Bwerani ku Msonkhano Wachigawo wa “Onyamula Kuunika”
“TAONA, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu.” (Yesaya 60:2) Ha, ngowona chotani nanga mawu amenewo! Mosakaikira, chipembedzo chonyenga chaika anthu mumdima ponena za kulambira kumene kumamkondweretsa Mulungu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Satana, mulungu wa dongosolo la zinthu liripoli, ‘wachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira.’—2 Akorinto 4:4.
Mboni za Yehova nzosiyana kotheratu ndi awo ochititsidwa khungu ndi Satana. Mawu a mneneri Yesaya amagwira ntchito pa izo akuti: ‘Yehova adzakutulukira, ndi ulemerero wake udzawoneka pa iwe.’ (Yesaya 60:2) Nzoyamikira chotani nanga Mbonizo kuti zinatuluka mumdima ndi kuloŵa m’kuunika kwa Mulungu kodabwitsa! Kuli kuunika kwauzimu, chowonadi cha Mawu a Mulungu amene amaunikira maganizo, kotero kuti ngakhale akhungu enieniwo akhoza kuchiwona chowonadicho.
Komabe, pamafunikiradi chithandizo. Sikotheka kwenikweni kuti munthu amene amangoŵerenga Baibulo popanda kugwiritsira ntchito zithandizo zoperekedwa ndi Mulungu angathe kukuwona kuunikako. Nchifukwa chake Yehova Mulungu wapereka “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” wonenedweratu pa Mateyu 24:45-47. Lerolino “kapolo” ameneyo amaimiridwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Msonkhano Wachigawo wa “Onyamula Kuunika” wakonzedwa pansi pa chitsogozo cha bungwe limeneli.
Chifuno cha msonkhano umenewu ndicho kuthandiza anthu a Yehova onse kukhala onyamula kuunika abwinopo, mogwirizana ndi Mawu a Paulo pa Afilipi 2:15. Pamenepo, Akristu akulangizidwa kuŵala monga “mauniko m’dziko lapansi.”—Mateyu 5:14, 16.
Mu Zambia, Misonkhano Yachigawo ya “Onyamula Kuunika” idzayamba pa Lachisanu, August 14. Pa 9:20 a.m., programu ya nyimbo zamalimba idzatsitsimula maganizo ndi mitima ya onse, kuwakonzekeretsa programu yauzimu yotsatira. Tsiku lirilonse liri ndi mutu wake, ndipo mutu wa Lachisanu udzakhala wakuti “Walitsani Kuunika Kwanu ndi Chowonadi Chanu.”—Salmo 43:3.
Programu ya pa Lachisanu mmaŵa idzakhala ndi nkhani yaikulu yakuti, “Onyamula Kuunika—Kaamba ka Chifuno Chotani?” Ndithudi, Akristu sali onyamula kuunika kaamba ka cholinga chaumwini chadyera chirichonse. Mmalomwake, iwo amatumikira pazifukwa zofanana ndi zimene Yesu Kristu, Wonyamula Kuunika Wamkulu, anadzera padziko lapansi, kudzachitira umboni chowonadi ndi kulemekeza dzina la Mlengi. Moyenerera, Yesu anati ponena za mwini yekha: ‘Pakukhala ine m’dziko lapansi, ndiri kuunika kwa dziko lapansi.’ (Yohane 9:5) Motero, iye anatisiira chitsanzo chakuti titsatire mapazi ake mosamalitsa. (1 Petro 2:21) Programu yamasana patsiku loyamba limenelo idzapereka nkhani ndi drama ya m’Baibulo yochita ndi Mfumu Yosiya, imene idzakhala ndi chifuno chapadera kwa achichepere.
Mutu wa pa Loŵeruka udzakhala wakuti “Ndinu Kuunika kwa Dziko Lapansi . . . Muwalitse Inu Kuunika Kwanu.” (Mateyu 5:14, 16) Programu yammaŵa idzakhala ndi nkhani yosiirana yakuti “Kuwalitsa Kuunika Kwanu.” Padzakhala mwaŵi wakubatizidwa kwa awo omwe adzipatulira kwa Yehova. Programu yamasana idzakhala ndi nkhani yosiirana yotsegula maso ya mutu wakuti “Kuwalitsa Kuunika pa Kukhalapo kwa Kristu ndi Chivumbulutso.”
Mutu wosankhidwa wa pa Sande, tsiku lachitatu ndi lomaliza la msonkhanowo, ngwakuti “Yendanibe Monga Ana a Kuunika.” (Aefeso 5:8) Programu yammaŵa idzakhala ndi nkhani yosiirana ya mutu wakuti “Kusamalirana m’Banja Lachikristu,” imene idzachita ndi mathayo a m’banja. Padzakhalanso nkhani yofotokoza zimene kugonjera kwa Mulungu ndi Kristu kumatanthauza.
Msonkhano udzafika pakaindeinde pa Sande masana ndi nkhani yapoyera ya mutu wakuti “Tsatirani Kuunika kwa Dziko.” Nkhani imeneyi idzakhala ndi kukambitsirana kwa Yohane 1:1-16 ndipo idzasonyeza kufunika kwa chidziŵitso cha Baibulo, kugogomezera mfundo yakuti Yesu Kristu ndiye kuunika kwa dziko. Msonkhano udzatha ndi chilimbikitso champhamvu chakuti “Yendanibe m’Kuunika.”
Sonyezani kuyamikira kwanu phwando lauzimu limeneli limene Yehova akugaŵira kupyolera mwa gulu lake lowoneka. Khalanipo kuyambira pa nyimbo yotsegulira pa Lachisanu mpaka pemphero lothera pa Sande masana. Tcherani khutu mosamalitsa ku zonse zimene zidzanenedwa papulatifomu. Lembani nsonga kuti zikuthandizeni kusumika maganizo ndi kuzigwiritsira ntchito mtsogolo. Chomalizira, konzekerani kukakhala ndi phande m’ntchito zina zodzifunira. Mwakutero, mudzasangalala osati ndi madalitso akulandira okha komaso ndi madalitso aakulu akupatsa.—Machitidwe 20:35.