Chifukwa Chake Muyenera Kufikapo
MUDZAKHALA ndi masiku anayi akulandira chilangizo chauzimu pa Msonkhano Wachigawo wa “Kuphunzitsa Kwaumulungu,” umene udzachitidwa m’chilimwe chino m’mizinda yambiri kuzungulira padziko lonse. Mu Zambia mokha, misonkhano yokwanira 48 idzachitidwa mu August ndi September. Programuyo idzayamba Lachinayi pa 1:00 p.m. ndi kutha pa Sande pa 4:15 p.m. Chapadera pamisonkhano ina chidzakhala malipoti operekedwa ndi amishonale, amene athandizidwa kubwerera ku maiko akwawo kaamba ka chochitika chosangalatsa chimenechi.
Kaya ndinu wachikulire kapena wachichepere—mwamuna wokwatira, mkazi wokwatiwa, atate, amayi, wa zaka zapakati pa 13 ndi 19, kapena mwana—mudzalandira chiphunzitso choperekedwa mwanjira yomvekera bwino, yosangalatsa imene idzakupindulitsani. Mwachitsanzo, ambiri lerolino amafunsa kuti, Kodi chifuno cha moyo nchiyani? Lachisanu m’maŵa, mudzasangalala kumva funsoli likuyankhidwa ndipo mudzasangalala ndi chimene mudzalandira kukathandizira ena kumvetsetsa nkhaniyi.
Programu ya Lachisanu masana idzakhala ndi mbali zakuti “Kupanga Ukwati Kukhala Chigwirizano Chachikhalire,” “Gwirani Ntchito Zolimba Kaamba ka Chipulumutso cha Banja Lanu,” ndi “Makolo—Ana Anu Amafunikira Chisamaliro Chapadera.” Mwamsanga pambuyo pa nkhani zimenezi, chisamaliro chachindunji chidzaperekedwa pa mavuto amene achichepere akukumana nawo ndi mmene angawalakire. Iwo adzalimbikitsidwa ndi drama lamakono lokhala ndi mutu wakuti Achichepere Amene Amakumbukira Mlengi Wawo Tsopano Lino.
Programu ya Loŵeruka idzakhala ndi ulosi wa Yesu wonena za masiku otsiriza ndipo makamaka mawu ake akuti: “Atapita masauko a masiku awo, dzuŵa lidzadetsedwa.” (Mateyu 24:29) Mudzafuna kumva kafotokozedwe kosonyeza pamene masauko amenewo adzachitika. Programu ya tsiku Loŵeruka idzapendanso mbiri ya Mboni za Yehova m’nthaŵi zamakono ndi kusonyeza zimene izo zakwaniritsa.
Pa Sande drama lina, lokhala ndi mutu wakuti Musasocheretsedwe Kapena Kunyoza Mulungu, lidzafotokoza vuto la kusunga umphumphu Wachikristu chifukwa cha mavidiyo ndi nyimbo zotchuka zamasiku ano. Nkhani yapoyera yodzaperekedwa masana idzakhala ndi mutu wakuti “Chiphunzitso Chopindulitsa cha Nthaŵi Zathu Zoŵaŵitsa.” Programuyo idzatha ndi uphungu wakuti “Pitirizani Kugwira Zolimba Chiphunzitso Chaumulungu.”
Ndithudi, mudzapindula mwakukhalapo masiku onse anayi! Mukuitanidwa mwachimwemwe kufikapo. Kuti mupeze malo akufupi ndi kwanu, pitani ku Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova yakwanuko kapena lemberani kalata ofalitsa magazini ino.