Chinthu Chabwino Koposa Chochita ndi Moyo Wanga
YOSIMBIDWA NDI BOB ANDERSON
Pafupifupi zaka khumi zapitazo, mabwenzi ena anandifunsa kuti: “Bob, kodi nchifukwa ninji wapitirizabe kwanthaŵi yaitali chotero monga mpainiya?” “Chabwino,” ndinamwetulira ndipo ndinati, “kodi mungaganize za kuchita kanthu kena kabwino kuposa kuchita upainiya?”
NDINALI ndi zaka 23 zakubadwa mu 1931 pamene ndinaloŵa mu utumiki waupainiya. Tsopano ndili m’chaka changa cha 87 ndipo ndikali kuchita upainiya. Ndidziŵa kuti palibe chinthu chabwino kwambiri kuposa chimenechi chimene ndikanachita ndi moyo wanga. Ndiloleni ndifotokoze chifukwa chake.
Mu 1914 trakiti lina linasiyidwa panyumba pathu. Linali lofalitsidwa ndi Ophunzira Baibulo a pa Dziko Lonse, monga momwe Mboni za Yehova zinkatchedwera panthaŵiyo. Pamene Mboniyo inabweranso, amayi anaifunsa za moto wa helo. Iwo analeredwa monga Mmethodist wa Wesley wamphamvu komano sankatha kugwirizanitsa chiphunzitso chimenechi cha chizunzo chosatha ndi Mulungu wachikondi. Pamene anangodziŵa choonadi cha nkhaniyo, iwo anati: “Ndikukondwera kwambiri kuposa mmene ndinachitira m’moyo wanga!”
Nthaŵi yomweyo amayi analeka kuphunzitsa Sande sukulu ya Methodist ndi kugwirizana ndi kagulu ka Ophunzira Baibulo. Anayamba kulalikira m’tauni ya kwathu ya Birkenhead, imene yayang’anizana ndi doko la Liverpool limene lili patsidya pa Mersey River, ndipo posakhalitsa anali kuyenda panjinga kumka kumatauni ambiri oyandikana nawo. Anachitira umboni m’dera lalikulu limeneli moyo wawo wonse ndipo anafikira pakudziŵika kwambiri, akumapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa ana awo. Anamwalira mu 1971 pausinkhu waukalamba wa zaka 97, ali Mboni yokangalika kufikira mapeto.
Ine ndi mlongo wanga, Kathleen, tinachotsedwa m’Sande sukulu ya Methodist kuti tizitsagana ndi Amayi kumisonkhano yawo ndi Ophunzira Baibulo. Pambuyo pake, pamene atate anagwirizana nafe, makolo anga analinganiza phunziro la Baibulo la banja lanthaŵi zonse m’buku lakuti Zeze wa Mulungu. Phunziro lotero linali chinthu chatsopano m’masiku amenewo, koma kuyala maziko a choonadi cha Baibulo cha maziko koyambirira kumeneku kunafupa kwambiri, popeza kuti tonsefe ine ndi mlongo wanga tinaloŵa mu utumiki waupainiya m’kupita kwa nthaŵi.
Amayi anali kunena nthaŵi zonse kuti kuona “Photo-Drama of Creation” ku Liverpool mu 1920 kunali posinthira pauzimu kwa anafe, ndipo analondoladi. Pokhala wachichepere, kanema ameneyo anakhomerezeka kwambiri m’maganizo mwanga. Chimene ndimakumbukira kwambiri ndicho chigawo chosonyeza moyo wa Yesu, makamaka pamene inamsonyeza akumka ku imfa. Chochitika chonsecho chinandithandiza kusumika maganizo pa ntchito yofunika koposa m’moyo—kulalikira!
Kuchiyambiyambi kwa ma 1920, ndinayamba kugaŵira matrakiti ndi amayi pa Sande masana. Poyamba tinalangizidwa kuwasiya panyumba; pambuyo pake tinauzidwa kuwapereka kwa eni nyumba ndi kubwereranso kwa awo amene anali okondwerera. Nthaŵi zonse ndaona zimenezi kukhala maziko oyambirira a ulendo wathu wobwereza ndi ntchito ya phunziro la Baibulo, imene ili yobala zipatso kwambiri lerolino.
Mu Utumiki Waupainiya!
Ine ndi Kathleen tinabatizidwa mu 1927. Ndinali kugwira ntchito monga wopenda za chemistry ku Liverpool pamene, mu 1931, ndinamva za chosankha cha kulandira dzina lakuti Mboni za Yehova. Kaŵirikaŵiri ndinkaona akoputala a Sosaite (tsopano otchedwa kuti apainiya) akumagwira ntchito m’magawo a malonda mu Liverpool, ndipo chitsanzo chawo chinanditenga mtima kwambiri. Ha, ndinakhumbira motani nanga kumasuka kuntchito yanga, kuthera moyo wanga mu utumiki wa Yehova!
Mkati mwa chilimwe cha chaka chimodzimodzicho, mnzanga wina Gerry Garrard anandiuza kuti anapatsidwa gawo ndi pulezidenti wachiŵiri wa Watch Tower Society, Joseph F. Rutherford, kukalalikira ku India. Asanayambe ulendo wapanyanja, anafika kudzandiona ndipo analankhula za thayo la utumiki wanthaŵi yonse. Pamene anali kunditsazika, anandilimbikitsanso mwa kunena kuti, “Bob, ndikhulupirira kuti udzakhala mpainiya posachedwapa.” Ndipo ndimo mmene zinayendera. Mu October chaka chimenecho ndinalembetsa. Ha, nchisangalalo chotani nanga, nkumasuka kotani nanga, kuyenda ndi njinga m’misewu yaing’ono ya m’midzi, kulalikira kumidzi yakutali! Pamenepo ndinadziŵa kuti ndinali kuloŵa mu ntchito yokha yofunika koposa kwa ine.
Gawo langa loyamba laupainiya linali ku South Wales kumene ndinagwirizana ndi Cyril Stentiford. Pambuyo pake Cyril anakwatirana ndi Kathleen, ndipo anachita upainiya pamodzi kwa zaka zingapo. Mwana wawo wamkazi, Ruth, nayenso anadzaloŵa mu utumiki waupainiya. Podzafika 1937, ndinali ku Fleetwood, Lancashire—bwenzi la Eric Cooke. Kufikira nthaŵiyo, apainiya anali kungogwira ntchito m’madera akumidzi a Britain, kunja kwa gawo la mpingo. Koma Albert D. Schroeder, amene panthaŵiyo anali woyang’anira ntchito ya Sosaite ku ofesi ya nthambi ya London, anasankha kutisamutsira kumzinda wa Bradford, Yorkshire. Imeneyi inali nthaŵi yoyamba kuti apainiya ku Britain agaŵiridwe kukasamalira mpingo wofuna thandizo.
Mu 1946, Eric anapita ku Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower ndipo anapatsidwa gawo la ku Southern Rhodesia, tsopano Zimbabwe, ndipo iye ndi mkazi wake adakatumikirabe mokhulupirika monga amishonale ku Durban, South Africa.
M’chaka cha 1938 ndinalandira gawo lina, panthaŵiyi monga mtumiki wadera (tsopano wotchedwa kuti woyang’anira dera) wa kumpoto chakumadzulo kwa Lancashire ndi Lake District wokongolayo. Kumeneko ndinakumana ndi Olive Duckett, ndipo titakwatirana, iye nthaŵi yomweyo anagwirizana nane m’ntchito yadera.
Ireland Mkati mwa Zaka za Nkhondo
Posapita nthaŵi Britain atalengeza kumenyana ndi Germany mu September 1939, gawo langa linasinthidwa kukhala Ireland. Kulembedwa usilikali kunali kutayamba m’Britain koma osati m’Republic of Ireland wa kummwera, amene anakhala dziko losatenga mbali mu nkhondoyo. Republic of Ireland ndi Northern Ireland linali kudzakhala dera limodzi. Komabe, panali ziletso, ndipo kunali kofunika kupeza ziphaso zololeza kuyenda kotero kuti tituluke m’Britain kumka kumbali iliyonse ya Ireland. Akuluakulu a boma anandiuza kuti ndipite, komano ndinayenera kuvomereza kudzabwerera msanga ku England pamene gulu la usinkhu wanga liyamba kulembedwa usilikali. Ndinangovomera mwapakamwa, koma ndinadabwa pamene chiphaso changa chachilolezo chinaperekedwa, panalibe zofunika zimene zinaphatikizidwapo!
Panthaŵiyo, panali Mboni zoposa 100 zokha mu Ireland monse. Titafika mu Dublin mu November 1939, Jack Corr, mpainiya wanthaŵi yaitali, anatilandira. Anatiuza kuti panali apainiya enanso aŵiri m’tauni yapafupi ndi anthu angapo okondwerera mu Dublin, pafupifupi 20 onse pamodzi. Jack anapeza chipinda chosonkhanira ku Dublin chimene onse anavomerezana kuti azisonkhanamo Sande lililonse. Makonzedwe ameneŵa anapitiriza kufikira mpingo unapangidwa mu 1940.
