Achichepere Amene ‘Amadalira Yehova’
ACHICHEPERE alibe ulamuliro wonse pakukongola, ndiponso achikulire sali ndi nzeru zonse. (Yerekezerani ndi Miyambo 11:22; Mlaliki 10:1.) Mmalo mwake, awo amene ali ndi kukongola kokhalitsa ndi nzeru yeniyeni ali awo amene amadalira Yehova ndipo ndi mtima wonse amanena za iye kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga.”—Salmo 31:14; Miyambo 9:10; 16:31.
Kuzungulira dziko lonse pali unyinji wa anthu okongola umene ukuwonjezereka, achichepere ndi achikulire omwe, amene amasonyeza nzeru yawo mwa kutumikira Mulungu ndi kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Mwachitsanzo, talingalirani za Sabrina wazaka zisanu ndi zitatu.
Sabrina amakhala ku Germany ndipo ali m’giredi lachiŵiri. Iye ndimmodzi wa Mboni za Yehova woyamba kuloŵa pasukulupo. Mwachisoni, iye anali munthu wotonzedwa ndi anzake akusukulu kufikira tsiku limene mphunzitsi anapempha ophunzira kuti adze ndi buku lawo lokondedwa m’kalasi. Sabrina anasankha kupita ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Usikuwo, ngakhale kuti anali ndi mantha, anakonzekera bwino lomwe zoti akachite m’kalasi. Popeza kuti panali ophunzira 26 m’kalasi mwake, iye anadziŵa kuti mwina sakakhala ndi nthaŵi yambiri. Koma anali wotsimikizira kusalola aliyense kudodometsa ulaliki wake ndipo anali wotsimikizira kuti Yehova akamthandiza. Patsiku losankhidwalo, mphunzitsi anafunsa za amene anali atadza ndi buku lake ndi amene akanakonda kukhala woyamba kulisonyeza. Modabwitsa, Sabrina yekha ndiye amene anadza ndi buku. Anaimirira patsogolo pa kalasiyo nayamba kulankhula, akumaŵerenga ndi kusonyeza zithunzithunzi za m’bukulo nafotokoza kuti zonsezo zinali zochokera m’Baibulo. Pomaliza iye anafunsa kuti: “Kodi ndani amene angakondwerere kukhala ndi buku limeneli?” Iye anagaŵira mphunzitsi kope limodzi, ndipo m’masiku angapo otsatira, anagaŵira mabuku ena owonjezereka khumi kwa anzake a m’kalasi. Ndemanga yokha ya mphunzitsiyo paulaliki wake inali yakuti: “Sindinaonepo zoterezi.” Anapatsa Sabrina giredi A chifukwa cha ntchito yake.
Kunena zowona, Mboni zambiri zachichepere zili ofalitsa achimwemwe a mbiri yabwino kusukulu. Chitsanzo china ncha Erika, wofalitsa wa zaka 11 wa ku Mexico. Iye waphunzitsidwa kukonda Yehova kuyambira paubwana. Amachita bwino kwambiri pantchito yake ya kusukulu. Imodzi ya ntchito zake inali kukonzekera nkhani yonena za AIDS ndi kumwerekera ndi fodya ndi moŵa. Anakonzekera bwino lomwe, akumagwiritsira ntchito magazini a Galamukani!, ndipo analandira magiredi apamwamba koposa. Mphunzitsi wake anamfunsa za kumene anapeza chidziŵitsocho ndipo iyeyo anapatsidwa magazini amene anali ndi nkhani zimenezo. Pambuyo pake, mphunzitsiyo anagwiritsira ntchito magazini ameneŵa kufotokozera nkhaniyo kalasi yake yonse. Chifukwa cha khalidwe la Erika, kulemekeza aphunzitsi ake, ndi magiredi ake apamwamba, iye wayenerera kulandira mphatso, madipuloma, ndi kulandira ndalama pang’ono zopititsira maphunziro patsogolo. Komabe, iye akulingalira kuti zipambano zake zazikulu koposa zakhala zakuti wadzidziŵikitsa monga mmodzi wa Mboni za Yehova, wakhoza kugaŵira mabuku ofotokoza Baibulo, ndipo wakwezetsa dzina la Mulungu.
Ndiyeno pali Shannon, mnyamata wazaka khumi amene amakhala ku New Zealand. Iye ali ndi diso limodzi lokha loona; lina linafa chifukwa cha kansa pamene anali kamwana. Pamene Shannon anali wazaka zisanu ndi ziŵiri amake anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Komabe, pasanapite nthaŵi yaitali atayamba kuphunzira Baibulo, iwo anayamba kukhala ndi mwamuna wina popanda ukwati ndipo anasankha kuleka kuphunzira kwawo. Shannon anachonderera kuti phunziro lake Labaibulo lipitirizebe. Pempho lakelo linavomerezedwa. Mbonizo zinapitirizabe kufika, ndipo potsirizira pake ziŵalo zonse zitatu za banjalo zinaphunzira Baibulo ndi kupita patsogolo mwauzimu. Atakwatirana mwalamulo, amake Shannon ndi atate wake omlera anabatizidwa.
Tsiku lina Shannon ndi mkazi wa woyang’anira dera anali muutumiki wakumunda. Mwininyumba wina anafunsa Shannon kuti: “Kodi nchiyani chimene chinachitikira diso lako?” “Linali ndi kansa, ndipo linachotsedwa,” iye anayankha motero. “Posachedwapa Yehova adzandipatsa latsopano m’Paradaiso, ndizo zimene tafikira pano kudzakuuzani.”