Chiŵalo China cha Bungwe Lolamulira
NDI cholinga cha kuwonjezera antchito m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, kuyambira pa July 1, 1994, chiŵalo china chawonjezedwa pa akulu 11 amene akutumikira tsopano lino. Chiŵalo chatsopanocho ndiye Gerrit Lösch.
Mbale Lösch analoŵa utumiki wanthaŵi yonse pa November 1, 1961, namaliza maphunziro m’kalasi ya 41 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower. Anatumikira m’ntchito yadera ndi ya chigawo ku Austria kuyambira 1963 mpaka 1976. Anakwatira mu 1967, ndipo iye ndi mkazi wake, Merete, pambuyo pake anatumikira kwa zaka 14 monga ziŵalo za banja la Beteli la ku Austria ku Vienna. Zaka zinayi zapitazo iwo anasamutsidwira ku malikulu a Sosaite ku Brooklyn, New York, kumene Mbale Lösch wakhala akutumikira m’Maofesi Oyang’anira ndipo monga wothandiza Komiti Yautumiki. Chifukwa cha kuzoloŵera kwake kwambiri munda wa ku Ulaya ndi kudziŵa kwake Chijeremani, Chingelezi, Chiromaniya, ndi Chitaliyana, iye adzathandiza kwambiri pantchito ya Bungwe Lolamulira.