Dalirani Yehova!
“Dalira [“Khulupirira,” Revised Nyanja Version] Yehova ndi mtima wako wonse.”—MIYAMBO 3:5, NW.
1. Kodi ndimotani mmene lemba la Miyambo 3:5 linakopera mnyamata wina, limodzi ndi chotulukapo chokhalitsa chotani?
MMISHONALE amene watumikira kwanthaŵi yaitali akulemba kuti: “‘DALIRA AMBUYE NDI MTIMA WAKO WONSE; NDIPO USACHIRIKIZIKE PA LUNTHA LAKO.’ Mawu amenewo otengedwa m’Baibulo, oikidwa m’feremu yokoloŵekedwa kukhoma m’nyumba mmene ndinali kucheza, anandikopa. Tsiku lonselo ndinawasinkhasinkha. Kodi ineyo, ndinadzifunsa, ndingadalire Mulungu ndi mtima wanga wonse?” Panthaŵiyo munthuyu anali wazaka 21 zakubadwa. Pausinkhu wazaka 90 zakubadwa ndipo akutumikirabe mokhulupirika monga mkulu ku Perth, Australia, iye angayang’ane kumbuyo pa moyo wolemeretsedwa ndi zipatso za kudalira Yehova ndi mtima wonse, kuphatikizapo zaka 26 zovuta za kuchita upainiya m’minda yatsopano yaumishonale ku Ceylon (tsopano Sri Lanka), Burma (tsopano Myanmar), Malaya, Thailand, India, ndi Pakistan.a
2. Kodi nchidaliro chotani chimene lemba la Miyambo 3:5 liyenera kukulitsa mwa ife?
2 “Dalira Yehova ndi mtima wako wonse”—mawu ameneŵa a pa Miyambo 3:5, monga momwe amasulidwira ndi New World Translation, ayenera kutisonkhezera ife tonse kupitiriza kupereka miyoyo yathu kwa Yehova ndi mtima wonse, tili ndi chidaliro chakuti akhoza kulimbitsa chikhulupiriro chathu, ngakhale kufikira pakulaka zopinga zonga mapiri. (Mateyu 17:20) Tiyeni tsopano tipende Miyambo 3:5 malinga ndi nkhani yake yonse.
Malangizo Autate
3. (a) Kodi nchilimbikitso chotani chimene chikupezeka m’machaputala asanu ndi anayi oyambirira a Miyambo? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupereka chisamaliro chachikulu pa Miyambo 3:1, 2?
3 Machaputala asanu ndi anayi oyambirira a buku Labaibulo la Miyambo ngodzala ndi malangizo autate, uphungu wanzeru wochokera kwa Yehova wa onse amene amayembekezera mwachidwi kukakhala ana ake kumwamba kapena “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu,” padziko lapansi laparadaiso. (Aroma 8:18-21, 23) Umenewu ndiuphungu wanzeru umene ungagwiritsiridwe ntchito ndi makolo polera ana aamuna ndi aakazi. Wapadera ndiuphungu wa pa Miyambo chaputala 3, umene umayamba ndi chenjezo lakuti: “Mwananga, usaiŵale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga.” Pamene masiku otsiriza a dziko loipa la Satana ayandikira mapeto ake, tiyenitu tisamalire kwambiri zikumbutso za Yehova. Ulendowo ungaoneke kukhala wautali, koma lonjezo kwa onse opirira nlakuti “adzakuwonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere”—moyo wamuyaya m’dongosolo latsopano la Yehova.—Miyambo 3:1, 2.
4, 5. (a) Kodi ndiunansi wachimwemwe wotani umene ukufotokozedwa pa Yohane 5:19, 20? (b) Kodi ndimotani mmene uphungu wa pa Deuteronomo 11:18-21 umagwirira ntchito kufikira m’tsiku lathu?
4 Unansi wachimwemwe pakati pa atate ndi mwana ungakhale wamtengo wapatali. Mlengi wathu, Yehova Mulungu, analinganiza kuti zikhalire momwemo. Kristu Yesu ananena za unansi wake wathithithi ndi Yehova kuti: “Sakhoza Mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene aona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene Iye azichita, zomwezo Mwananso azichita momwemo. Pakuti Atate akonda Mwana, namuonetsa zonse azichita yekha.” (Yohane 5:19, 20) Yehova analinganiza kuti unansi wofanana ukhalepo pakati pa iye mwini ndi banja lake lonse padziko lapansi, ndiponso pakati pa atate aumunthu ndi ana awo.
5 Unansi wodalirana wa m’banja unalimbikitsidwa m’Israyeli wakale. Panthaŵiyo Yehova analangiza atate kuti: “Muzisunga mawu anga awa mumtima mwanu ndi m’moyo mwanu; ndi kuwamanga ngati chizindikiro pamanja panu; ndipo zikhale zapamphumi pakati pa maso anu. Ndipo muziwaphunzitsa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala inu pansi m’nyumba mwanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pakuuka inu pomwe. Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu; kuti masiku anu ndi masiku a ana anu achuluke m’dziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzawapatsali, monga masiku a thambo liri pamwamba pa dziko.” (Deuteronomo 11:18-21) Mawu ouziridwa a Mlangizi wathu Wamkulu, Yehova Mulungu, angathandizedi kumgwirizanitsa mwathithithi ndi makolo ndi ana awo, limodzinso ndi ena onse amene akumtumikira mumpingo Wachikristu.—Yesaya 30:20, 21.
6. Kodi tingapeze motani chiyanjo cha Mulungu ndi anthu?
6 Uphungu wanzeru wautate kwa anthu a Mulungu, achikulire ndi achichepere, ukupitiriza m’mavesi 3 ndi 4 a Miyambo chaputala 3: “Chifundo ndi chowonadi zisakusiye; uzimange pakhosi pako; uzilembe pamtima pako; motero udzapeza chisomo ndi nzeru yabwino, pamaso pa Mulungu ndi anthu.” Yehova Mulungu mwiniyo apambana pa kusonyeza chifundo ndi chowonadi. Monga momwe Salmo 25:10 limafotokozera, “mayendedwe onse a Yehova ndiwo chifundo ndi chowonadi.” Potsanzira Yehova, tiyenera kuyamikira mikhalidwe imeneyi ndi mphamvu yake yotetezera, kuiona kukhala yamtengo wapatali monga momwe tingaonere unyolo wovala m’khosi kukhala wamtengo wake ndi kuikhomereza pamtima pathu kwachikhalire. Pamenepo, mwakhama, tingapemphere kuti: “Inu Yehova, . . . chifundo chanu ndi chowonadi chanu zindisunge chisungire.”—Salmo 40:11.
Chidaliro Chosatha
7. Kodi ndimwanjira zotani zimene Yehova wasonyeza kudalirika kwake?
7 Chidaliro chimamasuliridwa ndi Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary kukhala “kuyedzamira kotsimikizirika pa mkhalidwe, kukhoza, nyonga, kapena chowonadi cha munthu wina kapena kanthu kena.” Mkhalidwe wa Yehova ngwozikidwa zolimba pa chifundo chake. Ndipo tingakhale ndi chidaliro chonse m’kukhoza kwake kuchita zimene walonjeza, pakuti dzina lake lenilenilo, Yehova, limamdziŵikitsa kukhala Wachifuno wamkulu. (Eksodo 3:14; 6:2-8) Monga Mlengi, ndiye Magwero a nyonga ndi mphamvu zazikulu. (Yesaya 40:26, 29) Ndiye chitsanzo chenicheni cha chowonadi, pakuti “Mulungu sakhoza kunama.” (Ahebri 6:18) Chifukwa chake, tikulimbikitsidwa kuika chidaliro chosagwedera mwa Yehova, Mulungu wathu, Magwero aakulu a chowonadi chonse, amene ali ndi mphamvu zonse zotetezerera awo omdalira ndi kukwaniritsa zifuno zake zonse zazikulu zaulemerero.—Salmo 91:1, 2; Yesaya 55:8-11.
8, 9. Kodi nchifukwa ninji kudalirika kukusoŵeka momvetsa chisoni m’dziko, ndipo anthu a Yehova ali osiyana motani?
8 M’dziko loluluzika lotizinga, kudalirika kukusoŵeka momvetsa chisoni. Mmalo mwake, timaona umbombo ndi ukatangale kulikonse. Chikuto cha kope la May 1993 la magazini a World Press Review chinalembedwapo uthenga m’zilembo zazikulu kuti: “KUWONJEZEREKA KWA MACHITIDWE AUKATANGALE—Ndalama Zachiphuphu m’Dongosolo Ladziko Latsopano. Machitachita aukatangale afalikira kuchokera ku Brazil mpaka ku Germany, kuchokera ku United States mpaka ku Argentina, kuchokera ku Spain mpaka ku Peru, kuchokera ku Italy mpaka ku Mexico, kuchokera ku Vatican mpaka ku Russia.” Pokhala lozikidwa pa udani, umbombo, ndi kusadalirana, lonenedwa kukhala dongosolo ladziko latsopano la munthu silinatulutse zilizonse kusiyapo mavuto omawonjezereka a mtundu wa anthu.
9 Mosiyana ndi mitundu yandale, Mboni za Yehova nzachimwemwe kukhala “mtundu wa anthu umene Yehova ndiye Mulungu wawo.” Izo zokha nzimene zinganene mowona kuti, “Timadalira Mulungu.” Aliyense wa iwo angafuule mokondwa kuti: “Mwa Mulungu ndidzalemekeza mawu ake; . . . Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzawopa.”—Salmo 33:12; 56:4, 11.
10. Kodi nchiyani chimene chalimbikitsa Akristu achichepere ambiri kusunga umphumphu?
10 M’dziko lina ku Asia kumene zikwi zambiri za Mboni zachichepere zazunzika mwa kumenyedwa kowopsa ndi kuponyedwa m’ndende, kudalira Yehova kwatheketsa ochuluka kupirira. Usiku wina m’ndende, Mboni ina yachichepere imene inali itazunzika kowopsa inaganiza kuti siikanathanso kupirira. Koma wachichepere wina anadza mwakabisira kwa iye. Anati monong’oneza: “Usagonje; ine ndinagonja ndipo sindinakhale ndi mtendere wamaganizo chiyambire pamenepo.” Wachichepere woyambayo analimbitsanso kutsimikiza mtima kwake kwa kuchirimika. Tingakhale ndi chidaliro chonse mwa Yehova chakuti adzatithandiza kulaka zoyesayesa za Satana zamtundu uliwonse za kufooketsa umphumphu wathu.—Yeremiya 7:3-7; 17:1-8; 38:6-13, 15-17.
11. Kodi timasonkhezeredwa motani kudalira Yehova?
11 Mbali ya lamulo loyamba imati: “Uzikonda [Yehova, NW] Mulungu wako ndi mtima wako wonse.” (Marko 12:30) Pamene tisinkhasinkha pa Mawu a Mulungu, chowonadi chabwino koposa chimene timaphunzira chimazika mizu yakuya kwambiri mumtima mwathu kotero kuti timasonkhezeredwa kudzikhuthula muutumiki wa Mulungu wathu wabwino, Mfumu Ambuye Yehova. Mtima wodzala ndi chiyamikiro kwa iye—kaamba ka zonse zimene watiphunzitsa, watichitira, ndi zimene adzatichitirabe—ndiwo umatisonkhezera kudalira chipulumutso chake mosagwedera.—Yesaya 12:2.
12. Mkati mwa zaka zambiri, kodi ndimotani mmene Akristu ambiri asonyezera chidaliro mwa Yehova?
12 Chidaliro chimenechi chingakulitsidwe mkati mwa zaka zambiri. Mboni ya Yehova yodzichepetsa imene inatumikira kwa zaka zoposa 50 pamalikulu a Watch Tower Society ku Brooklyn, kuyambira mu April 1927, inalemba kuti: “Pamapeto a mweziwo ndinalandira alawansi yokwanira $5.00 m’invulopu limodzi ndi khadi lokongola lokhala ndi lemba la m’Baibulo la Miyambo 3:5, 6 . . . Panali zifukwa zambiri zodalira Yehova, pakuti pamalikulupo ndinafikira pakuzindikira mosataya nthaŵi kuti Yehova ali ndi ‘kapolo wokhulupirika ndi wanzeru’ amene mokhulupirika akusamalira zabwino za Ufumu pompano padziko lapansi.—Mateyu 24:45-47.”b Mtima wa Mkristu ameneyu unasumikidwa, osati pa chikondi cha pa ndalama, koma pa kulandira “chuma chosatha m’mwamba.” Mofanana lerolino, zikwi zambiri za awo otumikira panyumba za Beteli za Watch Tower Society padziko lonse akutero pansi pa choŵinda chalamulo cha umphaŵi. Iwo amadalira Yehova kugaŵira zosoŵa zawo za tsiku ndi tsiku.—Luka 12:29-31, 33, 34.
Chirikizikani pa Yehova
13, 14. (a) Kodi nkuti kokha kumene uphungu wauchikulire ungapezeke? (b) Kodi tiyenera kupeŵa chiyani kuti tipirire chizunzo?
13 Atate wathu wakumwamba akutilangiza kuti: “Osachirikizika pa luntha lako.” (Miyambo 3:5) Aphungu a dziko ndi akatswiri a zamaganizo sangayembekezere konse kupeza nzeru ndi luntha zimene Yehova amasonyeza. “Luntha lake silitha kusimbika.” (Salmo 147:5, NW) Mmalo mwa kuchirikizika pa nzeru ya amuna otchuka a dziko kapena pa mtima wathu wopulukira, tiyeni tiyang’ane kwa Yehova, Mawu ake, ndi akulu mumpingo Wachikristu kaamba ka uphungu wauchikulire.—Salmo 55:22; 1 Akorinto 2:5.
14 Nzeru zaumunthu kapena malo apamwamba sizidzatithandiza konse m’tsiku lomadza mofulumira la chiyeso chowopsa. (Yesaya 29:14; 1 Akorinto 2:14) Ku Japan mkati mwa Nkhondo Yadziko II, mbusa wokhoza koma wonyada wa anthu a Mulungu anasankha kuchirikizika pa luntha lake. Potsenderezedwa iye anakhala wampatuko, ndipo ochuluka m’gulu la nkhosa anafooka poyang’anizana ndi chizunzo. Mlongo wokhulupirika wa ku Japan, amene molimba mtima anapirira nkhanza m’zipinda zauve za m’ndende, anati: “Awo amene anakhalabe okhulupirika analibe maluso apadera ndipo anali osadzionetsera. Ndithudi tonsefe tiyenera nthaŵi zonse kudalira Yehova ndi mtima wathu wonse.”c
15. Kodi ndimkhalidwe waumulungu uti umene uli wofunika ngati titi tikondweretse Yehova?
15 Kudalira Yehova, mmalo mwa luntha lathu, kumaloŵetsamo kudzichepetsa. Mkhalidwe umenewu ngwofunika chotani nanga kwa onse ofuna kukondweretsa Yehova! Eya, nayenso Mulungu wathu, ngakhale kuti ndi Ambuye Mfumu wa chilengedwe chonse, amasonyeza kudzichepetsa m’zochita zake ndi zolengedwa zaluntha. Tikuyamikira zimenezo. “Nadzichepetsa apenye zam’mwamba ndi za padziko lapansi. Amene autsa wosauka kumchotsa kufumbi.” (Salmo 113:6, 7) Chifukwa cha chifundo chake chachikulu, iye amatikhululukira zophophonya zathu pamaziko a mphatso yake yaikulu koposa kwa anthu, nsembe ya dipo yamtengo wapatali ya Mwana wake wokondedwa, Kristu Yesu. Tiyenera kukhala oyamikira chotani nanga kaamba ka kukoma mtima kwaulere kumeneku!
16. Kodi ndimotani mmene abale angakalimirire mathayo mumpingo?
16 Yesu mwiniyo akutikumbutsa kuti: “Ndipo amene aliyense akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.” (Mateyu 23:12) Modzichepetsa, abale obatizidwa ayenera kukalimira mathayo mumpingo Wachikristu. Komabe, oyang’anira ayenera kuona kuikidwa kwawo, osati monga malo aulemu pantchito, koma monga mwaŵi wochitira ntchito, modzichepetsa, moyamikira, mofunitsitsa, monga mmene Yesu anachitira, amene anati: “Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, inenso ndigwira ntchito.”—Yohane 5:17; 1 Petro 5:2, 3.
17. Kodi nchiyani chimene tonsefe tiyenera kuzindikira, chikumatisonkhezera kuntchito yotani?
17 Nthaŵi zonse tizindikiretu modzichepetsa ndi mwapemphero kuti ndife fumbi ndithu m’maso mwa Yehova. Pamenepa, tiyenera kukhala okondwa chotani nanga, kuti “chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthaŵi yosayamba kufikira nthaŵi yosatha kwa iwo akumuwopa iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana”! (Salmo 103:14, 17) Chotero tonsefe tiyenera kukhala ophunzira aphamphu a Mawu a Mulungu. Nthaŵi yowonongedwera paphunziro laumwini ndi labanja, ndi pamisonkhano ya mpingo, iyenera kukhala mbali ya maola amtengo wapatali kopambana mlungu uliwonse. Mwanjira imeneyi timakulitsa “kudziŵa Woyerayo.” Kumeneko “ndiko luntha.”—Miyambo 9:10.
“M’Njira Zako Zonse . . . ”
18, 19. Kodi tingagwiritsire ntchito motani Miyambo 3:6 m’miyoyo yathu, ndipo limodzi ndi chotulukapo chotani?
18 Likumatisonyeza Yehova, Magwero aumulungu a luntha, lemba la Miyambo 3:6 limati: “M’njira zako zonse [umzindikire, NW], ndipo iye adzawongola mayendedwe ako.” Kuzindikira Yehova kumaloŵetsamo kuyandikira pafupi naye m’pemphero. Kulikonse kumene tingakhale ndipo mosasamala kanthu za mkhalidwe uliwonse umene ungabuke, tili ndi njira yomfikira m’pemphero panthaŵi yomweyo. Pamene tichita ntchito zathu za tsiku ndi tsiku, pokonzekera utumiki wakumunda, popita kunyumba ndi nyumba kulengeza Ufumu wake, pemphero lathu losalekeza likhaletu lakuti iye adalitse zochita zathu. Motero, tikhoza kukhala ndi mwaŵi ndi chimwemwe zosayerekezereka za ‘kuyenda ndi Mulungu,’ ndi chidaliro chakuti iye ‘adzawongola mayendedwe athu,’ monga momwe anachitira kwa Enoke ndi Nowa owopa Mulungu, ndi Aisrayeli okhulupirika, onga Yoswa ndi Danieli.—Genesis 5:22; 6:9; Deuteronomo 8:6; Yoswa 22:5; Danieli 6:23; onaninso Yakobo 4:8, 10.
19 Pamene tidziŵitsa Yehova zopempha zathu, tiyenera kukhala achidaliro kuti ‘mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yathu ndi maganizo athu mwa Kristu Yesu.’ (Afilipi 4:7) Mtendere wa Mulungu umenewu, wosonyezedwa pankhope yosangalala, ungakometsere uthenga wathu kwa eninyumba amene tikumana nawo m’ntchito yathu yolalikira. (Akolose 4:5, 6) Ungalimbikitsenso awo amene angakhale akuvutika ndi zipsinjo kapena chisalungamo zimene zili zofala kwambiri m’dziko lamakono, monga momwe nkhani yotsatira ikusonyezera.d
20, 21. (a) Mkati mwa nkhanza ya Nazi, kodi ndimotani mmene umphumphu wa Mboni za Yehova unalimbikitsira ena? (b) Kodi nkutsimikiza mtima kotani kumene liwu la Yehova liyenera kuchititsa mwa ife?
20 Max Liebster, Myuda wachibadwidwe amene mozizwitsa anapulumuka Chipululutso cha Anazi, anafotokoza ulendo wake wopita ku msasa wophera wa Nazi motere: “Anatikhomera m’ngolo za sitima zimene zinasinthidwa kukhala timalumande tating’onong’ono tambiri ta anthu aŵiriaŵiri. Nditaloŵetsedwa m’limodzi la ito mwa kupondedwa chidyali, ndinayang’anizana ndi mkaidi amene nkhope yake inasonyeza mtendere. Anali mmenemo chifukwa cha kulemekeza kwake lamulo la Mulungu, akumasankha ndende ndi imfa yothekera mmalo mokhetsa mwazi wa anthu ena. Anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Anali atalandidwa ana ake, ndipo mkazi wake anali atanyongedwa. Nayenso amayembekezera kunyongedwa. Ulendo wa masiku 14 unachititsa mapemphero anga kuyankhidwa, pakuti panali paulendo umenewu wa ku imfa pamene ndinapeza chiyembekezo cha moyo wosatha.”
21 Atavutika m’ndende yachibalo ya Auschwitz, imene anatcha “phanga la mikango,” ndi kubatizidwa, mbale ameneyu anakwatira mmodzi wa Mboni za Yehova amene nayenso anali ataponyedwapo m’ndende ndi amene atate wake anazunzika kundende yachibalo ku Dachau. Pamene atate a mkaziyo anali m’ndende, anamva kuti mkazi wake ndi mwana wake wamkazi wamng’ono anali atagwidwa nawonso. Iye anafotokoza mmene anamvera kuti: “Ndinada nkhaŵa kwambiri. Ndiyeno tsiku lina pamene ndinali pamzera wokasamba, ndinamva liwu likugwira mawu a lemba la Miyambo 3:5, 6 . . . Liwulo linamveka ngati kuti linali kuchokera kumwamba. Ndinafunikira zokhazo kuti ndilimbikenso.” Kwenikweni, liwulo linali la mkaidi wina amene anali kugwira mawu lembali, koma chochitikachi chimasonyeza mphamvu imene Mawu a Mulungu angakhale nayo pa ife. (Ahebri 4:12) Liwu la Yehova lilankhuletu mwamphamvu kwa ife lerolino kupyolera mwa mawu a lemba lathu lachaka cha 1994: “Dalira [“Khulupirira”] Yehova ndi mtima wako wonse”!
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Kudalira Yehova Ndi Mtima Wanga Wonse,” yosimbidwa ndi Claude S. Goodman, mu The Watchtower, December 15, 1973, masamba 760-5.
b Onani nkhani yakuti “Kutsimikiza Mtima Kutamanda Yehova,” yosimbidwa ndi Harry Peterson, mu The Watchtower, July 15, 1968, masamba 437-40.
c Onani nkhani yakuti “Yehova Samasiya Atumiki Ake,” yosimbidwa ndi Matsue Ishii, mu Nsanja ya Olonda, May 1, 1988, masamba 21-5.
d Onaninso nkhani yakuti “Chilanditso! Kudzisonyeza Ife Eni Kukhala Oyamikira,” yosimbidwa ndi Max Liebster, mu The Watchtower, October 1, 1978, masamba 20-4.
Mwachidule
◻ Kodi ndiuphungu wamtundu wotani umene ukuperekedwa m’Miyambo?
◻ Kodi kudalira Yehova kumatipindulitsa motani?
◻ Kodi kuchirikizika pa Yehova kumaloŵetsamo chiyani?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuzindikira Yehova m’njira zathu zonse?
◻ Kodi Yehova amawongolera motani mayendedwe athu?
[Zithunzi patsamba 15]
Uthenga wachisangalalo wa Ufumu umakopa anthu owona mtima