Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 8/15 tsamba 30
  • Kodi Mukukumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukukumbukira?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Gawo 4: “Anthufe”
    Galamukani!—1990
  • Kodi Mwapeza Chipembedzo Cholondola?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Mtsogolo Mosungika Mmene Mungamupezere
    M’tsogolo Mosungika—M’mene Mungamupezere
  • Kodi Nyumba Yanu Iri Malo a Mpumulo ndi Mtendere?
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 8/15 tsamba 30

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawalingalira mosamalitsa makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Ngati mwatero, kukumbukira zotsatirazi kudzakusangalatsani:

▫ Kodi kusiyana kwakukulu pakati pa munthu ndi nyama nkotani?

Kusiyana kwakukuluko kuli pa kaumbidwe, kukhoza, ndi kugwira ntchito kwa ubongo. Munyama pafupifupi kugwira ntchito konse kwa ubongo, kumene kumatchedwa nzeru yoikidwiratu, nkolinganizidwiratu. Zimenezi nzosiyana ndi anthu. Mulungu anapatsa anthu nzeru ya kudzisankhira. (Miyambo 30:24-28)​—4/15, tsamba 5.

▫ Kodi kuimba kunali ndi mbali yotani m’kulambira kwa Aisrayeli pakachisi?

Nyimbo, makamaka oimba, anali ndi mbali yaikulu m’kulambira, osati kwenikweni kuti amveketse nkhani zofunika kwambiri za Chilamulo, koma kuti adzutse mzimu woyenerera wa kulambira. Kunathandiza Aisrayeli kulambira Yehova m’njira yosonkhezereka maganizo. (1 Mbiri 23:4, 5; 25:7)​—5/1, masamba 10, 11.

▫ Kodi ndi chisamaliro cha mtundu wotani chimene ana afunikira kuyambira ukhanda?

Makolo ayenera kupereka chisamaliro chosalekeza kwa khanda lobadwa kumene. Paulo analemba kuti: “Kuyambira ukhanda wako wadziŵa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso.” (2 Timoteo 3:15) Chotero chisamaliro chaukholo chimene Timoteo anachilandira, kuyambiradi paukhanda weniweni, chinalinso cha mtundu wauzimu.​—5/15, tsamba 11.

▫ Kodi ndi maumboni anayi ati amene amasonyeza kuti Baibulo lili ndi uthenga wa Mulungu kaamba ka mtundu wa anthu?

(1) Kupezeka kwake. Baibulo limapezeka kwa anthu pafupifupi 98 peresenti a padziko lonse. (2) Kuona kwa mbiri yake. Baibulo lili ndi zochitika zenizeni za m’mbiri, osati nthano zosatsimikizirika. (3) Kugwira kwake ntchito. Malamulo ndi miyezo yake zimasonyeza njira ya moyo imene imadzetsa mapindu kwa awo amene amazimamatira. (4) Ulosi. Ndilo buku limene limasimba mwatsatanetsatane zimene zidzachitika mtsogolo.​—6/1, masamba 8, 9.

▫ Kodi ndi thayo lotani limene kudziŵa chipembedzo cholondola kumadzetsa?

Titangodziŵa chipembedzo cholondola, tiyenera kuumba miyoyo yathu pa icho. Chili njira ya moyo. (Salmo 119:105; Yesaya 2:3)​—6/1, tsamba 13.

▫ Kodi nchifukwa ninji phunziro la Baibulo laumwini lili lofunika kwambiri?

Atumiki onse a Mulungu afunikira kupangitsa chisangalalo chawo ndi nyonga kukhalanso zatsopano tsiku ndi tsiku mwa kupeza mbali zatsopano kapena zakuya za choonadi cha Mawu a Mulungu. Mwa kutero amapitiriza kudzisonkhezera mwauzimu.​—6/15, tsamba 8.

▫ Kodi liwulo “uchimo” limatanthauzanji monga momwe lagwiritsiridwa ntchito m’Baibulo?

Kaŵirikaŵiri aneni a m’Chihebri ndi Chigiriki a mawu ogwiritsiridwa ntchito m’Baibulo kutchulira “uchimo” amatanthauza “kuphonya,” m’lingaliro la kuphonya kapena kusafika pa chonulirapo, chizindikiro, kapena chandamale. Anthu aŵiri oyambirira anapereŵera pa ulemerero wa Mulungu, akumaphonya chifuno cha kulengedwa kwawo m’chifanizo cha Mulungu. M’mawu ena, iwo anachimwa. (Genesis 2:17; 3:6)​—6/15, tsamba 12.

▫ Kodi nchifukwa ninji sikuli kwanzeru konse kuŵerenga mabuku ampatuko?

Mabuku ena ampatuko amafotokoza mabodza mwa “mawu osalaza” ndi “mawu onyenga.” (Aroma 16:17, 18; 2 Petro 2:3) Zolemba zonse za ampatuko zimangosuliza ndi kulefula. Palibe zimene zili zomangirira.​—7/1, tsamba 12.

▫ Kodi Girisi anali magwero a demokrase?

M’Girisi wakale, demokrase inali kuchitidwa m’zigawo zoŵerengeka chabe, ndipo ngakhale mmenemu nzika zachimuna zokha ndizo zinkachita chisankho. Zimenezi zinatanthauza kuti anayi a magawo asanu a anthu anasiyidwa. Umenewo sunali konse uchifumu wa ambiri kapena demokrase!​—7/1, tsamba 16.

▫ Kodi nchiyani chimene chimachititsa ukwati Wachikristu kupambana?

Pamene mwamuna ndi mkazi alemekeza lingaliro la Mulungu la ukwati ndi kuyesayesa kutsatira malamulo a mkhalidwe a Mawu ake. (Aefeso 5:21-33)​—7/15, tsamba 10.

▫ Kodi ndimotani mmene phunziro lanu la banja lingakhalire losangalatsa?

Yesani kuloŵetsamo ana onse. Khalani wotsimikiza ndi womangirira, mukumayamikira ana anu mwachikondi chifukwa cha kutengamo mbali kwawo. Musamangofola chabe nkhaniyo, koma yesani kufika mtima wa ana anu.​—7/15, tsamba 18.

▫ Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa ndi mawu akuti: “Pamene angonena, Mtendere ndi [chisungiko, NW]”? (1 Atesalonika 5:3)

Onani kuti Baibulo silimanena kuti mitundu idzadzipezera “mtendere ndi chisungiko.” Koma idzakhala ikulankhula za izo m’njira yapadera, ikumasonyeza chiyembekezo ndi chikhutiro chimene sichinamvedwe papitapo. Mipata yopezera mtendere ndi chisungiko idzaonekera kukhala ili pafupi kwambiri koposa ndi kale lonse.​—8/1, tsamba 6.

▫ Tchulani njira zitatu zimene Yehova amasonyezera kulolera.

Yehova wasonyeza kukhala kwake wofunitsitsa kukhululukira. (Salmo 86:5) Iye wakhala wofunitsitsa kusintha njira yake ya kachitidwe pamene mikhalidwe yatsopano yabuka. (Onani Yona, chaputala 3.) Ndiponso, Yehova wadzisonyeza kukhala wololera pochita ulamuliro wake. (1 Mafumu 22:19-22)​—8/1, masamba 12-14.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena