Mmene Mungakhalire ndi Chiyembekezo Mutataya Mtima
YEREKEZERANI kuti zinthu izi zakuchitikirani: Katundu wanu yense wawonongeka, mwatsala mulibiretu kalikonse. Ana anu—chimwemwe cha moyo wanu—onse afa. Mwamuna wanu kapena mkazi wanu sakukulimbikitsani. Mukudwalanso kwambiri. Tsiku lililonse nlosautsa kwambiri.
Kodi mungafune kukhalabe ndi moyo ngati zinthu zinali choncho m’moyo wanu? Kapena kodi mungataye mtima?
Mavuto omvetsa chisoni amene angofotokozedwa kumenewo anamchitikiradi Yobu, mwamuna wina wa m’nthaŵi za Baibulo. (Yobu, machaputala 1, 2) Atachita tondovi kwambiri, Yobu analira nati: “Mtima wanga ulema nawo moyo wanga.” Iye anakhumba kufa. (Yobu 10:1; 14:13) Komabe, mosasamala kanthu za kuvutika kwake kwakukuluko, Yobu anasunga umphumphu wake kwa Mulungu. Kenako Yehova “anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake.” Chotero anamwalira mwamtendere, “wokalamba ndi wamasiku ochuluka.”—Yobu 42:12, 17.
Yobu anakhala chitsanzo cha kupirira chokhumbika mpaka lero. Mayesero ake anawongolera umunthu wake ndi kusonkhezera ena kuchita ntchito zabwino. (Yakobo 5:10, 11) Chachikulu koposa ndicho chakuti umphumphu weniweni wa Yobu unakondweretsa mtima wa Yehova. (Miyambo 27:11) Choncho m’kupita kwa nthaŵi, kuzunzika koopsa kunakhala chipambano chachikulu cha umulungu, chikhulupiriro, ndi umphumphu zimene zinadzetsa madalitso kwa Yobu ndi kwa onsewo amene asonkhezereka ndi chitsanzo chake.
Kukhala ndi Chiyembekezo m’Mayesero Osiyanasiyana
Mungavutike ndi mayesero amene Yobu anavutika nawo. Mungazunzike mtima kwambiri ndi imfa ya wokondedwa wanu. Matenda aakulu angachititse moyo wanu kukhala wopweteka kwambiri. Moyo wanu wonse ungaoneke wopanda pake kotheratu chifukwa cha chisudzulo chopweteka mtima. Kugwa kwa chuma kungakusiyeni mulibiretu kalikonse. Otsutsa kulambira koona anjiru angakuzunzeni mwankhanza. Chifukwa cha kulimbana kwanu ndi mayeserowa mungaone monga mtsogolo mwanu mulibe zabwino.—1 Petro 1:6.
M’malo motaya mtima, dzifunseni kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji ndikuvutika?’ Mukuvutika chifukwa chakuti muli m’dziko limene “ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Ndiye chifukwa chake aliyense akuvutika. M’njira ina yake tonsefe tikukhudzidwa ndi kuda uthenga wa Ufumu koyambidwa ndi Mdyerekezi, mawu oipa a ena, kapena zinthu zoopsa zomwe anthu ambiri osaopa Mulungu amachita mu ‘nthaŵi zino zoŵaŵitsa.’—2 Timoteo 3:1-5.
Ngati mwaona tsoka linalake m’moyo wanu, ndiye kuti mwina langochitika chifukwa cha “nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika.” (Mlaliki 9:11, NW) Komanso, nthaŵi zina zinthu zimatiipira chifukwa cha choloŵa chathu chauchimo. (Aroma 5:12) Ngakhale mutalakwitsa kwambiri koma mwalapa ndi kufunafuna thandizo lauzimu, musaone monga Mulungu wakusiyani. (Salmo 103:10-14; Yakobo 5:13-15) Iye amatisamalira kuposa mmene wina aliyense amachitira. (1 Petro 5:6, 7) Muyenera kukhala ndi chidaliro chakuti “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.” (Salmo 34:18) Kaya chiyeso chanu chakudzetsereni tsoka lotani kapena chikhale choipa motani, Yehova angakupatseni nzeru yokuthandizani kulimbana nacho. (Yakobo 1:5-8) Nthaŵi zonse kumbukirani kuti Yehova angachiritse kusweka mtima konse. Akakuyanjani, palibe chimene chingakulepheretseni kulandira mphotho ya moyo.—Aroma 8:38, 39.
Kodi Mayesero Angakhale ndi Phindu Lililonse?
Mwambi wina wakale umati: “Sunga khosi, mkanda woyera udzavala.” Imeneyo ndi njira yachidule yonenera kuti kaya zinthu zivute zitani, nthaŵi zonse pamakhala chifukwa chokhalira ndi chiyembekezo. Cholinga cha zonse zolembedwa m’Mawu a Mulungu ndicho kuti “tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Kaya mavuto anu akhale aakulu chotani, malonjezo ndi mapulinsipulo a m’Baibulo angakupatseninso chimwemwe ndi chiyembekezo.
Malemba amasonyeza kuti ‘chisautso nchopepuka, nchakanthaŵi’ pochiyerekezera ndi madalitso osatha amene awo okonda Mulungu adzalandira. (2 Akorinto 4:16-18, NW) Baibulo limasonyezanso kuti mikhalidwe yaumulungu yopezedwa pamene muli m’mayesero njofunika kwambiri kuposa kutchuka kapena chuma chakuthupi. (1 Yohane 2:15-17) Choncho, kuvutika nakonso kungakupindulitseni. (Ahebri 5:8) Kwenikweni, kuchita zimene mwaphunzira m’mayesero kungakudzetsereni mapindu osayembekezeka.
Chiyeso chovuta chingakupangeni kukhala wodekha. Mungavomereze kuti kale umunthu wanu unali ndi kaleya kenakake kamene kankanyansa ena ngakhale kuchedwetsa kupita kwanu patsogolo kwauzimu. Mwina munali kudzimva. Tsoka lina litakugwerani, mungazindikire mwamsanga kuti sindinu wolimba ndi kuti mumafunadi thandizo la ena. Ngati chiyeso chanu chakuphunzitsani phunziro limenelo ndipo mwasintha moyenerera, ndiye kuti mwapindula nacho.
Bwanjino ngati kale, ena amavutika kuchita nanu zinthu pamodzi chifukwa chakuti munali waukali? Mwinanso zimenezi munadwalapo nazo. (Miyambo 14:29, 30) Komabe, tsopano zinthu mwina zili bwinopo chifukwa mumadalira mzimu wa Mulungu kuti ukuthandizeni kudziletsa.—Agalatiya 5:22, 23.
Monga ena, mwinamwake panthaŵi ina simunali kuwachitira chifundo aja olakwa. Koma ngati inuyo munakhalapo mumkhalidwe wina umene munafuna kuchitiridwa chifundo, muyenera kuti tsopano mumachitira chifundo ena. Kumvetsa kotonthoza mtima, nkhaŵa, ndi chifundo, zimene anakusonyezani zinakuchititsani kuzindikira kuti muyenera kusonyeza mikhalidwe yofananayo kwa olakwa olapa. Ngati kupweteka mtima kwanu kunakusonkhezerani kuwongolera zofooka zimenezi mu umunthu wanu, limeneli ndi phindu limodzi limene mwapeza pazimene zakuchitikirani. Mwaphunzira kuti “chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.”—Yakobo 2:13; Mateyu 5:7.
Bwanji ngati chilango cha mumpingo wachikristu chakutayitsani udindo umene munali kuukonda ndi ulemu wa ena? Musataye mtima. Chilango chimathandizira kusungitsa chiyero mumpingo, koma zolinga zake zimaphatikizapo kukonzanso mkhalidwe wauzimu wa wolakwayo. Zoona, ‘chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwetsa, komatu choŵaŵa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloŵeretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.’ (Ahebri 12:11) Ngakhale kuti chilango chingakhale nkhonya yaikulu, chimasiyabe munthu wolapa modzichepetsayo ndi chiyembekezo. Mfumu ya Israyeli wakale, Davide, analangidwa koŵaŵa pacholakwa china, koma analapa ndipo m’kupita kwa nthaŵi analandira chiyamikiro chapadera monga mwamuna wachikhulupiriro chenicheni.—2 Samueli 12:7-12; Salmo 32:5; Ahebri 11:32-34.
Chiyeso chingakhudze kwambiri kaonedwe kanu ka zinthu. Mwina kale, munali kungolingalira za zinthu ndi zochita zakuthupi zimene zinakutchukitsani ndi kukudzetserani ulemu m’dziko lino. Mwinamwake chiyeso chokhudza kugwa kwa chuma kapena kutayikidwa katundu chakuchititsani kusumika maganizo anu pazinthu zofunika kwambiri. (Yerekezerani ndi Afilipi 1:10, NW.) Tsopano mwazindikira kuti zinthu zauzimu ndi zolinga mu utumiki wopatulika ndizo zokha zimene zimadzetsa chimwemwe chenicheni ndi chikhutiro chosatha.
Khulupirirani Yehova
Kuchita utumiki wopatulika kwa Yehova kungachititse kuzunzidwa ndi kuvutitsidwa ndi aja amene amatsutsa zikhulupiriro zanu zachikristu. Mungaone kuti ndinu wotsenderezeka chifukwa cha chiyeso chimenechi, koma pangatuluke zabwino pamenepo. Chiyeso chimenechi chingalimbitse chikhulupiriro chanu. Ndiponso, enanso amene akuvutika ndi chizunzo angalimbikitsidwe ndi kulimbitsidwa ataona kulimbikira kwanu. Amene akuona khalidwe lanu labwino angasonkhezereke kulemekeza Mulungu. Ngakhale okutsutsani angachite manyazi ndi kuvomereza kuti mukuchita ntchito zabwino!—1 Petro 2:12; 3:16.
Kuti musataye mtima pozunzidwa, muyenera kukhulupirira Yehova. Mawu ake amasonyeza kuti chiyeso chimathabe, koma mwina sichingathe msanga monga mmene mungafunire. Pakali pano, “musaleme pakuchita zabwino.” (2 Atesalonika 3:13) Pitirizanibe kufunafuna njira zolimbanira ndi chiyeso ndi kuchipirira. Ngakhale pataoneka kuti palibe zabwino zilizonse, “umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) M’malo mothedwa mphamvu ndi kudzichitira chisoni, ganizani za madalitso amene muli nawo podziŵa Yehova, kukhala ndi malo pakati pa anthu ake, ndi kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.—Yohane 3:16, 36.
Sumikani maganizo anu pazinthu zofunika. Masiku onse pitani kwa Yehova m’pemphero, kupempha nyonga kuti mupirire. (Afilipi 4:6, 7, 13) Kanizani malingaliro alionse akuti mubwezere awo amene akukuvutitsani. Siyani nkhaniyo m’manja mwa Yehova. (Aroma 12:19) Nthaŵi zonse funafunani njira zowongolera umunthu wanu, kukulitsa mikhalidwe yachikristu. (2 Petro 1:5-8) Yamikirani zonse zimene akuchitirani ena, kuphatikizapo akulu amene mwachikondi akusamalira zosoŵa zanu zauzimu. (Ahebri 13:7, 17) Khalani wokhulupirika kwa Mulungu, ndipo sumikani diso lanu pamphoto ya moyo, muli ndi chidaliro chakuti ngakhale imfa singakulandeni mphotoyo.—Yohane 5:28, 29; 17:3.
Ngati pali pano muli ndi chisoni chachikulu kapena muli m’mayesero aakulu, ‘khulupirirani Yehova ndi mtima wanu wonse,’ ndipo m’kupita kwa nthaŵi mudzakhala ndi chimwemwe chachikulu m’malo mwa chisoni ndi mavuto. (Miyambo 3:5, 6; Yohane 16:20) Pamene Mulungu adzakudalitsani monga Yobu, mudzasangalala m’malo mosautsidwa. Mavuto alipowa tsopano sali kanthu mutawayerekezera ndi mfupo yanu. (Yerekezerani ndi Aroma 8:18.) Chipiriro chanu chokhulupirika chingalimbikitse ena ndi kukuthandizani inuyo kukulitsa mikhalidwe yachikristu yokongola imene imadza ndi “munthu watsopano.” (Aefeso 4:23, 24; Akolose 3:10, 12-14) Choncho, lolani uphungu wanzeru wa mtumwi Petro kukulimbikitsani: “Iwo akumva zoŵaŵa monga mwa chifuniro cha Mulungu aike moyo wawo ndi kuchita zokoma m’manja a Wolenga wokhulupirika.”—1 Petro 4:19.
[Chithunzi patsamba 23]
Khalani monga Yobu. Musataye mtima
[Chithunzi patsamba 24]
Khulupirirani Yehova ndi mtima wanu wonse