Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 9/15 tsamba 3-7
  • Kodi Nchifukwa Ninji Anthu Abwino Amavutika?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchifukwa Ninji Anthu Abwino Amavutika?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mavuto a Yobu
  • Mulungu Alibe Chifukwa
  • Abwino ndi Oipa Omwe Amavutika
  • Chifukwa Chake Anthu Owopa Mulungu Amavutika
  • Mwamsanga​—Sipadzakhalanso Kuvutika!
  • Yobu Anali Munthu Wopirira ndi Wosunga Umphumphu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Mavuto
    Galamukani!—2015
  • Yobu Anapirira—Nafenso Tingatero!
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Yobu Analemekeza Dzina la Yehova
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 9/15 tsamba 3-7

Kodi Nchifukwa Ninji Anthu Abwino Amavutika?

CHAKACHO chinali 1914, ndipo dziko linali munkhondo. Mwadzidzidzi, malungo a typhus anabuka mumsasa wa asilikali ogwidwa ukaidi mu Serbia. Koma kumeneko kunali kuyamba chabe. Nthenda yoipa imeneyi inafalikira kwa anthu wamba ndi kupha anthu 150,000 m’miyezi isanu ndi umodzi yokha. Mkati mwa mikhalidwe ya nkhondo ndi chipanduko zimene zinachitika mu Russia, mamiliyoni atatu anafa ndi typhus. Mungagamule molondola kuti anthu abwino ambiri ndi ziŵalo za mabanja awo zamasiye zinali pakati pa mikholeyo.

Zimenezi ziri chitsanzo chimodzi chokha cha tsoka la anthu. Inu mwininu mungakhale mutavutika ndi mavuto omwe amakhalapo pamene okondedwa akhala mikhole ya matenda, ngozi, ndi masoka a mitundu yosiyanasiyana. Mwachiwonekere, mumavutika pamene munthu wolungama akanthidwa ndi vuto la nthenda yosachiritsika. Mwinamwake mumamva chisoni kwambiri pamene munthu wabwino​—mwinamwake munthu wina wabanja wogwira ntchito zolimba​—aphedwa m’ngozi. Kuchitira chisoni amasiye kungapangitse mtima wanu kuvutika.

Ambiri amalingalira kuti munthu amene amachita zabwino ayenera kufupidwa ndi kusavutika. Ena amalingaliradi kuvutika kukhala umboni wakuti mkholewo ndiwo wochita cholakwa. Chimenechi chinali chitsutso cha amuna ena atatu amene anakhalako zaka 3,600 zapitazo. Iwowa anali anzake a munthu wina wabwino wotchedwa Yobu amene anakhalapo panthaŵi yofananayo. Tiyeni tibwerere mmbuyo kutsiku lawo pamene tikuyamba kufunafuna kwathu yankho la funsolo, Kodi nchifukwa ninji anthu abwino amavutika?

Mavuto a Yobu

Pamene oyenera kukhala mabwezi atatu a Yobu anadzamzonda, iye anali kuvutika mosaneneka ndi ululu ndi matenda. Anali ataferedwa ndi ana ake khumi ndipo anali atatayikiridwa ndi chuma chake chonse chakuthupi. Anthu amene analemekeza kwambiri Yobu ananyansidwa naye. Ngakhale mkazi wake sanamchirikize ndipo anamfulumiza kutukwana Mulungu ndi kufa.​—Yobu 1:1–2:13; 19:13-19.

Kwamausana asanu ndi aŵiri ndi mausiku, odzazonda Yobuwo anamzonda mwakachetechete. Ndiyeno mmodzi wa iwo anamuimba mlandu wa khalidwe lina losalungama limene mwinamwake anali kulangidwira. “Takumbukira tsopano,” anatero munthuyo Elifazi: “Watayika ndani wosapalamula konse? Kapena owongoka mtima alikhidwa kuti? Monga umo ndawonera, olimira mphulupulu, nabzala vuto, akololapo zomwezo. Atayika ndi mpweya wa Mulungu, nathedwa ndi mpumo wa mkwiyo wake.”​—Yobu 4:7-9.

Chotero, Elifazi anaumirira kuti Mulungu anali kulanga Yobu chifukwa cha machimo ake. Lerolinonso, ena amanena kuti masoka ndiwo zochita za Mulungu zolinganizidwira kulanga anthu ochita zolakwa. Koma Yehova sanali kulanga Yobu chifukwa cha kuchita ntchito zolakwa. Timadziŵa zimenezi chifukwa chakuti pambuyo pake Mulungu anauza Elifazi kuti: “Mkwiyo wanga wakuyakira iwe ndi mabwenzi ako aŵiri, pakuti simunandinenera choyenera monga ananena mtumiki wanga Yobu.”​—Yobu 42:7.

Mulungu Alibe Chifukwa

Lerolino, mamiliyoni​—ndithudi kuphatikizapo anthu abwino ambiri​—ngaumphaŵi ndipo ali paupandu wakufa ndi njala. Anthu ena amakhala owaŵidwa mtima ndi kuimba mlandu Mulungu wa kuvutika kwawo. Koma iye sayenera kuimbidwa mlandu kaamba ka njala. Kwenikweni, iye Ndiye amene amagaŵira anthu chakudya.​—Salmo 65:9.

Dyera, umbombo, ndi zochititsa zina za anthu zingalepheretse kutengeredwa kwa chakudya kwa anthu anjala. Nkhondo iri pakati pa zochititsa njala. Mwachitsanzo, The World Book Encyclopedia imati: “Nkhondo ingachititse njala ngati alimi ambiri aleka kulima minda yawo nagwirizana ndi magulu ankhondo. M’zochitika zina, gulu lankhondo lachita dala kuti pakhale njala kukhaulitsa mdani kuti agonje. Gulu lankhondo limawononga chakudya chosungidwa ndi dzinthu dza m’munda ndi kutchinga njira kuimitsa chakudya cha mdani. Kutchingidwa kwa njira kunaletsa chakudya kufika m’chigawo cha Biafra mkati mwa Nkhondo Yachiŵeniŵeni ya Nigeria (1967-70). Njala inayambika, ndipo mwinamwake Abiafra oposa miliyoni anafa ndi njala.”

Ambiri anaimba mlandu Mulungu molakwa makamaka mkati mwa Nkhondo Yadziko II, pamene anthu abwino ambiri anavutika ndi kufa. Komabe, anthu amaswa malamulo a Mulungu mwa kudana ndi kumenyana. Pamene Yesu Kristu anafunsidwa kuti ndilamulo liti limene linali ‘loyambirira,’ iye anayankha kuti: “Lamtsogolo ndili, Mvera, Israyeli; Ambuye Mulungu wathu, Ambuye ndiye mmodzi; ndipo uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse. Lachiŵiri ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina la kuposa awa.”​—Marko 12:28-31.

Pamene anthu aswa malamulo a Mulungu mwa kuloŵa m’kupha kwa chipiyoyo, kodi pali munthu amene angamuimbe mlandu ngati kuvutika kuchitika? Ngati kholo liuza ana ake kusamenyana ndipo iwo nanyalanyaza uphungu wake wabwinowo, kodi ilo liri ndi mlandu ngati iwo avulala? Khololo liribe mlandu monga momwe Mulungu alibe mlandu wa kuvutika kwa anthu pamene iwo anyalanyaza malamulo a Mulungu.

Ngakhale kuti kuvutika kungachitike pamene malamulo a Yehova anyalanyazidwa, Baibulo silimasonyeza kuti masoka a wamba ali ntchito za Mulungu zolinganizidwira kulanga oipa. Pamene anthu aŵiri oyamba anachimwa, anatayikiridwa ndi madalitso ake apadera ndi chitetezo. Kusiyapo m’zochitika zina za kuloŵerera kwaumulungu kaamba ka kukwaniritsidwa kwa zifuno za Yehova, zimene zachitikira anthu tsiku ndi tsiku zalamuliridwa ndi lamulo la makhalidwe abwino Lamalemba iri: “Omwe athamanga msanga sapambana m’liŵiro ngakhale olimba sapambana m’nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziŵitsa sawakomera mtima; koma yense angowona zomgwera m’nthaŵi mwake.”​—Mlaliki 9:11.

Abwino ndi Oipa Omwe Amavutika

Kwenikweni, anthu abwino ndi oipa omwe amavutika chifukwa cha choloŵa cha uchimo ndi kupanda ungwiro. (Aroma 5:12) Mwachitsanzo, anthu olungama ndi oipa mofananamo amadwala nthenda zopweteka. Mkristu wokhulupirikayo Timoteo anavutika ndi ‘zofooka zobwera kaŵirikaŵiri.’ (1 Timoteo 5:23) Pamene mtumwi Paulo anatchula za “munga m’thupi” wa iye mwini, iye angakhale anali kusonya kunthenda ina yakuthupi. (2 Akorinto 12:7-9) Ngakhale kwa atumiki ake okhulupirika, Mulungu samachotsa choloŵa cha uchimo tsopano kapena kuyambukiridwa ndi nthenda.

Anthu owopa Mulungu angavutikenso chifukwa cha kugwiritsira ntchito chiweruzo choipa kapena kulephera kugwiritsira ntchito uphungu Wamalemba panthaŵi zina. Mwachitsanzo: Munthu amene samamvera Mulungu ndi kukwatirana ndi wosakhulupirira angavutike ndi mavuto a muukwati amene akanawapeŵa. (Deuteronomo 7:3, 4; 1 Akorinto 7:39) Ngati Mkristu samadya moyenera ndipo samapuma mokwanira, angavutike chifukwa cha kuwononga thanzi lake.

Kuvutika ndi malingaliro kungakhalepo ngati tigonjera uchimo ndi kuloŵa m’khalidwe loipa. Chigololo cha Mfumu Davide ndi Batiseba chinamdzetsera mavuto aakulu. (Salmo 51) Pamene anali kuyesa kubisa kuchitidwa kwa cholakwacho, iyeyu anasautsidwa kwambiri. “Pamene ndinakhala chete,” iye anatero, “mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse. . . . uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.” (Salmo 32:3, 4) Kuthedwa nzeru paliwongo lake kunachepetsa nyonga ya Davide monga momwe mtengo ungatayikiridwe ndi uwisi mkati mwa chilala kapena m’chilimwe. Mwachiwonekere iye anavutika m’malingaliro ndi kuthupi komwe. Koma Salmo 32 limasonyeza kuti kuvutika kotero kungachiritsidwe mwa kuulula tchimo kwa munthu ndi kulapa ndi kulandira chikhululukiro cha Mulungu.​—Miyambo 28:13.

Kaŵirikaŵiri anthu oipa amavutika chifukwa cha kulondola njira yachiwerewere, osati monga chilango cha Mulungu. Herode Wamkulu anali wodzazidwa ndi nthenda chifukwa cha zizolowezi zoipa. M’masiku ake otsiriza, Herode “anavutika ndi mazunzo owopsa,” anatero wolemba mbiri Wachiyuda Josephus. “Iye anali ndi chilakolako chachikulu cha kudzikanda, thumbo lake linachita zironda, ndipo mpheto yake inali ndi zironda zonyeka ndi ya mphutsi. Iye anayesayesa mosaphula kanthu kuloŵa m’dziwe la madzi otentha la ku Callirrhoe kuthetsa kusapuma bwino ndi kubwebweta. . . . Tsopano Herode anali kuvutika ndi ululu waukulu kwakuti anayesa kudzibaya, koma analetsedwa ndi msuwani wake.”​—Josephus: The Essential Writings, lotembenuzidwa ndi kukonzedwa ndi Paul L. Maier.

Kulabadira lamulo la Mulungu kumagaŵira chitetezo pa zinthu zonga nthenda zopatsirana mwa kugonana. Komabe, kodi nchifukwa ninji anthu abwino ofunafuna chiyanjo chake amawonekera kukhala ali ndi mbali yaikulu ya kuvutika?

Chifukwa Chake Anthu Owopa Mulungu Amavutika

Chifukwa chachikulu chimene anthu owopa Mulungu amavutikira nchakuti iwo ngolungama. Zimenezi zikufotokozedwa mwa fanizo m’nkhani ya Yosefe mwana wamwamuna wa khololo Yakobo. Ngakhale kuti mkazi wa Potifara mopitirizabe analimbikitsa Yosefe kugonana naye, iye anafunsa kuti: “Ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?” (Genesis 39:9) Zimenezi zinamchititsa kumangidwa kosayenera, ndipo Yosefe anavutika chifukwa chakuti anali wolungama.

Koma kodi nchifukwa ninji Mulungu amalola atumiki ake okhulupirika kuvutika? Yankho lake lagona m’nkhani imene inadzutsidwa ndi mngelo wopandukayo Satana Mdyerekezi. Nkhani imeneyi imakhudza umphumphu kwa Mulungu. Kodi timadziŵa motani? Chifukwa chakuti zimenezi zinasonyezedwa m’chochitika cha munthu wolungamayo Yobu, wotchulidwa poyambirira.

Pamsonkhano wa ana a Mulungu aungelo kumwamba, Yehova anafunsa Satana kuti: “Kodi wawonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi wowongoka, wakuwopa Mulungu ndi kupeŵa zoipa.” Yankho la Mdyerekezi limatsimikizira kuti panali mkangano wonena za kuti kaya anthu akasungabe umphumphu kwa Yehova poyesedwa. Satana anatsutsa kuti Yobu anatumikira Mulungu chifukwa cha madalitso a zinthu zakuthupi zimene anali nazo ndipo osati chifukwa cha chikondi. Ndiyeno Satana anati: “Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira [Yobu] zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pankhope panu.” Yehova anayankha kuti: “Tawona, zonse ali nazo zikhale m’dzanja mwako; pa iye pokha usatambasula dzanja lako.”​—Yobu 1:6-12.

Mosasamala kanthu ndi zonse zimene Satana anachita, Yobu anasunga njira yachilungamo ndi kutsimikizira kuti anatumikira Yehova chifukwa cha chikondi. Ndithudi, Yobu anauza omuimba mlandu kuti: “Sindivomereza konse kuti muli olungama; mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.” (Yobu 27:5) Inde, osunga umphumphu otero nthaŵi zonse akhala ofunitsitsa kuvutika kaamba ka chilungamo. (1 Petro 4:14-16) Baibulo limanena za anthu ambiri amene anali ndi chikondi chosalephera cha Mulungu ndi amene akhala ndi miyoyo yolungama kumlemekeza ndi kutsimikizira mawu a Satana akuti iye akanachotsa anthu onse kwa Yehova kukhala onama. Munthu aliyense amene amavutika chifukwa cha kusunga umphumphu kwa Mulungu angakhale wachimwemwe kuti akutsimikizira Mdyerekezi kukhala wabodza ndipo akupangitsa mtima wa Yehova kukondwera.​—Miyambo 27:11.

Sikuti Mulungu ngwosadera nkhaŵa ponena za kuvutika kwa atumiki ake okhulupirika. Davide wamasalmo anati: “Yehova agwiriziza onse akugwa, nawongoletsa onse owerama.” (Salmo 145:14) Awo amene ali odzipatulira kwa Yehova angasoŵe nyonga yokwanira kupirira mavuto a moyo ndi chizunzo chimene amakumana nacho monga anthu ake. Koma Mulungu amalimbikitsa ndi kuwachirikiza ndipo amawapatsa nzeru yofunika kupirira mayesero awo onse. (Salmo 121:1-3; Yakobo 1:5, 6) Ngati ozunzawo apha ena a atumiki okhulupirika a Yehova, iwo ali ndi chiyembekezo cha chiukiriro choperekedwa ndi Mulungu. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Ngakhale kufikira kumlingo umenewo, Mulungu angasinthe ziyambukiro za kuvutika kulikonse zochitikira awo amene amamkonda. Anathetsa kuvutika kwa Yobu ndipo anadalitsa kwambiri munthu wowongoka mtima ameneyo. Ndipo tingakhale achidaliro chakuti Yehova sadzasiya anthu ake m’tsiku lathu.​—Yobu 42:12-16; Salmo 94:14.

Mwamsanga​—Sipadzakhalanso Kuvutika!

Chotero, pamenepo, aliyense amavutika chifukwa cha kupanda ungwiro kwa choloŵa ndi moyo mkati mwa dongosolo lino loipa la zinthu. Anthu owopa Mulungu angayembekezerenso kuvutika chifukwa cha kusunga umphumphu kwa Yehova. (2 Timoteo 3:12) Koma angathe kusangalala, pakuti mwamsanga Mulungu adzachotsa misozi, imfa, maliro, kulira, ndi choŵaŵitsa. Ponena za zimenezi, mtumwi Yohane analemba kuti:

“Ndinawona mmwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti mmwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja. Ndipo ndinawona mzinda woyerawo, Yesusalemu watsopano, ulikutsika kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake. Ndipo ndinamva mawu aakulu ochokera kumpando wachifumu, ndi kunena Tawonani, chihema cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita. Ndipo iye wakukhala pampando wachifumu anati, Tawonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mawu awa ali okhulupirika ndi owona.”​—Chivumbulutso 21:1-5.

Mofananamo, mtumwi Petro analengeza kuti: “Koma monga mwa lonjezano lake [la Yehova Mulungu] tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Ndimadalitso aakulu chotani nanga omwe ali patsogolopa! Moyo m’paradaiso wapadziko lapansi ungakhale mwaŵi wanu wokondweretsa. (Luka 23:43) Chifukwa chake, musalole mavuto a lerolino kukulefulitsani maganizo. Mmalomwake, yang’anani mtsogolo ndi chitsimikizo. Ikani chiyembekezo chanu ndi chidaliro m’dziko latsopano la Mulungu limene liri pafupi kwambiri. Londolani njira yovomerezedwa ndi Yehova Mulungu, ndipo mungakhale ndi moyo kosatha m’dziko lopanda mavuto alionse.

[Chithunzi patsamba 4]

Ngakhale kuli kwakuti Yobu anavutika, iye analondola njira yovomerezedwa ndi Mulungu

[Chithunzi patsamba 7]

Mungakhale m’dziko lopanda mavuto alionse

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Collier’s Photograpic History of the European War

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena