Kodi Mudzalabadira Chenjezo la Mulungu?
KAŴIRIKAŴIRI anthu amanyalanyaza machenjezo opulumutsa moyo. Unyinji wanzika za Pompeii unasankha kunyalanyaza mapokoso amabingu a Phiri la Vesuvius. Mwanjira yofananayo, anthu ambiri lerolino akunyalanyaza machenjezo achiwonongeko chadziko lonse chirinkudza. Koma kwa awo amene ali ofunitsitsa kuyang’anizana ndi maumboni, chenjezolo nlenileni mofanana ndi kung’anima kwa mphezi ndi moto zimene zinatulutsidwa ndi Phiri la Vesuvius kalelo m’zaka za zana loyamba. Nkhondo zadziko ziŵiri, nkhondo zazing’ono zazida zocheperapo mazana ambiri, njala, zivomezi zazikulu, miliri, mafunde otsatizanatsatizana a upandu ndi chiwawa, ndi mkupiti wa kulalikira padziko lonse zonse pamodzi zimapanga chenjezo lamphamvu lakuti chitaganya cha anthu chikuyandikira mofulumira ku chipiyoyo chochititsa mantha.
Baibulo limapereka ulosi wolama uwu: “Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitike chiyambire chiyambi chadziko kufikira tsopano, inde, sichidzachitikanso.” (Mateyu 24:21, NW) Monga momwe kunaliri m’tsoka la ku Pompeii, padzakhala awo amene apulumuka—‘khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe,’ lidzapulumuka, ndiko kuti, ‘kutuluka mu chisautso chachikulu.’—Chivumbulutso 7:9, 14.
Funso nlakuti, Kodi ndi liti pamene chiwonongeko chimenechi chidzadza? Pali chifukwa champhamvu chakukhulupiririra kuti chisautsocho chayandikira pafupi. Mwachiwonekere, kuti azindikire nthaŵiyo, ophunzira a Yesu anafunsa kuti: ‘Chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?’ (Mateyu 24:3) Tamverani yankho limene Yesu Kristu anapereka.
Nkhondo—Mbali yaikulu ya Chizindikiro Chachiungwe
Yesu sadaneneretu chochitika chimodzi chokha chapadera. M’malo mwake, iye analankhula za mpambo wa zochitika zimene, ngati ziikidwa pamodzi, zikapanga chenjezo laumulungu—chizindikiro chachiungwe cha mapeto a dongosolo lazinthu. Chochitika choyamba choloseredwa chafotokozedwa pa Mateyu 24:7: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.” Mu ulosi wofanana pa Chivumbulutso 6:4, Baibulo linalosera kuti ‘mtendere ukachotsedwa padziko lapansi.’ Ichi chinatanthauza nkhondo pamlingo wosayerekezereka.
Mbiri ikutiuza kuti ulosi umenewu wankhondo yadziko lonse unayamba kukwaniritsidwa kwake kuyambira chaka chosaiŵalikacho cha 1914. Bukhu lakuti American Adventures limati ponena za zakazo 1914 isanafike: “Nzika za Amereka zambiri zinaloŵa m’zaka za zana latsopano ndi chidaliro chonse. Zimenezi zinali ‘zaka zachiyanjo’ ndipo zinakhalapo m’khumi lachiŵiri lazaka za zana lino. . . . Ndiyeno, pa July 28, 1914, mkhalidwewo unagwedezedwa ndi liwu limodzi lakuti: nkhondo.” Chotero Nkhondo ya Dziko I inayamba, imene inamenyedwa kuyambira 1914 mpaka 1918 ndipo ena anaitcha kuti “nkhondo yotha nkhondo zonse.” Maiko makumi aŵiri mphambu asanu ndi atatu anaphatikizidwa mwachindunji m’nkhondoyo. Ndipo ngati muphatikiza maiko amene anali kulamulidwa ndi maiko ena, mitundu yochita nkhondo inaphatikizapo pafupifupi 90 peresenti yanzika zadziko lapansi panthaŵiyo.
Mu Nkhondo ya Dziko I munagwiritsidwanso ntchito zida za nkhondo zatsopano ndi zakupha mopambanitsa, monga ngati mfuti zachiwaya, mpweya wapaizoni, zida zoponyera moto, akasinja, ndege, ndi masitima apamadzi. Pafupifupi asilikali mamiliyoni khumi anaphedwa—kuposa asilikali onse m’nkhondo zazikulu zonse zimene zinamenyedwa mkati mwa zaka 100 chisanafike chakachi! Pafupifupi asilikali mamiliyoni 21 anavulala. Ndithudi, inali nkhondo yadziko lonse, imene inachititsa 1914 kukhala chiyambi cha “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1) Komabe, nkhondo inali mbali imodzi yokha ya chizindikiro cha Yesu.
Mbali zina za Chizindikiro
Yesu anawonjezera kuti: ‘Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo akutiakuti. Koma ndizo zonsezi zoŵaŵa zoyamba.’ (Mateyu 24:7, 8) Luka 21:11 amawonjezera “miliri” kumpambo umenewu. Nkhondo ya Dziko I isanathe, chawola cha Fuluwenza ya Spanya chinayamba kufalikira mofulumira pa dziko lapansi. Potsirizira pake, chinapha anthu oposa mamiliyoni 20, ochuluka kwambiri kuposa amene anafa m’nkhondoyo.
Mkati ndi pambuyo pa nkhondoyo, mamiliyoni ena anafa ndi njala. Zivomezi nazonso zinapha ambirimbiri. Mu 1915 oposa 30,000 anafa mu Italiya; mu 1920 pafupifupi 200,000 anawonongeka mu China; mu 1923 pafupifupi 143,000 anafa mu Japan. Komabe, monga momwe Yesu anasonyezera, zonsezi zinali kokha chiyambi cha zoŵaŵa zansautso. Bukhu lina lotanthauzira mawu limafotokoza “choŵaŵa” kukhala “kupweteka kolasa momvetsa ululu kwakanthaŵi.” Chotero dzikoli lakhala likudzandira chifukwa cha kupweteka komvetsa ululu kotsatizanatsatizana mwa ukulu wowonjezerekawonjezereka ndi kubwerezedwa pamlingo wofulumirirapo kuyambira 1914. Mwachitsanzo, zaka 21 zokha pambuyo pa Nkhondo ya Dziko I panadza nkhondo yadziko yachiŵiri, imene inawonongetsa mikhole mamiliyoni 50 ndi kuloŵetsa anthu m’nyengo yanyukliya.
M’zaka zaposachedwapa zambiri zanenedwa ponena za magwero enabe ansautso: kuwononga malo okhala kwa anthu. Ngakhale kuti Yesu sanatchule mwachindunji mfundoyi muulosi wake, Chivumbulutso 11:18 chimasonyeza kuti chiwonongeko chirinkudza chisanachitike, anthu akakhala ali ‘kuwononga dziko.’ Umboni wakuti kuwononga kumeneku kukuchitika ngwambiri. Wogwidwa mawu mu bukhu lakuti State of the World 1988, katswiri wa malo okhala Norman Myers akupereka uthenga wochititsa mantha uwu: “Palibe mbadwo m’nthaŵi yapita umene unayang’anizana ndi chiyembekezo chakusolosedwa kwa anthu onse mkati mwa nyengo yamoyo wawo. Palibe mbadwo wina mtsogolo umene udzayang’anizananso ndi chitokoso chofanana: ngati mbadwo ulipowu ulephera kuthana ndi vutoli, chivulazo chidzakhala chitachitidwa ndipo sipadzakhala mpata ‘wakuyesa kwachiŵiri.’ “
Talingalirani lipoti m’kope la magazini a Newsweek la February 17, 1992, lonena zakuchepetsedwa kwa mpweya wa ozone m’mlengalenga. Katswiri wodziŵa za mpweya wa ozone m’bungwe la Greenpeace, Alexandra Allen anagwidwa mawu kukhala akuchenjeza kuti kutaikiridwa ndi ozone “tsopano ndiko chiopsezo cha mtsogolo mwa moyo uliwonse padziko lapansi.”—Kuti mupeze umboni wowonjezereka wakuipitsidwa kwa malo padziko lapansi wonani Bokosi patsamba lino.
Malo sakulola kuti tilongosole mwatsatanetsane mbali zonse zaulosi wa Yesu. (Wonani tchati patsamba 5 kuti mupeze lingaliro lonse la mbali zina za ulosi.) Komabe, mbali imodzi imene singanyalanyazidwe, yafotokozedwa pa Mateyu 24:14, (NW): “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” Palibe kukaikira ponena za amene akuchita ntchito yolalikira ya padziko lonse imeneyi. Mboni za Yehova m’maiko 229 zinathera maola oposa biliyoni imodzi m’ntchitoyi m’chaka cha 1992 chokha. Chotero ntchito yawo ikupanga chimodzi cha maumboni owoneka kwambiri akuti tiri m’masiku otsiriza.
Musanyengedwe!
Komabe, ena angatsutse, kuti nkhani yonseyi ya “masiku otsiriza” yangokhala chabe chiwopsezo cha masoka. ‘Bwanji ponena za kutha kwa Chikomyunizimu posachedwapa Kummaŵa kwa Yuropu?’ iwo akufunsa, ‘kapena zoyesayesa za maulamuliro apamwamba zakupanga mtendere? Kodi umenewu suli umboni wakuti zinthu zikuwongokera?’ Ayi. Wonani kuti Yesu sananene kuti dziko lonse likapitirizabe kukhala lokutidwa m’nkhondo, zivomezi, ndi njala mkati mwa masiku otsiriza. Kuti mbiri yabwino ilalikidwe padziko lonse lapansi, pakafunikira kukhalapo nyengo zabata pang’ono.
Ndiponso, kumbukirani kuti Yesu anayerekezera masiku otsiriza ndi masiku a Chigumula cha Nowa chisanafike. Panthaŵiyo anthu anali otanganitsidwa kwambiri ndi kudya, kumwa, ndi kukwatira—zochitika zozoloŵereka mu moyo. (Mateyu 24:37-39) Zimenezi zikasonyeza kuti pamene kuli kwakuti mikhalidwe m’masiku otsiriza ikakhala yosautsa, zinthu sizikanyonyosoka kufikira pamlingo wakuti zolondola za moyo watsiku ndi tsiku zikalekeka. Monga m’masiku a Nowa, anthu ambirimbiri ngotanganitsidwa kwambiri ndi zochitika zatsiku ndi tsiku kotero kuti sakulabadira tanthauzo lanthaŵi.
Chifukwa chake, kukakhala kwaupandu kuloŵa m’kuchita mphwayi chifukwa cha zowonekera kukhala zochitika zopereka chiyembekezo zandale zadziko. (Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 5:3.) Umboni ngwankhaninkhani wakuti ulosi wa Yesu ukukwaniritsidwa tsopano—chenjezo lakuti chiwonongeko chayandikira!
Ulemerero Pambuyo Pake
Chiwonongeko cha ku Pompeii chinachititsa imfa ndi chisoni. Komabe, mapeto a dongosolo liripoli lazinthu adzalambula njira ya moyo wamuyaya padziko lapansi la paradaiso wokongola. (Chivumbulutso 21:3, 4) Sipadzakhalanso maboma a anthu ogaŵanitsa osakaza dziko lapansi ndi nkhondo. Sipadzakhalanso anthu onjenjemera chifukwa cha chiopsezo cha chipiyoyo cha nyukliya. Mafakitale amene amatulutsira utsi wapayizoni mu mlengalenga adzakhala atachoka.—Danieli 2:44.
Panthaŵiyo munthu aliyense wamoyo adzakhala wokonda chilungamo ndi bwenzi lowona, womvera kotheratu lamulo la Ufumu. (Salmo 37:10, 11) Zipatala, nyumba zamaliro, ndi misitu zidzachoka. Chisudzulo, chilekaniro, kuchita tondovi, ndi kuchitira nkhanza ana nazonso sizidzakhalakonso.—Yesaya 25:8; 65:17.
Kodi inu mufuna kupulumuka masiku otsiriza ndi kukhala ndi moyo kuwona dziko latsopano la Mulungu laulemerero? Pamenepo “dikirani, . . . . pakuti simudziŵa nthaŵi yake.” (Marko 13:33) Komabe, zochitika zadziko zikukupangitsa kukhala kwachiwonekere kuti nthaŵi yoikidwiratuyo yayandikira—iripafupi mowononga kwa ochuluka. Musataye nthaŵi. Chotero chitanipo kanthu kupulumutsa moyo, ndi kufunafuna awo amene akulabadira chizindikiro cha padziko lonse cha masiku otsiriza. Ameneŵa ngosavuta kuwadziŵa, pakuti ndiwo okha amene akumvera lamulo la Yesu lakulalikira mbiri yabwino ya Ufumu padziko lonse. Limodzi ndi ameneŵa, inu mungachitetu kanthu kuima kumbali ya Mfumuyo, Kristu Yesu, ponena za amene kwanenedwa kuti: “Akunja adzakhulupirira dzina lake.”—Mateyu 12:18, 21.
[Bokosi patsamba 5]
Mbali Makumi Aŵiri Mphambu Zinayi za Chizindikiro
1. Nkhondo imene sinachitikepo ndi kalelonse—Mateyu 24:6, 7; Chivumbulutso 6:4
2. Zivomezi—Mateyu 24:7; Marko 13:8
3. Kupereŵera kwa chakudya—Mateyu 24:7; Marko 13:8
4. Miliri—Luka 21:11; Chivumbulutso 6:8
5. Kuwonjezereka kwa kusayeruzika—Mateyu 24:12
6. Kuipitsidwa kwa dziko lapansi—Chivumbulutso 11:18
7. Kuzilala kwa chikondi—Mateyu 24:12
8. Kuwona zinthu zochititsa mantha—Luka 21:11
9. Kukonda ndalama kopambanitsa—2 Timoteo 3:2
10. Kusamvera makolo—2 Timoteo 3:2
11. Kukonda zokondweretsa koposa kukonda Mulungu—2 Timoteo 3:4
12. Kudzikonda kukupitirira muyezo—2 Timoteo 3:2
13. Kupanda chikondi chachibadidwe kwa awunyinji—2 Timoteo 3:3
14. Anthu osayanjanitsika—2 Timoteo 3:3
15. Opanda kudziletsa pamilingo iriyonse yachitaganya—2 Timoteo 3:3
16. Kuwanda kwa kusakonda ubwino—2 Timoteo 3:3
17. Mwachinyengo ambiri akudzinenera kukhala Akristu—2 Timoteo 3:5
18. Kudya ndi kumwa kopambanitsa kochitidwa ndi ambiri—Luka 21:34
19. Oseka akukana chizindikirocho—2 Petro 3:3, 4
20. Aneneri onyenga ambiri pantchito—Mateyu 24:5, 11; Marko 13:6
21. Kulalikidwa kwa mbiri yabwino ya ufumu wokhazikitsidwa
wa Mulungu—Mateyu 24:14; Marko 13:10
22. Chizunzo cha Akristu owona—Mateyu 24:9; Luka 21:12
23. Mfuu ya mtendere ndi chitetezo kukhala chimake cha masiku
otsiriza—1 Atesalonika 5:3
24. Anthu sakuzindikira upandu—Mateyu 24:39
[Bokosi patsamba 6]
Mavuto Oipitsa Malo Okhala—Chizindikiro cha Nthaŵi
◻ Mpweya wotetezera wa ozone m’malo okhalidwa kwambirimbiri a Chigawo cha Kumpoto ukupyapyala mofulumira kuŵirikiza nthaŵi ziŵiri kuposa m’mene asayansi analingalirira zaka zochepekera zapitazo.
◻ Pafupifupi mitundu yazomera ndi zinyama 140 ikusolotsedwa tsiku lirilonse.
◻ Milingo ya mpweya wolamulira kutentha ya carbon dioxide tsopano iri yokwererapo ndi 26 peresenti kuposa pamene maindasitale anali asanachuluke, ndipo ikupitirizabe kukwera.
◻ Malo adziko lapansi anali ofunda kwambiri mu 1990 kuposa chaka china chirichonse kuyambira pamene kuŵerengera kunayamba chapakati pazaka za zana la 19; zisanu ndi chimodzi za zaka zisanu ndi ziŵiri za zaka zofunda koposa zodziŵika zayamba kuwoneka kuyambira 1980.
◻ Nkhalango zikuzimiririka pamlingo wa mahekitila mamiliyoni 17 pa chaka, malo okwanira pafupifupi theka la ukulu wa Finland.
◻ Nzika zapadziko lapansi zikuwonjezereka ndi anthu okwanira mamiliyoni 92 pachaka—pafupifupi zofanana ndi kuwonjezera Mexico wina chaka chirichonse; pachiwonkhetsochi, mamiliyoni 88 akuwonjezeredwa m’maiko osatukuka.
◻ Pafupifupi anthu mabiliyoni 1.2 sakupeza madzi abwino a kumwa.
Mogwirizana ndi bukhu la State of the World 1992, lolembedwa ndi Worldwatch Institute, tsamba 3, 4, W. W. Norton & Company, New York, London.
[Chithunzi patsamba 7]
Pambuyo pachiwonongeko dziko latsopano laulemerero la Mulungu lidzadza