthaŵi zonse.’—2 Akorinto 13:11; 1 Atesalonika 5:16.
4 Koma kodi ndimotani mmene munthu angakondwerere nthaŵi zonse? Ichi nchotheka chifukwa chakuti chimwemwe chenicheni chiri mkhalidwe wa mtima, mkhalidwe wamkati wozama, mkhalidwe wauzimu. (Deuteronomo 28:47; Miyambo 15:13; 17:22) Chiri chipatso cha mzimu wa Mulungu, chimene Paulo anandandalika pambuyo pa chikondi. (Agalatiya 5:22) Monga mkhalidwe wamkati, sichimadalira pa zinthu zakunja, osati ngakhale pa abale athu. Koma chimadaliradi pa mzimu woyera wa Mulungu. Ndipo chimachokera m’chikhutiro chozama chamkati chakudziŵa kuti muli nacho chowonadi, chiyembekezo cha Ufumu, ndikuti mukuchita zimene zimamkondweretsa Yehova. Chifukwa chake, chimwemwe simkhalidwe wamba wa munthu umene timabadwa nawo; uli mbali ya “[umunthu, NW] watsopano,” msanganizo wa mikhalidwe umene unasiyanitsa Yesu Kristu.—Aefeso 4:24; Akolose 3:10.
5. Kodi ndinthaŵi ziti ndipo ndimotani mmene chimwemwe chingasonyezedwere kunja?
5 Ngakhale kuti chimwemwe ndicho mkhalidwe wa mtima wophiphiritsira, nthaŵi zina chikhoza kusonyezedwa kunja. Kodi panthaŵi zina zimenezi, ndimotani mmene chimwemwe chimasonyezedwera kunja? Kungakhale mwanjira iriyonse kuyambira pa kuŵala kwa nkhope mpaka kulumpha kwenikweni ndi chisangalalo. (1 Mafumu 1:40; Luka 1:44; Machitidwe 3:8; 6:15) Pamenepa, kodi zimenezi zimatanthauza kuti anthu osakambakamba kapena amene samamwetulira nthaŵi zonse alibe chimwemwe? Ayi! Chimwemwe chenicheni sichimasonyezedwa ndi kuseketsa, chiphwete, kumwetulira kapena kunyevulira nthaŵi zonse. Mikhalidwe imapangitsa chimwemwe kuwonekera mwanjira zosiyanasiyana. Sichimwemwe chokha chimene chimatikhalitsa ogwirizana bwino pa Nyumba Yaufumu, koma mmalomwake, kuli kusamalirana kwaubale ndi chikondi.
6. Kodi nchifukwa ninji Akristu angamakondwere nthaŵi zonse ngakhale pamene ayang’anizana ndi mikhalidwe yoipa?
6 Mbali yosasintha ya chimwemwe ndiyo kukhalitsa kwake kwamkati monga mkhalidwe weniweni wa umunthu watsopano wa Mkristu. Ichi nchimene chimakupangitsa kukhala kotheka kukondwera nthaŵi zonse. Ndithudi, nthaŵi zina tikhoza kuvutitsidwa maganizo ndi chinachake, kapena tingakhale m’mikhalidwe yoipa. Komabe tingakhalebe ndi chimwemwe mumtima mwathu. Akristu oyambirira ena anali akapolo, okhala ndi ambuye ovuta kukondweretsa. Kodi Akristu oterowo akakhala okondwera nthaŵi zonse? Inde, chifukwa cha chiyembekezo chawo cha Ufumu ndi chimwemwe m’mitima mwawo.—Yohane 15:11; 16:24; 17:13.
7. (a) Kodi Yesu ananenanji ponena za chimwemwe m’masautso? (b) Kodi nchiyani chimene chimatithandiza kupirira pamene tiri m’sautso, ndipo ndani amene anapereka chitsanzo chabwino m’zimenezi?
7 Pamene mtumwi Paulo anati: ‘Kondwerani m’chiyembekezo,’ anawonjezera kuti: “Pirirani m’masautso.” (Aroma 12:12) Yesu analankhulanso za chimwemwe pokhala m’masautso pamene anati pa Mateyu 5:11, 12 (NW): “Achimwemwe muli inu pamene anthu akutonzani ndi kukuzunzani . . . Kondwerani ndi kulumpha chifukwa cha chisangalalo, popeza kuti mphotho yanu iri yaikulu kumwamba.” Kukondwera ndi kulumpha kaamba ka chimwemwe konenedwa panopa sikutofunikira kukhala kwenikweni kowonekera kunja; iko kulidi chiyamikiro chamkati chozama chimene munthu amakhala nacho chakukondweretsa Yehova ndi Yesu Kristu pamene achirimika m’chiyesero. (Machitidwe 5:41) Kwenikweni, chiri chimwemwe chimene chimatithandiza kupirira m’chisautso. (1 Atesalonika 1:6) M’zimenezi, Yesu anapereka chitsanzo chabwino koposa. Malemba amatiuza kuti: “Chifukwa cha chisangalalo chimene chinaikidwa pamaso pake iye anapirira mtengo wozunzirapo.”—Ahebri 12:2, NW.
Kukondwera m’Chiyembekezo Mosasamala Kanthu za Mavuto
8. Kodi ndimavuto otani amene Akristu angayang’anizane nawo, koma kodi nchifukwa ninji mavuto samalanda chimwemwe cha Mkristu?
8 Kukhala mtumiki wa Yehova sikumamasula munthu ku mavuto. Pangakhale mavuto abanja, a chuma, umoyo wamatenda, kapena imfa ya okondedwa. Pamene kuli kwakuti zinthu zoterozo zingatichititse kukhala achisoni, sizimatilanda zifukwa zokondwerera m’chiyembekezo cha Ufumu, chimwemwe cha mkati chimene tiri nacho mumtima mwathu.—1 Atesalonika 4:13.
9. Kodi ndimavuto otani amene Abrahamu anali nawo, ndipo kodi timadziŵa motani kuti iye anali ndi chimwemwe mumtima mwake?
9 Mwachitsanzo, talingalirani Abrahamu. Moyo sunali wokondweretsa nthaŵi zonse kwa iye. Anali ndi mavuto m’banja. Mkazi wake wamng’ono, Hagara, sankamvana ndi mkazi wake Sara. Iwo anali kumalongolola. (Genesis 16:4, 5) Ismayeli ankaseka Isake ndi kumzunza. (Genesis 21:8, 9; Agalatiya 4:29) Pomalizira pake, Sara, mkazi wokondedwa wa Abrahamu, anamwalira. (Genesis 23:2) Mosasamala kanthu za mavutowa, iye anakondwera m’chiyembekezo cha Mbewu ya Ufumu, Mbewu ya Abrahamu, mwa amene mabanja onse apadziko lapansi akadalitsika. (Genesis 22:15-18) Pokhala ndi chimwemwe mumtima mwake, iye anapirira muutumiki wa Yehova kwa zaka zana limodzi pambuyo posiya mzinda wakwawo wa Uri. Chifukwa chake zinalembedwa ponena za iye kuti: ‘Analindirira mudzi wokhala nawo maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.’ Chifukwa cha chikhulupiriro cha Abrahamu cha Ufumu Waumesiya womadzawo, Ambuye Yesu, ataikidwa kale ndi Mulungu kukhala Mfumu, anati: ‘Abrahamu anakondwera kuwona tsiku langa; ndipo anawona, nasangalala.’—Ahebri 11:10; Yohane 8:56.
10, 11. (a) Kodi ndikulimbana kotani kumene ife monga Akristu tiri nako, ndipo kodi timalanditsidwa motani? (b) Kodi nchiyani chimene chimathandiza mmene tilephera kumenya nkhondoyo mwachipambano motsutsana ndi thupi lathu lochimwa?
10 Monga anthu opanda ungwiro, nafenso tiri ndi thupi lochimwa lofunikira kulimbana nalo, ndipo nkhondo imeneyi yakuchita chimene chiri chabwino ingakhale yovutitsa kwambiri. Komabe, kulimbana kwathu ndi zifooko zathu, sikumatanthauza kuti tiribe chiyembekezo. Paulo anavutika ndi kulimbana kumeneku, ndipo anati: ‘Adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi? Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.’ (Aroma 7:24, 25) Kupyolera mwa Yesu Kristu ndi dipo limene analipereka, timalanditsidwa.—Aroma 5:19-21.
