Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 12/1 tsamba 28-31
  • “Kodi Ndalamazo Zimachokera Kuti?”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kodi Ndalamazo Zimachokera Kuti?”
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chitsanzo Chimene Israyeli Wakale Anapereka
  • Kufunika Kwake Lerolino
  • Kodi Ndalamazo Zimapita Kuti?
  • Yehova Adzakufupani
  • Mmene Ena Amapatsira Zopereka ku Ntchito Yolalikira Ufumu
    Nsanja ya Olonda—1994
  • “Lemekeza Yehova ndi Chuma Chako”—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Mpatsi wa “Mphatso Iliyonse Yabwino”
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Nkumpatsiranji Yehova?
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 12/1 tsamba 28-31

“Kodi Ndalamazo Zimachokera Kuti?”

OPENYERERA vidiyo ya Watch Tower Society yakuti “Jehovah’s Witnesses​—The Organization Behind the Name” amachita chidwi. Amaona amuna ndi akazi ooneka bwino a mafuko osiyanasiyana ndi ochokera kosiyanasiyana, akumwetulira ndi kugwira ntchito pamodzi mogwirizana. Zikwizikwi za antchito achimwemwe sindizo zokha zimene zimawakopa komanso nyumba zosanja zazikulu pamalikulu a Sosaite ku Brooklyn ndi mafamu ake ku Wallkill, New York. Vidiyo imeneyo imasonyeza kuti mkati mwa nyumba zimenezi muli makina amakono​—makina othamanga kwambiri osindikizira ndi opangira mabuku omatulutsa zofalitsa mamiliyoni ambiri mwezi uliwonse, makompyuta amitundumitundu, ndi madipatimenti ambiri owachirikiza.

Zimenezi zimasonyeza kuti ndalama zambiri zimawonongedwa. Chotero, ena amafunsa kuti, “Kodi ndalamazo zimachokera kuti?”

Alendo ofika ku malikulu a dziko lonse a Sosaite nawonso amachita chidwi. Amatukula mutu kuti aone nyumba yogona ya misanjo 30, ina ya nyumba zambiri zimene atumiki odzifunira oposa 3,000 ogwira ntchito kumeneko amakhalamo. Amene amapita kukaona malo atsopano a Malikulu a Maphunziro a Watchtower pafupifupi makilomita 110 kumpoto kwa Brooklyn nawonso amadabwa kwambiri. Pokhala malowo akumangidwa, pamakhala antchito 1,200. Makalasi aŵiri a amishonale adzayamba kuphunzirira kumeneko chaka ndi chaka ndi kutumizidwa ku maiko akunja ku magawo awo. Ndiponso chitsogozo chopita ku mipingo yoposa 10,000 ya Mboni za Yehova mu United States chimachokera kunoko. Ndipo nthambi zambiri padziko lonse zakuza malo awo posachedwapa kapena zikuwakuza kumene. Kuchita ntchito zonse zimenezi kumafuna ndalama zochuluka. Anthu amafunsa kuti, “Kodi ndalamazo zimachokera kuti?”

Yankho nlakuti zimachokera kwa anthu wamba monga ife. Ndi anthu apadziko lonse amene amafuna kuchita zonse zomwe angathe kuti apititse patsogolo ntchito Yachikristu yofunika kwambiri ya kulalikira ndi kuphunzitsa. Kusonyeza mzimu waufulu umenewu sindiko koyamba.

Chitsanzo Chimene Israyeli Wakale Anapereka

Zaka zoposa 3,500 zapitazo, panakhala kufunika kwa zopereka zochuluka. Yehova analangiza Mose kumanga chihema kapena “chihema chokomanako,” chogwiritsira ntchito polambira Iye. Mapulani ake operekedwa ndi Mulungu anafuna zinthu zosiyanasiyana zamtengo wapatali. Yehova analamula kuti: “Mumtengere Yehova chopereka cha mwa zanu; aliyense wa mtima womfunitsa mwini abwere nacho, ndicho chopereka cha Yehova.” (Eksodo 35:4-9) Kodi anthu anatani? Nkhaniyo imati “anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wamfunitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha ku ntchito ya chihema chokomanako, ndi ku utumiki wake wonse, ndi ku zovala zopatulika.” “Chopereka chofuna mwini” chimenechi popita nthaŵi chinawonjezeka kwambiri kwakuti ‘chinachuluka kuposa zoyenera ntchito imene Yehova anauza ichitike.’ (Eksodo 35:21-29; 36:3-5) Ha, anthuwo anasonyeza mzimu wodzimana wakuwoloŵa manja wotani nanga!

Zaka 500 zisanathe, pempho linaperekedwanso kwa Aisrayeli la chopereka chaufulu. Chifuno cha Mfumu Davide cha kumangira Yehova nyumba yachikhalire m’Yerusalemu chinali pafupi kukwaniritsidwa mwa mwana wake Solomo. Davide yekha anasonkhanitsa ndi kupereka zinthu zochuluka zimene zinafunika. Ena anagwapo pamene Davide anawapempha kubweretsa ‘mphatso ya Yehova.’ Chotulukapo chake? “Anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu; pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova; mfumu Davide yemwe anakondwera ndi chimwemwe chachikulu.” (1 Mbiri 22:14; 29:3-9) Siliva ndi golidi angakwane $50 biliyoni m’ndalama zamakono!​—2 Mbiri 5:1.

Pazitsanzo zimenezi tikuona kuti palibe amene anakakamizidwa kupereka. Zinayenera kukhala ‘zaufulu’ ndipo zoperekedwa ndi “mtima wangwiro.” Ndizo zokha zimene zikanakondweretsa Yehova. Momwemonso, pamene panakhala mwaŵi wakupereka ndalama zothandizira Akristu osoŵa, mtumwi Paulo analemba kuti sizinayenera kukhala “monga mwa kuumiriza.” Anawonjezera kuti: “Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwera.”​—2 Akorinto 9:5, 7.

Kufunika Kwake Lerolino

Kodi zopereka zikufunika lerolino? Inde ndithu, ndipo zidzafunikabe zambiri m’kupita kwa nthaŵi. Chifukwa ninji?

Akristu apatsidwa malangizo osiyana m’nthaŵi ino ya mapeto. Yesu analamula ophunzira ake kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu amitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”​—Mateyu 28:19, 20.

Kuchita ntchito yaikulu imeneyi yophunzitsa ndi kulalikira pamene nthaŵi zonse tikuyandikira chimake cha “chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano” kumafuna nthaŵi yochuluka ndi ndalama. Chifukwa ninji? Chifukwa cha zonse zofunika pa kupereka uthenga wa Ufumu wa Mulungu “kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Anthu ochuluka sadziŵa Malemba ngati mmene anawadziŵira Ayuda a m’zaka za zana loyamba. Ndipotu, chiŵerengero chachikulu cha okhala pa dziko lapansi salidziŵa nkomwe Baibulo ndipo samaliyesa Mawu a Mulungu. Alaliki ayenera kuphunzitsidwa ndi kutumizidwa kumaiko akutali. (Aroma 10:13-15) Ndipo tangolingalirani kuchuluka kwa zinenero zogwiritsiridwa ntchito! Awo olalikidwa ayenera kukhala ndi Baibulo ndi zofalitsa zozikidwa pa Baibulo zimene angaŵerenge ndi kuphunzira m’chinenero chawochawo. Pamafunika makonzedwe aakulu kuti onse afikiridwe mwa dongosolo ndi kuti athandizidwe pang’onopang’ono kufikira uchikulire wauzimu kuti akathandizenso ena.​—2 Timoteo 2:2.

Yesu anati ‘uthenga wabwino wa ufumu’ uyenera choyamba ‘ulalikidwe pa dziko lonse lapansi, ukhale umboni kwa anthu amitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.’ (Mateyu 24:14) Chotero ino ndiyo nthaŵi ya kupereka zonse zomwe tingathe kuti ntchito yofunika kwambiriyo ichitike. Palibe njira ina yabwino kuposa imeneyi imene tingagwiritsire ntchito chuma chathu chisanakhale chopanda phindu lililonse.​—Ezekieli 7:19; Luka 16:9.

Kodi Ndalamazo Zimapita Kuti?

Watch Tower Society imafalitsa mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero zoposa 230, limodzi ndi mabuku a akhungu ndi mavidiyo a chinenero cha manja kaamba ka ogontha. Zimenezo zimafuna magulu a otembenuza ndi oŵerengamo pachinenero chilichonse. Zimadabwitsa kwambiri kungoganiza zochita ntchito yonse imeneyi, makamaka ya magazini a Nsanja ya Olonda, ofalitsidwa mwezi uliwonse m’zinenero 121, omatuluka nthaŵi imodzi m’zinenero 101. Komabe njofunika kuti anthu pa dziko lonse lapansi akhale nacho chidziŵitso chimodzimodzi ndi kuchiŵerenga. Chaka ndi chaka mitengo imakwera ya mapepala ndi zinthu zina zogwiritsira ntchito popanga mabuku a uthenga wa Ufumu kapena makaseti ndi mavidiyo. Mitengo imeneyo iyenera kulipiriridwa mwa kugwiritsira ntchito zopereka za abale.

Ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa ikuchitika m’magawo ofoledwa ndi mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 75,000 padziko lonse. Kuti aimangirire ndi kuilimbikitsa, oyang’anira oyendayenda ophunzitsidwa amachezera mpingo uliwonse pafupifupi kaŵiri pachaka. Misonkhano yaikulu imathandizanso kwambiri kupereka chiphunzitso. Pamafunika kuchita haya malo aakulu ochitiramo misonkhano yachigawo yolimbitsa chikhulupiriro. Zopereka zanu zimagwiranso ntchito pa chifuno chimenechi.

Pamene misonkhano yaikulu nthaŵi zambiri imachitika katatu kokha pachaka, mpingo uliwonse umakhala ndi misonkhano isanu mlungu ndi mlungu. (Yerekezerani ndi Eksodo 34:23, 24.) Unyinji wa atsopano olabadira uthenga wabwino wachititsa kuwonjezeka kwa mipingo yatsopano zikwi zambiri chaka chilichonse. Mwa chithandizo cha maloni operekedwa kupyolera mwa Sosaite okwana ndalama madola mamiliyoni ambiri, Nyumba za Ufumu zatsopano mazana ambiri zikumangidwa chaka chilichonse, ndipo zina zambiri zikukonzedwa ndi kufutukulidwa. Ngakhale kuti thumba limeneli amatapamo ndi kubwezeramo nthaŵi ndi nthaŵi, nyumba zofuna kumanga zikuwonjezereka.

Dera lina kumene kwakhala chiwonjezeko chimene sichinachitikepo ndilo maiko a ku Eastern Europe amene anali pansi pa dziko lomwe kale linali Soviet Union. Tinasangalala chotani nanga kumva mbiri ya kupita patsogolo kwake yakuti ntchito inatseguka kumalo ameneŵa! Tsopano amishonale akutumizidwa ku maiko ochuluka mwa ameneŵa. Nthambi zatsopano zakhazikitsidwa m’maiko ena, zikumawonjezera chiŵerengero cha atumiki odzifunira opanga banja la Beteli padziko lonse kuposa pa 15,000. Ndithudi, nyumba za nthambi zokhalamo iwo ziyenera kugulidwa kapena kumangidwa. Zopereka zanu zimathandizira kukwaniritsa kusoŵako.

Sikuti Satana ndi ziŵanda zake sakuiona ntchito yonseyi. Akuchita zomwe angathe kulepheretsa zoyesayesa za atumiki okhulupirika a Yehova kapena kuwadzetsera zovuta. (Chivumbulutso 12:17) Zimenezi zikutanthauza nkhondo zochuluka za milandu zotetezera ufulu wa anthu a Mulungu kuti azilalikira ndi kutsatira malamulo ake olungama. Ndiponso, nkhondo zosakaza m’dongosolo la zinthu la Satana, limodzi ndi masoka achilengedwe, zimachititsa kuti pakhale kufunika kwa kupereka chithandizo kwa abale ndi alongo athu ovutika ndi ena okhala nawo. Zopereka zanu zimathandizira kupereka thandizo lofunika kwambiri limeneli.

Yehova Adzakufupani

Kugwiritsira ntchito nthaŵi yathu ndi chuma mwaufulu kuchirikizira ntchito ya Ambuye kumadzetsa madalitso aakulu. Motani? Chifukwa chakuti Mulungu, amene ndiye mwini zonse, adzatifupa. Miyambo 11:25 imati: “Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.” Yehova amakondwera kwambiri pamene tichita mbali yathu kupititsa patsogolo kulambira kwake. (Ahebri 13:15, 16) Iye anawalonjeza Aisrayeli akale amene anali kubweretsa zopereka zofunika m’pangano la Chilamulo kuti: “Mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera akumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoŵeka malo akuulandira.” (Malaki 3:10) Kukhupuka kwauzimu kumene atumiki a Yehova ali nako lerolino ndiko umboni wakuti Mulungu amasunga lonjezo lake.

Ntchito yaikulu imeneyi yolengeza kwa onse za tsiku la chipulumutso ndi kusonyeza oona mtima njira ya ku moyo sidzapitiriza kosatha. (Mateyu 7:14; 2 Akorinto 6:2) Koma onse a “nkhosa zina” za Ambuye ayenera kusonkhanitsidwa. (Yohane 10:16) Ha, nkofunika chotani nanga kuchita ntchito yaikuluyo lerolino! Ndipo aliyense wa ife adzakondwa chotani nanga kunena kuti, ‘Ndinatengamo mbali yaikulu m’ntchito yomaliza imeneyo yakututa’ atayang’ana kumbuyo ali m’dziko latsopano lolungama limenelo!​—2 Petro 3:13.

[Bokosi pamasamba 30, 31]

MMENE Ena Amachitira Zopereka Za Ntchito Yolalikira Ufumu

ZOPEREKA ZA NTCHITO YA PADZIKO LONSE: Ambiri amaika pambali kapena kulinganiza ndalama zimene amaika m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse ya Sosaite​—Mateyu 24:14.” Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalamazi ku malikulu a dziko lonse ku Brooklyn, New York, kapena ku ofesi ya nthambi yakwawo.

MPHATSO: Zopereka zaufulu za ndalama zingatumizidwe mwachindunji ku Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, 25 Columbia Heights, Brooklyn, New York 11201-2483, kapena ku ofesi ya Sosaite ya m’dziko lanu. Majuwelo kapena zinthu zina zamtengo wapatali zingaperekedwenso. Kalata yachidule yofotokoza kuti zimenezo zaperekedwa monga mphatso iyenera kutsagana ndi zoperekazo.

CHOPEREKA CHOTCHEDWA CONDITIONAL-DONATION: Ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society kuiikizira kufikira imfa ya woperekayo, limodzi ndi makonzedwe akuti ngati pakhala kusoŵa kwaumwini, zidzabwezeredwa kwa woperekayo.

INSHUWALANSI: Watch Tower Society ingalembetsedwe kuti ndiyo idzapatsidwa mapindu a inshuwalansi kapena penshoni. Sosaite iyenera kudziŵitsidwa za makonzedwe alionse otero.

MAAKAUNTI A KU BANKI: Maakaunti a ku banki, zikalata zoikizira ndalama, kapena maakaunti a anthu opuma pantchito angaikiziridwe kapena kulipiridwa pambuyo pa imfa ku Watch Tower Society, mogwirizana ndi malamulo a mabanki akwanu. Sosaite iyenera kudziŵitsidwa za makonzedwe alionse.

STOCK NDI BOND: Stock ndi bond ingapatsidwe monga chopereka ku Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni kapena mwa kakonzedwe kamene woperekayo angapitirize kumalipiridwa ndalama zopindulidwa.

REAL ESTATE: Chuma chotchedwa real estate chokhoza kugulitsidwa chingaperekedwe ku Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni kapena mwa kuchisunga chumacho mwini wake, amene angapitirizebe kuchigwiritsira ntchito kufikira imfa yake. Munthuyo ayenera kudziŵitsa Sosaite asanailoŵetse m’pangano la real estate iliyonse.

WILL NDI TRUST: Chuma kapena ndalama zingakhale choloŵa cha Watch Tower Society kudzera mwa pangano la amene adzatenga chuma chamasiye lochitidwa mwa lamulo, kapena Sosaite ingalembedwe kukhala yodzapindula ndi pangano loikizira chuma. Pangano loikizira chuma lopindulitsa gulu la chipembedzo lingakhale ndi mapindu ena akuchepetsa msonkho. Kope la pangano la will kapena trust liyenera kutumizidwa ku Sosaite.

KUPATSA KOLINGANIZA: Sosaite yakonza brosha Lachingelezi lamutu wakuti “Planned Giving.” Awo okhala ku United States amene akulinganiza kupatsa Sosaite chopereka chapadera tsopano kapena kusiya choloŵa pa imfa chidziŵitso chimenechi chingawathandize. Zimenezi nzoona makamaka ngati iwo ali ndi chonulirapo cha banja kapena cholinga cha amene adzasiyira chuma chamasiye pamene akugwiritsira ntchito makonzedwe a lamulo akuchepetsa msonkho wofunika.

Kuti mudziŵe zowonjezereka pankhani zili pamwambazi, lemberani ku Treasurer’s Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku ofesi ya Sosaite ya m’dziko lanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena