Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 12/1 tsamba 3-5
  • Kodi Ndianthu Otani Amene Mumayanja?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndianthu Otani Amene Mumayanja?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Miyezo Yofala ya Kufunika kwa Munthu
  • Kodi Imeneyi Ndiyo Miyezo Yoyenera?
  • Kodi Ndani Ali ndi Chiyanjo cha Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi a Mboni za Yehova Amaiona Bwanji Nkhani ya Maphunziro?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Kodi Maphunziro Ndi Ndalama Zingatithandize Kukhala Ndi Tsogolo Labwino?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
  • Maphunziro—Agwiritsireni Ntchito Kutamanda Yehova
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 12/1 tsamba 3-5

Kodi Ndianthu Otani Amene Mumayanja?

“MKWATIBWI AKUFUNIKA. Ayenera kukhala woyera ndi wochepa thupi, wadigiri kapena amene akuphunzira kupeza digiri ina. Ayenera kukhala wochokera ku banja lapamwamba lokhala ndi chuma. Makamaka wafuko lofanana.”

CHIMATERO chilengezo chozoloŵereka chofunsira ukwati chimene mungawone mu nyuzipepala ku Indiya. Mwachiwonekere, mukawona zofananazo m’mbali zina zambiri zadziko. Kaŵirikaŵiri ku Indiya chilengezocho chimaperekedwa ndi makolo amwamuna woyembekezera kukwatira. Mayankho angaphatikizepo chithunzithunzi cha msungwana wovala sari ya chibakuwa ndi majuwelo agolidi ambirimbiri. Ngati banja la mnyamata livomereza, kukambitsirana ndi cholinga chaukwati kukayamba.

Miyezo Yofala ya Kufunika kwa Munthu

Mu Indiya zifunsiro zamkwatibwi wa khungu loyera nzofalikira kwambiri. Zimenezi ziri chifukwa cha chikhulupiriro chozama chakuti otchedwa kuti afuko lotsikirapo a anthu Achihindu ngakhungu lodera. Posachedwapa, programu pa wailesi yakanema ya ku Indiya inasimba nkhani za asungwana aŵiri, mmodzi wakhungu loyera ndi wina lodera. Msungwana woyerayo anali wankhalwe ndi wamakhalidwe oipa; msungwana woderayo anali wokoma mtima ndi wodekha. Masinthidwe amatsenga anachitika, ndipo msungwana woyera anasanduka wodera monga chilango, pamene msungwana woderayo anapangidwa kukhala woyera monga mphotho. Mwachiwonekere tanthauzo la nthanoyo linali lakuti, pamene kuli kwakuti potsirizira pake ubwino umapeza chipambano, khungu loyera ndilo mphotho yolakalakika.

Kaŵirikaŵiri, malingaliro aufuko otero ngozika mizu kuposa mmene munthu angalingalirire. Mwachitsanzo, munthu wa ku Asiya angakacheze ku dziko Lakumadzulo ndi kudandaula kuti anachitiridwa moipa chifukwa cha mawonekedwe akhungu lake kapena kupendeka kwa maso ake. Zochitika zotero zimamvutitsa maganizo, ndipo amadzimva kukhala wochitiridwa mwatsankho. Koma pamene abwerera kudziko lakwawo, iye angachitire anthu afuko lina mwanjira yofananayo. Ngakhale lerolino mawonekedwe akhungu ndi fuko lina ziri maziko aakulu amene anthu ambiri amawonerapo kufunika kwa munthu wina.

“Ndalama zivomera zonse,” analemba motero Mfumu Solomo wa nthaŵi zakale. (Mlaliki 10:19) Nzowona chotani nanga zimenezo! Chuma chimayambukiranso mmene anthu amawonedwera. Kaŵirikaŵiri, sipamakhala kulingalira za magwero achumacho. Kodi munthuyo walemera chifukwa cha kugwira ntchito zolimba kapena kulinganiza kosamalitsa kapena kusawona mtima? Zimenezo sizimakhala kathu konse. Chuma, kaya chinapezeka moipa kapena ayi, chimachititsa anthu ambiri kuyanja amene ali nacho.

Maphunziro apamwamba nawonso aikidwa pa mlingo wapamwamba m’dziko lampikisano lino. Mwana atangobadwa, makolo amalimbikitsidwa kuyamba kusunga ndalama zambiri zomphunzitsira. Podzafika zaka ziŵiri kapena zitatu zakubadwa, iwo amayamba kudera nkhaŵa za kumloŵetsa sukulu ya nasale monga sitepe loyamba la ulendo wautali wakukapeza digiri ku yunivesite. Anthu ena amawonekera kuganiza kuti diploma lonyaditsa limawayeneretsa kuyanjidwa ndi kupatsidwa ulemu ndi ena.

Inde, mawonekedwe akhungu, maphunziro, ndalama, fuko​—zonsezi zakhala miyezo imene anthu ambiri amaweruzirapo ena, kapena, kuchitira tsankho munthu wina. Zimenezi ndizo zinthu zimene amadziŵirapo awo amene iwo ayenera kuwasonyeza chiyanjo ndi kwa amene sayenera kutero. Bwanji za inu? Kodi mumayanja yani? Kodi mumalingalira munthu wokhala ndi ndalama, wakhungu loyera, kapena wophunzira kwambiri kukhala woyenerera chiyanjo ndi ulemu koposerapo? Ngati ndichoncho, mufunikira kulingalira mwamphamvu maziko amalingaliro anuwo.

Kodi Imeneyi Ndiyo Miyezo Yoyenera?

Bukhu lakuti Hindu World limati: “Aliyense wamafuko otsikirapo atapha wafuko lapamwamba koposa akazunzidwa kufikira imfa ndipo chuma chake kufunkhidwa, ndipo moyo wake unatembereredwa kosatha. Wafuko lapamwamba koposa, amene anapha munthu aliyense, akalipiritsidwa faindi yokha ndipo sakapatsidwa konse chilango cha imfa.” Ngakhale kuti bukhuli likulankhula za nthaŵi zakale, bwanji za lerolino? Tsankho la ufuko ndi chitsenderezo cha m’chitaganya zachititsa kukhetsedwa kwa mwazi wochuluka ngakhale m’zaka za zana la 20 lino. Ndipo zimenezi sizinalekezere ku Indiya. Udani ndi chiwawa zopitirizabe ndi kupatulana mitundu mu South Africa, tsankho laufuko mu United States, tsankho la utundu m’maiko a Baltic​—ndandanda imapitirizabe​—zonsezi zikumachititsidwa ndi malingaliro akudziwona kukhala woposa ena. Ndithudi, kuyanja munthu wina kotere kuposa wina chifukwa cha fuko lake kapena mtundu sikunatulutse zipatso zabwino, kapena zipatso za mtendere.

Bwanji za chuma? Mosakaikira, ambiri amalemera mwa ntchito yowona mtima ndi yamphamvu. Komabe, chuma chochuluka chakundikidwa ndi apandu enieni, ogulitsa zinthu mwakatangale, ogulitsa anamgoneka, ogulitsa mfuti popanda lamulo, ndi ena otero. Ndithudi, ena a amenewa amapereka chithandizo kumagulu othandiza osoŵa kapena kuchirikiza makonzedwe othandiza osauka. Komabe, ntchito zawo zaupandu zachititsa kuvutika kosaneneka ndi nsautso kwa oberedwawo. Ngakhale ochita motero mwakamodzikamodzi, monga awo amene amalandira ziphuphu kapena kukhala ndi phande m’machitachita a bizinesi yosawona mtima, achititsa zogwiritsa mwala, zivulazo, ndi imfa pamene zinthu zawo kapena mautumiki zilephera ndi kusagwira ntchito bwino. Ndithudi, chuma mwa icho chokha sindicho maziko akulingalirira munthu kukhala woyenera chiyanjo.

Pamenepa, kodi bwanji za maphunziro? Kodi kukhala ndi madigiri ochuluka ndi maina aulemu ambiri kumatsimikizira kuti munthuyo ngwowona mtima ndi wolungama? Kodi amatanthauza kuti iye ayenera kuwonedwa mwachiyanjo? Ndithudi, maphunziro angachititse munthu kukhala wodziŵa zambiri, ndipo ambiri amene agwiritsira ntchito maphunziro awo kupindulitsa ena ngoyenera kulandira ulemu. Komatu mbiri njodzala ndi zitsanzo za kudyeredwa masuku pamutu ndi kutsenderezedwa kwa makamu a anthu zochitidwa ndi anthu ophunzira. Ndipo talingalirani zimene zikuchitika m’koleji kapena m’mayunivesite lerolino. Malo a yunivesite ngodzala mavuto akugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka ndi nthenda zopatsirana mwakugonana, ndipo ophunzira ambiri amadziloŵetsa m’kulondola chuma, ulamuliro ndi kutchuka. Maphunziro amunthu mwa iwo okha sali konse chisonyezero chodalirika cha makhalidwe ake owona.

Ayi, mawonekedwe akhungu, maphunziro, ndalama, fuko, kapena zinthu zina zotero sindizo maziko oyenera odziŵirapo kufunika kwake kwa munthu. Akristu sayenera kutanganitsidwa ndi nkhani zimenezi kuti apeze chiyanjo kwa ena. Pamenepa, kodi munthu, ayenera kudera nkhaŵa chiyani? Kodi ndimiyezo yotani imene munthu ayenera kutsatira?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena