Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 4/15 tsamba 3-4
  • Kodi Chitsogozo cha Anthu Chalephera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chitsogozo cha Anthu Chalephera?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Akapolo a Umphaŵi
    Galamukani!—1998
  • Kodi Nkuti Kumene Mungapeze Chitsogozo Chodalirika?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Zimene Ena Achita Pofuna Kuthetsa Umphawi
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kuyankha Mafunso a m’Baibulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 4/15 tsamba 3-4

Kodi Chitsogozo cha Anthu Chalephera?

KODI ndani amene analenga zinthu zonse? Ngati yankho lanu lili lakuti “Mulungu,” pamenepo mukugwirizana ndi mamiliyoni amene amakhulupirira mwa Mulungu wa Baibulo, Mlengi.

Komabe, ambiri amene amakhulupirira mwa Mulungu amavutika kuvomereza kuti iye ali wophatikizidwa mokangalika m’kuthetsa mavuto a anthu. Kodi nkwanzeru kuganiza kuti Mulungu akulinganiza makonzedwe amene adzadzetsa mpumulo kumtundu wa anthu? Ambiri samapeza umboni weniweni wakuti zimenezi zili choncho.

Kwazaka zikwi zambiri, anthu ayesa njira zambirimbiri za kudzithandiza pofufuza mayankho a mavuto, akumakankhira Mulungu pambali. Koma kodi anthu apeza mayankhowo? Kapena kodi mavutowo akukulirakulirabe mowonjezereka ndi kukhala ovuta kuwathetsa? Kodi ndimotani mmene anthu akusamalirira mavuto ofuna chithandizo cha mwamsanga m’dziko lerolino?

Katswiri wina wodziŵa zinthu akunena motere: “Chiyambire pa kuyambika kwa luso la Maindastale, maiko achuma awononga kwambiri zinthu zachilengedwe kupyolera m’njira zosatetezereka za kupanga zinthu ndi kugwiritsira ntchito, zikumawononga malo okhala apadziko, moika paupandu maiko omatukuka kumene.”

Anthu akupitirizabe kuwononga dziko lapansi. Nyuzipepala ina ya ku Argentina yotchedwa Clarín inapereka ndemanga yakuti: “M’theka lachiŵiri la zaka za zana lino, kusirira chuma, kusoŵeka kwa chenjezo, ndi kulekerera ndizo zinachititsa masoka aakulu amene sanangochititsa imfa za anthu komanso kuwononga malo okhala, kaŵirikaŵiri kufikira pamlingo waukulu kwambiri.”

Umphaŵi waukulu tsopano ukuonekera kukhala wachikhalire m’chitaganya chamakono. Ngakhale otchedwa maiko olemera a dzikoli akugonjera pavuto lalikulukulu la umphaŵi. Malinga ndi kunena kwa The Globe and Mail ya ku Toronto, Canada, kukuyerekezeredwa kuti “chigawo chimodzi mwa zitatu cha Akanada chidzaloŵa muumphaŵi chidakali ndi moyo wakuti chikhoza kugwira ntchito.” Nyuzipepalayo ikuwonjezera kuti “kusweka kwa mabanja kuli chifukwa chimodzi chochititsa umphaŵiwo, ndipo mkhalidwewo waŵirikiza kuchitika m’zaka zaposachedwapa.”

Kugwiritsira ntchito mankhwala molakwa kuli chizindikiro china cha kunyonyotsoka kwa chitaganya. Kodi anthu angachitenji pamenepa? Mwachionekere zochepa kwambiri. Mamiliyoni akupitirizabe kudwala mwakuthupi, mwamaganizo ndi mwamakhalidwe monga chotulukapo chachindunji cha kugwiritsira ntchito kwawo molakwa anamgoneka. Ndipo vutolo likufalikira konse mofulumira.

Asayansi akuonekera kukhala akulephera m’nkhondo yawo yolimbana ndi matenda. Zowonadi, luso la zopangapanga lamakono lapambana m’nkhondo zambiri. Komabe, njira zina zausayansi zenizenizo zachititsa kubuka kwa mtundu wina wowopsa wa tizilombo tosamva mankhwala.

Maboma a anthu sangaletse kuwanda kwa kuswedwa kwa zoyenera za munthu. Mwachitsanzo, mosasamala kanthu za malonjezo ndi malamulo olinganizidwa kuletsa ukapolo, kukuyerekezeredwa kuti kuzungulira dziko lonse anthu oposa mamiliyoni zana amaumirizidwa kugwira ntchito pansi pa mikhalidwe imene ili yaukapolo kotheratu.

Koma kodi nchifukwa ninji chitsogozo cha anthu chalephera? Lingalirani mfundo izi. Chitsogozo cha anthu chimachokera kwa anthu​—anthu amene akhoza kuchita zochepa kwambiri. Zokumana nazo za m’moyo nzochepa kwambiri ndipo kaŵirikaŵiri zimachepetsedwa ndi miyambo yakutiyakuti kapena malo okhala. Nachonso chidziŵitso chawo nchochepa. Chitsogozo chilichonse chimene angakhale nacho chimasonyeza kukhoza kwawo kuchita zochepa kumeneko. Monga momwe mtumwi Paulo ananenera, “onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.”​—Aroma 3:23.

Kwenikweni ochuluka a mavuto ndi zovuta zimene mbali yaikulu ya mtundu wa anthu ikukumana nazo ndizo zotulukapo zachindunji kapena zosakhala zachindunji za kunyalanyaza chitsogozo cha Mulungu. Komabe, kodi nkuti kumene chitsogozo chotero chingapezeke? Kodi ndimotani mmene Mulungu amatipatsira chitsogozo lerolino? Nkhani yotsatira idzapereka mayankho.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena