Kodi Nchisungiko cha Mtundu Wotani Chimene Mumachikhumba?
ANTHU osiyanasiyana ali ndi malingaliro osiyana ponena za chisungiko. Ena amachiwona kukhala kumvana kwa maulamuliro otsutsana amphamvu koposa m’zankhondo. Mwachitsanzo, maulamuliro amene ali amphamvu koposa padziko lonse pamodzi ndi ogwirizana nawo a ku Yuropu amamvana panjira zambiri zochepetsera upandu umene ungapangitse zochitika zazing’ono kubutsa nkhondo yanyukliya padziko lonse. Stockholm International Peace Research Institute Yearbook 1990 inasonyeza kudabwa ponena za kusakondwera ndi njira zoterozo kwa maiko a “m’madera ena a dziko lapansi.”
Komabe, kwa mamiliyoni okhala m’maiko osauka, “chisungiko” chimatanthauza chakudya chokwanira ndi chisamaliro chazamankhwala. “Polingalira za ‘mtendere ndi chisungiko,’” akulongosola tero katswiri wa zandale Yash Tandon, “malingaliro ofala a kutsungula kowonekeratu kwa Kumadzulo amapambana. . . . ‘Chisungiko’ chimawonedwa kukhala nkhani ya zida ndi kuchepetsa kapena kuziwononga zidazo, lingaliro losiyana kotheratu ndi nkhaŵa za chisungiko za anthu anjala ndi opanda nyumba opanga zigawo ziŵiri mwa zitatu za anthu padziko lonse.”
Ponena za Baibulo, limalonjeza kuti mu Ufumu wa Mulungu simudzakhalanso nkhondo. “Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magareta ndi moto.” (Salmo 46:9; Yesaya 2:4) Kudwala kwakuthupi kudzakhala mbiri yakale. ‘Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala m’menemo, adzakhululukidwa mphulupulu zawo.’—Yesaya 33:24.
Mu Ufumuwo, palibe amene adzakhala wopanda chisungika cachuma. ‘Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya.’—Yesaya 65:21, 22.
Komabe, chofunika koposa chimene Ufumuwo udzachita ndicho kuchotsa maziko enieni osoŵetsa mtendere ndi chisungiko. Kodi ndani yemwe wakhala kumbuyo kwa mbiri ya munthu ya maboma otsendereza ndi olepherawo? Ngakhale kuti Mulungu wawalola kukhalako pachifukwa chabwino, Satana yemwe ndiye wokhala ndi thayo, pakuti Baibulo limati ‘dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.’—1 Yohane 5:19.
Pamenepo, padzakhala mpumulo wotani nanga pamene mawu a Paulo kwa Aroma adzakwaniritsidwa potsirizira pake mu Ufumu wa Mulungu: “Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino”! (Aroma 16:20) Ufumu wakumwamba wa Mulungu wokha, wolamuliridwa ndi Mfumu Yesu Kristu, udzachita zimenezo. Chifukwa chake, Ufumu wokhawo ndiwo udzasanduliza dziko lapansi kukhala paradaiso.—Genesis 1:28; Luka 23:43.
Inde, chisungiko cholonjezedwa m’Baibulo nchopambana ndi chokhudza mbali zonse kuposa chirichonse cholinganizidwapo ndi anthu. Eya, timaŵerenga kuti ‘sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa’! (Chivumbulutso 21:4) Kodi tingakhulupirire malonjezo otero? Inde, chifukwa chakuti achokera kwa Mlengi wamphamvuyonse, Yehova Mulungu, amenenso akulengeza kuti: ‘ . . . Mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.’ (Yesaya 55:11) Chipambano chotsimikizirika chikuwonekera m’zimene Yehova Mulungu akuchita ngakhale tsopano lino kudzetsera anthu mtendere wosangalatsa ndi wachikhalire, chisungiko, ndi kukhupuka kotero kuti uchifumu Wake wosatha ulemekezedwe.