Pamene Amaliŵerenga ndi Mmene Amapindulira
Mmamaŵa:
Banja lina, onse aŵiriwo amagwira ntchito yolembedwa, anasankha kudzuka kukali mphindi khumi mmaŵa uliwonse ndi kugwiritsira ntchito nthaŵiyo kuŵerengera Baibulo pamodzi asanachoke mwamsangamsanga panyumba. Zimene amaŵerenga zimakhala maziko a kukambitsirana atachoka panyumba.
Mkulu wina ku Nigeria amagwiritsira ntchito ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki monga maziko a kuŵerengera Baibulo panyumba pake. Iwo amaŵerenga chigawo chake masiku onse atakambitsirana lemba la tsiku, kaŵirikaŵiri mmaŵa. Ana amapemphedwa kusinthana kuŵerenga zigawo zina zosankhidwa. Ndiyeno amapemphedwa kufunsa mafunso pa mavesi amene aŵerenga.
Mkazi wina wapanyumba ku Japan waŵerenga Baibulo lonse kamodzi pachaka chiyambire 1985. Programu yake ndi ya kuŵerenga kwa mphindi 20 kapena 30 kuyamba ndi 5:00 a.m. tsiku ndi tsiku. Ponena za mapindu ake, iye akuti: “Chikhulupiriro changa chalimba. Kumandithandiza kuiŵala matenda anga ndi kusumika maganizo pa chiyembekezo cha Paradaiso.”
Mlongo wina amene wakhala mpainiya kwa zaka 30 koma amene mwamuna wake sali Mboni amadzuka ndi 5 koloko mmaŵa uliwonse kuti aŵerenge Baibulo. Programu yake ndi ya kuŵerenga pafupifupi masamba anayi m’Malemba Achihebri, chaputala chimodzi m’Malemba Achigiriki, ndi vesi limodzi m’Miyambo. Waŵerenga Baibulo lonse chaka ndi chaka chiyambire 1959. Iye akuti: “Chifukwa cha kuŵerenga kwanga, ndimamva kukhala wokondedwa ndi Yehova . . . Ndimapeza chilimbikitso, chitonthozo, ndi kuwongoleredwa.” Akuwonjezera: “Kuŵerenga Baibulo kuli ngati kuti Yehova akukunga sipuling’i ya moyo wanga tsiku ndi tsiku.”
Mlongo wina amene anaphunzira choonadi m’dziko limene ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa alinso ndi mwamuna amene amatsutsa zikhulupiriro zake. Amaŵerenga Baibulo kuyambira pa Lolemba mpaka Lachisanu, pakati pa 6:00 ndi 7:00 a.m. Zimenezi zampatsa nyonga ya mkati. Polankhula za mmene kuŵerenga kwakeko kwamkhudzira, iye akuti: “Timaphunzira kukonda Yehova ndi Yesu ndi kukhala ndi moyo wachimwemwe, ngakhale pamene tili ndi zothetsa nzeru ndi mavuto, podziŵa kuti malonjezo a Yehova salephera.”
Mlongo wina amene analoŵa Sukulu ya Utumiki Waupainiya anatsimikiza mtima kutsatira uphungu umene unaperekedwa wa kukhala ndi chizoloŵezi cha kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. Poyamba, anali kuchita zimenezo pakati pa 5:00 ndi 6:00 a.m. Pamene kusintha kwa ntchito kunasokoneza zimenezo, iye anayamba kuŵerenga pakati pa 9:00 ndi 10:00 p.m. Pamene mikhalidwe ina yovuta inabuka, iye akuti, “Ndinapitiriza kumasintha ndandanda yanga malinga ndi mikhalidwe.”
Masana:
Alongo aŵiri paubale wawo amenenso ali abanja la Beteli ku Brazil ali ndi chizoloŵezi cha kuŵerengera Baibulo pamodzi kwa pafupifupi mphindi 20 tsiku ndi tsiku pambuyo pa chakudya cha masana. Iwo aŵerenga Baibulo lonse pafupifupi nthaŵi 25; komabe akulemba kuti: “Nthaŵi zonse timapeza kanthu kena katsopano, choncho kuŵerenga Baibulo sikumakhala kogwetsa ulesi.”
Mlongo wina mbeta ku Japan, anazindikira kuti ngakhale kuti analeredwa monga Mboni, sanadziŵe Malemba kwambiri; pamene anakhala mpainiya, anatsimikiza kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse. Tsopano amaŵerenga kaamba ka Sukulu Yautumiki Wateokratiki popita kuchipatala kukachiritsidwa tsiku limodzi pamlungu. Pambuyo pake kunyumba, amawonjezera pa zimenezo mwa kufufuza. Chakumapeto kwa mlungu, amaŵerenganso Baibulo, akumasankha mabuku malinga ndi ndandanda imene analembedwamo.
Wazaka 13 wina amene waŵerenga kale Baibulo lonse katatu tsopano akuŵerenga chaputala chimodzi masiku onse ataŵeruka kusukulu. Iye akuti zimenezi zamthandiza “kukonda Yehova kwambiri.”
Mboni ina imene ili ndi ndandanda yopanikiza monga mwamuna wapantchito, mkulu, wokwatira, ndi atate imamvetsera makaseti a Baibulo popita kuntchito pasitima. Ndiyeno kunyumba, imadziŵerengera yokha mbali zimodzimodzizo.
Kuwonjezera pa kuŵerenga kwake kwaumwini, mpainiya wina ku France amamvetsera makaseti a Baibulo pokonza chakudya, poyendetsa galimoto, pamene akuvutika, kapena kungoti asangalale.
Mpainiya wina wazaka 21 ku Japan akukumbukira kuti amayi ake anali kumuumiriza kuŵerenga zauzimu tsiku ndi tsiku, ndipo wakhala akuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kuyambira pamene anali ndi zaka zitatu, ngakhale kuti wachita zimenezo panthaŵi zosiyana. Ataŵerenga chigawo chimene wasankha kuŵerenga tsikulo, amaŵerenganso mavesi ofunika kwambiri, ndiyeno amapatula mphindi zingapo za kusinkhasinkha zimene waŵerenga.
Mboni ina, mpainiya, yaŵerenga Baibulo pafupifupi nthaŵi khumi m’zaka 12 zapitazi. Mwamuna wake ngwosakhulupirira, choncho imaŵerenga masana.
Madzulo:
Mkulu wina ndiponso mpainiya wokhazikika ku Japan amene amaŵerenga Baibulo lake usiku uliwonse asanakagone wakhala akuchita zimenezi kwa zaka zisanu ndi zitatu zapitazi. Iye akuti: “Ndimakonda kwambiri malemba amene amasonyeza mmene Yehova amalingalirira, mmene amaonera zinthu, ndi mmene amachitira ndi mikhalidwe yosiyanasiyana. Mwa kusinkhasinkha malemba ameneŵa, ndathandizidwa kulingalira monga Yehova ndi kuthandiza abale ndi alongo anga Achikristu ndi a m’banja langa.”
Mkulu wina ku France wakhala akuŵerenga Baibulo kwa ola limodzi madzulo aliwonse chiyambire 1979. Kaŵirikaŵiri amatsegula matembenuzidwe asanu kapena asanu ndi limodzi kuti aziwayerekezera. Iye akuti kuŵerenga kwake kosamalitsa kwamthandiza kuzindikira “mmene angagwiritsirire ntchito chidziŵitso cha Baibulo m’mikhalidwe ya tsiku ndi tsiku.” Zimenezi zamthandizanso kukhala wogwira mtima kwambiri popereka uphungu wa m’Malemba.
Kwa zaka 28 zapitazo, mbale wina ku Nigeria wakhala ndi chizoloŵezi cha kuŵerenga madzulo Lemba loperekedwa mu Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku limene lidzakambitsiridwa mmaŵa wotsatira. Ndiponso, amaŵerenga chaputala chonse m’Baibulo chimene lembalo latengedwamo. Atakwatira, anapitiriza chizoloŵezi chimenechi, akumaŵerenga ndi kukambitsirana nkhaniyo ndi mkazi wake.
Mtsikana wina amene makolo ake sali Mboni wakhala ndi chizoloŵezi cha kuŵerenga kwa mphindi zisanu kapena khumi usiku uliwonse asanakagone. Mphindi zimenezo nzamtengo wapatali kwa iye, ndipo amapemphera asanayambe kuŵerenga ndi pambuyo pake. Cholinga chake ndicho kudziŵa uthenga umene Yehova anauza aliyense wa alembi a Baibulo kulemba.
Mbale wina wokwatira, amene ali mu utumiki wa pa Beteli, akunena kuti waŵerenga Baibulo kamodzi pachaka kwa zaka zisanu ndi zitatu zapitazo. Amaŵerenga kwa mphindi 20 kapena 30 asanagone usiku. Ngakhale atatopa kwambiri, amapeza kuti ngati wapita kukagona popanda kuŵerenga, tulo samationa. Amadzuka ndi kukhutiritsa njala yauzimu imeneyo.