Fikani pa Msonkhano Wachigawo Wakuti “Mantha Aumulungu”!
Kodi mwapanga makonzedwe akufika pa Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 1994 wakuti “Mantha Aumulungu”? Kunena zoona, mudzapindula mwa kupezekapo masiku onse atatu! Pokhala ndi misonkhano 49 yolinganizidwa m’Zambia mokha, mwinamwake msonkhano udzachitidwira pafupi ndi kumene mukukhala.
Mantha ena angaluluze kulimba mtima ndi kuwononga chiyembekezo; komabe, nkhani yaikulu ya mmaŵa pa Tsiku Loyamba idzapereka tanthauzo la mantha aumulungu ndi kufotokoza mapindu ake ambiri. Ndithudi, programu yonse ya msonkhano idzasonyeza mapindu ameneŵa.
Tsiku Loyamba masana mudzamva mmene mantha aumulungu angalimbitsire ukwati ndi moyo wabanja, ndiponso mmene angathandizire achichepere kukhalabe ochirimika pa kukhulupirika kwawo kwa Mulungu. Gawo lamasana lidzatha ndi nkhani yogwira mtima yakuti “Chitonthozo kwa Ofedwa.” Mudzayamikira chidziŵitso chothandiza choperekedwa m’nkhani imeneyo kuthandiza awo amene ataya okondedwa awo mu imfa.
Programu ya Tsiku Lachiŵiri Loweruka idzasonyeza mmene mantha aumulngu angachirikizire kumamatira kwathu ku chitsogozo cha Yehova ponena za mpingo ndi utumiki wathu. M’nkhani yakuti “Ŵerengani Mawu a Mulungu, Baibulo Loyera, Tsiku ndi Tsiku,” nthumwi zidzalandira malingaliro ogwira ntchito a kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo. Programu ya Tsiku Lachiŵiri idzatha ndi nkhani yochititsa chidwi ya mutu wakuti “Tsiku Lowopsa la Yehova Lili Pafupi.”
Mbali yaikulu paprogramu ya Tsiku Lomalira ndi nkhani yakuti “Kudzakhala Kuuka kwa Olungama.” M’nkhani yotsatira yakuti, “Kupulumutsidwa Amoyo Kupyola Chisautso Chachikulu,” malongosoledwe adzaperekedwa ponena za lonjezo labwino koposa la Yesu lokhudza awo amene sadzafa konse.—Yohane 11:26.
Gawo lammaŵa pa Tsiku Lomalira lidzamalizidwa ndi drama yosonkhezera maganizo yamphindi 40 ya mutu wakuti Zosankha Zimene Mukuyang’anizana Nazo. Omvetsera adzatengeredwa ku tsiku la Yoswa ndipo adzaona chosankha chake chotsimikiza cha kutumikira Yehova chikusonyezedwa. Ndiponso chiyeso cha moto m’masiku a Eliya chidzasonyezedwa, ndipo maphunziro amene adzathandiza nthumwizo kusonyeza mantha aumulungu lerolino adzaperekedwa ndi zochitika ziŵiri zimenezi. Masana, nkhani yapoyera yakuti, “Chifukwa Chake Tiyenera Kuwopa Mulungu Woona Tsopano Lino,” idzakhala mbali yaikulu ya msonkhanowo.
Pangani makonzedwe akufikapo tsopano lino. Kuti mupeze malo apafupi ndi kwanu, kafunseni ku Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova yakwanuko kapena lemberani ofalitsa magazini ano.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
T. Rosenthal/SUPERSTOCK