Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 12/1 tsamba 20-24
  • Njira ya Moyo ya Chifuno

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira ya Moyo ya Chifuno
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Gawo Langa la Moyo Wonse
  • Maseŵero Anakhala Moyo Wanga
  • Chifuno Chosiyana ndi cha Maseŵero
  • Kuchita Mogwirizana ndi Zotsimikiza Mtima
  • Utumiki pa Nthambi
  • Moyo Wachifuno Upitirizabe
  • Kodi Ntchito Iyi Ingakhale Yabwino Kwambiri kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Mukuitanidwa!
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Tinkachitira Zinthu Limodzi
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kupenya ndi Chiyamikiro pa “Nyumba ya Mulungu”
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 12/1 tsamba 20-24

Njira ya Moyo ya Chifuno

YOSIMBIDWA NDI MELVA A. WIELAND

M’March 1940, miyezi yoŵerengeka nditabatizidwa, mng’ono wanga Phyllis anadza kwa ine nandifunsa kuti: “Kodi ukulekeranji kuchita upainiya?” “Kuchita upainiya?” ndinafunsa motero. “Kodi ukutanthauza za kulalikira kwanthaŵi yonse, pafupifupi tsiku lililonse?”

‘KODI ndingakhale bwanji mpainiya,’ ndinaganiza motero, ‘ndi chidziŵitso changa chochepa cha Baibulo ndiponso ndi ndalama zochepa kubanki?’ Komabe, funso la Phyllis linandiyambitsa kuganiza. Ndinapemphereranso zimenezo kwambiri.

Potsirizira pake ndinaganiza kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji sindingathe kukhulupirira Mulungu pamene akutilonjeza kutisamalira ngati tifuna Ufumu wake choyamba?’ (Mateyu 6:33) Chotero mu June 1940, ndinapereka chidziŵitso cha kuleka ntchito yanga yosoka madiresi. Ndiyeno ndinalembera ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society ku Australia, ndikumapempha gawo laupainiya.

Gawo Langa la Moyo Wonse

Milungu ingapo pambuyo pake, ndinalandira yankho, londidziŵitsa kuti ndidzapatsidwa gawo nditachoka kumsonkhano wachigawo umene unayembekezeredwa kuchitikira pabwalo la malikulu a Mboni za Yehova mu Strathfield, mlaga wa mzinda waukulu koposa wa Australia, Sydney. Mmaŵa msonkhano utatha, ndinafika ku ofesi kukapatsidwa gawo langa.

Munthu amene anali mu ofesi anafotokoza kuti: “Pakali pano tili otanganitsidwa kwambiri m’chipinda chochapira zovala. Kodi ungakonde kukhala kuno kwa milungu ingapo ndi kuthandiza?” Mmenemo munali mu August 1940​—ndipo ndidakali kugwirabe ntchito m’chipinda chochapira zovala! Panthaŵiyo munali anthu 35 okha m’banja la malikululo; tsopano muli 276.

Koma inu mungadabwe chifukwa chake ndimalingalira kugwira ntchito m’chipinda chochapira zovala kukhala “njira ya moyo ya chifuno,” makamaka popeza kuti imeneyi yakhala ntchito yanga kwa zaka zoposa 50 tsopano. Ndisanafotokoze chifukwa chake, ndiloleni ndikuuzeni zimene ndinali kulondola poyamba.

Maseŵero Anakhala Moyo Wanga

Ndinabadwira mu Melbourne pa January 1, 1914, wachisamba wa ana asanu. Tinali ndi makolo achikondi amene anakhala ndi moyo mogwirizana ndi malamulo amkhalidwe abwino olemekezeka ndi kupereka chilango pamene chinafunikira. Tinalinso ndi chimene chingatchedwe kuti kuleredwa wamba kwachipembedzo, popeza kuti makolo athu sanali anthu opita kutchalitchi. Komabe, iwo anaumirira kuti anafe tidzifika pa makalasi a Sande sukulu ya Church of England.

Pamene ndinasiya sukulu mu 1928 ndi kuyamba kugwira ntchito monga wosoka madiresi, ndinasankha zothera nthaŵi yanga yochuluka yosanguluka pa kuseŵera maseŵero, ndikumakhulupirira kuti zimenezi zingandithandize kuthetsa manyazi anga. Ndinaloŵa m’kalabu ya tenesi ndi kuseŵera chaka chonse. M’nyengo yozizira ndinaseŵeranso basketball ndi baseball, ndipo m’nyengo yotentha ndinaseŵera m’timu ya akazi ya cricket. Kuseŵera cricket ndinakukondadi, ndipo ndinayesetsa kuwongolera luso langa monga woseŵera mpirawo mwaliŵiro kuti ndisankhidwe m’timu yoseŵera ndi matimu ena a m’maboma osiyanasiyana.

Chifuno Chosiyana ndi cha Maseŵero

Poyambirira m’moyo ndinavutika maganizo ndi chiphunzitso chakuti Mulungu wachikondi anali ndi malo otchedwa helo kumene awo amene anachita zinthu zoipa akazunzidwa kosatha. Zimenezi sizinamveke kukhala zanzeru kwa ine. Chotero tangolingalirani kukondwa kwanga pamene mosayembekezereka ndinadziŵa kuchokera m’Baibulo tanthauzo lenileni la “helo.” Zinachitika motere:

Mng’ono wanga Phyllis, amene ndili wosiyana naye ndi zaka zisanu zakubadwa, ankakonda kwambirinso maseŵero, ndipo tinali m’timu imodzi ya cricket ya akazi. Mu 1936 mnzathu wina wa m’timu anadziŵanitsa Phyllis ndi mnyamata wina wotchedwa Jim amene ankadziŵika kukhala wachipembedzo kwambiri. Posapita nthaŵi Jim anayamba kulankhula kwa Phyllis za ziphunzitso za Baibulo. Iye anachita chidwi. “Nzanzeru kwambiri ndiponso zabwino,” Phyllis ankandiuza motero.

Panthaŵiyo Phyllis ndi ine tinkagona m’chipinda chimodzi kunyumba, ndipo iye anayesetsa kusonkhezera chikondwerero changa m’zimene Jim anali kumuuza ponena za Ufumu wa Mulungu. “Udzachita zimene maboma a anthu alephera kuchita,” iyeyo ankandiuza choncho mokondwa. Komabe, ndinkatsutsana naye, ndikumanena kuti chimenechi changokhala chipembedzo china chotisokoneza maganizo ndi kuti palibe aliyense amene amadziŵa kwenikweni zamtsogolo. Koma Phyllis anali wosatopa ndipo anasiya mabuku paliponse m’chipindamo, akumayembekezera kuti mwina ndingawaŵerenge.

Ndinali ndi chidwi cha kufuna kudziŵa chifukwa chake Phyllis anali wotenthedwa maganizo chotero ndi chiphunzitso chatsopano chimenechi, chotero tsiku lina ndinatenga kabuku kena. Kanali ndi mutu woyambitsa chidwi wakuti Hereafter. Chidwi changa chinasonkhezereka pamene ndinali kutsegula masamba ake ndi kuona liwulo “helo.” Ndinadabwa kuona kuti liwu la Baibulo limenelo “helo” kwenikweni limatanthauza manda wamba a mtundu wa anthu ndi kuti anthu abwino ndi oipa omwe amapita kumeneko. Ndinadziŵanso kuti helo sali malo achizunzo; akufa sadziŵa kanthu ndipo sangamve chilichonse.​—Mlaliki 9:5, 10; Salmo 146:3, 4.

Zimenezi zinamveka kukhala zanzeru kwa ine, makamaka pamene kabukuko kanafotokoza kuti Mulungu wachikondi ndi wamphamvu walonjeza kuutsa akufa mwa chozizwitsa chotchedwa chiukiriro. (Yohane 5:28, 29) Tsopano nanenso ndinafuna kudziŵa zinthu zambiri zimene Jim anali kuuza Phyllis. Ndinapeza kabaibulo kakang’ono ka King James Version kamene atate anandipatsa pamene ndinali mwana ndi kuŵerenga malemba oikidwa m’kabukuko. Zimenezi zinatsimikiziritsa zimene zinanenedwa ponena za helo ndi mkhalidwe wa akufa.

Chinthu china chokondweretsa ndi chodabwitsa kwa ine chinali kudziŵa kuti Mulungu ali ndi dzina laumwini, Yehova. (Salmo 83:18) Ndinathanso kuona kuti Mulungu anali ndi chifuno kapena chifukwa cha zinthu zonse zimene anachita kapena analola kuchitika. Zimenezi zinandichititsa kudzifunsa kuti, ‘Kodi kwenikweni nchiyani chimene chili chifuno changa m’moyo?’ Kuyambira pamenepo kumka mtsogolo ndinayamba kudabwa ngati kunali kwabwino koposa kwa ine kuona maseŵero mwamphamvu​—pafupifupi kukankhira chinthu chilichonse pambali.

Kuchita Mogwirizana ndi Zotsimikiza Mtima

Jim ndi Phyllis sanadziŵe mpang’ono pomwe kuti lingaliro langa la moyo linasintha, komano anadzadziŵa pamene banja lathu linaitanidwa kuphwando la bwenzi lina. M’masiku amenewo panthaŵi zotero onse amene analipo ankaimirira, ndipo wina ankachita toast yolemekeza Mfumu ya England, ndipo onse ankatukulira m’mwamba matambula awo ndi kuyamba kumwera toast imeneyo. Komabe, ndinasankha kukhalabe pansi ndi Jim ndi Phyllis. Iwo sanakhulupirire zimene anaona pamene anandiona ndili chikhalire! Zoonadi, sikuti ife tinali kusonyeza chipongwe, koma monga Akristu tinalingalira kuti tiyenera kukhala auchete ndi kusakhala ndi phande m’miyambo yautundu yotero.​—Yohane 17:16.

Komabe, makolo anga ndi banja lonse anawopsedwa. Iwo anati tinali osakhulupirika, kapena osokonezeka maganizo​—kapena zonse zimene! Ndiyeno pamene Phyllis ndi ine tinali pa mwambo wa kupereka mphotho wachaka ndi chaka wa timu ya cricket ya akazi, chinthu chofananacho chinachitika mkati mwa mwambo wautundu. Chotulukapo chake chinali chakuti aŵiri tonsefe tinatuluka m’timuyo. Zimenezi sizinali zovuta monga momwe ndinalingalirira, pakuti ndinafikira pa kuzindikira kuti kukhulupirika kwanga kunali kwa Kristu Yesu, Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu.

Tsopano Phyllis anandisonyeza kuti ndifunikira kufika pamisonkhano ya Mboni za Yehova mokhazikika kuti ndikulitse chikhulupiriro changa ndi chidziŵitso chowonjezereka cha Baibulo. Panthaŵiyo mu Melbourne munali mpingo umodzi wokha, chotero ndinayamba kufika pamisonkhano kumeneko Sande lililonse masana. Posapita nthaŵi ndinakhutiritsidwa maganizo kuti limeneli linali gulu la Mulungu loona la padziko lapansi.

Posapita nthaŵi ndinapemphedwa kukhala ndi phande mu ntchito ya mpingo ya kulalikira kukhomo ndi khomo. Poyamba ndinali wokayikira, komano tsiku lina pa Sande mmaŵa ndinasankha kumka nawo kungoti ndikaone mmene inkachitidwira. Ndinali wokondwa pamene ndinagaŵiridwa kutsagana ndi Mboni ina yodziŵa bwino imene inalankhula mwachidaliro pakhomo loyamba ndi kulandiridwa mwansangala ndi mwininyumba. Ndinalingalira kuti, ‘Aha, zimene zija nzosavuta kwambiri, komano ndidzafunikira kuyeseza kwambiri ndisanayambe kuchita bwino chonchija.’ Chotero tangoganizani mmene ndinadabwira pamene, titangochoka pa khomo loyambalo, Mboniyo inati kwa ine, “Tsopano ungathe kupita kukalalikira wekha.”

“Ndekha?” ndinafunsa motero, ndili kakasi! “Ayi simukunenetsa! Kodi ndikati bwanji ngati munthu akandifunsa funso limene sindikudziŵa yankho lake?” Koma wofalitsa mnzangayo anaumirirabe. Chotero, ndikunjenjemeradi, ndinapita kukalalikira ndekhandekha, pamene iyeyo anali kupitiriza kuchitira umboni kwa anthu kutsidya lina la msewu. Komabe ndinayesayesabe mmaŵa woyamba umenewo.

Kuyambira pamenepo kumka mtsogolo ndinayamba kukhala ndi phande mu ntchito yolalikira mmaŵa uliwonse pa Sande. Pamene munthu anandifunsa funso limene sindinathe kuyankha pakhomo, ndinkanena kuti, “Ndikalifufuza ndipo ndidzabweranso kudzaonana nanu.” Ayi, Yehova anapitirizabe kundipatsa nyonga ndi chilimbikitso cha kupitirizabe ndi moyo wanga watsopano wachifuno. Ndinapatulira moyo wanga kwa iye, ndipo mu October 1939, ndinabatizidwa pa dziŵe losambira la mzinda wa Melbourne. Posakhalitsa Phyllis, amene panthaŵiyo anali atakwatirana ndi Jim, anafunsa chifukwa chake sindinayambe upainiya.

Utumiki pa Nthambi

Mu January 1941, nditangoyamba kumene kugwira ntchito pa Beteli, monga momwe timatchulira ofesi ya nthambi, ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa mu Australia. Pambuyo pake asilikali ankhondo analanda Nyumba yathu ya Beteli ku Strathfield, ndipo ndinatumizidwa ku famu ya Sosaite ku Ingleburn, pafupifupi makilomita 48 kunja kwa mzindawo. Mu June 1943 bwalo la milandu linachotsera mlandu Watch Tower Society ndi kuchotsa chiletso. Podzafika mapeto a chaka chimenecho, 25 a ife tinaitanidwanso ku Beteli ya Strathfield. Kumeneko ndinapitiriza kugwira ntchito m’chipinda chochapira, ndiponso kugwira nawo ntchito zina za panyumbapo.

Zaka khumi zotsatirapo zinaonekera kukhala zikupyola mofulumira. Ndiyeno mu 1956, ndinakwatiwa ndi wa ntchito mnzanga wa pa Beteli, Ted Wieland. Ted anali mwamuna wofatsa kwambiri, woleza mtima, ndipo tinali okondwa pamene tinalandira chivomerezo cha kupitirizabe kukhala pa Beteli monga mwamuna ndi mkazi. Tonsefe tinasamalira kwambiri moyo wathu wachifuno, tili achimwemwe chifukwa cha mwaŵi wa kutumikira pa nthambi ya Australia. Ndithudi, kuwonjezera pa ntchito yathu ya pa Beteli, tinali ndi chisangalalo cha kugwira ntchito pamodzi kuthandiza ena kukhala ophunzira a Kristu. Monga chitsanzo chimodzi, mungaŵerenge za banja la a Weekes m’kope la Awake! la October 22, 1993.

Kukula kosalekeza kwa kulalikira Ufumu kunafunikiritsa kuwonjezeredwa kwa anthu 10 kapena 12 okha pa gulu lathu la antchito mkati mwa zaka zanga 30 zoyamba za pa Beteli. Komano mkhalidwewo unasintha mofulumira m’ma 1970 pamene tinayamba kusindikiza magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! konkuno. Ntchito yomanga fakitale yatsopano yosindikizira inayamba mu January 1972. Posapita nthaŵi makina osindikizira a matani 40 anafika kuchokera ku Japan, ndipo podzafika 1973 tinali kusindikiza pafupifupi magazini 700,000 pamwezi. Tsopano banja lathu la Beteli linayambadi kukula.

Ma 1970 anadzetsanso chisoni kwa ine. Choyamba, mwamuna wanga wokondedwa, Ted, anamwalira mu 1975 pausinkhu wazaka 80. Ndiyeno, chosakwanira chaka pambuyo pake, atate wanga okalamba nawonso anagona m’tulo ta imfa. Ndinapeza chitonthozo chachikulu kwa Yehova ndi Mawu ake, Baibulo, ndi kwa abale ndi alongo anga auzimu. Kukhala wotanganitsidwa pa Beteli ndi ntchito yanga ya chifuno mkati mwa nthaŵi yachisoni imeneyi m’moyo wanga kunandithandizanso kwambiri.

Komabe, moyo umapitirizabe, ndipo kachiŵirinso ndinayamba kukhala ndi chikhutiro ndi madalitso, tsopano monga mkazi wamasiye. Mu 1978, ndinafika pamsonkhano wachigawo mu London, England, ndipo pambuyo pake ndinapita kukaona malikulu apadziko lonse a Watch Tower Society ku Brooklyn, New York. Kuona abale ndi alongo anga mazana akumagwira ntchito mwachimwemwe kumeneko ku Beteli ya Brooklyn kwakhala kosonkhezera kwa ine kufikira lerolino.

Pamene ma 1970 anafika kumapeto, tinamva kuti chifutukuko chowonjezereka chinali kulinganizidwa pa nyumba ya Beteli ya Australia. Komabe, chifutukukocho sichinali kudzachitikira ku Strathfield, kumene tinali ochepekeredwa ndi malo. M’malo mwake, nyumba yaikulu yatsopanoyo inayembekezeredwa kukamangidwa pa malo athu a ku Ingleburn, kumene ndinagwirako ntchito mkati mwa chiletso kuchiyambiyambi kwa ma 1940.

Moyo Wachifuno Upitirizabe

Panali chisangalalo chotani nanga mu January wa 1982 pamene tinasamukira kumalo athu atsopanowo! Zoonadi, poyamba panali chisoni pang’ono chifukwa cha kusiya malo ozoloŵereka, koma posapita nthaŵi tinakondwera ndi malo athu atsopano a zipinda zogona 73 zabwino kwambiri. Tsopano mmalo mwa kuona makoma anjerwa ndi misewu ya m’milaga, timaona minda yobiriŵira ndi mitengo, ng’ombe zikumadya msipu, ndi kutuluka ndi kuloŵa kwa dzuŵa kokongola​—mkhalidwe wosangalatsa kopambana.

Pa March 19, 1983, tinali ndi kupatuliridwa kokondweretsa kwa nyumba zatsopanozo m’nyengo yabwino kwambiri yotentha ya dzuŵa. Lloyd Barry wa Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anapereka nkhani yopatulira yosonkhezera mtima kwambiri. Ineyo pandekha ndinayamikira kukhala naye ndi mkazi wake pa programu ya kupatulirayo, popeza kuti ndidagwirapo nawo ntchito ku Beteli ya Strathfield pamene tonsefe tinali ocheperapo.

Kukula kwa ntchito yolalikira Ufumu komapitirizabe kunafunikiritsa chifutukuko chinanso cha malo athu kuno ku Ingleburn. Mu 1987 ofesi inakulitsidwa. Ndiyeno, pa November 25, 1989, nyumba yokhalamo ya zipinda zosanja zisanu ndi fakitale yatsopano ya zipinda zosanja zitatu yowonjezeredwa zinapatuliridwa. Ha, tawonjezereka chotani nanga​—kuyambira pa osafikira pa atumiki 4,000 mu Australia pamene ndiyanamba utumiki wanga kufikira pa 59,000!

Posachedwapa nthambi ya Australia yapangidwa kukhala imodzi ya maofesi atatu a Sosaite a Regional Engineering Office, limodzi ndi Japan ndi Germany. Zimenezi zapangitsa kukhala koyenera kuwonjezeradi nyumba ya Beteli. Ofesi ina ya zipinda zitatu zosanja tsopano yatha, ndipo ntchito yomanga nyumba yokhala ya zipinda zosanja zisanu ili pafupi kutha, imene idzakhala ndi zipinda zinanso 80 zokhalamo banja lathu lomakula mosalekeza.

Tili ndi gulu lalikulu la ogwira ntchito m’chipinda chochapira, koma kaŵirikaŵiri ndimakumbukira tsiku la August limenelo mu 1940 pamene ndinapemphedwa kudzathandiza m’dipatimenti imeneyi kwa milungu iŵiri. Ndikuyamikira kwambiri kuti milungu iŵiri imeneyo yatalika kufikira ku zaka zoposa 50 ndi kuti Yehova Mulungu anatsogoza mapazi anga kumka kumoyo wachifuno wotero.

[Chithunzi patsamba 21]

Pamene ndinali ndi zaka 25

[Chithunzi patsamba 23]

Tsiku lathu la phwando laukwati mu 1956

[Zithunzi patsamba 24]

Mu 1938 mng’ono wanga ndi ine tinali omwerekera kwambiri m’maseŵero, koma tsopano moyo wanga ngwopindulitsa kwambiri

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena