Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 3/1 tsamba 31
  • “Mulungu Alibe Tsankhu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mulungu Alibe Tsankhu”
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Chikondi Chigwirizanitsa Mabanja
    Nsanja ya Olonda—1989
  • “Wodala Ndiwopeza Nzeru”
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Nsanja ya Olonda—1994
w94 3/1 tsamba 31

Lipoti la Olengeza Ufumu

“Mulungu Alibe Tsankhu”

ZAKA mazana 19 zapitazo, mtumwi Petro wouziridwa, analemba kuti: “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Pakati pa Mboni za Yehova pali anthu ochokera m’mafuko onse ndi zipembedzo. Amafuna chilungamo, ndipo amawopa Mulungu. Yehova amawalandira onsewo m’chitaganya cha dziko latsopano, mwachitsanzo, monga momwe anachitira kwa mkazi wina ku Chad.

Mkaziyu anali wosakhutira ndi chipembedzo chake. Zaka zambiri pasadakhale anali atalandira kope la buku lakuti Your Youth​—Getting the Best Out Of It, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, ndipo anayamikira uphungu wabwino umene bukulo lili nawo. Phunziro la Baibulo linayambidwa, ndipo anali kukhala ndi phunziro nthaŵi zonse. Komabe, atalimbikitsidwa kupezeka pamisonkhano pa Nyumba Yaufumu, sanachitepo kanthu. Chifukwa? Ngakhale kuti mwamuna wake sanatsutse phunziro lake, anakana kumlola kupezeka pamisonkhano pa Nyumba Yaufumu.

Pamene mkaziyo anafuna kukapezeka pamsonkhano wadera, Mboni yochititsa phunzirolo inasonyeza mwamunayo programu, yosonyeza uphungu wabwino umene ukaperekedwa. Iye analola mkazi wake kupita “kamodzi kokha.” Mkaziyo anapezekapo ndipo anasangalala kwambiri ndi programuyo. Atafotokozera mwamuna wake zimene anaphunzira, iye sanamletse kupezeka pamisonkhano ina. Mkaziyo anachita chidwi kwambiri poona kuti mpingo unali ndi anthu ochokera m’mafuko osiyanasiyana amene anasamalirana kwambiri. Pambuyo pake anakapezeka pamsonkhano wachigawo ndipo anakondwera kwabasi kuona ana ake atakhala pamiyendo ya Mboni za kumaiko ena. Mbonizo zinadya chakudya ndi anawo, ndipo zinawatenga monga banja. Pamenepa panali posinthira pa mkaziyo.

Koma panatsatira chitsutso. Ngakhale kuti ngwachinthenthe mwachibadwa, mkaziyo anayamba kuyankha pamisonkhano ndi kupirira molimba mtima ndemanga zoipa zoperekedwa ndi achibale ake ndi anansi. Pamene kuli kwakuti anakhala ndi mwamuna wake kwazaka zambiri, ukwati wawo unali wongovomerezana mwamwambo popanda kulembetsedwa. Kodi akaitchula motani nkhani ya kukwatirana mwalamulo? Atapemphera mwakhama kwa Yehova, anauza mwamuna wake, yemwe anati akaipenda nkhaniyo. Pomalizira pake anatero, ndipo banjalo linakwatirana mwalamulo.

Mulamu wake wamkazi yemwe anali kukhala nawo anadzetsa mavuto ambiri, koma mwamuna wake anachirikiza mkazi wake. Ndiyeno atate a mwamuna anadzacheza. Iwo analamula mwana wawo kusudzula mkazi wake, popeza anali atasintha chipembedzo chake. Atatewo anauza mwana wawo kuti akamlipilira malowolo a “mkazi wina wabwino kwambiri.” Yankho la mwanayo linali lakuti: “Ayi, sindidzachita zimenezo. Iye ndimkazi wabwino. Nzosiyana ngati iye afuna kupita, koma ine sindidzamuuza kupita.” Mkaziyo anali waulemu kwambiri kwa apongozi ake, ndipo iwo anachita manyazi ndi khalidwe lawo. Komabe, atabwerera kumudzi kwawo, analembera mwana wawo, panthaŵiyi akumpatsa chosankha. Iwo anati ngati mwana wawo wakana kuthamangitsa mkazi wake, iye sanalinso mwana wawo. Panonso mwanayo anachirikiza mkazi wake. Talingalirani chimwemwe cha mkaziyo poona mwamuna wake akumchirikiza motsimikizirika.

Tsopano tiana tawo tatimuna tiŵiri timakonda kupita ndi amayi awo ku Nyumba Yaufumu. Ndipo tinapempha ngakhale mataye kwa atate wawo, popeza kuti tinaona kuti abale onse okamba nkhani anavala mataye. Lerolino mkazi ameneyu ndimlongo wobatizidwa.

Ali mmodzi wa Mboni zachimwemwe 345 m’Chad zimene zikulengeza mbiri yabwino ya Ufumu wa Yehova ndi kuzindikira kuti, ndithudi, “Mulungu alibe tsankhu.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena