Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 7/1 tsamba 4-7
  • Tchalitchi Chogaŵanika Kodi Chingapulumuke?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tchalitchi Chogaŵanika Kodi Chingapulumuke?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Munthu Wosayeruzika”
  • Tirigu ndi Namsongole
  • Magaŵano Atsopano
  • “Tulukani Mmenemo, Anthu Anga”
  • Pali Mpingo Woona Umodzi Wokha Wachikristu
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Chikhristu Chili ndi Tsogolo Lotani?
    Galamukani!—2007
  • “Olungama Adzawala Ngwee Ngati Dzuwa”
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Fanizo la Tirigu ndi Namsongole
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 7/1 tsamba 4-7

Tchalitchi Chogaŵanika Kodi Chingapulumuke?

“ONSE amene amakhulupirira choonadi chopulumutsa cha Kristu ali mbali ya Tchalitchi chooneka. Magaŵano a Dziko Lachikristu​—pakati pa Kummaŵa ndi Kumadzulo, ndi pakati pa Roma ndi matchalitchi a Reformation​—ali magaŵano a mkati mwa Tchalitchi chimodzi.” (Christians in Communion) Mmenemo ndi mmene wolemba wina amaonera Chikristu​—monga banja lomwazikana kwambiri la zipembedzo, zonse zodzinenera kukhala ndi mtundu winawake wa chikhulupiriro mwa Yesu Kristu.

Komabe, lili banja logaŵanika, lokhala ndi zikhulupiriro ndi miyezo ya kakhalidwe yowombana. “Chikristu chamakono . . . chili ndi miyezo yotsika ya umembala wa tchalitchi kuposa ija yokwerera basi,” akutero wopenyerera wina. Pamenepo, kodi tiyenera kupima motani mkhalidwe wake wauzimu? Bishopu wa Katolika Basil Butler akuti: “Chikristu chogaŵanika nchodwala kwambiri.” (The Church and Unity) Kodi matendawo anayamba motani? Kodi pali chiyembekezo cha kuchira?

“Munthu Wosayeruzika”

Mtumwi Paulo anachenjeza kuti kusagwirizana kukabuka. Kwa Akristu a m’Tesalonika amene analingalira kuti kukhalapo kwa Kristu kunayandikira, iye analemba kuti: “Munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika [tsiku la Yehova], koma chiyambe chifike chipatukocho, navumbulutsike munthu wosayeruzika, mwana wa chiwonongeko.”​—2 Atesalonika 2:3.

“Munthu wosayeruzika” ameneyu anayambitsa mpatuko ndi chipanduko mumpingo Wachikristu. Kodi iye ndani? Osati munthu mmodzi wina aliyense koma, mmalomwake, kagulu ka atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu. Kagulu kameneka kanadzikweza pamwamba pa mpingo wopatuka pafupifupi mwamsanga pambuyo pa kufa kwa atumwi a Yesu, ndipo pomalizira pake kanafikira pakuphunzitsa nthanthi zachikunja, monga ngati Utatu ndi kusafa kwa moyo wa munthu. (Machitidwe 20:29, 30; 2 Petro 2:1-3) Mofanana ndi kachilombo kosaoneka kakupha, iko kanayambukira mpingo wodzinenera kukhala Wachikristu ndi malingaliro ouziridwa ndi ziŵanda amene akatsogolera mosapeŵeka ku kusagwirizana.​—Agalatiya 5:7-10.

Kuyambukira koipako kunali kutayamba kale m’tsiku la mtumwi Paulo. Iye analemba kuti: “Pakuti chinsinsi cha kusayeruzika chayambadi kuchita; chokhachi pali womletsa tsopano, kufikira akamchotsa pakati.” (2 Atesalonika 2:7) Atumwiwo anachita ngati oletsa poizoni ya mpatuko. Pamene chisonkhezero chawo chogwirizanitsa chinachotsedwa, mpatuko wosaletsedwawo unafalikira ngati chilonda chonyeka.​—1 Timoteo 4:1-3; 2 Timoteo 2:16-18.

Zochita za “munthu wosayeruzika” ameneyu zikupitiriza mosaletseka. M’lipoti laposachedwapa lonena za “tchalitchi chokhala m’chizunzo cha kugonana ndi zaumulungu,” dikoni wamkulu wina wa Church of England akugwidwa mawu kukhala akudandaula kuti: “Mapempho operekedwa kufunsira atsogoleri achipembedzo kusadziloŵetsa m’machitachita akugonana kunja kwa ukwati akutayidwa kunja. Ogonana ofanana ziŵalo amaikidwa pa udindo. Iwo apanga zabwino kukhala zoipa ndi zoipa kukhala zabwino.”​—The Sunday Times Magazine, London, November 22, 1992.

Tirigu ndi Namsongole

Yesu Kristu mwiniyo anaphunzitsa kuti Chikristu choona chikazimiririka kwa kanthaŵi. Iye anati kukhazikitsidwa kwa mpingo Wachikristu kunali ngati munthu amene anafesa mbewu zabwino m’munda mwake. Koma, Yesu anati, “mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu.” Pamene akapolo ake anafunsa ngati angayese kuzula namsongoleyo, mwini mundayo anati: “Iyayi, kuti kapena mmene mukasonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye.” Kodi kusanganikirana kwa tirigu ndi namsongole kumeneku kukapitiriza kwa utali wotani? Mwini wa mundayo anati: “Kazilekeni zonse ziŵiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa.”​—Mateyu 13:25, 29, 30.

Kufikira “pakututa,” kapena nthaŵi ya kulekanitsa mkati mwa masiku otsiriza a “dongosolo la zinthu,” Akristu onyengezera anakulira pamodzi ndi Akristu oona. (Mateyu 28:20, NW) Satana Mdyerekezi anagwiritsira ntchito ampatuko kupanga mpingo Wachikristu wonyengezera woipa ndi wogaŵanika. (Mateyu 13:36-39) Iwo anapanga chonyenga chochititsa manyazi cha Chikristu chenicheni. (2 Akorinto 11:3, 13-15; Akolose 2:8) Pamene tchalitchi chinanyonyotsoka m’kupita kwa zaka mazana, kunakhala kovuta kwambiri kudziŵa Akristu oona.

Magaŵano Atsopano

M’nthaŵi zamakono kwambiri, likutero The Testing of the Churches​—1932-1982, “magaŵano [atsopano] aonekera, makamaka m’magulu otengeka maganizo, ndi kugogomezera maganizo kwake pa chikhulupiriro ndi chidziŵitso.” Mokondweretsa, ena amaona magulu a obadwanso, otengeka maganizo kukhala zizindikiro za kuchira kwauzimu mmalo mwa kukhala magaŵano atsopano. Mwachitsanzo, Northern Ireland anakumana ndi kutsitsimula koteroko m’ma 1850. Ziyembekezo zazikulu zinadzutsidwa. Lipoti lina linanena za “kugwirizana kwaubale . . . pakati pa atumiki a Presbyterian, Wesleyan, ndi Independent” ndipo linanena kuti “tsiku lililonse linabweretsa mbiri zatsopano za atulo, kugona, masomphenya, maloto ndi zozizwitsa.”​—Religious Revivals.

Ambiri anaona zionetsero zamphamvu zimenezi kukhala umboni wa kugwira ntchito kwa mzimu wa Mulungu kutsitsimula tchalitchi chake. “Tchalitchi cha Mulungu,” anatero wopenyerera wina, “m’lingaliro lake lapamwamba kopambana chatsitsimulidwa m’zigawo zimenezi.” Komabe, ngakhale kuti kutsitsimula kumeneku kunalengezedwa kukhala “nyengo yaulemerero ndi yosayerekezeredwa m’mbiri yachipembedzo ya Ulster,” iko ndi kutsitsimula kwina kofanana nako sikunatulutse kugwirizana kwachipembedzo pakati pa awo amene anadzinenera kukhala atabadwanso mwauzimu.

Oterowo adzatsutsa kuti ali ogwirizana m’nkhani zazikulu. Koma chimenechi ndi chigomeko chimodzimodzi chimene chimagwiritsiridwa ntchito ndi Dziko Lachikristu lonse, limene limadzikhululukira kuti “zimene zimagwirizanitsa Akristu zili kale zofunika kwambiri kuposa nkhani zimene zimaŵagaŵanitsabe.” (The Church and Unity) Dziko Lachikristu limati: “Kugwirizana kwathu kwakukulu ndi wina ndi mnzake ndi Akristu anzathu onse nkozikidwa pa ubatizo wathu mwa Kristu.” (Christians in Communion) Komabe, kunena kuti magaŵano ali osadetsa nkhaŵa kwenikweni chifukwa cha chikhulupiriro chofala mwa Yesu, kuli kofanana ndi kunena kuti kansa sili yowopsa malinga ngati mtima wako uli wamphamvu.

Chenicheni nchakuti magulu achipembedzo amakono otero awonjezera chisokonezo ndi kuchititsa ulamuliro wankhalwe wauzimu pamene aphunzitsi oumirira adzisonkhanitsira otsatira. Jim Jones ndi David Koresh ali zitsanzo zaposachedwapa za atsogoleri auzimu amene anasokeretsa zikwi zambiri. (Mateyu 15:14) Mtumiki wina wa Baptist ali chiŵalo chotsogolera cha Ku Klux Klan. Iye amagwirizanitsa mkupiti wake wa upamwamba wa azungu ndi kutsitsimula kwachipembedzo ndi kunena kuti awo amene amatengamo mbali “adzapatsidwa mphamvu ya umulungu, adzapatsidwa kulimba mtima kwa Uyo amene anafa pa Kalvari [Yesu Kristu].”

Bwanji ponena za zonenedwa kuti zozizwitsazo, ntchito zamphamvu, ndi zizindikiro zochitidwa m’dzina la Yesu? Kumbukirani chenjezo lamphamvu la Yesu Kristu lakuti, si awo ongonena kuti “Ambuye, Ambuye” amene amalandira chivomerezo chake, koma, mmalomwake, ‘awo amene amachita chifuniro cha Atate wake.’ Ambiri lerolino samadziŵa konse ngakhale dzina la Atate wake, Yehova. Yesu anachenjeza za awo amene ‘akutulutsa mizimu yoipa m’dzina lake, ndi kuchita zamphamvu m’dzina limeneli’ ndipo komabe akakhala “akuchita kusayeruzika.”​—Mateyu 7:21-23.

“Tulukani Mmenemo, Anthu Anga”

Kodi chiyembekezo cha kuchira kwa Dziko Lachikristu lodwala nchotani? Choipa kwambiri. Pamenepo, kodi tiyenera kulandira uphungu wa bishopu wa Chikatolika Butler, wa “kugwirizana ndi [tchalitchi] popanda kukayikira ndi kupereka chithandizo chathu ku ‘kuyeretsedwa’ kwake kopitiriza mkati mwa maudindo ake”? Ayi! Dziko Lachikristu logaŵanika ndi logaŵanitsa silidzapulumuka. (Marko 3:24, 25) Ilo lili mbali ya ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga wotchedwa Babulo Wamkulu. (Chivumbulutso 18:2, 3) Dongosolo lachipembedzo la liwongo la mwazi limeneli likuyang’anizana ndi chiwonongeko chomayandikira pa dzanja la Mulungu.

Baibulo silimapereka lingaliro lakuti Akristu enieni akhale mkati mwa gulu lachipembedzo loipa limeneli ndi kuyesayesa kulisintha ali mkati. Mmalomwake, limafulumiza kuti: “Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake; pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira m’Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.”​—Chivumbulutso 18:4, 5.

‘Kutuluka’ kumka kuti? Kumbukirani, Yesu analonjeza kuti pa nthaŵi yakututa, Akristu oona akasonkhanitsidwanso pamodzi mu umodzi wapadziko lonse. Mneneri Mika ananeneratunso za kusonkhanitsidwanso kumeneko ndi mawu awa: “Ndidzawaika pamodzi . . . ngati zoŵeta pakati pa busa.” (Mika 2:12) Kodi zimenezi zachitika?

Inde! Akristu enieni akusonkhanitsidwa tsopano mu ubale wogwirizana padziko lonse lapansi. Kodi iwo ndani? Iwo ali mpingo Wachikristu wa Mboni za Yehova, umene umalengeza mogwirizana mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu m’maiko 231. Iwo akana ziphunzitso zogaŵanitsa za Dziko Lachikristu ndi kufunafuna kulambira Mulungu mogwirizana ndi choonadi cha Mawu ake.​—Yohane 8:31, 32; 17:17.

Mukupemphedwa mosangalala kulankhula nawo. Ngati mungakonde kudziŵa zambiri ponena za Mboni za Yehova, chonde zifikireni kwanuko kapena kupyolera m’keyala yoyenerera patsamba 2 la magazini ano.

[Chithunzi patsamba 7]

“Mulungu anakumbuka zosalungama zake”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena