Mfupo za Kulimbikira
ANALI mkazi Wachigiriki wokhala ku Foinike m’chaka cha 32 C.E. Mwana wake wamkazi anali kudwala kwambiri, ndipo mkaziyo anali kufunafuna mankhwala ochiritsa. Pomva za munthu wina wachilendo amene anafika m’chigawo cha kwawo—munthu wa kudziko lina amene anatchuka ndi mphamvu za kuchiritsa odwala—anatsimikiza kuonana naye ndi kupempha thandizo lake.
Atampeza, anagwa pamapazi pake, akumachonderera kuti: “Mundichitire ine chifundo Ambuye, [M]wana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa kowopsa ndi chiŵanda.” Mwanjira imeneyo, mkazi Wachigirikiyo anapempha Yesu kuchiritsa mwana wake wamkazi.
Kodi mungalingalire za kulimba mtima ndi kudzichepetsa kumene kunafunika kwa iye kuti achite zimenezi? Yesu anali munthu wokhala ndi mphamvu ndi wodziŵika, ndipo pachiyambipo anali atadziŵikitsa kuti sakufuna aliyense kudziŵa kumene anali. Anapita ndi atumwi ake ku Foinike kuti akapeze mpumulo umene anafunikira kwambiri, osati kukagwira ntchito pakati pa Akunja osakhulupirira. Ndiponso, Yesu anali Myuda ndipo mkaziyo anali Wakunja, ndipo mkaziyo mosakayikira anadziŵa za kuipidwa kwa Ayuda kuyanjana ndi anthu onyozedwa a mitundu. Komabe, iye anachirimika pa chosankha chake cha kupeza machiritso a mwana wake.
Yesu ndi atumwi ake anayesayesa kuletsa mkaziyo kupeza thandizo panthaŵiyo. Poyamba, Yesu sananene chilichonse kwa iye. Ndiyeno, chifukwa cha kuchonderera kwake kobwerezabwereza ndi kulimbikira, atumwi moipidwa anauza Yesu kuti: “Mumuuze amuke; pakuti afuula pambuyo pathu.”
Koma mkaziyo sanaleke. M’malo mwake, anagwada pamapazi a Yesu, akumati: “Ambuye, ndithangateni ine.”
Posonyeza thayo lake lalikulu kwa ana a Israyeli ndipo, panthaŵi imodzimodziyo, akumayesa chikhulupiriro ndi kutsimikiza mtima kwake, Yesu mokoma mtima anamfotokozera kuti: “Si chabwino kutenga mkate wa ana [a Israyeli], ndi kuuponyera tiagalu [Akunja].”
M’malo mokwiya ndi kuyerekezera fuko lake moipa chotero, iye modzichepetsa anaumirira pa kufuna kwake thandizolo mwa kuyankha kuti: “Eetu, Ambuye, pakutinso tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye awo.”
Yesu anafupa kulimbikira kwa mkazi Wachigiriki ameneyo mwa kuyamikira chikhulupiriro chake ndi kumchitira mokoma mtima pa kuchonderera kwake. Tangolingalirani za chisangalalo chake pamene anabwerera kwawo kukapeza mwana wake wamkaziyo atachira!—Mateyu 15:21-28; Marko 7:24-30.
Mofanana ndi mkazi wa m’zaka za zana loyambayo, tifunikira kukhala olimbikira m’zoyesayesa zathu kukondweretsa Yehova ndi kupeza chiyanjo chake. Monga mmene zinalili kwa mkazi Wachigiriki, Baibulo limatitsimikizira kuti kulimbikira kwathu “pakuchita zabwino” kudzafupidwa.—Agalatiya 6:9.
Kodi kulimbikira nchiyani? Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika? Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatitayitse mkhalidwe umenewu, kuleka kapena kugonja? Kodi ndi mfupo zotani zimene tingayembekezere kulandira ngati tisonyeza kulimbikira potumikira Mlengi ndi Atate, Yehova tsopano lino?
Dikishonale ina imamasulira verebuyo “limbikira” kukhala “kugwiritsitsa mwaphamvu pa chifuno china, mkhalidwe, kapena pa ntchito, ngakhale pali zopinga, machenjezo, kapena zododometsa. . . . kupitiriza kukhalako; kukhalitsa.”
Baibulo mobwerezabwereza limalimbikitsa atumiki a Yehova kulimbikira pa kuchita chifuniro chake. Mwachitsanzo, timauzidwa ‘kuthanga tafuna Ufumu wake,’ ‘kusunga chokoma,’ ‘kulimbika chilimbikire m’kupemphera,’ ndi ‘kusalema’ pa kuchita zabwino.—Mateyu 6:33; 1 Atesalonika 5:21; Aroma 12:12; Agalatiya 6:9.
M’zochitika za moyo watsiku ndi tsiku, kulimbikira kuli mkhalidwe umene tonsefe tiyenera kukhala nawo ndi kukulitsa kuti zitiyendere bwino. Popanda iko sitingapeze kanthu kalikonse kenikeni, kofunika ndi kokhalitsa. Talingalirani za chitsanzo cha khanda limene likuyesa kuimirira ndi kuyamba kuyenda modzandira. Palibe khanda limene limaphunzira kuimirira ndi kuyenda bwinobwino patsiku limodzi lokha. Pamene tinali makanda, tonsefe mwinamwake tinayesa ndi kulephera nthaŵi zambiri tisanayambe kudziŵa kuyenda. Kodi nchiyani chimene chikanachitika ngati tikanaleka kuyesa pamene tinagwa kwanthaŵi yoyamba? Bwenzi tikukwaŵabe ndi manja ndi mawondo! Kulimbikira nkofunika kuti tifikire zonulirapo zoyenera ndi kuwonjezera maluso ndi kusunga ulemu wathu. Kuli monga momwe mwambi wina umanenera, “Ofuna kupambana samaleka, ndipo oleka samapambana.”
Apainiya anthaŵi yaitali amazindikira kuti chipambano sichimadza chifukwa cha maluso chabe. Chimafuna mzimu wa kumamatira pa chinthu, kutsimikiza mtima kuchita chifuniro cha Yehova mokwanira, ndi kulimba mtima poyang’anizana ndi zododometsa zakanthaŵi, ngakhale kupsinjika mtima. Chonulirapo cha kusangalala ndi madalitso a Mulungu kosatha chiyenera kukhala choonekera bwino m’maganizo.
Inde, ife tonse amene tikufuna kupeza chiyanjo cha Yehova ndi amene tikufuna kupambana m’makani a moyo tifunikira kulimbikira, khama, ndi chipiriro. Popanda mikhalidwe imeneyi, mwina tingataye chiyanjo cha Yehova ndi mfupo ya moyo weniweni.—Salmo 18:20; Mateyu 24:13; 1 Timoteo 6:18, 19.
Kaŵirikaŵiri kumakhala kovuta kwambiri kwa Mkristu kulimbikira pa ntchito zake zauzimu kuposa pa zochitika zake zina. Munthu angakhale akugwira ntchito zolimba pamalo ake olembedwapo ntchito kuti apezere banja lake zofunika zakuthupi, komano angakhale ‘wotopa kwambiri’ kuti achititse phunziro la Baibulo lanthaŵi zonse ndi mkazi wake ndi ana. Kodi ndi zinthu zotani zimene zimachititsa kulimbikira kukhala kovuta kwambiri mu ntchito Zachikristu kwa ambiri?
Chimodzi cha izo ndicho kulefulidwa maganizo, kumene kumakhalapo chifukwa cha kulephera kwathu ndi kufooka. Ngati tilingalira mopitiriza za zophophonya zathu, tingataye mtima ndi kuleka, tikumalingalira kuti Yehova sadzakhululukira machimo athu onse.
Chinthu china ndicho mkhalidwe wadziko wa makhalidwe oipa, chinyengo, ndi udani. (1 Yohane 2:15, 16) “Makhalidwe okoma” ena amene zisonkhezero za dziko zingaipse kapena kuwononga ndiwo kulimbikira Kwachikristu.—1 Akorinto 15:33.
Kulimbikira kwathu mu ntchito yolalikira kungafooketsedwe ndi kutsutsa kwa anthu kapena mphwayi yawo ku utumiki wathu wopatulika. Chifukwa cha kugwiritsidwa mwala, tingalingalire kuti anthu a m’gawo lathu sakufuna choonadi. Zimenezi zingatichititse kufunsa kuti: ‘Kodi phindu lake nchiyani?’ ndi kuleka mwaŵi wathu wapadera wa ntchito ya kutumikira.
Tingasonkhezeredwenso ndi mzimu wa dziko wa kudzikhutiritsa. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuvutika chonchi ndi kudzimana kwambiri pamene ena onse akusangalala kapena sakuvutika?—Yerekezerani ndi Mateyu 16:23, 24.
Kuti tilimbikire pa kuchita chifuniro cha Yehova, tifunikira kuvala umunthu Wachikristu ndi kuchita mogwirizana ndi mzimu, osati ndi thupi. (Aroma 8:4-8; Akolose 3:10, 12, 14) Kukhala ndi lingaliro la Yehova la nkhaniyo kudzatikhozetsa kupitiriza kuchita ntchito zathu zauzimu zofunika.—1 Akorinto 16:13.
Zitsanzo za Kulimbikira
Yehova watipatsa zitsanzo zambiri zosonkhezera za atumiki amene anakhalabe okhulupirika kwa iye m’mayesero aakulu ambiri. Mwa kuzilingalira, timaona mmene tingakulitsire ndi kusonyezera kulimbikira Kwachikristu ndi chifukwa chake kuli kofunika kwambiri.
Chitsanzo chachikulu koposa ndicho Yesu, amene anavutika kwambiri polemekeza dzina la Yehova. Baibulo limatilimbikitsa kupenda mosamalitsa zochita zake za kudzipereka kolimbikira: “Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira [mtengo wozunzirapo, NW], nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu. Pakuti talingirirani iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m’moyo mwanu.”—Ahebri 12:1-3.
Makani a moyo ngamtunda wautali, osati waufupi. Nchifukwa chake timafunikira kulimbikira konga kwa Kristu. Chonulirapo chake, mapeto ake, sitingawaone pambali yokulira ya makaniwo. Chonulirapo chake chiyenera kukhala chooneka bwino ndi maso athu a maganizo kotero kuti tithe kuchifikira m’njira yake yonse yovutayo. Yesu anali ndi chithunzithunzi chotero cha maganizo pamaso pake, ndiko kuti, “chimwemwe choikidwacho pamaso pake.”
Kodi nchiyani chimene chikuphatikizidwa pa chimwemwe chimenechi kwa Akristu lerolino? Choyamba, ndicho mfupo ya moyo wosafa kumwamba kwa oŵerengeka ndipo moyo wosatha pa dziko lapansi kwa ambiri. Ndiponso, kudziŵa kuti munthuwe wakondweretsa mtima wa Yehova ndipo wachita mbali yako pa kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu kumadzetsa chikhutiro.—Miyambo 27:11; Yohane 17:4.
Chophatikizidwanso pa chimwemwe chimenechi ndicho unansi wapafupi ndi wokondweretsa ndi Yehova. (Salmo 40:8; Yohane 4:34) Unansi wotero uli wopereka nyonga ndi wochirikiza moyo, ukumapatsa munthu mphamvu ya kuthamanga m’makani mwachipiriro ndi kusaleka. Ndiponso, Yehova amadalitsa unansiwo mwa kutsanulira mzimu wake woyera pa atumiki ake, ukumadzetsa kuwonjezereka kwa chimwemwe ndi ntchito yosangalatsa.—Aroma 12:11; Agalatiya 5:22.
Kulingalira za chitsanzo cha Yobu cha chikhulupiriro cholimbikira nkopindulitsa. Anali wopanda ungwiro ndipo sanadziŵe zambiri za mkhalidwe wakewo. Chotero nthaŵi zina, anagwera mu mkhalidwe wa kudzilungamitsa ndi wa kutaya mtima. Komabe, iye nthaŵi yonse anasonyeza kutsimikiza mtima pa kusunga umphumphu wake kwa Yehova ndi kusamsiya Iye. (Yobu 1:20-22; 2:9, 10; 27:2-6) Yehova anafupa Yobu chifukwa cha kudzipereka kwake kolimbikira, akumampatsa madalitso auzimu ndi akuthupi ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. (Yobu 42:10-17; Yakobo 5:10, 11) Monga Yobu, ifenso tingakumane ndi mavuto ambiri ndi kutaya zinthu m’moyo wathu tsopano lino, koma tingakhulupirirenso za dalitso la Yehova pa kupirira kwathu kokhulupirika.—Ahebri 6:10-12.
M’nthaŵi zamakonozi, Mboni za Yehova zonse pamodzi zasonyeza kulimbikira Kwachikristu pochita chifuniro cha Yehova. Mwachitsanzo, ntchito yawo ya kunyumba ndi nyumba ya khamayo ndi kulalikira poyera yachititsa kuti dziko lonse lizidziŵe ndi uthenga wawo. Ofalitsa nkhani atchula nthaŵi zambiri za changu chawo ndi kutsimikiza mtima kulalikira uthenga wabwino ngakhale potsutsidwa ndi poyesedwa. Mmodzi wa iwo wojambula zithunzi zoseketsa analembadi mawu akuti “Palibe amene angazembe Mboni za Yehova!”—Mateyu 5:16.
Yehova wadalitsa zoyesayesa zakhama za Mboni zake ndi zipatso zowonjezereka mu utumiki. Taonani chochitika cha Mboni zokangalika ku Italy kalelo m’ma 1960 pamene munali Mboni 10,000 zolalikira m’dziko la anthu oposa 53,000,000. M’tauni ina ya anthu 6,000, munalibe Mboni. Abale amene anafikamo anachitiridwa nkhanza pa utumiki wawo.
Nthaŵi zonse pamene abale anapita kukalalikira kumeneko, akazi ambiri, ndipo ngakhale amuna a m’tauniyo anali kusonkhanitsa anyamata, akumawalimbikitsa kutsatira Mboni ndi kuwalizira malikhweru ndi kuchita phokoso kwambiri. Patapita mphindi zoŵerengeka, abalewo anali kuumirizidwa kuchoka ndi kumka ku tauni ina. Poyesayesa kupereka umboni umodzi chabe wokwanira kwa anthu onse a m’tauniyi, abale anaganiza zomalalikira kumeneko pamasiku amvula yambiri okha, kotero kuti asavutitsidwe ndi anyamata. Anaona kuti anthu a m’tauniyo anali osafuna kuvumbidwa ndi mvula kokha kuti adodometse ofalitsawo. Mwanjira imeneyi uthenga wabwino unaperekedwa. Anthu okondwerera anapezedwa. Maphunziro a Baibulo atsopano anayambitsidwa. Chotero, si mpingo womakula wokha umene unapangidwa m’tauni yaing’onoyo komanso ntchito yolalikira inayamba kuchitidwa ngakhale pamasiku opanda mvula. Yehova wapitiriza kudalitsa khama la Mboni zake m’dera limenelo ndi mu Italy monse. Tsopano m’dzikolo muli Mboni za Yehova zoposa 200,000.
Mfupo za kulimbikira pochita zinthu zabwino nzazikulu. Mwa mphamvu ya mzimu wa Mulungu, Mboni za Yehova zakhoza kuchita chinthu chosayerekezeredwa ndi china mu mbiri ya anthu, chija cha kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu, pamakomo a anthu ndi mu njira zina, kwa anthu ambirimbiri. (Zekariya 4:6) Izo zaona mwachisangalalo ulosi wa Baibulo ukukwaniritsidwa pa kukula ndi mphamvu ya gulu la Yehova la pa dziko lapansi. (Yesaya 54:2; 60:22) Zili ndi chikumbumtima chabwino kulinga kwa Mulungu, ndipo zimakondwa ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Kuposa zonsezo, zimasangalala ndi unansi wapafupi ndi Mlengi, Yehova Mulungu.—Salmo 11:7.
[Zithunzi patsamba 25]
Yesu anafupa mkazi uyu Wachigiriki pa kulimbikira kwake kodzichepetsa
[Chithunzi patsamba 26]
Chimwemwe choikidwa pamaso pa Akristu lerolino chimaphatikizapo moyo m’Paradaiso