Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 2/1 tsamba 3
  • Chipembedzo Chanu Kodi Ndi Chombo Chosayenera Kutulukamo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chipembedzo Chanu Kodi Ndi Chombo Chosayenera Kutulukamo?
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • “Palibe Amene Ataye Moyo Wake”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Chikondi Chimene Chimamangirira
    Galamukani!—1996
  • Olimba Ngati Nangula Chifukwa cha Chiyembekezo, Osonkhezeredwa ndi Chikondi
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Paulo Anatumizidwa ku Roma
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 2/1 tsamba 3

Chipembedzo Chanu Kodi Ndi Chombo Chosayenera Kutulukamo?

CHOMBO chili pakati pa namondwe. Oyendetsa ake, amene akuyesayesa mothedwa nzeru kupulumutsa chombocho, akuyang’anizana ndi chosankha chodetsa nkhaŵa: kaya akhalebe m’chombocho kapena atulukemo kuti adzipulumutse. Kodi munadziŵa kuti chithunzi chowopsa chimenechi chimagwiritsiridwa ntchito monga fanizo la zaumulungu?

Ophunzitsa zaumulungu, makamaka akatswiri Achikatolika, kaŵirikaŵiri amayerekezera tchalitchi chawo ndi chombo chimene chikulimbana ndi namondwe. Iwo amanena kuti chombo chimenechi, chokhala ndi Yesu ndi Petro monga oyendetsa ake, chimaimira njira yokha ya chipulumutso. Chilengezo cha atsogoleri achipembedzo nchakuti, ‘Musatuluke m’chombocho. Tchalitchi chapyola m’mavuto owopsa, koma ndi chombo chimene chalimbana ndi anamondwe onse a m’mbiri.’ Ena amanena kuti, ‘Kodi nkutulukiramonji? Kodi ndi kuti kwinanso kumene munthu angapite? Bwanji osangokhala mmenemo ndi kuthandiza kuchiwongolerera ku madzi abata?’

Mogwirizana ndi chilankhulo chophiphiritsira chimenecho, anthu ambiri a zipembedzo zosiyanasiyana amalingalira kuti, ‘Ndimadziŵa kuti chipembedzo changa ncholakwa m’zinthu zambiri, koma ndikhulupirira kuti chidzasintha. Sindifuna kuchisiya. Ndikufuna kukhala ndi phande pakuthandiza kulaka mavuto ake.’ Kalingaliridwe ka mtundu umenewu kangachititsidwe ndi kukonda chipembedzo cha makolo koona mtima kapena kuwopadi “kuchivumbula.”

Chitsanzo chenicheni ndi chija cha Hans Küng, amene anali wophunzitsa zaumulungu wotchuka ndi wotsutsa Wachikatolika, yemwe anasinkhasinkha kuti: “Kodi ndisiye bwatolo mkati mwa namondwe, ndi kusiira thayo la kulimbana ndi mphepo ndi mobooka awo amene ndayenda nawo panyanja kufikira tsopano lino, ndipo mwinamwake kumenyera nkhondo kupulumuka?” Iye anayankha kuti: “Sindidzataya kudzipereka kwanga mu tchalitchi.” Njira ina ikakhala “kuchoka mu tchalitchi chimenechi, chifukwa cha machenjera ake, kaamba ka kukonda mikhalidwe yapamwamba koposerapo, ndipo mwinamwake, kukhala Akristu oona koposerapo.”​—Die Hoffnung bewahren.

Koma kodi munthu angakhalebe m’bwato la tchalitchi chake ndi chiyembekezo chakuti, mwa chifundo chake, Mulungu adzapatsa zipembedzo zonse nyengo ya nthaŵi yamuyaya ya kukonzanso zinthu? Limenelo ndi funso lalikulu kwambiri. Monga momwe fanizolo lasonyezera, kuchoka mofulumira m’chombo chokhala pangozi ndi kuthaŵira m’mabwato opulumutsa osakhala bwino kungakhale kwangozi mofanana ndi kukhalabe m’chombo chimene chikumira. Kodi nkwanzeru kukhala m’tchalitchi mosasamala kanthu za zimene zingachitike, mosasamala kanthu za mkhalidwe wake? Kodi zipembedzo zamakono zikupereka ziyembekezo za kusintha zotani? Kodi Mulungu adzazilola kwa utali wotani kuchita motsutsana ndi chifuniro chake?

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Chesnot/​Sipa Press

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena