Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 12/1 tsamba 19
  • Mmene Ena Amapatsira Zopereka ku Ntchito Yolalikira Ufumu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Ena Amapatsira Zopereka ku Ntchito Yolalikira Ufumu
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Nkhani Yofanana
  • “Kodi Ndalamazo Zimachokera Kuti?”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kodi Mumasangalala ndi “Mwayi Wopereka Nawo Mphatso Zachifundo”?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Mpatsi wa “Mphatso Iliyonse Yabwino”
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kupereka Mokondwera Kuchokera Pansi pa Mtima
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 12/1 tsamba 19

Mmene Ena Amapatsira Zopereka ku Ntchito Yolalikira Ufumu

◻ ZOPEREKA ZA NTCHITO YAPADZIKO LONSE: Ambiri amaika pambali kapena kulinganiza ndalama zimene amaika m’mabokosi azopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Ntchito Yapadziko Lonse ya Sosaite​—Mateyu 24:14.” Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalamazi ku malikulu a dziko lonse ku Brooklyn, New York, kapena ku ofesi yanthambi yapafupi.

◻ MPHATSO: Zopereka zodzifunira za ndalama zingatumizidwe mwachindunji ku Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, 25 Columbia Heights, Brooklyn, New York 11201-2483, kapena ku ofesi ya Sosaite ya nthambi yakwanuko. Zokongoletsa kapena zinthu zina zamtengo wapatali zingaperekedwenso. Kalata yachidule yofotokoza kuti zimenezo zaperekedwa monga mphatso iyenera kutsagana ndi zoperekazo.

◻ CHOPEREKA CHOTCHEDWA CONDITIONAL-DONATION: Ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society kuti ziyikiziridwe kumeneko kufikira imfa ya woperekayo, limodzi ndi makonzedwe akuti ngati pakhala kusoŵa kwaumwini, zidzabwezeredwa kwa woperekayo.

◻ INSHUWALANSI: Watch Tower Society ingalembetsedwe kuti ndiyo idzapatsidwa mapindu a inshuwalansi kapena penshoni. Sosaite iyenera kuuzidwa za makonzedwe alionse otero.

◻ MAAKAUNTI A KU BANKI: Maakaunti a banki, zikalata zoikizira ndalama, kapena maakaunti a anthu opuma pantchito angalembedwe moikizira ku Watch Tower Society kapena kulembedwa kuti wolipiridwa pambuyo pa imfa akhale Watch Tower Society, mogwirizana ndi malamulo a mabanki akomweko. Sosaite iyenera kuuzidwa za makonzedwe aliwonse.

◻ STOCK NDI BOND: Stock ndi bond ingapatsidwe monga chopereka ku Watch Tower Society monga mphatso yachindunji kapena mwa kakonzedwe kamene ndalama zolandiridwa zikupitirizabe kulipiridwa kwa woperekayo.

◻ REAL ESTATE: Chuma chotchedwa real estate chokhoza kugulitsidwa chingaperekedwe ku Watch Tower Society mwa kuchipereka monga mphatso yachindunji kapena mwa kusungidwa kwa chumacho ndi mwini wake amene angapitirizebe kukhala nacho kufikira imfa yake. Munthuyo ayenera kuuza Sosaite asanailoŵetse m’pangano la chuma chilichonse chotero.

◻ WILL NDI TRUST: Chuma kapena ndalama zingakhale choloŵa cha Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania kudzera mwa pangano la amene adzatenga chuma chamasiye lovomerezedwa mwa lamulo, kapena Sosaite ingalembetsedwe kukhala yodzapindula ndi pangano loikizira chuma. Pangano loikizira chuma lopindulitsa gulu lachipembedzo lingakhale ndi mapindu ena akuchepetsa msonkho. Kope la pangano la will kapena trust liyenera kutumizidwa ku Sosaite.

Kuti mupeze chidziŵitso chowonjezereka pankhani zotere, lemberani ku Treasurer’s Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku ofesi ya Sosaite imene ikutumikira m’dziko lanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena