Kutumikira ndi LIngaliro la Kufulumira kwa Nthaŵi
YOSIMBIDWA NDI HANS VAN VUURE
Tsiku lina mmaŵa mu 1962, Paul Kushnir, woyang’anira nthambi ya Watch Tower Society ku Netherlands, anakumana nane m’dera la doko la Rotterdam. Akumandiyang’ana pathebulo lomwe tinakhalapo m’kantini younikiridwa pang’ono, iye anati: “Kodi ukudziŵa, Hans, kuti utalandira gawo limeneli, iweyo ndi mkazi wako mudzapatsidwa tikiti yopitira yokha?”
“INDE, ndipo ndikhulupirira kuti nayenso Susie adzavomereza zimenezo.”
“Chabwino, kakambitsiraneni ndi Susie. Kudzakhala bwino koposa kundidziŵitsa msanga za chosankha chanu.”
Mmaŵa wotsatira iye analandira yankho lathu lakuti: “Tidzapita.” Chotero pa December 26, 1962, tinalaŵirana mwakukupatirana ndi achibale ndi mabwenzi pabwalo la ndege lokutidwa ndi chipale chofeŵa la Schiphol la ku Amsterdam, ndipo tinauluka kupita kugawo limene linalibe amishonale—Netherlands New Guinea (tsopano lotchedwa West Irian, Indonesia)—dziko la anthu a fuko la Papuan.
Kodi tinali ndi zikayikiro ponena za kulandira gawo lovuta limeneli? Osati kwenikweni. Tinapatulira miyoyo yathu ndi mtima wonse kuchita chifuniro cha Mulungu, ndipo tinakhulupirira kuti iye akatichilikiza. Poyang’ana m’mbuyo kupenda miyoyo yathu, timaona kuti chidaliro chathu mwa Yehova sichinatigwiritse mwala nthaŵi zonse. Koma ndisanasimbe zimene zinachitika ku Indonesia, tandilolani ndikuuzeni za zaka zathu zoyambirira.
Kuphunzira Zinthu m’Nthaŵi ya Nkhondo
Pamene banja lathu linachezeredwa nthaŵi yoyamba mu 1940 ndi Mboni yolimba mtimayo Arthur Winkler, ndinali ndi zaka khumi zokha. Makolo anga anadabwa kwambiri pamene anaona zimene Baibulo limanena pa ziphunzitso zonama za Dziko Lachikristu. Popeza kuti panthaŵiyo Netherlands anali m’manja mwa Germany wa Nazi ndipo Mboni za Yehova zinali kuzunzidwa, makolo anga anafunikira kusankha kaya kugwirizana ndi gulu loletsedwalo kapena ayi. Iwo anasankha kutero.
Pambuyo pa zimenezo, kulimba mtima kwa amayi ndi kufunitsitsa kwawo kuika ufulu wawo ndi moyo wawo womwe pachiswe kunandichititsa chidwi. Panthaŵi ina anapalasa njinga kwa makilomita 11 nayembekezera pamalo ena mumdima ndi thumba la matrakiti ophunzirira Baibulo. Panthaŵi yoikika yoyambira mkupiti wapadera, anapalasa njingayo mwaliŵiro malinga nkukhoza kwawo, akumaloŵetsa dzanja m’thumba lawo, namamwaza matrakiti m’makwalala. Wopalasa njinga wina wowalondola anawapeza pomalizira pake ndipo, ali ŵefuŵefu, anafuula kuti: “Amayi, amayi inu, mukutaya zinthu!” Tinaseka kwambiri pamene Amayi anasimba nkhaniyo.
Ndinali wamng’ono, koma ndinadziŵa zimene ndinafuna kuchita ndi moyo wanga. Pamsonkhano wathu wina chapakati pa 1942, pamene wochititsa anafunsa kuti, “Kodi ndani afuna kudzabatizidwa pamsonkhano wotsatira?” Ndinatukula dzanja langa. Makolo anga anayang’anana moda nkhaŵa, akumakayikira ngati ndinamvetsetsa tanthauzo la chosankha chimenecho. Komabe ngakhale kuti ndinali ndi zaka 12 zokha, ndinadziŵa zimene kudzipatulira kwa Mulungu kunatanthauza.
Kulalikira kunyumba ndi nyumba Anazi akutilondola kunafuna kuchenjera kwambiri. Kuti tipeŵe kufika panyumba za awo amene mwina akanatipereka, pamasiku amene ochilikiza Anazi anali kumamatiza zikwangwani pamazenera awo, ndinayendera mudzi wonsewo ndi njinga ndi kulemba makeyala awo. Panthaŵi ina mwamuna wina anandiona nafuula kuti: “Ukuchita bwino mwana wanga. Lemba maina awo—onse!” Ndinali wofunitsitsa koma osati wochenjera kwambiri! Pamene nkhondo inatha mu 1945, tinakondwera ndi chiyembekezo cha ufulu wokulirapo wa kulalikira.
Kuyamba kwa Ntchito
Pa November 1, 1948, nditatsiriza sukulu, ndinalandira gawo langa loyamba la kulalikira kwa nthaŵi yonse monga mpainiya. Patapita mwezi umodzi Mbale Winkler anachezera banja limene ndinali kukhala nalo. Iye ayenera kukhala atabwera kudzatsimikizira mtundu wa munthu amene ndinali chifukwa mwamsanga pambuyo pake ndinaitanidwa kukagwira ntchito paofesi ya nthambi ya Sosaite ku Amsterdam.
Pambuyo pake ndinapemphedwa kukachezera mipingo ya Mboni za Yehova monga woyang’anira dera. Ndiyeno, m’nyengo ya phukuto ya 1952, ndinalandira chiitano chokaloŵa kalasi ya 21 ya Sukulu ya Baibulo ya Gileadi ya Watchtower ku New York kukalandira maphunziro aumishonale. Chotero, chakumapeto kwa 1952, asanu ndi atatu a ifeyo ochokera ku Netherlands tinakwera sitima yapamadzi yotchedwa Nieuw Amsterdam ndi kupita ku America.
Chakumapeto kwa kosi ya sukulu imeneyo, Maxwell Friend, mmodzi wa alangizi, anati: “Mudzaiŵala zambiri za zinthu zimene mwaphunzira kuno, koma tikhulupirira kuti zinthu zitatu zidzakhalabe ndi inu: chikhulupiriro, chiyembekezo, ndi chikondi.” Ndiponso zimene ndasunga m’maganizo ndi mumtima mwanga ndizo zikumbukiro zamtengo wapatali za gulu la Yehova lomagwira ntchito ndi lingaliro la kufulumira kwa nthaŵi.
Zitatha zimenezo ndinagwiritsidwa mwala kwambiri. Theka la gulu lathu la Adatchi—kuphatikizapo ineyo—tinagaŵiridwa kukatumikiranso ku Netherlands. Ngakhale kuti ndinagwiritsidwa mwala, sindinakwiye. Koma sindinafune kuyembekezera, mofanana ndi Mose wakale, kwa zaka 40 ndisanalandire gawo langa la kudziko lina.—Machitidwe 7:23-30.
Wothangata Wokondedwa
Pamene Fritz Hartstang, bwenzi langa longa atate, anadziŵa za zolinga zanga za kukwatira, anandiuza mwachidaliro kuti: “Sinditha kuganiza za amene angakuyenerere.” Atate a Susie, a Casey Stoové, anali womenya nkhondo wotchuka m’gulu la Resistance lotsutsa Anazi m’Nkhondo Yadziko II. Koma pamene Mboni zinawafikira mu 1946, analandira chowonadi cha Baibulo mwamsanga. Posapita nthaŵi iwo ndi atatu a ana awo asanu ndi mmodzi—Susie, Marian, ndi Kenneth—anabatizidwa. Pa May 1, 1947, ana onse ameneŵa anayamba utumiki wanthaŵi yonse monga apainiya. Mu 1948, a Casey anagulitsa bizinesi yawo, ndipo nawonso anayamba upainiya. Pambuyo pake iwo anati: “Zaka zimenezo zinali zosangalatsa koposa m’moyo wanga!”
Ndinadziŵana ndi Susie mu 1949, pamene anaitanidwa kudzagwira ntchito paofesi yanthambi ya Amsterdam. Komabe, chaka chotsatira iye ndi mchemwali wake Marian anapita kukaloŵa kalasi ya 16 ya Gileadi ndipo anapita kugawo lawo la umishonale—Indonesia. M’February 1957, pambuyo potumikira kumeneko kwa zaka zisanu muutumiki waumishonale, Susie anabwerera ku Netherlands kudzakwatiwa ndi ine. Panthaŵiyo, ndinali kutumikira monga woyang’anira dera, ndipo m’zaka zonse za ukwati wathu, iye nthaŵi zambiri wasonyeza kufunitsitsa kudzimana iye mwini kaamba ka utumiki wa Ufumu.
Titakwatirana, tinapitiriza kuchezera mipingo m’mbali zosiyanasiyana za Netherlands. Zaka zimene Susie anathera m’ntchito yaumishonale m’magawo ovuta zinamkonzekeretsa bwino lomwe kaamba ka maulendo athu a panjinga kuchokera pampingo wina kumka ku wotsatira. Inali nthaŵi imeneyi pamene tinali m’ntchito yadera mu 1962 pamene Mbale Kushnir anandichezera ku Rotterdam ndi kutipempha kusamukira ku West Irian, Indonesia.
Utumiki Waumishonale ku Indonesia
Tinafika m’tauni ya Manokwari—malo achilendo kotheratu! Munali kumveka phokoso lozoloŵereka usiku m’madera otenthawo ndiponso munali motentha ndi mwa fumbi. Ndiyeno kunali anthu a fuko la Papuan a kumtunda amene anali kuvala nkhwende zokha, atanyamula mipeni, ndipo anakonda kutilondola m’mbuyo ndi kuyesa kukhudza khungu lathu loyera—zimene zinali zovuta kuzoloŵera.
Patapita milungu ingapo titafika kumeneko, atsogoleri achipembedzo anaŵerenga kalata paguwa la m’tchalitchi akumachenjeza anthu za Mboni za Yehova, ndipo anagaŵira kope lake kwa aliyense amene analipo. Ndipo nyumba ya wailesi ya komweko inaulutsadi kalatayo. Ndiyeno atsogoleri achipembedzo atatu anatichezera natilamula kusamukira chakumtunda kukagwira ntchito pakati pa amene anawatcha “akunja.” Nayenso mkulu wa apolisi wa fuko la Papuan anatifulumiza kuchoka, ndipo chiŵalo cha apolisi achinsinsi chinatiuza kuti anali kulinganiza zotipha.
Komabe, sionse amene anatsutsana nafe. Phungu wa zandale wolangiza anthu a fuko la Papuan, Mdatchi yemwe anali pafupi kupita ku Netherlands, anatidziŵitsa kwa mafumu angapo a fuko la Papuan. “Mboni za Yehova zidzabweretsa mtundu wabwino kwambiri wa chipembedzo Chachikristu kuposa chimene mudziŵa,” iye anawauza motero. “Chotero, muyenera kuzilandira.”
Pambuyo pake, mkulu wina wa boma anafika kwa Susie m’khwalala namnong’oneza kuti: “Tauzidwa kuti mwayamba ntchito yatsopano kunoko, ndipo, chotero, sitingakuloleni kukhala. Koma, ee, . . . mukanakhala ndi tchalitchi.” Linali lingaliro labwino limenelo! Mwamsanga tinagumula zipupa m’nyumba yathu, kundandalika mabenchi, kuika gome la wokamba nkhani, ndi kuika chikwangwani kutsogolo chakuti “Nyumba Yaufumu.” Ndiyeno tinaitana mkuluyo kudzacheza. Iye anagwedeza mutu, kumwetulira, nagogoda mutu wake ndi chala chankombaphala, monga ngati akunena kuti, ‘Ndinu ochenjera, eti.’
Pa June 26, 1964, patapita chaka chimodzi ndi theka kuyambira pamene tinafika, ophunzira athu a Baibulo oyambirira 12 a fuko la Papuan anabatizidwa. Posapita nthaŵi, panatsatira ena 10, ndipo avareji ya ofika pamisonkhano yathu inali 40. Apainiya aŵiri a ku Indonesia anatumizidwa kudzatithandiza. Pamene mpingo unakhazikitsidwa bwino lomwe ku Manokwari, nthambi ya Sosaite ya Indonesia inatipatsa gawo lina lolalikira, mu December 1964.
Tisanapite, mkulu wa Public Relations Department ya boma anatitengera mseri nati: “Ndili ndi chisoni kuti mukupita. Mlungu uliwonse atsogoleri achipembedzo anandichonderera kuti ndikupitikitseni chifukwa anati munali kuthyola zipatso zawo. Koma ndinali kuwauza kuti: ‘Ayi, mmalomwake, iwo akuika feteleza m’mitengo yanu.’” Iye anawonjezera kuti: “Kulikonse kumene mupita, mupitirizebe kumenya nkhondo. Mudzapambana!”
Mkati mwa Kulanda Boma
Usiku wina mu September 1965, pamene tinali kutumikira m’likulu la dzikolo, Djakarta, zigaŵenga Zachikomyunizimu zinapha akuluakulu a nkhondo ambiri, kutentha Djakarta yense, ndi kuyambitsa nkhondo m’dziko lonselo imene m’kupita kwa nthaŵi inachititsa prezidenti wa dzikolo, Sukarno, kulandidwa mpando. Pafupifupi anthu 400,000 anataya miyoyo yawo!
Panthaŵi ina tinali kulalikira pamene mfuti zinali kulira ndipo moto unali kuyaka m’khwalala lotsatira. Tsiku lotsatira tinamva kuti asilikali anali pafupi kuwononga nyumba ya pafupi Yachikomyunizimu. Eninyumba anaoneka kukhala amantha pamene tinawafikira, koma pamene anamva uthenga wathu wa Baibulo, anamasuka natiloŵetsa m’nyumba. Anadzimva kukhala otetezereka kukhala pamodzi nafe. Nyengo imeneyo inatiphunzitsa tonsefe kudalira pa Yehova ndi kukhala osatekeseka m’mikhalidwe yowopsa.
Chitsutso Chowonjezereka Chigonjetsedwa
Kumapeto kwa 1966 tinasamukira kumzinda wa Ambon kuzisumbu zokongola zakummwera za Molucca. Kumeneko, pakati pa anthu aubwenzi ndi okonda kuchereza, tinapeza chikondwerero chachikulu chauzimu. Mpingo wathu waung’ono unakula mofulumira, ndipo chiŵerengero cha opezeka pamsonkhano chinayandikira pa zana limodzi. Chotero akuluakulu a matchalitchi a Dziko Lachikristu anapita ku Office for Religious Affairs kukakakamiza mkulu wake kutipitikitsa mu Ambon. Koma padesiki la mkuluyo, anaonapo mabuku a Watch Tower Society oikidwa poyera! Polephera kugonjetsa mkuluyo, iwo anafika kwa nduna za Ministry of Religion ku Djakarta, akumafunafuna kuti tipitikitsidwe osati mu Ambon mokha komanso mu Indonesia yense.
Nthaŵiyi kunaonekera kuti anapambana, pakuti February 1, 1968, inaikidwa kukhala deti la kupitikitsidwa kwathu. Komabe, abale athu Achikristu ku Djakarta anafikira nduna yaikulu Yachisilamu ku Ministry of Religion, ndipo inathandizira kusintha chigamulocho. Ndiponso, lamulo lakale linasinthidwa, ndipo amishonale ena analoledwa kuloŵa m’dzikolo.
Chotero, m’zaka khumi zotsatira, m’malo a mapiri aatali, nkhalango zazikulu, ndi nyanja kumpoto kwa Sumatra, tinagwira ntchito ndi amishonale ochokera ku Australia, Austria, Germany, Philippines, Sweden, ndi United States. Ntchito yolalikira inafutukuka, makamaka pakati pa fuko lalikulu m’deralo, la Batak.
Komabe, ochita chiwembu achipembedzo pomalizira pake anapambana m’kuchititsa ntchito yathu yolalikira kuletsedwa mu December 1976, ndipo chaka chotsatira amishonale ochuluka anapita kukatumikira kumaiko ena. Pomalizira pake, mu 1979, nafenso tinafunikira kupita.
Kupita ku South America
Panthaŵiyo tinali pafupifupi ndi zaka 50 zakubadwa, ndipo tinakayikira ngati tikakhoza kusinthira kudziko lina. “Kodi tilandire gawo latsopanoli kapena mmalomwake tipeze malo okhala?” Susie anafunsa motero.
“Eya, Susie,” ndinayankha motero, “kulikonse kumene Yehova anatiuza kupita, anatisamalira. Kodi ndani adziŵa madalitso omwe ali mtsogolo?” Chotero, tinafika kugawo lathu latsopano, m’dziko la ku South America la Suriname. Mkati mwa miyezi iŵiri tinakhalanso m’ntchito yoyendayenda ndipo posapita nthaŵi tinazoloŵera.
Popendanso zaka zoposa 45 za utumiki wa nthaŵi yonse, ineyo ndi Susie timazindikira mmene chichilikizo cha makolo athu chinaliri chofunika kutithandiza kupitirizabe m’ntchito yaumishonale. Mu 1969, pamene ndinaonananso ndi makolo anga pambuyo pa zaka zisanu ndi chimodzi, atate ananditengera pambali nati: “Ngati zingachitike kuti Amako ndiwo ayamba kufa, sudzafunikira kubwera kumudzi kuno. Ukakhale m’gawo lako. Ndidzakhoza kudzisamalira. Koma ngati ndine ndayamba, udzafunikira kufunsa Amako.” Amayi ananena chimodzimodzinso.
Makolo a Susie anali ndi mkhalidwe wopanda dyera umodzimodziwo. Panthaŵi ina iwo sanaonane ndi Susie kwa zaka 17, koma sanamlembere ngakhale liwu limodzi lolefula. Ndithudi, ngati makolo athu analibe chithandizo chilichonse, tikanabwerera kumudzi. Mfundo njakuti, makolo athu nawonso anaiona ntchito yaumishonale kukhala yamtengo wapatali ndipo, kufikira imfa yawo, anatumikira Yehova ndi lingaliro limodzimodzilo la kufulumira kwa nthaŵi limene anakhomereza m’mitima yathu.—Yerekezerani ndi 1 Samueli 1:26-28.
Talimbikitsidwanso ndi anthu okhulupirika otilembera makalata. Alipo angapo amene sanaphonye ngakhale mwezi umodzi osatilembera kalata m’zaka zathu zoposa 30 za utumiki waumishonale! Koma koposa onse, timakumbukira Atate wathu wakumwamba wachikondi, Yehova, amene adziŵa mmene angachilikizire atumiki ake padziko lapansi. Chifukwa chake, pamene tiyandikira chimake cha zochitika zimene takhala tikuyembekezera mwachidwi, ineyo ndi Susie tifuna kupitiriza “kuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la [Yehova, NW]” mwakupitiriza kutumikira Yehova ndi lingaliro la kufulumira kwa nthaŵi.—2 Petro 3:12.
[Chithunzi patsamba 26]
Tinakwatirana mu 1957
[Chithunzi patsamba 29]
Nzosangalatsa chotani nanga—achichepere asanu ndi mmodzi kukhala apainiya!