Northern Ireland, monga mbali ya United Kingdom, anali pankhondo ndi Germany, chotero pamene tinamka kumpoto ku Belfast, tinali ndi mabuku a matikiti a chakudya ndipo tinapirira ndi mdima usiku chifukwa cha kuzimidwa kwa magetsi. Ngakhale kuti ndege za Nazi zinali kuuluka mtunda woposa makilomita 1,600 kuti zifike ku Belfast ndi kubwerera kumalo ake ku Ulaya, zinakhoza kuphulitsira mabomba mwamphamvu pamzindawo. Mkati mwa kuukira koyamba, Nyumba yathu Yaufumu inawonongedwa ndipo nyumba yathu inaphwasulidwa pamene tinali kuona abale kumbali ina ya mzinda, chotero tinapulumuka modabwitsa. Usiku umodzimodziwo, banja lina la Mboni linathaŵira m’malo obisaliramo mabomba a anthu onse. Pamene linafika kumeneko, linapeza kuti anali odzaza ndipo linabwerera kunyumba kwawo. Malo obisaliramo mabombawo anaphulitsidwa ndi bomba, ndipo onse amene analimo anaphedwa, koma abale athu anapulumuka atatemekatemeka pang’ono. Mkati mwa zaka zovuta za nkhondo zimenezi, panalibe ngakhale mmodzi wa abale athu amene anavulala kwambiri, chinthu chimene tinathokoza nacho Yehova.
Magwero a Chakudya Chauzimu
Pamene nkhondo inali kuchitika, ziletso zinawonjezereka, ndipo pomalizira pake lamulo la kufufuza m’makalata linaikidwa. Zimenezi zinatanthauza kuti Nsanja ya Olonda inalandidwa ndipo sinaloledwe kuloŵa m’dziko. Ngakhale kuti tinali osadziŵa chimene tikanachita, mkono wa Yehova sunafupike. Tsiku lina mmaŵa ndinalandira kalata kuchokera kwa “mnsuwani” wa ku Canada amene ankandilembera ponena za nkhani za m’banja. Sindinadziŵe kuti anali yani, koma m’mawu ake ophatikizidwa atamaliza kulemba kalatayo anati anali atatsekeramo “nkhani yokondweretsa ya Baibulo” yoti ndiŵerenge. Inali kope la Nsanja ya Olonda, koma chifukwa chakuti inali ndi chikuto chopanda kanthu, sinatulutsidwemo ndi mkulu wofufuza makalata.
Nthaŵi yomweyo ine ndi mkazi wanga, ndi thandizo la Mboni zakumaloko, kuphatikizapo Maggie Cooper amene anali mu ntchito ya “Photo-Drama,” tinayamba kupanga makope ena a nkhanizo. Posapita nthaŵi tinakonzekera kukapereka makope 120 m’dziko lonselo, pamene magazini a Nsanja ya Olonda a chikuto chopanda kanthu ankafika nthaŵi zonse kuchokera kwa mabwenzi ambiri atsopano a ku Canada, Australia, ndi United States. Chifukwa cha thandizo lawo lakhama ndi lokoma mtima, sitinaphonye konse kope lililonse mkati mwa nyengo yonseyo ya nkhondo.
Tinakhoza kuchitanso misonkhano. Wosaiŵalika ndiwo msonkhano wachigawo wa 1941 pamene chofalitsidwa chatsopano chotchedwa Children chinatulutsidwa. Kunaonekera ngati kuti mkulu wofufuza makalata sanakanize buku limene analingalira kukhala lonena za ana, chotero tinakhoza kuloŵetsa mtokoma wathu m’dziko popanda vuto lililonse! Pa nthaŵi ina, tinasindikizitsa kabuku kakuti Peace—Can It Last? m’dziko momwemo chifukwa chakuti kunali kosatheka kuloŵetsa makope ake m’dziko kuchokera ku London. Mosasamala kanthu za ziletso zonse zoikidwa pa ife, tinasamaliridwa bwino mwauzimu.
Kugonjetsa Chitsutso
Mtsogoleri wina wachipembedzo wokhala kunyumba yosamalira nkhalamba ku Belfast yoyang’aniridwa ndi mmodzi wa Mboni za Yehova anatumiza kope la buku lakuti Chuma kwa mkazi wake ku England. Mkaziyo anatsutsa choonadi, ndipo yankho lake limene anapereka linasonyeza bwino zimenezo. Iye ananenanso kuti ife tinali “gulu losakonda dziko lawo.” Mkulu wofufuza makalata anatulukira zimenezi ndi kupereka nkhaniyo ku Criminal Investigation Department. Chotero, ndinaitanidwa ku polisi kuti ndikafotokoze bwino ndipo ndinapemphedwa kubweretsa kope la Chuma. Chimene chinandikondweretsa chinali chakuti, pamene bukulo linabwezedwa, ndinaona kuti mbali zokha zolembedwa mizere pansi zinali zonena za Tchalitchi cha Roma Katolika. Ndinaona kuti zimenezi zinali ndi tanthauzo lina, popeza ndinadziŵa kuti apolisiwo anali kupenyetsetsa zochita za IRA (Irish Republican Army).
Ndinafunsidwa kwambiri ponena za uchete wathu m’nthaŵi ya nkhondo, popeza kuti apolisi anapeza vuto kumvetsetsa kaimidwe kathu. Koma akuluakulu a boma sanachitepo kanthu kalikonse pa ife. Pambuyo pake, pamene ndinali kupempha chilolezo cha kuchita msonkhano, apolisi anaumirira kuti akatumiza amtolankhani aŵiri apolisi. Ndinati, “Tidzawalandira!” Chotero anabwera ndipo anakhala pamenepo kufikira pa kusonkhana kwa masana konse, akumalemba manotsi. Pamapeto a gawolo, anafunsa kuti, “Kodi anatitumiziranji kuno? Tikusangalala ndi zonse!” Iwo anafikanso tsiku lotsatira ndipo mokondwa analandira kope laulere la kabuku kathu kakuti Peace—Can It Last? Msonkhano wonsewo unatha popanda kanthu kododometsa.
Nkhondo itangotha ndipo ziletso za kuyenda zitachepetsedwa, Pryce Hughes wa ku Beteli ya London anafika ku Belfast. Iye anali limodzi ndi Harold King, amene pambuyo pake anatumizidwa ku China monga mmishonale. Patapita zaka zisanu ndi chimodzi za kulekanitsidwa ndi ofesi ya nthambi ya London, tonsefe tinalimbikitsidwa kwambiri ndi nkhani zimene abale ameneŵa anapereka. Mwamsanga pambuyo pake, Harold Duerden, mpainiya wina wokhulupirika, anatumizidwa kuchokera ku England kudzalimbitsa ntchito ya Ufumu mu Belfast.
Kubwerera ku England
Tinakonda abale athu Achiairishi, ndipo kubwerera ku England kunali kovuta. Koma ine ndi mkazi wanga tinagaŵiridwanso gawo ku Manchester ndipo pambuyo pake tinasamukira ku Newton-le-Willows, tauni ina ya Lancashire kumene kunali kusoŵa kokulirapo. Lois, mwana wathu wamkazi, anabadwa mu 1953, ndipo kunali kosangalatsa mtima kumuona akuloŵa mu utumiki waupainiya pausinkhu wa zaka 16. Atakwatiwa ndi mpainiya wina David Parkinson, anapitiriza utumiki wawo wanthaŵi yonse ku Northern Ireland, akumatsatira kwambiri njira imene ine ndi Olive tinatenga. Tsopano, limodzi ndi ana awo, ali kuno ku England, ndipo tonsefe tikutumikira mu mpingo umodzi.
Mosasamala kanthu za kusintha kwa mikhalidwe yathu, sindinasiye kuchita upainiya—Olive sanafune zimenezo ayi, ngakhalenso ine. Nthaŵi zonse ndalingalira kuti mbiri yanga ya upainiya yachirikizidwa moyenerera ndi mkazi wanga chifukwa chakuti popanda chichirikizo chake chachikondi ndi chanthaŵi zonse, sindikanatha kupitiriza utumiki wanthaŵi yonse. Zoonadi, tonse aŵirife timatopa msanga tsopano, koma kuchitira umboni kudakali kosangalatsa, makamaka pamene tili tonse, tikumachititsa maphunziro a Baibulo ndi anansi athu. M’zaka zonse zapita, takhala ndi mwaŵi wa kuthandiza anthu pafupifupi zana limodzi kukhala atumiki a Yehova odzipatulira ndi obatizidwa. Zimenezo zakhala zosangalatsa chotani nanga! Ndipo ndiganiza kuti chiŵerengero chimenechi pofika tsopano lino chiyenera kukhala chikuwonjezereka kwambiri pamene mabanjawo akukhala ndi zidzukulu ndi zidzukulu tudzi zimenenso zakhala Mboni.
Ine ndi Olive kaŵirikaŵiri timalankhula za zinthu zambiri zimene tapeza ndi zokumana nazo mkati mwa zakazi. Zakhala zaka zodzetsa chimwemwe chotani nanga, ndipo ha, mmene zapyolera mwamsanga nanga! Ndikudziŵa kuti sindikanapeza chinthu china chabwino kwambiri chochita ndi moyo wanga kuposa kutumikira Mulungu wanga, Yehova, monga mpainiya zaka zonsezi. Tsopano, kaya ndikuganiza za kumbuyoku mothokoza kapena kuyembekezera zamtsogolo, ndimapeza kuti mawu a Yeremiya ali ndi tanthauzo lalikulu: “Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka; chioneka chatsopano m’mawa ndi m’mawa; . . . chifukwa chake ndidzakhulupirira.”—Maliro 3:22-24.
[Chithunzi patsamba 26]
Bob ndi Olive Anderson