Kanizani Miyambo Yachikunja!
“CHOONADI chidzakumasulani,” anatero Yesu Kristu. (Yohane 8:32) Inde, Chikristu chimamasula anthu—kuwamasula ku ukapolo wa miyambo, kuwamasula ku kukhulupirira ziphunzitso ndi ziyembekezo zonama, kuwamasula ku ukapolo wa machitachita onyansa.
Komabe, mofanana ndi nthaŵi zakale, Akristu lerolino amakakamizidwa kaŵirikaŵiri kuti abwerere ku miyambo yakale. (Agalatiya 4:9, 10) Sikuti miyambo yonse yofala ili yoipa. Ndithudi, Mkristu angasankhe kutsatira miyambo yakwawo imene ili yoyenera ndi yopindulitsa. Koma pamene miyambo isemphana ndi Mawu a Mulungu, Akristu samagonja. Nchifukwa chake Mboni za Yehova zikudziŵika ndi kusakondwerera kwawo Krisimasi, masiku a kubadwa, ndi miyambo ina imene imawombana ndi Mawu a Mulungu.
Kaimidwe kolimba mtima kameneka kaŵirikaŵiri kawachititsa kutonzedwa ndi kutsutsidwa ndi mabwenzi, anansi, ndi achibale awo osakhulupirira. Zimenezi zachitika makamaka m’maiko ena a m’Afirika, kumene ambiri amasunga miyambo yochuluka yosiyanasiyana pa maliro, maukwati, ndi pobadwa mwana. Zikakamizo zakuti agonje zingakhale zazikulu—kaŵirikaŵiri zikumaphatikizapo kuwopseza ndi chiwawa. Kodi Akristu kumeneko angachirimike motani? Kodi nkotheka kupeŵa mkangano popanda kugonja? Kuti tiyankhe, tiyeni tipende mmene Akristu okhulupirika achitira ndi miyambo ina yotsutsana ndi malemba.
Miyambo ya Maliro ya Kuwopa Akufa
Kummwera kwa Afirika kuli miyambo yamitundumitundu ya maliro ndi yoikira maliro. Nthaŵi zambiri olira amachezera usiku wonse—kapena masiku angapo—panyumba ya maliro, pamene pamayaka moto wosazima. Ofedwawo amawaletsa kuphika, kumeta tsitsi, kapena ngakhale kusamba kufikira ataika malirowo. Pambuyo pake, ayenera kusamba mankhwala apadera. Kodi miyambo yotero ili yovomerezeka kwa Akristu? Ayi. Yonseyo imasonyeza kukhulupirira kusafa kwa moyo ndi kuwopa akufa.
Mlaliki 9:5 amati: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.” Kudziŵa choonadi chimenechi kumatimasula ku kuwopa ‘mizimu ya akufa.’ Koma kodi Mkristu ayenera kuchitanji pamene achibale ake mosadziŵa kuipa kwake amupempha kuchita madzoma oterowo?
Talingalirani chomwe chinachitikira Mboni ina Yachiafirika yotchedwa Jane, amene atate wake anamwalira. Atafika panyumba ya maliro, anamuuza nthaŵi yomweyo kuti iye ndi ena onse abanjalo anayenera kuvina usiku wonse akumazungulira mtembo kutonthoza mzimu wa wakufayo. “Ndinawauza kuti pokhala Mboni ya Yehova, sindikanadziloŵetsa m’machitachita otero,” akutero Jane. “Komabe, mmaŵa mwake pambuyo pa kuika malirowo, akuluakulu apabanja anati adzasambitsa onse abanja lofedwalo kuwatetezeranso ku mzimu wa wakufayo. Ndinakananso kuchita zimenezo. Panthaŵi imodzimodzi, Mayi anali obindikira m’nyumba ina. Aliyense amene anafuna kuwaona anafunikira choyamba kumwa moŵa umene unaphikidwa chifukwa cha zimenezo.
“Ndinakana kuchitako zonse zimenezi. M’malo mwake ndinapita kunyumba kukakonza chakudya, chimene ndinaperekera Mayi kunyumba imene anali kukhala. Zimenezi zinakhumudwitsa kwambiri banja lathu. Achibale anaganiza kuti ndachita msala.” Ndiponso, anamnyodola ndi kumtemberera, akumati: “Popeza wakana mwambo wathu chifukwa cha chipembedzo chako, mzimu wa atate wako udzakuzunza. Ndipotu, mwina sudzaonanso ndi mwana wina.” Chikhalirechobe, Jane sanawope. Chotulukapo chake? Akuti: “Panthaŵiyo ndinali ndi ana aŵiri. Tsopano ndili nawo asanu ndi mmodzi! Zimenezi zanyazitsa aja amene anati sindidzaonanso ana.”
“Kuyeretsa” mwa Kugona Malo Amodzi
Mwambo wina ndi wa dzoma la kuyeretsa pambuyo pa imfa ya wa mu ukwati. Mkazi akamwalira, akubanja lake amabweretsa mlamu kwa wofedwayo kapena mkazi wina wachibale wa mkazi wake wakufayo. Iye ayenera kugona naye. Mpokhapo pamene angakwatire aliyense amene afuna. Ndi zimenenso zimachitika ngati mwamuna wamwalira. Mchitidwewo amati umachotsa “mzimu” wa wakufayo kwa wotsalayo.
Aliyense wokana “kuyeretsa” kumeneko amaputa mkwiyo wa achibale. Angapatulidwe ndi kunyodoledwa ndi kutembereredwa. Komabe, Akristu amakana kutsatira mwambo umenewu. Amadziŵa kuti pamaso pa Mulungu kugona ndi munthu wa kunja kwa ukwati nkodetsa, sindiko “kuyeretsa” ayi. (1 Akorinto 6:18-20) Ndiponso, Akristu amakwatira “[kokha, NW] mwa Ambuye.”—1 Akorinto 7:39.
Mkazi wina Wachikristu wa m’Zambia wotchedwa Violet anafedwa mwamuna wake. Pambuyo pake, achibale anambweretsera mwamuna wina, akumamuumiriza kugona naye. Violet anakana, ndipo anamlanga mwa kumletsa kutunga madzi pachitsime cha pamudzi. Anamuwopsezanso kusayenda mumsewu waukulu, kuti adzaona tsoka. Komabe, sanawope achibale ake kapena anzake apamudzipo.
Pambuyo pake Violet anaitanidwa kukhoti la kumaloko. Kumeneko anafotokoza molimba mtima zifukwa zake za Malemba zokanira kuchita chisembwere. Khotilo linapereka chigamulo chomuyanja, likumati silikanamkakamiza kusunga miyambo yawo imene inasemphana ndi zikhulupiriro zake. Zosangalatsa nzakuti, kukana kwake kugonja kwa mtu wagaluko kunachepetsa vutolo pa Mboni zina pamudzipo zimene pambuyo pake zinayang’anizana ndi nkhani imodzimodziyo.
Mboni ina Yachiafirika yotchedwa Monika inapirira vuto longa limenelo pambuyo pa imfa ya mwamuna wake. Banja la mwamunayo linaumirira kuti limpatse mwamuna wina. Monika akuti: “Ndinakana, ndili wotsimikiza mtima kutsatira lamulo la pa 1 Akorinto 7:39.” Komabe sanasiye kumkakamiza. “Anandiwopsa,” Monika akukumbukira. “Anati: ‘Ukakana, sudzakwatiwanso.’ Anafika ngakhale ponena kuti Akristu anzanga ena anayeretsedwa mwanjira imeneyi mseri malinga ndi mwambo.” Komabe, Monika anachirimika. “Ndinakhala mbeta zaka ziŵiri, pambuyo pake ndinakwatiwa m’njira Yachikristu,” akutero. Tsopano Monika ndi mpainiya wokhazikika.
Kupita Padera ndi Nthayo
Akristu akummwera kwa Afirika amalimbananso ndi miyambo yokhudza kupita padera ndi nthayo. Masoka amenewo amachitika chifukwa cha kupanda ungwiro kwa munthu—si chilango cha Mulungu ayi. (Aroma 3:23) Koma ngati mkazi wapita padera, miyambo ina ya mu Afirika imafuna kuti ayesedwe nthodwa kwa nyengo yakutiyakuti.
Mkazi wina amene anali atangopita padera anadabwa kwambiri kuona Mboni ina ikulinga kunyumba kwake. Pamene mwamunayo anafika pafupi, mkaziyo anafuula kuti: “Musafike kuno! Malinga ndi mwambo wathu, mkazi amene wangopita padera sayenera kuchezeredwa.” Komabe, Mboniyo inamuuza kuti Mboni za Yehova zimapereka uthenga wa Baibulo kwa anthu amtundu uliwonse ndi kuti sizimasunga miyambo yokhudza kupita padera. Ndiyeno anamuŵerengera Yesaya 65:20, 23, nafotokoza kuti mu Ufumu wa Mulungu simudzakhala kupita padera kapena nthayo. Chotero, mkaziyo anavomereza phunziro la Baibulo lapanyumba.
Miyambo ya kuwopa akufa ingachitikenso poika nthayo. Pamene Joseph, Mboni ina, anapezekapo poika maliro otero, anamuuza kuti onse opezekapo anayenera kusamba kumanja mankhwala ndi kudzola mankhwalawo pa chifuwa. Anati zimenezi zimaletsa “mzimu” wa khandalo kubwera ndi kuwavulaza. Joseph mwa ulemu anakana, podziŵa chiphunzitso cha Baibulo chakuti akufa sangavulaze amoyo. Komabe, ena anayesabe kumkakamiza kudzola mankhwala. Joseph anakananso. Poona kaimidwe kolimba ka Mkristu ameneyu, ena omwe analipo anakananso mankhwalawo.
Peŵani Mikangano, Koma Chirimikani
Kuwopa amoyo ndi kuwopa kuyesedwa nthodwa kungasonkhezere kwambiri kugonja. Miyambo 29:25 imati: “Kuwopa anthu kutchera msampha.” Zochitika zotchulidwazo zimasonyeza choonadi cha mbali yomalizira ya vesi limenelo: “Koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.”
Komabe, mkangano kaŵirikaŵiri ungapeŵedwe. Mwachitsanzo, ngati Mkristu wapita kumaliro a wachibale, sayenera kuyembekezera kufikira mkhalidwe utafika poti akhoza kugonja. “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.”—Miyambo 27:12.
Kungakhale kwanzeru kufunsa mochenjera za miyambo imene adzachita. Ngati ili yosayenera, Mkristu angagwiritsire ntchito mwaŵi umenewo kufotokoza chimene sangachitire zimenezo, akumatero “ndi chifatso ndi [ulemu waukulu, NW].” (1 Petro 3:15) Pamene Mkristu mwa ulemu afotokoza kaimidwe kake kozikidwa pa Baibulo pasadakhale, nthaŵi zambiri achibale ake amafuna kulemekeza zikhulupiriro zake ndipo samafuna kumuwopsa.
Kaya achibale anene zotani, Mkristu sayenera kugonja mwa kutsatira miyambo yosalemekeza Mulungu—ngakhale ngati angamuwopse ndi kumtukwana motani. Tinamasuka ku kuwopa akufa. Mtumwi Paulo analangiza kuti: “Kristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chirimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.”—Agalatiya 5:1.
[Chithunzi patsamba 29]
Ambiri amakhulupirira kuti munthu amene wangomwalira kumene angakhale nkhoswe namapereka mauthenga kwa achibale amene anafa kalekale