OLENGEZA UFUMU AKUSIMBA
Mawu a Mulungu Ali ndi Mphamvu
“MAWU a Mulungu ngamoyo ndipo ali ndi mphamvu.” (Ahebri 4:12, NW) Mawu ameneŵa akhala oona nthaŵi zambiri pamene anthu amene anyengedwa ndi chipembedzo chonyenga asonyezedwa choonadi cha Baibulo. Monga momwe chokumana nacho chotsatira cha ku Dominican Republic chikusonyezera, mphamvu ya Baibulo ingasinthe miyoyo ya anthu ndi kuwapatsa chiyembekezo.
Mboni za Yehova zinachezera mkazi wina wotchuka Wachikatolika amene anali atangotayikidwa kumene ana aang’ono aŵiri mu imfa. Anali wachisoni ndipo anadandaula za tsoka lake masiku onse. Mbonizo zinamsonyeza zimene Baibulo limanena pa Yohane 5:28, 29 ponena za chiyembekezo cha chiukiriro. Pambuyo pa makambitsirano owonjezereka ndi Mbonizo, mkaziyo sanangopeza chitonthozo m’chiyembekezo cha chiukiriro koma anazindikiranso kuti atsogoleri ake achipembedzo Achikatolika anali kumnyengeza.
Iye sanazengereze kuchoka m’Tchalitchi cha Katolika, ndipo anavomera kuchititsidwa phunziro la Baibulo lokhazikika ndi Mboni za Yehova. Komabe, mwamuna wake sanagwirizane ndi malingaliro ake. Popeza kuti nayenso anali Mkatolika wotchuka, analinganiza kuti mabwenzi ake andale ndi achipembedzo omveka aonane ndi mkazi wake poyesa kumletsa kutsatira njira yake ndi kumbwezera m’Chikatolika. Pambuyo pake iye anamuwopseza kuti akamsudzula, panthaŵi ina akumadziŵitsa ngakhale achibale ake ndi ziŵalo zinzake za tchalitchi kuti akasudzulana.
Koma machenjero ake sanaphule kanthu. Mosiyana ndi zimenezo, mkaziyo anatsimikiza mtima kwambiri kupitiriza maphunziro ake a Baibulo. Chifukwa cha kukula kwake kwauzimu ndi kukulitsa kwake mikhalidwe yabwino Yachikristu, mwamunayo anasankha kukhalabe naye mmalo mwa kumsudzula. Tsiku lina anavomeradi kupenda mabuku a Baibulo amene mkaziyo anali kuphunzira—koma kudalira pachinthu chimodzi. Iye anafuna kugwiritsira ntchito Baibulo lake la matembenuzidwe Achikatolika.
Iye anadabwa kuti, mothandizidwa ndi mabuku a Mboni za Yehova, anayamba kudziŵa zinthu zatsopano kuchokera m’Baibulo lake lenilenilo. Anazindikira kuti mkazi wake anasankha njira yolondola, ndipo posapita nthaŵi anali wokonzekera kutsanzira chitsanzo chake. Ndithudi, anaona kufunika kwa kupanga masinthidwe m’moyo wake weniweniwo. Vuto lalikulu limodzi limene anali nalo linali la kusiya chizoloŵezi chake cha ndudu. Ataŵerenga kope la magazini a Galamukani! la July 8, 1989, lokhala ndi mutu wapachikuto wakuti “Imfa Yogulitsa—Njira Khumi Zolekera Kusuta,” anatsimikiza mtima kusiya chizoloŵezi chotsutsana ndi malemba chimenechi. Mmalo mwa paketi yachizoloŵezi ya fodya imene kaŵirikaŵiri inkapezeka m’thumba mwake, iye anayamba kunyamula kope limenelo la Galamukani! Panthaŵi iliyonse imene anali ndi chilakolako cha kusuta fodya, anaŵerenga nkhani zonena za kusuta fodya. Njirayo inagwira ntchito! Pambuyo poŵerenga nkhanizo nthaŵi zambiri, anakhoza kusiya kusuta fodya.
Lerolino onse aŵiri mwamuna ndi mkazi wakeyo akutumikira Yehova monga atumiki obatizidwa. Pamene mikhalidwe ilola, mwamunayo amatumikira monga mtumiki wanthaŵi yonse, akumapatulira nthaŵi yake yochuluka pa kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu, ndipo akutumikira monga mtumiki wotumikira mumpingo wakwawo wa Mboni za Yehova. Iye ndi mkazi wake akuyembekezera chiukiriro pamene adzalandira ana awo amoyo m’dziko latsopano. Inde, Mawu a Mulungu, Baibulo, ngamoyo ndipo ali ndi mphamvu!