Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 8/1 tsamba 3-4
  • Moyo—Mphatso Yochokera kwa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Moyo—Mphatso Yochokera kwa Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Moyo wa Munthu Umayamba Liti?
    Galamukani!—2009
  • Kubadwira M’dziko Lopanda Chikondi!
    Galamukani!—2004
  • Kodi Ndiliti Pamene Moyo wa Munthu Umayambika?
    Galamukani!—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 8/1 tsamba 3-4

Moyo​—Mphatso Yochokera kwa Mulungu

KWA MAOLA makumi aŵiri ndi anayi patsiku, mtima wathu umapopera m’thupi lathu mwazi wamtengo wapatali. Timagona tulo, ndipo mapapu athu amafutukuka nachepa mopitirizabe. Timadya chakudya, ndipo chakudyacho chimapukusika chokha. Zonsezi zimachitika tsiku lirilonse, movutikira pang’ono kapena mosavutikira nkomwe kumbali yathu. Zochitika zachinsinsi ndi zozizwitsa zimenezi, zimene mosavuta zimangolingaliridwa mosasamala, ziri mbali ya mphatso imene timaitcha moyo. M’kunena kwina ndimphatso imene ingatchedwe yozizwitsa.

Talingalirani za kachitidwe ka kutenga pathupi ndi kubala. Ngakhale kuti thupi mwachibadwa limakana mnofu wachilendo, chibereko chimapatulapo dzila lopatsidwa mphamvu ya moyo. Mmalo mwakukana mluza womakulawo monga mnofu wachilendo, chimaudyetsa ndi kuutetezera kufikira pamene ukonzeka kutuluka monga khanda. Popanda luso la chibereko lakupanga kupatula kodabwitsa koteroko mosasamala kanthu za lamulo lakukana mnofu wachilendo, kubadwa kwa anthu kukanakhala kosatheka.

Ngakhale ziri choncho, moyo wa khanda lobadwa kumene ukanakhala waufupi popanda zimene zimachitika m’mimba pamene kamwana kosabadwako kali pafupifupi miyezi inayi yokha. Panthaŵi imeneyo kamayamba kuyamwa chala chake chamanthu, kumazoloŵeza minyewa imene pambuyo pake idzakakhozetsa kuyamwa maŵere a amayi ake. Ndipo iyi ndi imodzi ya nkhani zakukhala ndi moyo kapena kufa zimene zimathetsedweratu khandalo lisanabadwe.

Kamwana kosabadwako kakali m’mimba, pamakhala chibowo pamtima wake. Komabe, chibowochi chimatsekeka chokha pakubadwa. Ndiponso, mtsempha waukulu wamwazi umene umadutsa mapapu kamwanako kakali m’mimba umanyombotoka pakubadwa; tsopano mwazi umapita ku mapapu, kumene umakatenga okosijeni pamene khandalo liyamba kupuma.

Zonsezi ndichiyambi chabe. M’moyo wonse, madongosolo olinganizidwa mozizwitsa (onga madongosolo a kupuma, kuyenda kwa mwazi, minyewa, ndi lakutulutsa mahomoni) amagwira ntchito ndi kugwirizanitsa ntchito zake mwaluso limene palibe munthu akhoza kulimvetsetsa​—zonsenzotu kuchitira kuti moyo upitirizebe. Mposadabwitsa kuti wolemba wamakedzana ananena mawu aŵa ponena za Mulungu: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchowopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu.”​—Salmo 139:14.

Mwachiwonekere, wolemba mawu abwino amenewo sanakhulupirire kuti moyo uli kanthu kodzichitikira kokha, kapena kongosinthika mwangozi. Zikadakhala choncho, sitikadakhala ndi zotikakamiza zenizeni kapena mathayo ponena za mmene tiyenera kugwiritsirira ntchito miyoyo yathu. Komabe, kapangidwe ka ziwalo zathupi ndi mmene zimagwirira ntchito kamasonyeza bwino lomwe kuti panali kulinganiza, ndipo kulinganizako kumafunikira wolinganiza. Baibulo limapereka mkhalidwe uwu: “Pakuti nyumba iriyonse iri naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.” (Ahebri 3:4) Chotero kuli kofunika kwambiri ‘kudziŵa kuti Yehova ndiye Mulungu; iyeyu anatilenga, ndipo siife eni.’ (Salmo 100:3) Inde, moyo singozi yochitika yokha; uli mphatso yochokera kwa Mulungu iyemwini.​—Salmo 36:9.

Popeza kuti ziri motero, kodi ndizotikakamiza zotani zimene tiri nazo kulinga kwa Mpatsi wa moyo? Kodi amatiyembekezera kugwiritsira ntchito miyoyo yathu motani? Awa ndi mafunso ena ofanana adzalingaliridwa m’nkhani yotsatira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena