Chikristu Chadziko ndi Malonda a Akapolo
M’ZAKA za zana la 19, amishonale Achikatolika ndi Achiprotesitanti anali ogwirizana m’kutsutsa kwawo malonda a akapolo. Komabe, kameneko sikanali kaimidwe kawo kanthaŵi zonse. M’zaka mazana zoyambirira, iwo anavomereza ndi kutenga mbali m’malonda a akapolo mosasamala kanthu za mavuto owopsa amene malondawo anadzetsa.
Amishonale anayamba kufika kugombe la kum’maŵa ndi kumadzulo kwa Afirika pamene njira yapanyanja ya malonda yodzera ku Cape of Good Hope inatulukiridwa m’zaka za zana la 15. Komabe, patapita zaka mazana atatu, ntchito yaumishonale mu Afirika inatsala pang’ono kutha. Munali otembenuka oŵerengeka mu Afirika. Chimodzi cha zifukwa za kulepheraku chinali kuloŵetsedwa kwa Chikristu Chadziko m’malonda a akapolo. C.P. Groves anafotokoza motere mu The Planting of Christianity in Africa:
“Kulondola mwachangu malonda a akapolo kunatsagana ndi amishoni Achikristu ndipo sikunalingaliridwe kukhala kolakwika. Ndithudi, amishoni enieniwo anali ndi akapolo awo; nyumba ya agulupa Achijezwiti ku Loanda [tsopano Luanda, likulu la Angola] inali ndi okwanira 12,000. Pamene malonda a akapolo anayamba pakati pa Angola ndi Brazil, bishopu wa Loanda, atakhala pampando wamwala m’mbali mwa doko, anapereka dalitso lake laubishopu kwa akatundu okhala paulendo, akumawalonjeza chimwemwe chamtsogolo zitatha ziyeso zowopsa za moyo.”
Amishonale Achijezwiti “[sana]tsutse kugwidwa ukapolo kwa Akuda,” anatsimikizira motero C. R. Boxer wogwidwa mawu m’bukhu la Africa From Early Times to 1800. Ku Luanda, akapolowo asanakwere zombo zopita kumaiko olamuliridwa ndi Aspanya ndi Apwitikizi, anawonjezera motero Boxer, “anatengeredwa kutchalitchi chapafupi . . . ndipo kumeneko anabatizidwa ndi wansembe wa deralo m’timagulu mazanamazana panthaŵi imodzi.” Ndiyeno, atawazidwa “madzi oyera,” akopolowo anauzidwa kuti: “Tawonani anthunu kuti muli kale ana a Mulungu; mukupita kudziko la Aspanya kumene mudzaphunzira zinthu za Chikhulupiriro. Musakumbukirenso za kumene munachokera . . . Pitani ndi mtima wokondwera.”
Ndithudi, sanali amishonale a Chikristu Chadziko okha amene anavomereza malonda a akapolo. “Kufikira theka lomalizira la zaka za mazana khumi ndi asanu mphambu atatu,” akufotokoza motero Geoffrey Moorhouse m’bukhu lake la The Missionaries, “unali mkhalidwe wa dziko lonse.” Moorhouse akutchula chitsanzo cha mmishonale Wachiprotesitanti wa m’zaka za zana la 18, Thomas Thompson, amene analemba trakiti lotchedwa The African Trade for Negro Slaves Shown to Be Consistent With the Principles of Humanity and With the Laws of Revealed Religion.
Chikhalirechobe, mwakutengamo mbali kwake Chikristu Chadziko chirinso ndi thayo la kuvutika kowopsa kumene kunali pa mamiliyoni ambiri a akapolo Achifirika. “Kusiyapo akapolo amene anafa asanayambe ulendo wapanyanja kuchoka mu Afirika,” imatero The Encyclopædia Britannica, “121/2% anafera paulendo wawo wa ku West Indies; ku Jamaica 41/2% anafa ali pamadoko kapena asanagulitsidwe ndiponso chigawo chimodzi mwa zitatu anafa ‘pozoloŵeretsedwa.’”
Posachedwapa Yehova Mulungu adzaŵerengera mlandu ponse paŵiri Chikristu Chadziko ndi mipangidwe ina ya chipembedzo chonyenga chifukwa cha zochita zawo zankhanza za kukhetsa mwazi kumene zalolera ndipo ngakhale kudalitsa.—Chivumbulutso 18:8, 24.
[Chithunzi patsamba 8]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Chithunzithunzi chosonyeza mmene akapolo anali kulongedwera m’chombo cha akapolo
[Mawu a Chithunzi]
Schomburg Center for Research in Black Culture / The New York Public Library / Astor, Lenox and Tilden Foundations