11 Nsembe yadipo ya Kristu ndiyo imathandiza mmene tilephera kumenya nkhondoyo mwachipambano. Tingathe kukondwera m’dipo limeneli chifukwa chakuti limatheketsa kukhala ndi chikumbutima choyera ndi kukhululukidwa kwa machimo athu. Pa Ahebri 9:14, Paulo akulankhula za “mwazi wa Kristu” umene uli ndi mphamvu ya ‘kuyeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa.’ Chifukwa chake, zikumbumtima za Akristu siziyenera kulemetsedwa ndi zoipa ndi malingaliro aliŵongo. Ichi, pamodzi ndi chiyembekezo chimene tiri nacho, zimapereka chisonkhezero champhamvu cha chimwemwe chachikulu. (Salmo 103:8-14; Aroma 8:1, 2, 32) Tikamasinkhasinkha pa chiyembekezo chathu, tonsefe tidzalimbikitsidwa kumenya nkhondo mwachipambano.
Kusunga Chiyembekezo Chathu Chiri Choŵala m’Maganizo
12. Kodi Akristu odzozedwa angasinkhesinkhe pa chiyembekezo chotani?
12 Nkofunika kwambiri ponse paŵiri kwa otsalira odzozedwa ndi mzimu ndi nkhosa zina kusunga ‘chiyembekezo cha chipulumutso’ chiri choŵala m’maganizo mwawo, kuchivala monga chisoti chotetezera. (1 Atesalonika 5:8) Akristu odzozedwa angasinkhesinkhe pa mwaŵi wabwino koposa wakulandira moyo wosakhoza kufa kumwamba, akumamfikira Yehova Mulungu, kuyanjana mwaumwini ndi Yesu Kristu wolemekezedwayo ndi atumwi ndi ena onse a 144,000, omwe anasunga umphumphu wawo m’zaka mazana ambiri. Ha, ndimayanjano abwino osaneneka chotani nanga!
13. Kodi odzozedwa okhalabe padziko lapansi amamva motani ponena za chiyembekezo chawo?
13 Kodi odzozedwa ochepa omwe adakali padziko lapansi amamva bwanji ponena za chiyembekezo chawo cha Ufumu? Yankho lake likhoza kuikidwa mwachidule m’mawu a F. W. Franz, prezidenti wa Watch Tower Society, yemwe anabatizidwa mu 1913 akuti: “Chiyembekezo chathu ndichinthu chotsimikizirika, ndipo chidzakwaniritsidwa kotheratu kwa womalizira aliyense wa ziŵalo za a 144,000 a kagulu ka nkhosa kuposa mmene tikulingalirira. Otsalirafe amene tinalipo m’chaka cha 1914, pamene tinayembekezera kuti tonsefe tikapita kumwamba, sitinaleke kuwona kufunika kwa chiyembekezo chimenecho. Koma tichigwiritsabe zolimba, ndipo tikuchimvetsetsa mowonjezereka kwa utali wonse umene tiyenera kuyembekezera. Ndichinthu choyenerera kuchiyembekezera, ngakhale kwa zaka miliyoni. Ndimakwezadi chiyembekezo chathu kuposa ndi kale lonse, ndipo sindimafuna konse kutaya chiyamikiro changa pa icho. Chiyembekezo cha kagulu ka nkhosa chimaperekanso chitsimikizo chakuti chiyembekezo cha khamu lalikulu la nkhosa zina, sichidzalephera konse kukwaniritsidwa koposa zolingalira zathu zabwino koposa. Ndicho chifukwa chake tikugwiritsa kufikira nthaŵi ino, ndipo tidzagwiritsabe kufikira pamene Mulungu atsimikizira kwenikweni kuti ali wowona ku ‘malonjezo a mtengo wake ndi aakulu.’”—2 Petro 1:4; Numeri 23:19; Aroma 5:5.
Kukondwera Tsopano m’Chiyembekezo cha Paradaiso
14. Kodi nchiyembekezo chotani chimene khamu lalikulu limafunikira kusunga m’maganizo?
14 Kusonyeza chikhulupiriro koteroko kodzala ndi chimwemwe kumapatsa akhamu lalikulu a nkhosa zina zifukwa zazikulu zokondwerera. (Chibvumbulutso 7:15, 16) Oterowo ayenera kusumika maganizo pa chiyembekezo cha kupulumuka Armagedo. Inde, penyani kutsogolo kudzawona Ufumu wa Mulungu ukulemekeza ulamuliro wa chilengedwe chonse wa Yehova Mulungu ndi kuyeretsa dzina lake laulemerero mwakubweretsa chisautso chachikulu, chimene chidzachotsa oipa padziko lapansi amene Mdyerekezi wakhala mulungu wawo. Ha, chidzakhala chimwemwe chotani nanga kupulumuka chisautso chachikulu chimenecho!—Danieli 2:44; Chibvumbulutso 7:14.
15. (a) Kodi ndintchito yakuchiritsa yotani imene Yesu anaichita pamene anali padziko lapansi, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi zosoŵa zaumoyo za opulumuka Armagedo zidzakhala zotani, ndipo nchifukwa ninji ziri zosiyana ndi za amene adzaukitsidwa?
15 Ponena za khamu lalikulu, Chibvumbulutso 7:17 chimati: ‘Mwanawankhosa . . . adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi a moyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pawo.’ Ngakhale kuti ulosi umenewu uli ndi kukwaniritsidwa kwauzimu tsopano, opulumuka Armagedo adzauwona ukukwaniritsidwa m’lingaliro lenileni. Motani? Eya, kodi Yesu anachitanji pamene anali padziko lapansi? Iye anachiritsa opunduka, nayendetsa olemala, kutsegula makutu a ogontha ndi maso a akhungu, ndipo anachiritsa khate, manjenje, ndi ‘nthenda iriyonse ndi zofooka zonse.’ (Mateyu 9:35; 15:30, 31) Kodi zimenezo sindizo zimene Akristu afunikira lerolino? Akhamu lalikulu adzaloŵa m’dziko latsopano ndi zifooko zawo za dziko lakale. Kodi muganiza kuti Mwanawankhosa adzachitanji ponena za chimenechi? Zosoŵa za opulumuka Armagedo zidzasiyana kwambiri ndi zosoŵa za awo amene adzaukitsidwa. Oukitsidwawo mwachiwonekere adzalengedwanso ndi matupi athunthu abwino, athanzi, ngakhale kuti adzakhalabe opanda ungwiro waumunthu. Chifukwa cha chozizwitsa cha chiukiriro, iwo mwachiwonekere sadzafunikira kukonzedwanso kwa zifooko zakale mwakuchiritsidwa kozizwitsa. Kumbali ina, chifukwa cha chokumana nacho chawo chapadera cha kupulumuka Armagedo, ambiri a khamu lalikulu adzafunikira kuchiritsa kozizwitsa ndipo adzakulandira. Chifukwa chake, chifuno chachikulu cha kuchiritsa kwa Yesu chinali kusonyeza chiyembekezo chosangalatsa cha khamu lalikulu chakuti sadzangopulumuka koma adzachiritsidwa pambuyo pake.
16. (a) Kodi kuchiritsa kozizwitsa kwa opulumuka Armagedo kuyenera kuti kudzachitika liti, ndipo ndi chotulukapo chotani? (b) Kodi tidzapitirizabe kukondwera m’chiyembekezo chotani m’Zaka Chikwi?
16 Moyenerera, kuchiritsa kozizwitsa koteroko kwa opulumuka Armagedo kuyenera kuti kudzachitika osati kutsogolo kwambiri pambuyo pa Armagedo ndipo pamene nthaŵi ikadalipo chiukiriro chisanayambe. (Yesaya 33:24; 35:5, 6; Chibvumbulutso 21:4; yerekezerani ndi Marko 5:25-29.) Pamenepo anthu adzataya magalasi amaso, ndodo zoyendera, mipando yamagudumu, mano opanga, zothandizira kumvera, ndi zina zotero. Ha, nchifukwa chopereka chimwemwe chotani nanga! Eya, kachitidwe kakukonzanso koyambirira ka Yesu koteroko kamawayeneretsa chotani nanga opulumuka Armagedo kukhala maziko a dziko lapansi latsopano! Matenda ofooketsa adzachotsedwa kotero kuti opulumuka ameneŵa apite patsogolo ndi nyonga yeniyeni, akuyang’ana kutsogolo molakalaka kuwona ntchito yozizwitsa ya m’Zaka Chikwi zokhala patsogolo pawo, osafooketsedwa ndi mavuto amene dziko lakale linachititsa pa iwo. Ndipo M’zaka Chikwi zonsezo, iwo adzakondwera m’chiyembekezo chakufikira ungwiro wokwanira wa moyo wa munthu pofika kumapeto kwa zaka chikwizo.
17. Kodi nchimwemwe chotani chimene chidzakhalapo pamene ntchito yakubwezeretsa Paradaiso ikuchitika?
17 Ngati chimenecho ndicho chiyembekezo chanu, sinkhasinkhaninso pa chimwemwe cha kukhala ndi phande m’kubwezeretsa Paradaiso padziko lapansi. (Luka 23:42, 43) Mosakaikira, opulumuka Armagedo adzathandiza kuyeretsa dziko lapansi ndipo motero kupereka malo abwino kumene akufa adzaukitsidwira. Maliro adzaloŵedwa m’malo ndi zikondwerero zakulandira oukitsidwa, kuphatikizapo okondedwa athu amene anatengedwa ndi imfa. Ndipo talingalirani chisangalalo cha kuyanjana ndi amuna ndi akazi okhulupirika a m’zaka za mazana akale. Kodi ndani makamaka amene mufuna kukambitsirana naye? Kodi ndi Abele, Enoke, Nowa, Yobu, Abrahamu, Sara, Isake, Yakobo, Yosefe, Mose, Yoswa, Rahabi, Debora, Samsoni, Davide, Eliya, Elisa, Yeremiya, Ezekieli, Danieli, kapena Yohane Mbatizi? Eya, pamenepo, chinthu chosangalatsa chimenechi chirinso mbali ya chiyembekezo chanu. Mudzatha kukambitsirana nawo, kuphunzira kwa iwo, ndi kugwira nawo ntchito kupanga dziko lonse lapansi kukhala paradaiso.
18. Kodi nchimwemwe china chotani chimene tingasinkhesinkhe?
18 Talingaliraninso, zakudya zabwino, madzi oyera, ndi mpweya woyera, apo nkuti dziko lathu lapansi litabwezeretsedwa pamkhalidwe wolinganizika mmene Yehova analengera. Moyo panthaŵiyo udzakhala, osati chisangalalo cha ungwiro wa manja lende, koma kukhala ndi phande kokangalika m’ntchito zokondweretsa zaphindu. Chiwoneni m’maganizo mwanu chitaganyacho cha anthu omasuka ku upandu, kunyada, kaduka, kukangana—ubale umene zipatso za mzimu zikukulitsidwa ndi kusonyezedwa ndi onse. Ha, nzochititsa nthumanzi chotani nanga!—Agalatiya 5:22, 23.
Chiyembekezo Chopatsa Chifuno Chokhalira Ndimoyo
19. (a) Kodi nliti pamene kukondwera kotchulidwa pa Aroma 12:12 kudzakhalako? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala otsimikiza mtima kusalola zovuta za moyo kukankhira padera chiyembekezo chathu?
19 Chinthu chimene chakwaniritsidwa sichirinso chiyembekezo, chotero kukondwera kumene kukulimbikitsidwa ndi Paulo pa Aroma 12:12 kuyenera kuchitidwa tsopano. (Aroma 8:24) Kungoganizira madalitso amtsogolo amene Ufumu wa Mulungu udzabweretsa kuyenera kutipangitsa kukondwera m’chiyembekezo tsopano. Chotero tsimikizani mtima kusalola zovuta za moyo m’dziko lino lovunda kukankhira padera chiyembekezo chanu chaulemerero. Musataye mtima ndi kusiya, mukuleka kuwona chiyembekezo chiri patsogolo. (Ahebri 12:3) Kusiya njira Yachikristu sikudzathetsa mavuto anu. Kumbukirani, ngati wina aleka kutumikira Mulungu chifukwa cha zovuta za moyo tsopano, iye akali nazobe zovutazo, komanso amataya chiyembekezo ndipo amalephera panjira ya kudzakondwera m’zinthu zabwino koposa mtsogolo.
20. Kodi chiyembekezo cha Ufumu chiri ndi chiyambukiro chotani pa okhala nacho, ndipo chifukwa ninji?
20 Anthu a Yehova ali ndi zifukwa zabwino zokhalira ndi moyo wachimwemwe. Chiyembekezo chawo choŵala, chochititsa kaso chimapatsa chifuno chokhalira ndimoyo. Ndipo samangokhala nacho okha chiyembekezo chokondweretsa chimenechi. Ayi, amakhala ofunitsitsa kugaŵana ndi ena. (2 Akorinto 3:12) Choncho ziri tero kuti awo okhala ndi chiyembekezo cha Ufumu ali anthu okhala ndi chidaliro, ndipo amafuna kulimbikitsa ena mwakuwauza mbiri yabwino yochokera kwa Mulungu. Ichi chimadzaza miyoyo ya awo amene amalandira uthengawo ndi chiyembekezo chabwino koposa chimene sichinapatsidwepo kwa anthu onse—chiyembekezo cha Ufumu umene udzabwezeretsa Paradaiso padziko lapansi. Ngati anthu saulandira, ife tipitirizabe kukondwera chifukwa chakuti tiri nacho chiyembekezo. Amene amatseka makutu awo ndiwo amene akulephera; sindife ayi.—2 Akorinto 4:3, 4.
21. Kodi nchiyani chimene chiri pafupi, ndipo kodi tiyenera kuchiwona motani chiyembekezo chathu?
21 Lonjezo la Mulungu nlakuti: “Tawonani! ndikupanga zinthu zonse zatsopano.” (Chibvumbulutso 21:5, NW) Dziko latsopano ndi madalitso ake onse ochititsa chidwi ndi osatha ziri pafupi. Chiyembekezo chathu—cha moyo wakumwamba kapena padziko lapansi laparadaiso—chamtengo wapatali; chigwiritsenitu. M’masiku otsiriza ovuta ano, kuposa ndi kalelonse, chiwoneni ‘ngati nangula ya moyo, chokhazikika ndi cholimba.’ Pokhala kuti chiyembekezo chathu chakoloŵekedwa mwa Yehova, “thanthwe losatha—Thanthwe la nyengo za nyengo,” tiridi ndi chifukwa champhamvu ndi chosangalatsa tsopano cha ‘kukondwera m’chiyembekezo’ choikidwa patsogolo pathu.—Ahebri 6:19; Yesaya 26:4, The Amplified Bible.
[Mawu a M’munsi]
a Mu 1992, Mboni za Yehova padziko lonse zidzakhala ndi lemba lachaka lakuti: ‘Kondwerani m’chiyembekezo, . . . limbikani chilimbikire m’kupemphera.’—Aroma 12:12.
Mafunso Openda
◻ Kodi chiyembekezo chachikulu cha anthu nchotani?
◻ Kodi chimwemwe chenicheni nchotani?
◻ Kodi kuchiritsa opulumuka Armagedo kuyenera kuti kudzachitika liti?
◻ Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kulola zovuta za moyo kukankhira padera chiyembekezo chathu?
◻ Kodi nchimwemwe chotani chimene mukuyembekezera m’dziko latsopano?
[Chithunzi patsamba 9]
Kodi mtima wanu sudzasefukira ndi chimwemwe pamene mudzadziwonera mtundu wa kuchiritsa kumene Yesu anakuchita?
[Chithunzi patsamba 10]
Awo okondwera mu Ufumu amalimbikitsa ena mwakugaŵana chiyembekezo chawo