Msonkhano wa Pachaka
OCTOBER 1, 1994
MSONKHANO WA PACHAKA wa ziŵalo za Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania udzachitidwa pa October 1, 1994, pa Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova, 2932 Kennedy Boulevard, Jersey City, New Jersey. Kukumana koyambirira kwa ziŵalo zokhazokha kudzakhalako pa 9:30 a.m., motsatiridwa ndi msonkhano wa onse wa pachaka pa 10:00 a.m.
Ziŵalo za Bungweli ziyenera kudziŵitsa Ofesi ya Mlembi tsopano lino za kusintha kulikonse kwa makeyala awo a makalata mkati mwa chaka chapita kotero kuti makalata odziŵitsa anthaŵi zonse ndi mapepala a voti awapeze mkati mwa July.
Mapepala a voti, amene adzatumizidwa ku ziŵalozo limodzi ndi chidziŵitso cha msonkhano wa pachaka, ziyenera kubwezeredwa kotero kuti zifike ku Ofesi ya Mlembi wa Sosaite August 1 asanakwane. Chiŵalo chilichonse chiyenera kudzaza ndi kutumiza pepala lake la voti nthaŵi yomweyo, chikumafotokoza kaya ngati chidzapezeka pamsonkhanowo kapena ayi. Chidziŵitso choperekedwa pa pepala la voti lililonse chiyenera kukhala chotsimikizirika panthaŵiyi, popeza kuti chidzakhala chodziŵira amene adzapezekapo.
Kukuyembekezeredwa kuti programu yonse, kuphatikizapo msonkhano wa kayendetsedwe ka zinthu ndi malipoti, zidzamalizidwa pa 1:00 p.m. kapena kupitirira pang’ono pamenepo. Sipadzakhala programu yamasana. Chifukwa cha kuchepa kwa malo, okhala ndi matikiti okha ndiwo amene adzaloledwa kuloŵa. Sipadzapangidwa makonzedwe akugwirizanitsa matelefoni ndi nyumba zina zosonkhanira pa msonkhano wa pachaka.