Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 12/1 tsamba 5-6
  • Kodi Ndani Ali ndi Chiyanjo cha Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndani Ali ndi Chiyanjo cha Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Miyezo ya Mulungu Yapamwamba
  • Tingapeze Chiyanjo cha Mulungu
  • Kodi Ndianthu Otani Amene Mumayanja?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Mulungu Amakondera Mitundu ina ya Anthu?
    Galamukani!—2005
  • Kodi Ndinu “Wolemera kwa Mulungu”?
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi AKristu Amafunika Kuti Azikhala Osauka?
    Galamukani!—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 12/1 tsamba 5-6

Kodi Ndani Ali ndi Chiyanjo cha Mulungu?

TONSEFE timafuna kukondedwa ndi atsamwali athu. Kwa Mkristu chikhumbo champhamvu kwambiri ndicho kupeza chiyanjo cha Mulungu. Ponena za Yehova Mulungu, kwafotokozedwa pa Salmo 84:11, (NW) kuti: “Chiyanjo ndi ulemerero ndizo zimene amapereka. Yehova mwiniyo sadzamana chinthu chokoma chirichonse awo oyenda muungwiro.” Pakubadwa kwa Yesu, mfuu yachisangalalo ya angelo akumwamba inalonjeza “mtendere padziko lapansi kwa anthu amene iye amawayanja!”​—Luka 2:14, Moffatt.

Koma kodi ndani amene Mulungu amayanja? Kodi miyezo ya Mulungu njofanana ndi ya anthu? Momvekera bwino, siiri, monga momwe tawonera m’nkhani yapitayo. M’chenicheni, popeza Akristu akulangizidwa kukhala ‘otsanzira Mulungu,’ aliyense wa ife ayenera kudzifunsa kuti, Kodi ndimasonyeza chiyanjo kwa anthu amene Mulungu amayanja, kapena kodi ndimakhoterera pamiyezo yadziko m’kulingalira kwanga anthu? (Aefeso 5:1) Kuti tipeze chiyanjo cha Yehova ndi chivomerezo, tiyenera kusamala kuwona zinthu mogwirizana ndi lingaliro lake.

Miyezo ya Mulungu Yapamwamba

“Mulungu alibe tsankho,” anatero mtumwi Petro, “koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” Ndiponso, mtumwi Paulo anachitira umboni kuti ‘mwa munthu mmodzi Mulungu analenga mitundu yonse ya anthu.’ (Machitidwe 10:34, 35; 17:26) Chifukwa chake, kulidi kwanzeru kugamula kuti anthu onse ngofanana pamaso pa Mulungu mosasamala kanthu za mikhalidwe yawo yakuthupi. Chifukwa chake, sikukakhala koyenera kwa Mkristu kuyanja munthu kokha chifukwa cha chipembedzo chake, mawonekedwe akhungu, kapena fuko lake. Mmalomwake, iye akachita bwino kulondola Wopereka Chitsanzo wake, Yesu Kristu, amene ngakhale adani anavomereza kuti iye sanasonyeze tsankho lirilonse.​—Mateyu 22:16.

Mawu akuti “chiphamaso” nthaŵi zina amagwiritsidwa ntchito kufotokoza chinthu chopanda phindu lenileni kapena chosayenera. Mawonekedwe akhungu ali chomwecho kumene; ngachiphamaso chabe. Mawonekedwe akhungu la munthu samasonyeza mwanjira iriyonse umunthu wake kapena mikhalidwe ya mtima wake. Ponena za kusankha amene mungayanjane naye, kudya naye, kapena kupatsana naye moni wachanza, ndithudi sitiyenera kuyang’ana makamaka mawonekedwe akhungu. Kumbukirani kuti, namwali wina amene anachititsa kulembedwa kwa zina za ndakatulo zokongola koposa ndi zosonyeza chikondi zimene zinalembedwapo anati ponena za iye mwini: “Wakuda ine, koma wokongola, . . . Ndada, pakuti dzuŵa landidetsa.” (Nyimbo ya Solomo 1:5, 6) Fuko kapena mawonekedwe akhungu sindiwo maziko oyenerera akusonyezera chiyanjo. Chofunika kwambiri nchakuti munthuyo amawopa Mulungu nachita chilungamo.

Kodi Mulungu amalingalira motani kukhala ndi chuma chakuthupi? Pa anthu onse amene Mulungu amakonda ndi kuyanja, Mwana wake, Yesu Kristu, amaposa onse. Komabe, pamene anali padziko lapansi, Yesu analibe “potsamira mutu wake.” (Mateyu 8:20) Iye analibe chuma mumpangidwe wa fama, nyumba, minda, mitengo yazipatso, kapena zifuyo. Komabe, Yehova anamlemekeza namkwezera pamalo apamwamba kuposa munthu wina aliyense m’chilengedwe chonse kusiyapo Mulungu mwiniyo.​—Afilipi 2:9.

Yesu Kristu anapeza chiyanjo cha Mulungu osati chifukwa chakuti anali wolemera ndi zinthu zakuthupi koma m’ntchito zabwino. (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 6:17, 18.) Iye analangiza otsatira ake kuti: “Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziwononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba. Koma mudzikundikire nokha chuma m’mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba.” (Mateyu 6:19, 20) Chotero, mmalo mwakusonyeza chiyanjo kokha kwa olemera ndi chuma chadziko lino, Akristu sadzasiyanitsa anthu pamaziko achuma chakudziko. Iwo adzafunafuna awo amene ali olemera kwa Mulungu mosasamala kanthu kuti kaya iwo ngolemera kapena ngosauka mwanjira yakuthupi. Musaiŵale konse kuti ‘Mulungu anasankha osauka m’zadziko lapansi akhale olemera m’chikhulupiriro ndi oloŵa nyumba a Ufumu.’ (Yakobo 2:5) Ngati inu mukhala ndi lingaliro la Mulungu, simudzagwera konse mumsampha wofala wa kuyanja kapena kuyesa kupeza chiyanjo cha olemera.

Ponena za maphunziro, Baibulo limasonyeza momvekera bwino kuti Mulungu amatichichiza kufunafuna chidziŵitso ndi nzeru ndi kuti Yesu Kristu anali mphunzitsi wamkulu koposa onse amene anakhalako pa dziko lapansi. (Miyambo 4:7; Mateyu 7:29; Yohane 7:46) Koma sindiyo nzeru yadziko kapena maphunziro zimene zimapezetsa chiyanjo ndi Mulungu. Mmalo mwake, Paulo akutiuza kuti “sanaitanidwa ambiri anzeru, monga mwathupi; . . . koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru.”​—1 Akorinto 1:26, 27.

Mulungu amayanja awo amene ali ophunzira kwambiri, osati maphunziro adziko ophunzitsidwa m’masukulu amaphunziro apamwamba kwambiri, koma “chinenero choyera” cha chowonadi chopezeka m’Mawu ake Baibulo. (Zefaniya 3:9, NW) Kunena zowona, Yehova mwiniyo akuphunzitsa anthu ake lerolino mwa programu yamaphunziro imene yafikira ngondya zakutali za dziko lapansi. Monga momwe kudanenedweratu ndi mneneri Yesaya, anthu amitundu yonse akulabadira mwakunena kuti: “Tiyeni tikwere kumka ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.” Chifukwa chake, mmalo mwakudzitamandira m’maphunziro akudziko, Akristu adzafunafuna awo amene amasonyeza mwa mawu ndi ntchito zawo kuti alidi “anthu ophunzitsidwa ndi Yehova.” Mwakutero, adzakhala ndi ‘mtendere waukulu’ umene Mulungu amapereka.​—Yesaya 2:3; 54:13.

Tingapeze Chiyanjo cha Mulungu

Inde, miyezo ya Mulungu yoyanjira anthu ena njosiyana kwambiri ndi ya anthu. Komabe, tiyenera kuyesayesa kutsogozedwa ndi njira zake ngati tifuna kupeza chiyanjo chake. Zimenezo zitanthauza kuti tiyenera kuphunzira kuwona ena mogwirizana ndi lingaliro la Mulungu ndipo osati mwa miyezo ya anthu, yosonkhezeredwa ndi dyera ndi tsankho. Kodi tingachite motani zimenezo?

Yehova Mulungu amapenda mtima wa munthu ndi kuyanja amene amasonyeza mikhalidwe yonga chikondi, ubwino, chifundo, ndi kuleza mtima. Tiyenera kutero nafenso. (1 Samueli 16:7; Agalatiya 5:22, 23) Tifunikira kuyang’ana munthu wamkati, kumlingo umene tingathe monga anthu, ndipo osati pamawonekedwe akhungu lake kapena fuko lake. Mmalo mwakufunafuna olemera m’zinthu zakuthupi, tidzachita bwino kukumbukira lingaliro la Mulungu ponena za chuma ndi kuyesayesa ‘kuchuluka m’ntchito zabwino, ndi kukondwera kugaŵira ena, ndi kuyanjana.’ (1 Timoteo 6:18) Kuti tipeze chiyanjo cha Mulungu, tiyenera kupitirizabe kufunafuna chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, tikumakhala ophunzira kwambiri chinenero choyera cha chowonadi. (Yohane 17:3, 17) Tikatero, nafenso tidzakhala pakati pa awo amene Mulungu amayanja.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena