Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 7/1 tsamba 3-4
  • Tchalitchi Chogaŵanika Kodi Mkhalidwewo Waipa Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tchalitchi Chogaŵanika Kodi Mkhalidwewo Waipa Motani?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Tchalitchi Nchogaŵanika Motani?
  • Miyezo Yapaŵiri
  • “Pasakhale Malekano Pakati pa Inu”
  • Kodi Nchifukwa Ninji Pali Kugaŵanikana?
    Galamukani!—1990
  • Tchalitchi Chogaŵanika Kodi Chingapulumuke?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Carici Coona ndi Maziko Ace
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
Nsanja ya Olonda—1994
w94 7/1 tsamba 3-4

Tchalitchi Chogaŵanika Kodi Mkhalidwewo Waipa Motani?

“MOFANANA ndi banja lalikulu lodabwitsidwa, lokhala m’nyumba yakale yopasuka imene khoma lake lakutsogolo lagwa mwadzidzidzi, pakuonekera kuti pali mkangano umene ukuchitika pafupifupi m’chipinda chilichonse​—malingaka akuimbidwa mwamphamvu ana a Yesu akukuŵira ogonana ofanana ziŵalo olemekezeka a Anglo-Catholic ovala masuti akuda a silika.”​—The Sunday Times, London, April 11, 1993.

Banja limeneli ndilo Church of England. Mkanganowo uli wonena za kuvomereza akazi kuloŵa unsembe. Malongosoledwe opereka chithunzithunzi a kusagwirizana kwakukuluwo amagwiranso ntchito ku Dziko Lachikristu lonse. Pokhala ndi atsogoleri a Orthodox Church ndi papa otsutsa chosankha cha kulola akazi kukhala ansembe, chotulukapo chonse, likutero lipoti lina, nchakuti “loto la kugwirizananso ndi Dziko Lachikristu lonse lili patali kwambiri koposa ndi kale lonse.”

Kodi Tchalitchi Nchogaŵanika Motani?

Monga momwe timaŵerengera pa Mateyu 7:21, Yesu Kristu ananena kuti ambiri akadzinenera kukhala ndi chikhulupiriro mwa iye monga Ambuye komabe nkulephera ‘kuchita chifuniro cha Atate wake.’ Magazini a Maclean’s akuti: “Oŵerenga a Mateyu ofunafuna chipulumutso angapatulidwe chifukwa cha msokonezo wonena za chimene kwenikweni chili chifuniro cha Mulungu, pamene Akristu, ndi matchalitchi awo, asiyana kwambiri motero pa funsolo.” Pambuyo pa kufunsa kochitidwa pakati pa anthu a ku Canada, iwo anati pali “kusiyana kwakukulu m’zikhulupiriro ndi zochita za Akristu a ku Canada​—kusiyana kokulirapo pakati pa ziŵalo za chipembedzo chilichonse, kwenikweni, kuposa kusiyana kwa pakati pa zipembedzo zenizenizo.”

Malinga ndi kufufuza kwake, 91 peresenti ya Akatolika imavomereza kugwiritsira ntchito njira zoletsa kutenga mimba zosakhala zachibadwa ngakhale kuti tchalitchi chawo chimatsutsa zimenezo; 78 peresenti imaganiza kuti akazi ayenera kuloledwa kukhala ansembe; ndipo 41 peresenti imavomereza kuchotsa mimba “m’mikhalidwe inayake.” Kusagwirizana mkati mwa zipembedzo zosiyanasiyana pa “mafunso ambiri azaumulungu,” ikutero Maclean’s, “kumagogomezera magaŵano amene akuchititsa kusweka kwa matchalitchi aakulu.”

Miyezo Yapaŵiri

Pali miyezo yapaŵiri limodzinso ndi miyezo yowombana ponena za makhalidwe. Ena amadzinenera kuti amachirikiza malamulo a mkhalidwe a Baibulo, koma ena amawanyoza. Mwachitsanzo, kodi phwando la “ukwati” lochitidwa kaamba ka akazi ogonana aŵiri mu Metropolitan Church of Toronto, linali logwirizana ndi chifuniro cha Mulungu? Mwachionekere otengamo mbaliwo anaganiza choncho. “Tikufuna kusangalalira chikondi chathu poyera ndi pamaso pa Mulungu,” iwo anatero.

Wolemba nkhani wina anafunsa kuti zinachitika motani kuti “akibishopu wa Katolika amene analandira madandaulo ambirimbiri, anasamutsira ansembe ogona ana ku gulu lina losiyana la anyamata otumikira pa guwa.” Wansembe Andrew Greeley akupereka lingaliro lakuti ansembe oyambira pa 2,000 kufika pa 4,000 angakhale atagonapo ana aang’ono okwanira 100,000, kaŵirikaŵiri mkhalidwewo ukumangolekereredwa.

Tchalitchi chosagwirizana chimatulutsa anthu osagwirizana. Ku Balkans, “Akristu” Achiserb ndi Achicroat amalingalira kuti Kristu ali nawo m’nkhondo yawo “yolungama.” Ambiri amavala mitanda munkhondo; kwasimbidwa kuti winawake, “nthaŵi zonse anaika mtanda wake m’kamwa mwake pamene kumenyanako kunaopsa kwambiri.”

“Pasakhale Malekano Pakati pa Inu”

Zoona, Baibulo limasiyira nkhani zina chikumbumtima, koma zimenezi siziyenera kusiya mpata wa kugaŵikana koteroko. Mtumwi Paulo akulongosola momvekera bwino kuti: “Munene [ndi kuchita] chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu.”​—1 Akorinto 1:10; Aefeso 4:15, 16.

Kupenda “Chikristu” moona mtima zaka pafupifupi zikwi ziŵiri pambuyo pa kulemba kwa mtumwi Paulo mawu amenewo kumadzutsa mafunso ena aakulu kwambiri. Kodi nchifukwa ninji “Akristu” ali ogaŵanika? Kodi tchalitchi chogaŵanika motero chingapulumuke? Kodi padzakhala konse Dziko Lachikristu logwirizana? Nkhani yotsatira idzapenda mafunso ameneŵa.

[Chithunzi patsamba 3]

Chionetsero cha ansembe chotsutsa kuchotsa mimba

[Mawu a Chithunzi]

Chikuto ndi pamwambapa: Eleftherios/​Sipa Press

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena