Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 9/15 tsamba 28-31
  • Mungathe Kulimbana ndi Kugwiritsidwa Mwala!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mungathe Kulimbana ndi Kugwiritsidwa Mwala!
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Njira Zina Zolimbanirana ndi Kugwiritsidwa Mwala
  • Amphamvu Mosasamala Kanthu za Kugwiritsidwa Mwala
  • Mpumulo ku Kugwiritsidwa Mwala​—Uli Pafupi!
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala Oganiza Bwino pa Zoyembekeza Zathu?
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Mukhoza Kulimbana ndi Vuto la Kusatsimikizika kwa Zinthu
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Mmene Mungakhalire ndi Chiyembekezo Mutataya Mtima
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Sandikonda?
    Galamukani!—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 9/15 tsamba 28-31

Mungathe Kulimbana ndi Kugwiritsidwa Mwala!

TALINGALIRANI mkhalidwe wachisoni wa mwamuna wina wazaka 23 zakubadwa. Iye anaphunzira pang’ono chabe ndipo akugwira ntchito yamalipiro ochepa. Malingaliro a kukwatira ndi moyo wokhutiritsa akuwonekera kukhala osalingalirika kwa iye. Ndicho chifukwa chake amake akunena kuti: “Iye ngwachisoni kopambana ndi wogwiritsidwa mwala.” Mkhalidwe wa mwamuna wachichepere umenewu uli chitsanzo cha wa ena mamiliyoni ambiriwo. Kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana, anthu m’mbali zonse za moyo amagwiritsidwa mwala.

Kugwiritsidwa mwala ndiko “lingaliro lakuya lamphamvu kapena mkhalidwe wa kupanda chisungiko, kuda mtima, ndi kusakhutira kochititsidwa ndi zikhumbo zododometsedwa, kuwombana kwamkati, kapena mavuto ena osathetsedwa.” (Webster’s Third New International Dictionary) Timagwiritsidwa mwala pamene tikuyesa mwamphamvu kuchita kanthu kena koma sitikupambana. Timadzimva kukhala otsekerezedwa kumbali iriyonse, monga ngati kuti tinali kuwombetsa mutu wathu pakhoma lamwala, popanda chiyembekezo cha chipambano. Tonsefe timadziŵa mmene kuliri.

Ogwira ntchito zowonekera kukhala zosakhutiritsa angadzimve kukhala achabe. Ngati awonedwa kukhala osanunkha kanthu, akazi okwatibwa kapena anakubala omalimbana ndi nkhaŵa zatsiku ndi tsiku ndi ntchito zolefulitsa angalingalire kukhala osakhutiritsidwa, osayamikiridwa. Achichepere amene akuyang’anizana ndi mayesero kusukulu angalingalire kukhala ogwiritsidwa mwala m’zoyesayesa za kupeza maphunziro. Ziŵalo za timagulu ta ochepa zingakwiye, pokhulupirira kuti ndizo mikhole ya tsankho. Enimabizinesi amene mowona mtima akuyesayesa kupanga zinthu zabwino kapena mautumiki angavulazidwe ndi ampikisano ouma mtima ndi osawona mtima. Zokumana nazo zimenezi ndi zina zofanana nazo zimapangitsa kugwiritsidwa mwala ndi kusiya ambiri ali ndi malingaliro a kupanda chiyembekezo.

Munthu wina wanzeru yemwe anakhalako zaka mazana ambiri zapitazo anali wokhoza kufotokoza kugwiritsidwa mwala kwake mwa mawu amene tingazindikire. Mfumu ya Israyeli Solomo anati: “Pamenepo ndinayang’ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo tawona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno. Pakuti munthu ali ndi chiyani m’ntchito zake zonse, ndi m’kusauka kwa mtima wake amasauka nazozo kunja kuno? Pakuti masiku ake onse ndi zisoni, vuto lake ndi kumliritsa; ngakhale usiku mtima wake supuma. Ichinso ndichabe.” (Mlaliki 2:11, 22, 23) Mawu a Solomo akufotokoza kuchita thondovi kumene ochuluka kwambiri amakhala nako poyesayesa kulimbana ndi zogwiritsa mwala zimene zimawabera moyo wopindulitsa.

Anthu ogwiritsidwa mwala angataye mtima. M’zochitika zoipitsitsa ena amasiya nkhondoyo, akumaleka kukhala ndi moyo wa onse ndi kuyamba kukhala moyo wosazoloŵereka. Kuti apeze zimene amalingalira kukhala zowayenerera, ena amayamba kuchita zaupandu ndi chiwawa. Zitsenderezo zosalekeza zawononga maukwati ndi zomangira zabanja.

Ambiri a ife tingafunikire kupanga kuyesayesa kwamphamvu pofunafuna njira zolimbanirana ndi kugwiritsidwa mwala. Mosasamala kanthu za zimene tichita, zinthu zingawonekere kukhala zikumaipiraipirabe. Miyambo 13:12 imati: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima.” Mkhalidwe wathu wakuthupi ndi wauzimu ungaikidwe pachiswe. Kodi mkhalidwewo ngwopanda chiyembekezo? Kodi tiyenera kukhala ndi moyo wogwiritsidwa mwala mosalekeza monga kulipsiridwa kaamba ka kulephera kwathu kapena zophophonya? Kodi masitepe ogwira ntchito angatengedwe kulimbana ndi kugwiritsidwa mwala kotero kuti tisangalale ndi moyo wokhutiritsa mowonjezereka? Tiyeni tiwone.

Njira Zina Zolimbanirana ndi Kugwiritsidwa Mwala

Pamene tiri ndi vuto ndipo tifunikira uphungu, kaŵirikaŵiri timapita kwa munthu wanzeru, wachidziŵitso amene tingadalire. Miyambo 3:5, 6 ikuvomereza kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe ako.” Uphungu wogwira ntchito ungapezedwe m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Talingalirani zitsanzo zina za chidziŵitso chimene limapereka.

Kugwiritsidwa mwala kungaphatikizepo kupeza ndalama zochirikiza moyo. Mwachitsanzo, ntchito yathu yakudziko ingakhale yokhutiritsa, koma malipiro ochepa angakhale magwero a chipsinjo. Timakonda mabanja athu ndipo tikuwafunira zowakomera. Chikhalirechobe, nkhaŵa sizikuwonekera kukhala zikutha ponena za kukwaniritsa mathayo athu andalama. Tingagwire ntchito kwa maola owonjezereka ndipo ngakhale kugwira ntchito yachiŵiri. Pambuyo panthaŵi yakutiyakuti moyo umawonekera kukhala mchitidwe wothodwetsa wosalekeza wa kudya, kugona, ndi kugwira ntchito. Komabe, ngongole zikuchuluka, mangaŵa akuwonjezereka, ndipo kugwiritsiridwa mwala kumakula.

Chifuno chachikulu cha ntchito yakudziko ndicho kuti tipeze zofunika za moyo. Koma kodi tikufuna zochuluka motani? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Sitinatenga kanthu polowa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.” Kodi tikuyesayesa kupeza zoposa zimenezo ndi kulingana ndi zimene ena ali nazo kapena zimene ali okhoza kuchita? Ngati ziri choncho, tingakhale tikututa zotulukapozo mumpangidwe wa kugwiritsidwa mwala. Paulo anachenjeza kuti: “Koma iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi mumsampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza ambiri m’chiwonongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasokera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.” (1 Timoteo 6:7-10) Kupenda kowona mtima kwa zonulirapo zathu za zinthu zakuthupi kungavumbule zinthu zina zosafunika. Masinthidwe achikatikati angapo a kukhala wosamala ndi moyo wachikatikati kwambiri angathandizire kwambiri kuchepetsa kugwiritsidwa mwala kwathu.

Zikhumbo zachibadwa zotsenderezedwa zapangitsa kugwiritsidwa mwala kwakukulu. Mwachitsanzo, nkwachibadwa kwa mkazi wachichepere kukhala ndi chisonkhezero champhamvu cha kukwatibwa ndi kupeza chisungiko ndi chikondi zimene zimadzera limodzi ndi moyo wabanja. Iye angapange kuyesayesa kwakukulu kwa kudzipangitsa kukhala wokongola ndi mafashoni amakono kapena zothandizira kukongola ndipo angakhale woŵerenga wachangu mabukhu otuluka panthaŵi ndi nthaŵi opereka uphungu kwa wofuna mnzawo wa muukwati. Mkaziyo angafike mosalekeza pamasonkhano ocheza ambirimbiri akumayembekezera kupeza winawake woyenerera​—zonsezo mosaphula kanthu. Zaka zimapita, ndipo kugwiritsidwa mwalako kumafikira kukhala kosapiririka. Motaya mtima iye angayesedwe kukwatirana ndi winawake wosayenerera. Zoipirapobe, kuti akhutiritse chikhumbo chake cha chikondi, iye angaphatikizidwe mumkhalidwe wachisembwere.

M’chochitika choterocho, kuleza mtima ndi kulama maganizo nzofunika. Kukwatirana ndi munthu wosayenerera​—makamaka wopanda chikhulupiriro mwa Yehova​—kungakhale kulakwa kwakukulu. (1 Akorinto 7:39; 2 Akorinto 6:14, 15) Chisembwere mosapeweka sichimatsogolera kwina kusiyapo kuzopweteka mtima ndi tondovi. (Miyambo 6:32, 33) Kudzipenda kowona mtima, limodzi ndi njira yanzeru yosamalilira nkhaniyo, zingathandize. “Mzimu wofatsa ndi wachete” ungakope mtundu wabwino wa mzanu wa muukwati bwino kwambiri koposa mmene zovala zamasitayela ndi zodzoladzola zopambanitsa zingachitire. (1 Petro 3:3, 4) Mmalo mwa kudalira pa uphungu umene kaŵirikaŵiri uli wosawona patali kapena wopanda phindu wa akatswiri akudziko, nkofunika kupita kwa Woyambitsa ukwati kuti muphunzire zofunika kuti mukhale mkazi wokwatibwa amene amakondedwa ndi kusamaliridwa. (Miyambo, chaputala 31) Amuna ndi akazi osakwatira ayenera kuyesayesa kusonyeza makhalidwe amene iwo angafune mwa anzawo a muukwati. Nkwanzeru chotani nanga kufunafuna mayanjano abwino ndi anthu amene amalemekeza malamulo amakhalidwe abwino Abaibulo. Ngati tigwiritsira ntchito amenewa m’moyo, ziyembekezo zathu za ukwati wachimwemwe zidzakhala zabwinopo kwambiri. Ngakhale ngati ukwati sukuchitika mwamsanga, kuchita mogwirizana ndi Malemba kudzatibweretsera chisangalalo ndi kupangitsa moyo waumbeta kukhala wofupa kwambiri.

Mtolo wolemera wa mathayo ungatikwiyitse. Pangakhale chipsinjo chochokera kumbali zonse. Timaderera nkhaŵa zosowa zazikulu za banja lathu, ndipo wotilemba ntchito angakhale wosakhutiritsidwa konse. Achibale angatiyembekezere kuwathandiza panthaŵi iriyonse pamene vuto libuka. Chifukwa cha zipsinjo zambiri, mpambo wautali wa nkhani zaumwini zonyalanyazidwa zifunikira chisamaliro chathu. Kungawonekere monga ngati kuti nthaŵi yathu ndi nyonga ziyenera kulunjikitsidwa pazinthu zosiyanasiyana panthaŵi imodzimodzi. Kugwiritsidwa mwala kungasandulike mkwiyo, ndipo tingamve monga ngati kuti tingosiya. Chotero, kodi tiyenera kuchitanji?

Tingakhale anzeru kupendanso zofunika zathu zazikulu. Popeza kuti tingachite zochepa chabe panthaŵi, nkosatheka kuchita chifunsiro chirichonse chopangidwa ndi ena. Tifunikira kusumika maganizo pa “zinthu zofunika kwambiri.” (Afilipi 1:10, NW) Ndiiko komwe, “galu wamoyo aposa mkango wakufa.” (Mlaliki 9:4) Mathayo ena ngofunika kwambiri ndipo sangakankhidwire pambali, pamene kuli kwakuti awo amene sali ofunika kwambiri angafunikire kuyembekezera. Tingakhale titasenza thayo lonse la ntchito zina zimene ziyenera kugaŵiridwa ena. Mathayo ena angalekedweretu ngati sali ofunika. Ngakhale kuti zimenezi poyamba zingasokoneze zinthu kapena zingakhumudwitse ena, tifunikira kulemekeza zoperewera zathu zakuthupi ndi zamalingaliro.

Nthenda yofooketsa ingapangitse kugwiritsidwa mwala kopweteka mtima kwambiri, pakuti kungatibindikiritse pakama kwamasiku angapo kapena kwamilungu ingapo panthaŵi imodzi. Kupweteka kwakukulu kungatipangitse kukhala achisoni. Pofunafuna mankhwala, tingapite kumadokotala osiyanasiyana kapena tingamwe mankhwala ambiri kapena mavitamini tikumayembekezera kuti adzathandiza. Komabe, tingapitirizebe kudwala ndi kuyamba kudabwa ngati moyowo ngwofunikira kuyesayesako.

Limeneli lingakhale vuto limene lingathetsedwe kokha m’dziko latsopano la Mulungu. (2 Petro 3:13; yerekezerani ndi Yesaya 33:24.) Popeza kuti anthu ali opanda ungwiro, madokotala ndi mankhwala angachite zochepa chabe. Panthaŵi zina tingafunikire kuvomereza kudwala kwathu monga mbali ya moyo. Mtumwi Paulo anali ndi “munga m’thupi,” mwinamwake nthenda ya maso ake kapena mbali ya thupi lake, yovuta kwambiri kotero kuti iye anapempherera mpumulo mobwerezabwereza. (2 Akorinto 12:7-10) Koma Mulungu sanachiritse Paulo, ndipo mwinamwake mtumwiyo anafunikira kulimbana ndi nthendayo kufikira atafa. Iye anapirira mavuto ake, sanapemphe kuchitiridwa chifundo, ndipo sanataikiridwe konse ndi chisangalalo chake. (2 Akorinto 7:4) Ngakhale kuti mwamuna wowongoka mtimayo Yobu anazunzika kwambiri, iye anasungabe chikhulupiriro chake mwa Yehova, ndipo zimenezi zinadzetsa mphotho yaikulu. (Yobu 42:12, 13) Ngati tiri atumiki a Mulungu, tingapeze nyonga ya kupitirizabe mwa kusinkhasinkha pa zitsanzo zimenezi ndi kupempherera chithandizo cha Yehova.​—Psalm 41:1-3.

Amphamvu Mosasamala Kanthu za Kugwiritsidwa Mwala

Anthu a Yehova angakhale amphamvu mwauzimu mosasamala kanthu za zogwiritsa mwala zirizonse. Mwachitsanzo, ngakhale kuti tingafunikire kupirira matenda, tingakhalebe “olama m’chikhulupiriro” mwa kugwiritsira ntchito kotheratu makonzedwe auzimu a Mulungu. (Tito 2:1, 2) Pamene kuli kwakuti tingakhale opanda zinthu zakuthupi mogwiritsidwa mwala, tingakhale olemera kwambiri mwauzimu.

Mwa kudalira Mulungu kaamba ka nzeru ndi nyonga, tingathe kulimbana ndi zogwiritsa mwala zimene zingabuke m’mikhalidwe yapabanja. Mwachitsanzo, talingalirani Abigayeli, mkazi wa Nabala. Mwamunayo anali “waphunzo ndi woipa machitidwe ake,” ndipo dzina lake lenilenilo limatanthauza “Wosalingalira; Wopusa.” Kuyenera kukhala kunali kogwiritsa mwala chotani nanga kukhala ndi mwamuna woteroyo! Komabe, Abigayeli anakhalabe “wanzeru yabwino” ndipo sanataye mtima. Ndithudi, mawu ake ndi zochita zake zinali zaluntha kwambiri pachochitika china chowopsa kotero kuti iye anakhutiritsa Davide kusalipsira kutonza ndi kusayamikira kwa Nabala mwa kukhetsa mwazi ndi kulephera kudalira mwa Yehova.​—1 Samueli 25:2-38.

Ngakhale ngati mkhalidwe wophatikizapo winawake wogwirizana ndi mpingo Wachikristu ukutipangitsa kukhala ogwiritsidwa mwala, tingathe kupirira mwa nyonga imene Yehova amapereka. Zimenezi zikusonyezedwa ndi chenicheni chakuti mkhalidwe wogwiritsa mwala wothekera wa Diotrefe suunaletse mwamuna wowopa Mulunguyo Gayo kuchita zabwino ndipo chotero akumapeza chimwemwe ndi mfupo zolemera zauzimu.​—Machitidwe 20:35; 3 Yohane 1-10.

Kugwiritsidwa mwala kungachitike ngati tikufuna kutumikira okhulupirira anzathu mumpingo koma tikumasiidwa pamene ena akuikidwa monga akulu kapena atumiki otumikira. Komabe, mmalo mwa kulola kugwiritsidwa mwala kutiposa mphamvu, tiyenitu tiyeseyese kudzilimbikitsa mwauzimu ndi kulola mzimu wa Mulungu kubala chipatso chake mwa ife kumlingo waukulu koposerapo. (Agalatiya 5:22, 23) Mkati mwa zaka 40 zimene Mose anathera ku Midiyani, Mulungu anakulitsa mwa iye kumlingo waukulu kudekha, kuleza mtima, ndi makhalidwe ena ofunikira kulimbana ndi mavuto ndi zogwiritsa mwala zimene iye anali kudzakumana nazo monga mtsogoleri wa Aisrayeli. Mofananamo, Yehova angakhale akutikonzekeretsa kaamba ka mwaŵi wautumiki wamtsogolo umene ungadzakhale wathu ngati tikhalabe amphamvu mwauzimu ndi osagonjera kuzogwiritsa mwala.

Mpumulo ku Kugwiritsidwa Mwala​—Uli Pafupi!

Mulimonse mmene ziliri, kodi zogwiritsa mwala zathu zidzatha konse? Kwa ife, mkhalidwe wathu ungawonekere kukhala wopanda chiyembekezo koma osati kwa Mlengi wathu, Yehova Mulungu. Iye samagonjera kuzogwiritsa mwala. Kupyolera mwa mneneri Yesaya, Mulungu anati: “Momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.” (Yesaya 55:11) Popeza kuti Yehova ali ndi mphamvu zonse ndi ulamuliro, palibe kanthu kamene kali kosatheka kwa iye. (Marko 10:27) Malonjezo ake a kubweretsa madalitso osatha kwa anthu ake ngotsimikizirika kudzakwaniritsidwa.​—Yoswa 21:45.

Chikaikiro ndi kusatsimikizirika ndizo zochititsa zazikulu za kugwiritsidwa mwala. Komabe, mosiyana, “chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka.” (Ahebri 11:1) Chikhulupiriro mwa Mulungu chimapereka chitsimikiziro chakuti ziyembekezo zathu zonse zozikidwa pa Baibulo zidzakwaniritsidwa kotheratu. Mutu wa Baibulo lathunthu umagogomezera lonjezo la Yehova la ulamuliro Waufumu, muumene dziko lapansi lidzakhala paradaiso wangwiro mmene anthu olungama mosangalala adzakhala ndi moyo kosatha. (Salmo 37:11, 29) Chinthu choipa chirichonse​—kuphatikizapo kugwiritsidwa mwala​—chidzakhala chitapita, pakuti Mulungu ‘adzakhutiritsa zokhumba za chamoyo chirichonse.’​—Salmo 145:16.

Kufikira pamene madalitsowo akwaniritsidwa, tonsefe tidzayambukiridwa ndi zogwiritsa mwala. Koma chiyembekezo Chamalemba chingatipatse mphamvu ndi kulimba mtima kuti tipirire. Uphungu wolama umene timapeza m’Baibulo ungatisonyeze mmene luntha ndi uchikatikati zingagwiritsidwire ntchito m’njira imene idzapangitsa miyoyo yathu kukhazikika ndi kutidzetsera mtendere m’mitima yathu. Mosasamala kanthu za zokhumudwitsa zathu, tingapeze “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse.” (Afilipi 4:6, 7) Chotero nkhondo yomenyana ndi zogwiritsa mwala siiri yopanda chiyembekezo. Mwachithandizo cha Yehova tingalimbane nazo lerolino ndi kuzigonjetsa mtsogolo.

[Mawu Otsindika patsamba 31]

Mulungu angakuthandizeni kulimbana ndi zogwiritsa mwala, monga momwedi anathandizira Yobu, Mose, Abigayeli, ndi Paulo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena