“Sitimalankhulana!”
MICHAEL, amene ali loya, anafunikira kukhala wolankhula wamphamvu. Ntchito yake inafuna zimenezo. Koma pambuyo pa zaka 16 za ukwati, Michael anakakamizika kuzindikira kuti pamene anafika panyumba kwa mkazi wake, Adrian, maluso ake akulankhulana anawonekera kukhala akuzimiririka. “Kupezerana zifukwa, kusulizana, kunamizirana,” Michael akukumbukira motero, “Adrian ndi ine tinali kukangana nthaŵi zonse, ndipo ndinaganiza kuti kukatitopetsa. Ndinakaikira ngati umenewo ndiwo unali ukwati, kusakhutiritsidwa ndi kunyong’onyeka komapitirizabe. Ngati umenewo ukanakhala mkhalidwe wathu m’miyoyo yathu yonse, ndinafuna kuuthetsa—sindikusekayi. Sindikanatha kukhala zaka 20, 30, 40 mumkhalidwe wotero wa kunyong’onyeka kosalekeza ndi chitsenderezo.”
Michael ndi Adrian sindiwo okha amene amanena mawu onga ameneŵa. Ameneŵa amanenedwa ndi okwatirana ambiri amene unansi wawo uli woyambana nthaŵi zonse. Makambitsirano abwino angabuke kukhala kulalatirana. Iwo “amamva” zinthu zimene sizinanenedwe. Amanena zinthu zimene sanafune kunena. Amaputana ndi kuimbana mlandu, ndiyeno kukhala duu, monyanyala. Samalekana, komanso sali kwenikweni “thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Unansiwo ngwa anthu ongokhalitsana. Kubwerera m’mbuyo kukakhala kulekana, kupita nawo patsogolo kukatanthauza kuvutana. Kuti apeŵe mavuto onsewo, okwatirana ameneŵa amasankha kunyalanyazana mwa malingaliro.
Okwatirana otero amafunikira kuti “afikire kuuphungu” wabwino mu ukwati wawo. (Miyambo 1:5) Uphungu umenewu umapezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Kalata yachiŵiri ya Paulo kwa Timoteo imatsimikizira kuti Baibulo “lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero.” (2 Timoteo 3:16) Zimenezi zimatsimikizira kukhala mbali imene imathandiza kusalekeka kwa kulankhulana m’banja, monga momwe tidzawonera.