Kodi Amphaŵi Adzafunikira Kuyembekezera Kwautali Wotani?
“Ngati chitaganya chaufulu sichingathe kuthandiza anthu ambiri amene ali amphaŵi, sichingathenso kupulumutsa anthu oŵerengeka olemera.”—John F. Kennedy.
“NDIKUFUNA kuti mtsogolo mukhale mwabwino kwa aliyense—mopanda umphaŵi, mopanda munthu wogona m’paki, paradaiso!” Umo ndimo mmene mnyamata wina wazaka 12 wa ku São Paulo, Brazil ananenera. Koma kodi kuchotsa umphaŵi nkotheka? Kodi amphaŵi adzafunikira kuyembekezera kwautali wotani?
Ena amadziona kukhala amphaŵi chifukwa chakuti sangathe kugula zinthu zimene amafuna. Komabe, taganizani za mkhalidwe womvetsa chisoni wa awo amene alidi paumphaŵi weniweni. Kodi mungathe kulingalira za mavuto aakulu ndi chisoni za anthu amenewo? Ena amalimbirana zakudya ndi akakoŵa akunyanja ndi makoswe pamene amafukula m’malo otayira zinyalala! Kodi umphaŵi wotero udzasautsa anthu kwautali wotani? Pempho la Federico Mayor, mkulu wa UNESCO (United Nations Educational, Scientific, and Cultural Organization), lili loyenera: “Tiyeni tisiye kulekerera koipa kumeneko kumene kukutiloleza kupirira ndi zosapiririka—umphaŵi, njala ndi kuvutika kwa anthu ambirimbiri.”
Kodi lingaliro la ubwino wa onse lidzakwaniritsidwa? Kodi amphaŵi ali ndi chiyembekezo chotani?
Kodi ndi Mwaŵi Wotani Umene Ulipo kwa Amphaŵi?
Atsogoleri okhala ndi zolinga zabwino amapereka malingaliro a kupezeka kwa ntchito kosavuta, malipiro abwino, makonzedwe abwino a zakakhalidwe ka anthu, ndi malo olimapo. Iwo angavomerezane ndi yemwe kale anali pulezidenti wa United States John F. Kennedy: “Ngati chitaganya chaufulu sichingathe kuthandiza anthu ambiri amene ali amphaŵi, sichingathenso kupulumutsa anthu oŵerengeka olemera.” Komabe, zolinga zabwino sizili zokwanira kuthetsera umphaŵi. Mwachitsanzo, kodi kuwonjezereka kwa chuma kungathandize amphaŵi ambiri? Osati kwenikweni. Yemwe kale anali mtsogoleri wa India Jawaharlal Nehru anati: “Ngati chisonkhezero cha chitaganya cha chuma sichichenjereredwa, chikhoza kuchititsa anthu olemera kukhala olemera kwambiri ndipo amphaŵi kukhala aumphaŵi kwambiri.” Komanso, kuwonjezera pa zovuta ndi kusoŵa zinthu, mkhalidwe wa kusadziŵerengera umawonjezera zothodwetsa za amphaŵi. Kodi atsogoleri aumunthu angathandize amphaŵi kuthetsa malingaliro a kukhala osoŵa thandizo ndi opanda chiyembekezo?
Kwenikweni, amphaŵi ambiri othedwa nzeru aphunzira kupirira ndi moyo waumphaŵi ndi kuchotsa kusadzilemekeza kwawo poyang’anizana ndi mavuto aakulu, monga ngati kukwera mtengo kwa zinthu ndi ulova. Ndiponso, njala, kusoŵa pokhala, ndi nsautso zina zidzachotsedwadi. Kodi zimenezi zikukudabwitsani? Tikukupemphani kuŵerenga nkhani yotsatirayo: “Posachedwapa, Sikudzakhalanso Mmphaŵi!”